Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

Anthu ena amaona kuti kupemphera n’kungotaya nthawi chifukwa palibe aliyense amene amamvetsera. Pomwe ena amayesetsa kupemphera, koma amaona kuti sayankhidwa. Munthu wina amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu, nthawi ina anangoyerekezera kuti Mulungu aliko, n’kupemphera. Iye ananena kuti: “Ndinapemphera kuti, ‘ngati mulikodi mungondinong’oneza.’ Koma nditapemphera, sindinamve kalikonse ndipo kunali zii.”

Komabe Baibulo limanena kuti kuli Mulungu, yemwe amamvetsera tikamapemphera. Limati: “Iye [Mulungu] adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.” (Yesaya 30:19) Ndipo vesi linanso limati: “Pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa.”—Miyambo 15:8.

Yesu atapemphera, Mulungu “anamumvera.”—Aheberi 5:7

Baibulo limanenanso za anthu ena omwe Mulungu anayankha mapemphero awo. Vesi lina limanena kuti Yesu anapereka “mapemphero opembedzera . . . kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa,” ndipo Mulungu “anamumvera.” (Aheberi 5:7) Zitsanzo zina za anthu omwe mapemphero awo anayankhidwa, zikupezeka pa Danieli 9:21 ndi pa 2 Mbiri 7:1.

Komano n’chifukwa chiyani anthu ena amaona kuti mapemphero awo sayankhidwa? Kuti mapemphero athu ayankhidwe, tiyenera kupemphera kwa Yehova * Mulungu yekha, osati kwa milungu ina kapena kwa mizimu ya makolo. Ndipo Mulungu amayankha ngati “tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake.” Tikamachita zimenezi, Mulunguyo “amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Choncho ngati timafuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kumudziwa bwino komanso kudziwa zimene amafuna.

Anthu ambiri amaona kuti kupemphera si mwambo chabe wa chipembedzo koma amakhulupirira kuti Mulungu amamvetsera komanso kuyankha mapemphero awo. Mwachitsanzo, a Isaac a ku Kenya, ananena kuti: “Ndinkapemphera kuti Mulungu andithandize kumvetsa Baibulo. Ndipo pasanapite nthawi, kunatulukira munthu wina yemwe anandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo.” Komanso a Hilda, omwe amakhala ku Philippines, ankafunitsitsa kuti asiye kusuta fodya. Atalephera kusiya khalidweli, mwamuna wawo ananena kuti: “Bwanji osangopemphera kwa Mulungu.” A Hilda anachitadi zimenezo ndipo kenako anati: “Ndinadabwa kwambiri ndi mmene Mulungu anandithandizira. Pang’onopang’ono chibaba chinayamba kuchepa ndipo patapita nthawi ndinasiyadi kusuta.”

Choncho Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani ngati mapemphero anu atakhala ogwirizana ndi chifuniro chake.