Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera?

Mulungu amafuna kuti tikhale anzake.

Anthu omwe ndi mabwenzi amagwirizana kwambiri ngati amalankhulana. Nayenso Mulungu amafuna kuti tizilankhula naye m’pemphero kuti tikhale anzake apamtima. Ndipo amanena kuti: “Mudzaitanira pa ine komanso mudzabwera ndi kupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.” (Yeremiya 29:12) Mukamapeza nthawi yolankhula ndi Mulungu, ‘mudzamuyandikira ndipo iyenso adzakuyandikirani.’ (Yakobo 4:8) Ndipotu Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” (Salimo 145:18) Nthawi zonse tikamayesetsa kulankhulana ndi Mulungu, m’pamenenso timakhala anzake apamtima.

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”—Salimo 145:18

Mulungu amafunitsitsa kutithandiza.

Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? Chotero ngati inuyo, . . . mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!” (Mateyu 7:9-11) Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye chifukwa “amakuderani nkhawa” ndipo amafuna kukuthandizani. (1 Petulo 5:7) Amafuna kuti muzimufotokozera mavuto anu. Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6.

Tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu.

Akatswiri ena ananena kuti anthu ambiri padzikoli amaona kuti kupemphera n’kofunika. Anati ngakhale anthu omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso amene amakayikira zoti kuli Mulungu, nawonso amapemphera. * Zimenezi zimasonyeza kuti anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kulambira Mulungu. Ndipotu Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Choncho kupemphera ndi njira ina imene timalambirira Mulungu.

Ndiye kodi tingapeze phindu lanji tikamapemphera kwa Yehova?

^ ndime 8 M’chaka cha 2012, bungwe lina linachita kafukufuku ku United States. Bungweli linapeza kuti anthu 11 pa anthu 100 alionse omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu kapena omwe amakayikira zoti kuli Mulungu, amapemphera kamodzi pa mwezi.