Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsankho Lidzatha Liti?

Kodi Tsankho Lidzatha Liti?

ZAKA 50 zapitazo, pa August 28, 1963, munthu wina wa ku America womenyera ufulu wa anthu, dzina lake Martin Luther King, Jr, ananena kuti: “Ndili ndi masomphenya.” Mawu amenewa ndi otchuka kwambiri padziko lonse. Martin Luther King ananena mawu amenewa pofotokoza masomphenya kapena chiyembekezo chimene anali nacho kuti tsiku lina anthu onse adzakhala m’dziko lopanda tsankho. Ngakhale kuti iye ankalankhula mawu amenewa kwa anthu ochepa a ku United States, koma anthu m’mayiko osiyanasiyana amalakalaka ataona zimene Martin Luther ananena zikuchitika padziko lonse.

Martin Luther King, Jr, akulankhula zokhudza ufulu wa anthu

Patatha miyezi itatu, Martin Luther atanena mawu amenewa, pa November 20, 1963, mayiko oposa 100, anasaina pangano lothetsa tsankho komanso kusalana padziko lonse. (United Nations Declaration on the Elimination of All Forms of Racial Discrimination) Kuyambira nthawi imeneyo, mayiko osiyanasiyana akhala akusainirana mapangano osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Komabe, funso n’lakuti kodi mapangano amenewa athandiza kuthetsa tsankho?

Pa March 21, 2012, a Ban Ki-moon, omwe ndi mkulu wa bungwe la United Nations, ananena kuti: “Tili ndi zinthu zambiri zimene zingatithandize kupewa ndiponso kuthetsa tsankho, kusalana, kuchitira nkhanza anthu a kumayiko ena komanso mavuto ena okhudza tsankho. Komabe, anthu mamiliyoni ambiri akupitirizabe kuvutika chifukwa cha tsankho.”

N’zoona kuti mayiko ena ayesetsa kulimbana ndi khalidwe la tsankho komanso kusalana, koma funso ndi lakuti: Kodi mayikowa athetsadi tsankho m’mitima ya anthu kapena angouza anthu kuti asamachite tsankho? Ena amanena kuti zimene mayikowa achita zangothandiza anthu kupewa kusalana koma sizinathetseretu tsankho. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa choti sizivuta kudziwa kapena kulanga munthu amene akusala anthu ena pomwe tsankho ndi lovuta chifukwa limayambira mumtima.

Choncho, kuthetsa tsankho si nkhani yongothetsa kusalana koma tifunika kusintha maganizo olakwika, odana ndi anthu amtundu wina kapena gulu linalake. Koma kodi zimenezi n’zotheka? Kodi zingatheke bwanji? Tiyeni tione zitsanzo za anthu omwe anakwanitsa kuthana ndi khalidwe la tsankho. Zitsanzozi zitithandiza kuona kuti n’zotheka kuthana ndi tsankho komanso zitithandiza kudziwa chimene chinawathandiza.

BAIBULO LINAWATHANDIZA KUTHETSA TSANKHO

“Panopa ndimaona kuti ndinamasuka ku ukapolo wa tsankho.”—Linda

Linda: Ndinabadwira ku South Africa. Poyamba ndinkaona kuti munthu aliyense yemwe si mzungu ndi wotsika, wosaphunzira, wosadalirika ndipo ndinkangomuona kuti ndi wantchito wa azungu basi. Ndinali watsankho loopsa ndipo sindinkaona kuti ndi zolakwika. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndinayamba kusintha maganizo amenewo. Ndinaphunzira kuti, “Mulungu alibe tsankho” komanso kuti chofunika kwambiri ndi zimene zili mumtima mwa munthu osati kaonekedwe ka khungu kapena chilankhulo chake. (Machitidwe 10:34, 35; Miyambo 17:3) Lemba la Afilipi 2:3, linandithandiza kuona kuti ndikhoza kuthana ndi tsankho ngati nditayamba kuona kuti ena ndi ondiposa. Mfundo za m’Baibulo ngati zimenezi zandithandiza kuti ndizikonda anthu onse ngakhale osiyana nawo khungu.  Panopa ndimaona kuti ndinamasuka ku ukapolo wa tsankho.

“Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuyamba kuona anthu mmene Yehova amawaonera.”—Michael

Michael: Ndinakulira m’dera limene munkakhala azungu ambiri a ku Australia, ndipo ndinkadana kwambiri ndi anthu a ku Asia makamaka matchaina. Ndinkati ndikamayendetsa galimoto, n’kuona munthu wooneka kuti ndi wa ku Asia, ndinkatsitsa galasi la galimoto n’kunena mawu achipongwe ngati akuti: “Muzipita kwanu matchaina inu!” Koma kuphunzira Baibulo kunandithandiza kuyamba kuona anthu mmene Yehova amawaonera. Ndinaphunzira kuti Mulungu amakonda aliyense mosaganizira kumene akuchokera kapena mmene akuonekera. Mfundo imeneyi inandikhudza kwambiri moti nanenso ndinayamba kukonda aliyense. Munthu umasangalala kwambiri ukasiya tsankho. Panopa ndimasangalala kucheza ndi anthu ochokera m’mayiko onse komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana.

