Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chuma chomwe chinabisika kwa zaka zambiri

Chuma chomwe chinabisika kwa zaka zambiri

Katswiri wina wofufuza zinthu zakale anachita chidwi kwambiri ndi zimene anapeza. Iye anawerenga mobwerezabwereza zilembo zakale zimene zinali pampukutu umene anapeza. Zilembozo zinkasonyeza kuti mpukutuwo unali chidutswa cha Baibulo lakale kwambiri lomwe linamasuliridwa m’Chijojiya.

KATSWIRIYU, yemwe dzina lake ndi Ivané Javakhishvili, anapeza mpukutuwo mu December, 1922. Pa nthawi imeneyi n’kuti akufufuza mmene zilembo za Chijojiya zinapangidwira ndipo anapeza buku la ku Yerusalemu lotchedwa Talmud, lomwe linalembedwa m’Chiheberi. Atayang’anitsitsa anapeza kuti pansi pa zilembo za Chiheberizo panali zilembo za Chijojiya zomwe zinkaoneka kuti zinafufutidwa. *

Mawu ofufutikawo, omwe analembedwa m’zaka za m’ma 400 C.E., anali kachigawo ka buku la m’Baibulo la Yeremiya. Mpukutu umenewu usanapezeke, Baibulo la Chijojiya lomwe anthu ankaona kuti ndi lakale kwambiri linali la m’zaka za m’ma 800 C.E. Pasanapite nthawi, akatswiri anatulukira tizigawo tina ta m’mabuku a m’Baibulo tomwe tinalembedwa mu 400 C.E. kapena zaka zimenezi zisanafike. Zinali zosangalatsa kupeza mipukutu ya Baibulo yakale kwambiri yomwe inalembedwa patangodutsa zaka mahandiredi ochepa kuchokera m’nthawi ya Yesu ndi atumwi.

Kodi ndani anamasulira mpukutuwu m’Chijojiya? Kodi anali munthu mmodzi kapena kanali kagulu? Pakali pano palibe amene amadziwa. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti Baibulo kapena mbali zina za Baibulo zinali zitamasuliridwa m’Chijojiya pofika m’zaka za m’ma 300 C.E. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu a ku Georgia akhala akuwerenga Mawu a Mulungu m’chinenero chawo kuchokera nthawi imeneyi.

Buku lina, lomwe liyenera kuti linalembedwa m’zaka za m’ma 400 C.E., limasonyeza mmene anthu a ku Georgia ankadziwira Malemba. (The Martyrdom of St. Shushanik the Queen) Bukuli limafotokoza zimene zinachitikira mfumukazi Shushanik ndipo pofotokoza zimene zinachitikazo, anagwiritsa ntchito mawu ena opezeka m’buku la Masalimo, m’mabuku a Uthenga Wabwino komanso m’mabuku ena a m’Baibulo. Bukuli limanenanso kuti pofuna kusangalatsa nduna za ku Perisiya, mwamuna wake wa mfumukazi Shushanik, dzina lake Varsken, yemwe anali bwanamkubwa wa chigawo cha Kartli, anasiya “Chikhristu” n’kulowa chipembedzo cha ku Perisiya. Kenako anakakamiza mkazi wakeyo kuti achitenso chimodzimodzi. Koma bukuli limanena kuti mkaziyo anakana  kusiya Chikhristu ndipo analamulidwa kuti aphedwe. Limanenanso kuti mkaziyu ankalimbikitsidwa kwambiri ndi malemba a m’Baibulo pa nthawi imene ankayembekezera kuphedwa.

Zikuoneka kuti kuyambira m’ma 400 C.E., ntchito yomasulira ndi kukopera Baibulo la Chijojiya inapitirirabe. Umboni wa zimenezi ndi kuchuluka kwa mipukutu ya Baibulo imene inamasuliridwa m’Chijojiya. Tsopano tiyeni tikambirane mmene ntchito yomasulira komanso kusindikiza Mabaibulo inayendera.

ANTHU AMBIRI ANAYAMBA KUMASULIRA BAIBULO

Munthu wina, dzina lake Giorgi Mtatsmindeli, yemwe anali wansembe wa m’zaka za m’ma 1000 C.E., analemba kuti: “Ine Giorgi, wansembe wodzichepetsa, ndamasulira buku la Masalimo m’Chijojiya kuchokera ku Chigiriki ndipo ndagwira ntchito imeneyi modzipereka ndiponso mwakhama kwambiri.” Komano n’chifukwa chiyani panafunika kumasulira Baibulo m’Chijojiya ngakhale kuti linali litamasulilidwa kale m’chinenerochi?

Pofika m’ma 1000 C.E., panali patatsala mipukutu yochepa ya Baibulo la Chijojiya ndipo mabuku ena a m’Baibulo anali asakupezekanso. Komanso zinali zovuta kuti anthu amvetse Mabaibulo akale a m’Chijojiya chifukwa chinenerochi chinali chitasintha. Ngakhale kuti panali anthu ambiri omwe anagwira ntchito yomasulira Baibulo m’Chijojiya chosavuta kumva, Giorgi ndi amene anali wodziwika kwambiri. Pomasulira iye ankayerekezera Mabaibulo a m’Chijojiya omwe analipo pa nthawiyo ndi mipukutu ya m’Chigiriki. Akatero ankamasulira zigawo kapena buku lonse la m’Baibulo lomwe silinkapezeka. Masana iye ankagwira ntchito yake yaunsembe ndipo madzulo ankamasulira Baibulo.

