Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Mumalemekeza Zipembedzo Zina?

Kodi Mumalemekeza Zipembedzo Zina?

Timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti, “lemekezani anthu [onse]” mosayang’ana chipembedzo chawo. (1 Petulo 2:17) Mwachitsanzo, m’mayiko ena muli a Mboni za Yehova ambirimbiri. Ngakhale zili choncho, sitikakamiza andale kapena anthu opanga malamulo kuti aletse zipembedzo zina kapena ntchito imene zipembedzozo zikuchita. Komanso sitiyesa kukopa akuluakulu a boma kuti aike malamulo okakamiza anthu kuti azitsatira mfundo zathu zokhudza makhalidwe abwino komanso zikhulupiriro zachipembedzo chathu. M’malomwake, timalemekeza zikhulupiriro za anthu ena monga mmene timafunira kuti nawonso azilemekeza zimene timakhulupirira.—Mateyu 7:12.