Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera?

Bambo wina wa ku Kenya, dzina lake Samuel, * anati: “Ndinkakonda kutchova juga kwambiri. Tisanayambe kusewera, ndinkapemphera kaye kwa Mulungu kuti ndiwine, koma ayi ndithu, anthu ankangondidyera ndalama zanga.”

Mayi wina wa ku Philippines, dzina lake Teresa, anati: “Tili kusukulu, aphunzitsi ankatiuza kuti tiloweze mapemphero ndipo nthawi zonse tinkangobwereza mapemphero omweomwewo.”

Mayi wina wa ku Ghana, dzina lake Magdalene, anati: “Ndimapemphera ndikakumana ndi mavuto. Ndimapempha Mulungu kuti andikhululukire machimo anga komanso kuti ndikhale Mkhristu wabwino.”

Zimene anthuwa ananena zikusonyeza kuti anthu amapemphera pa zifukwa zosiyanasiyana. Mwachitsanzo enanso amapemphera kuti akhoze mayeso, kuti timu yawo iwine komanso kuti Mulungu adalitse banja lawo. Anthu ena amapemphera pongofuna kuti apeze zinazake, pomwe ena amapemphera pa zifukwa zomveka ndithu. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri amaona kuti kupemphera n’kofunika. Kafukufuku wina anasonyeza kuti ngakhale anthu ena amene sachita chidwi ndi zachipembedzo, nawonso amapemphera nthawi zambiri.

Kodi nanunso mumapemphera? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani mumapemphera? Kaya mumakonda kupemphera kapena ayi, mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi kupemphera n’kothandizadi? Kodi pali aliyense amene amamvetsera ndikamapemphera?’ Wolemba mabuku wina ananena kuti kupemphera, “kuli ngati mankhwala ongokuthandiza kuti maganizo akhale m’malo. Zimenezi n’zofanana ndi munthu amene akuuza chiweto chake mavuto amene akukumana nawo kuti amveko bwino.” Komanso madokotala ena amanena zofanana ndi zimenezi. Amanena kuti kupemphera kuli ngati njira ina yothandiza kuti munthu apeze bwino. Ndiye kodi tinganene kuti anthu amene amapemphera amangotaya nthawi yawo? Kapena zimene amachita akamapemphera n’zimene zimawathandiza kuti apezeko bwino?

Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganizazi, Baibulo limanena kuti kupemphera n’kothandiza kwambiri. Limati pali winawake amene amamvetsera tikamapemphera ndi zolinga zabwino komanso mogwirizana ndi zimene amafuna. Zimenezitu si nkhambakamwa chabe. Tiyeni tione umboni wake.

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhaniyi.