NSANJA YA OLONDA October 2015 | Kodi Kupemphera N’kothandizadi?

Wolemba mabuku wina ananena kuti kupemphera kuli ngati kuuza chiweto chako mavuto amene ukukumana nawo n’cholinga choti umveko bwino. Kodi zimenezi n’zoona?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera?

Anthu amapemphera pa zifukwa zosiyanasiyana.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Pali Aliyense Amene Amamvetsera Tikamapemphera?

Pali zinthu ziwiri zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu amve mapemphero athu.

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?

Kupemphera kumatithandiza kwambiri kuposa china chilichonse

NKHANI YAPACHIKUTO

Kupemphera N’kothandiza Kwambiri

Kodi mungapeze phindu lanji ngati mutamapemphera nthawi zonse?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Herode anagwira ntchito yaikulu bwanji pokonza kachisi wa ku Yerusalemu? N’chifukwa chiyani anthu a pachilumba cha Melita ankaganiza kuti Paulo ndi chigawenga?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Panopa Ndimaona Kuti Ndingathe Kuthandiza Ena

Julio Corio anachita ngozi ndipo ankaona kuti Mulungu samuganizira. Lemba la Ekisodo 3:7 linamuthandiza kuti asinthe maganizo.

Kodi Mulungu Ndi Wosamvetsetseka?

Zinthu zina zimene n’zovuta kumvetsa ponena za Mulungu zimatithandiza kuti timuyandikire.

MFUNDO ZAKALE KOMA ZOTHANDIZA MASIKU ANO

Muzikhululuka Ndi Mtima Wonse

Kodi kukhululukira ena kumatanthauza kuti tikuchepetsa kapena kunyalanyaza zoipa zimene ena atichitira?

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kodi ndani angathetsedi umphawi?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mwambo wa Halowini Unayamba Bwanji?

Kodi kudziwa kuti Halowini inayambira kuchikunja kuli ndi vuto lililonse?