Katswiri wina womasulira mabuku, dzina lake Ephrem Mtsire, anapitiriza ntchito ya Giorgi ndiponso analemba buku la malangizo othandiza pomasulira. Bukuli linafotokoza kuti omasulira ayenera kumasulira pogwiritsa ntchito chinenero chimene anagwiritsa ntchito polemba buku limene akufuna kumasuliralo. Linafotokozanso kuti pochita zimenezi omasulira azionetsetsa kuti zimene akumasulirazo n’zosavuta kumva. Ephrem Mtsire ndi amene anayambitsa zoika mawu a m’munsi komanso mawu ofotokozera m’Mabaibulo a Chijojiya. Iye anamasuliranso kachiwiri mabuku ena a m’Baibulo. Akatswiri ena omasulira anayamba kutengera njira zimene Giorgi ndi Ephrem ankagwiritsa ntchito pomasulira.

Kenako anthu ambiri a ku Georgia anayamba kumasulira komanso kusindikiza mabuku. Masukulu ophunzitsa kumasulira anatsegulidwa m’matauni a Gelati ndi Ikalto. N’chifukwa chake akatswiri ambiri amakhulupirira kuti Baibulo lotchedwa Gelati linamasuliridwa ndi katswiri wa ku Gelati kapena wa ku Ikalto. Baibuloli limapezeka kumalo osungira mipukutu yakale ku Georgia.

Kodi ntchito yomasulira Baibulo inakhudza bwanji anthu a ku Georgia? Wolemba ndakatulo wa m’zaka za m’ma 1100 C.E., dzina lake Shota Rustaveli, analemba buku lotchedwa Vepkhis-tqaosani. Anthu ambiri ankalikonda kwambiri bukuli moti anthu anafika pomaliona  ngati Baibulo lachiwiri la ku Georgia. Wolemba mabuku wina, dzina lake K. Kekelidze, ananena kuti, “Zinthu zina zimene analemba zimasonyeza kuti anazitenga m’Baibulo.” Ngakhale kuti m’ndakatulomo analemba zinthu mokokomeza kwambiri, ananenamo za mmene anthu angakhalire bwino ndi anzawo, kukhala wopatsa, kulemekeza azimayi komanso kukonda anthu ena. Mfundo zimenezi komanso mfundo zina za m’Baibulo zinathandiza kwambiri anthu a ku Georgia ndipo akhala akutsatira mfundo zimenezi mpaka pano.

BANJA LACHIFUMU LINALIMBIKITSA NTCHITO YOSINDIKIZA BAIBULO

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1600 C.E., banja lachifumu la ku Georgia linakonza zoti Baibulo lisindikizidwe. Kuti zimenezi zitheke, Mfumu Vakhtang wanambala 6, anamanga nyumba yosindikizira mabuku mumzinda wa Tbilisi, womwe unali likulu la Georgia. Koma pa nthawi imeneyi mabuku ena a m’Baibulo anali asanamasuliridwebe. Zinali ngati kuti Baibulo la m’Chijojiya labisikanso. Mipukutu imene inalipo inali yoti sinamalizidwe kumasuliridwa komanso Chijojiya chake chinali chakale. Ntchito yomasuliranso mabuku ena a m’Baibulowo inaperekedwa kwa Sulkhan-Saba Orbeliani, yemwe anali katswiri wa zilankhulo.

Orbeliani anayesetsa kugwira ntchito yake mosamala kwambiri. Chifukwa chakuti ankadziwa zilankhulo zambiri, kuphatikizapo Chigiriki ndi Chilatini, iye ankatha kufufuza m’mabuku komanso kwa anthu a zinenero zina kuonjezera pa mipukutu yakale yomwe inalembedwa m’Chijojiya. Koma zimenezi sizinasangalatse akuluakulu a chipembedzo cha Orthodox. Iwo anamuimba mlandu wophwanya malamulo achipembedzo ndipo anauza mfumu kuti iletse Orbeliani kumasulira Baibulo. Anthu ena amati pamsonkhano umene akuluakulu a chipembedzochi anachititsa, anakakamiza Orbeliani kuotcha Baibulo limene anali atalimasulira kwa zaka zambiri.

Koma chosangalatsa n’chakuti mpukutu wina wa Mtskheta (Mcxeta), womwe umadziwikanso kuti Saba’s Bible, ulipo mpaka pano ndipo muli zinthu zina zimene Orbeliani analemba pamanja. Ena amaganiza kuti Baibuloli ndi limene akuluakulu a chipembedzo cha Orthodox anamuuza kuti aotche lija. Koma pali umboni wosonyeza kuti Orbeliani ndi amene analemba mawu ofotokozera a m’Baibuloli.

Ngakhale kuti panali mavuto osiyanasiyana, anthu ena a m’banja lachifumu anakonzabe zoti Baibulo la m’Chijojiya lisindikizidwe. Pakati pa 1705 ndi 1711, mabuku ena a m’Baibulo anasindikizidwa. Ndipo Bakari ndi Vakhushti, omwe anali a m’banja lachifumu, anathandiza pa ntchito yosindikiza Baibulo moti Baibulo lonse linasindikizidwa mu 1743. Kuyambira nthawi imeneyi Baibulo la m’Chijojiya silinabisikenso.

^ ndime 3 Kale mapepala ankasowa komanso anali okwera mtengo. Choncho anthu ankakonda kufufuta zimene analemba kale n’cholinga choti alembepo zina. Mapepala oterowo ankawatchula kuti palimpsests, kuchokera ku mawu a m’Chigiriki otanthauza kuti “zofufutidwa.”