Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndi Wosamvetsetseka?

Kodi Mulungu Ndi Wosamvetsetseka?

Wafilosofi wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Philo anati: “Mulungu ndi wosamvetsetseka.”

Saulo wa ku Tariso, anauza afilosofi a ku Atene kuti: “[Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.”

PA ZIMENE anthu awiriwa ananena, ndi ziti zimene inuyo mukugwirizana nazo? Ambiri amaona kuti mawu amene Saulo wa ku Tariso ananena ndi omveka. (Machitidwe 17:26, 27) Ndipo m’Baibulo mulinso mavesi ena osonyeza kuti n’zotheka kudziwa bwino Mulungu. Mwachitsanzo zimene Yesu ananena m’pemphero lake lina, zimasonyeza kuti n’zotheka kumudziwa Mulungu komanso kudzalandira madalitso amene analonjeza.—Yohane 17:3.

Komabe Philo limodzi ndi afilosofi ena sankagwirizana ndi zimenezi. Ankanena kuti Mulungu ndi wosamvetsetseka ndipo n’zosatheka kuti anthu amudziwe bwino. Ndiye kodi zoona zenizeni ndi ziti?

Baibulo limasonyeza kuti pali zinthu zina zokhudza Mulungu zomwe anthufe sitingathedi kuzimvetsa. Mwachitsanzo, n’zovuta kumvetsa kuti Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto, ndiponso n’zovuta kudziwa kuchuluka kwa nzeru zake. Komabe sikuti zimenezi zingatilepheretse kudziwa bwino Mulungu. Ndipotu kuganizira zinthu zimenezi kungatithandize kuti ‘timuyandikire.’ (Yakobo 4:8) Tiyeni tione zitsanzo zingapo za zinthu zovuta kumvetsa zokhudza Mulungu. Kenako tionanso zinthu zomwe tingathe kuzimvetsa.

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Sitingathe Kuzimvetsa?

MULUNGU ALIBE CHIYAMBI KOMANSO MAPETO: Baibulo limanena kuti Mulungu wakhala alipo “kuyambira kalekale” ndipo adzakhalapo “mpaka kalekale.” (Salimo 90:2) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto. Anthufe sitingathe kumvetsa zimenezi chifukwa “zaka zake n’zosawerengeka.”—Yobu 36:26.

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Mulungu amatilonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha ngati titamudziwa n’kumachita zimene amafuna. (Yohane 17:3) Kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu alonjeze anthu moyo wosatha zikanakhala kuti Mulunguyo sadzakhalapo mpaka kalekale? Ndi “Mfumu yamuyaya” yokha yomwe ingalonjeze zimenezi.—1 Timoteyo 1:17.

NZERU ZA MULUNGU: Baibulo limanena kuti ‘palibe amene angamvetse zimene iyeyo amamvetsa’ chifukwa nzeru zake ndi zapamwamba kuposa za anthufe. (Yesaya 40:28; 55:9) N’chifukwa chake limanenanso kuti: “Ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti amulangize?”—1 Akorinto 2:16.

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Mulungu amatha kumva mapemphero a anthu ambirimbiri nthawi imodzi. (Salimo 65:2) Amathanso kudziwa ngati mpheta imodzi yagwa pansi. Ndiye n’zosatheka kuti Mulungu achulukidwe mpaka kulephera kumva mapemphero athu. Ndipotu Baibulo limati: “Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”—Mateyu 10:29, 31.

ZOCHITA ZA MULUNGU: Baibulo limaphunzitsa kuti ‘ntchito imene Mulungu woona wagwira, anthu sangaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.’ (Mlaliki 3:11) Choncho sitingathe kudziwa zonse zokhudza Mulungu chifukwa nzeru zake “ndi zosasanthulika.” (Aroma 11:33) Komabe Yehova amathandiza anthu a mtima wabwino kuti amudziwe.—Amosi 3:7.

Tikamawerenga komanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse, timadziwa zinthu zatsopano zokhudza Mulungu

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Tikamawerenga komanso kuphunzira Baibulo nthawi zonse, timadziwa zinthu zatsopano zokhudza Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti tidzapitirizabe kuphunzira za Atate wathu wakumwamba mpaka kalekale.

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Tingathe Kuzimvetsa?