“Ndinasintha maganizo anga ndipo ndinayambiranso kucheza ndi anthu akwawo kwa bambo anga.”—Sandra

Sandra: Mayi anga anali ochokera ku Umunede, m’chigawo cha Delta, ku Nigeria. Koma bambo anga anachokera m’chigawo cha Edo ndipo amalankhula Chiesani. Chifukwa cha kusiyana kumeneku, anthu a kwawo kwa bambo anga ankasala kwambiri mayi anga mpaka pamene anamwalira. Chifukwa cha zimenezi, ndinalumbira kuti sindidzalankhulanso ndi aliyense wolankhula Chiesani kapena kukwatiwa ndi aliyense wochokera m’chigawo cha Edo. Koma ndinasintha maganizo nditayamba kuphunzira Baibulo. Popeza Baibulo limanena kuti Mulungu alibe tsankho ndipo amalandira munthu aliyense yemwe amamuopa, ndinadzifunsa kuti, ‘Ineyo ndi ndani kuti ndizidana ndi anthu chifukwa cha mtundu kapena chilankhulo chawo?’ Kenako ndinayambiranso kucheza ndi anthu akwawo kwa bambo anga. Panopa ndine wosangalala komanso ndili ndi mtendere wamumtima chifukwa ndimatsatira zimene Baibulo limanena. Baibulo landithandizanso kuti ndizicheza ndi aliyense mosayang’ana mtundu, chilankhulo kapena dziko limene akuchokera. Ndipo chosangalatsa kwambiri n’chakuti, mwamuna wanga amachokera m’chigawo cha Edo ndipo amalankhula Chiesani.

Koma n’chifukwa chiyani Baibulo lathandiza anthu amenewa kuthetsa mtima wa tsankho? Chifukwa  chakuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Lili ndi mphamvu zothandiza munthu kusintha mmene amaganizira komanso mmene amaonera anthu ena. Koma Baibulo limanenanso zina zimene zingathandize kuthetseratu tsankho.

UFUMU WA MULUNGU UDZATHETSERATU TSANKHO

Ngakhale kuti Baibulo limathandiza munthu kupewa komanso kuthetsa tsankho, palinso zinthu ziwiri zimene ziyenera kuchotsedwa kuti tsankho litheretu. Choyamba ndi uchimo umene tinabadwa nawo. Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Palibe munthu amene sachimwa.” (1 Mafumu 8:46) Choncho, ngakhale titayesetsa bwanji kuthana ndi tsankho, timakumanabe ndi vuto limene mtumwi Paulo anakumana nalo. Iye ananena kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” (Aroma 7:21) Chifukwa chakuti tinabadwa ochimwa, nthawi zina tikhoza kukhala ndi “maganizo oipa” omwe angachititse kuti tizichita zinthu mwatsankho.—Maliko 7:21.

Chachiwiri ndi Satana Mdyerekezi. Pofotokoza za iye, Baibulo limati Satana ndi “wopha anthu” komanso kuti ndi “amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) N’chifukwa chake tsankho lili paliponse ndipo anthu akulephera kulithetsa. N’chifukwa chakenso anthu akulephera kuthetsa kusalana, kudana ndi anthu a zipembedzo zina, kuphana chifukwa chosiyana mtundu komanso makhalidwe ena amene amabwera chifukwa cha tsankho.

Choncho, kuti tsankho litheretu, m’pofunika kuthetsa uchimo komanso kumuwonongeratu Satana Mdyerekezi. Baibulo limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzachita zimenezi.

Yesu Khristu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo kuphatikizapo kusalana komanso tsankho.

Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padziko lapansi, Satana ‘adzamangidwa’ n’cholinga choti “asasocheretsenso mitundu ya anthu.” (Chivumbulutso 20:2, 3) Kenako kudzabwera “dziko lapansi latsopano” mmene “mudzakhala chilungamo.” *2 Petulo 3:13.

Anthu amene adzakhale m’dziko latsopano limenelo adzathandizidwa kuti akhale angwiro komanso opanda uchimo. (Aroma 8:21) Monga nzika za Ufumu umenewu, ‘sadzavulazana kapena kuwonongana’ chifukwa “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yesaya 11:9) Pa nthawi imeneyo anthu onse adzaphunzira zimene Yehova amafuna ndipo aliyense azidzachita zinthu potengera makhalidwe a Yehova. Zimenezi zidzachititsa kuti tsankho litheretu chifukwa “Mulungu alibe tsankho.”—Aroma 2:11.

^ ndime 17 Kuti mudziwe zambiri za Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite, onani mutu 3, 8 ndi 9 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.