Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

Yehova “Alibe Tsankho”

Yehova “Alibe Tsankho”

Kodi anthu ena anakuchitiranipo zinthu zimene munaona kuti ndi tsankho? Kodi munakanizidwapo zinthu zina chifukwa cha mtundu wanu kapena chifukwa chakuti ndinu wosauka? Ngati zimenezi zinakuchitikirani musaganize kuti ndi inu nokha chifukwa pali anthu ambiri amene amasalidwa. Komabe dziwani kuti Mulungu alibe tsankho. Mtumwi Petulo analemba motsimikiza kuti: “Mulungu alibe tsankho.”—Werengani Machitidwe 10:34, 35.

Petulo ananena mawu amenewa ali kunyumba ya Koneliyo yemwe sanali Myuda. Zinali zodabwitsa kuti Petulo ananena mawu amenewa chifukwa iye anali Myuda ndipo pa nthawiyi, Ayuda ankaona kuti anthu a mitundu ina anali odetsedwa komanso osafunika kucheza nawo. Komano n’chifukwa chiyani Petulo anapita ku nyumba ya Koneliyo? Yankho lachidule ndi lakuti Yehova Mulungu ndi amene anachititsa zimenezi. Mulungu anaonetsa Petulo masomphenya ndipo anamuuza kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.” Petulo sanadziwe kuti iye asanaone masomphenya amenewa, Koneliyo anali atauzidwa kale ndi mngelo kuti aitane Petulo. (Machitidwe 10:1-15) Petulo sanakane kupita chifukwa anadziwa kuti ndi zimene Yehova wafuna.

N’chifukwa chake Petulo anati: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho.” (Machitidwe 10:34) Mawu Achigiriki amene anawamasulira kuti “tsankho” amatanthauza “kuyang’ana nkhope.” (The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures) Katswiri wina wa nkhani za m’Baibulo ananena kuti: “Mawu amenewa amanena za woweruza yemwe amayang’ana nkhope poweruza milandu.” Koma Mulungu poweruza sayang’ana nkhope, mtundu, dziko limene munthu akuchokera kapena kuti ndi wolemera kapena wosauka.

M’malo mwake Yehova amaona zimene zili mu mtima mwa munthu. (1 Samueli 16:7; Miyambo 21:2) Kenako Petulo ananena kuti: “[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:35) Kuopa Mulungu kumatanthauza kumulemekeza, kumukhulupirira komanso kupewa kuchita zinthu zimene zingamukhumudwitse. Kuchita chilungamo kumatanthauza kuchita zimene Mulungu amafuna ndi mtima wonse. Yehova amasangalala ndi munthu amene amamuopa komanso amene amafunitsitsa kuchita chifuniro chake.—Deuteronomo 10:12, 13.

Yehova akamayang’ana padziko lapansi amaona kuti anthu onse ndi a mtundu umodzi basi, womwe ndi mtundu wa ana a anthu

Ngati ena anakuchitiranipo zinthu mwatsankho, mawu a Petulo onena mmene Mulungu amaonera tsankho angakulimbikitseni ndipotu Yehova akufuna kuti anthu a mitundu yonse azimulambira. (Yohane 6:44; Machitidwe 17:26, 27) Iye amamva komanso kuyankha mapemphero a atumiki ake mosayang’ana mtundu umene akuchokera, kaya ndi olemera kapena osauka. (1 Mafumu 8:41-43) Sitikukayikira kuti Yehova akamayang’ana padziko lapansi amaona kuti anthu onse ndi a mtundu umodzi basi, womwe ndi mtundu wa ana a anthu. Kodi simungakonde kudziwa zambiri za Mulungu wopanda tsankho ameneyu?

Mavesi amene mungawerenge mu June

Yohane 17-21Machitidwe 1-10