N’zoona kuti pali zinthu zina zokhudza Mulungu zimene sitingazimvetse. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti sitingathe kumudziwa. M’Baibulo muli mavesi osiyanasiyana omwe angatithandize kumudziwa bwino Mulungu. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

DZINA LA MULUNGU: Baibulo limanena kuti Mulungu ali ndi dzina. Mulungu anadzipatsa yekha dzina limeneli ndipo anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” Dzinali limapezeka m’Baibulo kuposa ka 7,000 ndipo palibenso dzina lina lomwe limapezeka kambirimbiri chonchi m’Baibulo.—Yesaya 42:8.

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? M’pemphero lachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Choncho ifenso tikamapemphera, tizitchula dzina la Mulungu chifukwa adzatipulumutsa tikamalemekeza dzina lake.—Aroma 10:13.

KUMENE MULUNGU AMAKHALA: Baibulo limanena kuti Yehova analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kumwamba kuli angelo omwe ali ndi thupi losaoneka, pomwe padziko lapansi ndi pamene pamakhala anthufe. (Yohane 8:23; 1 Akorinto 15:44) Nthawi zambiri Baibulo likamanena za “kumwamba,” limatanthauza malo amene kumakhala angelo. Ndipo ‘kumwambako’ n’kumenenso Mulungu ‘amakhala.’—1 Mafumu 8:43.

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Zimenezi zimatithandiza kuti timudziwe bwino Mulungu. Si zoona kuti Mulungu ndi mphamvu chabe imene imakhala paliponse. Koma Mulungu ndi weniweni ndipo ali ndi malo amene amakhala. Ngakhale kuti ali kumwamba, Baibulo limati: “Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.”—Aheberi 4:13.

MAKHALIDWE A MULUNGU: Baibulo limanena kuti Mulungu ali ndi makhalidwe abwino kwambiri. Mwachitsanzo limati, “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Komanso Mulungu sanama. (Tito 1:2) Limanenanso kuti iye alibe tsankho, ndi wachifundo, wachisomo ndiponso wosakwiya msanga. (Ekisodo 34:6; Machitidwe 10:34) Ngakhale kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, amafuna kuti anthu amene amamulemekeza akhale naye pa “ubwenzi wolimba.”—Salimo 25:14.

Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Mutha kukhala mnzake wa Yehova. (Yakobo 2:23) Mukakhala mnzake, mumadziwa bwino makhalidwe ake ndipo mumathanso kumvetsa bwino nkhani za m’Baibulo.

‘FUNAFUNANI MULUNGU’

Baibulo limatithandiza kudziwa bwino Yehova Mulungu. Iye amafuna kuti timudziwe ndipo si zoona kuti ndi wosamvetsetseka. Mawu ake amanena kuti: ‘Mukam’funafuna, adzalola kuti mum’peze.’ (1 Mbiri 28:9) Choncho mukamawerenga ndi kuganizira nkhani za m’Baibulo, mudzamudziwa bwino Mulungu. Ndipo Baibulo limanena kuti mukamachita zimenezi, iye “adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

N’zovuta kumvetsa kuti Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto ndiponso n’zovuta kudziwa kuchuluka kwa nzeru zake

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi n’zotheka kukhala mnzake wa Mulungu ngakhale pali zinthu zina zimene sindizimvetsa bwino?’ Tiyerekeze kuti mnzanu wina ndi dokotala. Kodi kuti akhale mnzanu, zinachita kufuna kuti inunso muzidziwa zonse zimene madokotala amachita? Ayi. Tikutero chifukwa si nthawi zonse pamene mnzathu amakhala munthu amene ali ndi luso kapena amene amagwira ntchito yofanana ndi yathu. Choncho ngakhale titasiyana pa zinthu zina, atha kukhalabe mnzathu chifukwa timadziwa makhalidwe ake komanso zinthu zimene amakonda. Ndi mmenenso zimakhalira ngati tikufuna kukhala mnzake wa Mulungu. Tikamaphunzira Baibulo timadziwa makhalidwe ake, ndipo izi zimatithandiza kuti tikhale mnzake.

Choncho Baibulo lingatithandize kuti tikhale anzake a Mulungu chifukwa limatiuza zinthu zomwe zingatithandize kumudziwa bwino. Kodi mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Yehova Mulungu? A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Ngati inunso mungafune kuphunzira Baibulo, funsani wa Mboni za Yehova wakufupi ndi kwanuko kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.