Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”

“Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”

Kodi Yehova amayamikira zimene atumiki ake amachita pofuna kumusangalatsa? Ena anganene kuti ayi, Mulungu alibe chidwi ndi zimene anthufe timachita. Koma maganizo amenewa amapangitsa anthu kuganiza zolakwika ponena za Mulungu. Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, limatithandiza kudziwa zoona pa nkhaniyi. Limatitsimikizira kuti Yehova amaona komanso amayamikira zimene atumiki ake amachita. Tiyeni tikambirane zimene mtumwi Paulo ananena pa Aheberi 11:6.

Kodi pamafunika chiyani kuti munthu asangalatse Yehova? Paulo ananena kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” Onani kuti Paulo sananene kuti popanda chikhulupiriro n’zovuta kukondweretsa Mulungu. M’malomwake, iye ananena kuti n’zosatheka kukondweretsa Mulungu popanda chikhulupiriro. M’mawu ena tingati, chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti munthu akondweretse Mulungu.

Koma kodi tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chotani kuti tikondweretse Yehova? Pakufunika zinthu ziwiri. Choyamba, tiyenera “kukhulupirira kuti iye alikodi.” Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti tiyenera “kukhulupirira kuti iye ndi weniweni.” N’zosatheka kusangalatsa Mulungu ngati sitikhulupirira kuti iyeyo alipo. Komabe chikhulupiriro chenicheni chimafuna zambiri, chifukwa ngakhale ziwanda nazonso, zimakhulupirira kuti Yehova alipo. (Yakobo 2:19) Chikhulupiriro chakuti Mulungu alipo, chiyenera kutilimbikitsa kuchita zomukondweretsa. Zimenezi zingasonyeze kuti chikhulupiriro chathu ndi champhamvu ndipo chikhulupiriro choterechi chimakondweretsa Mulungu.—Yakobo 2:20, 26.

Chachiwiri, ‘tiyenera kukhulupirira kuti,’ Mulungu “amapereka mphoto.” Munthu amene ali ndi chikhulupiriro chenicheni amadziwa kuti zimene akuchita posangalatsa Mulungu, sizidzapita pachabe. (1 Akorinto 15:58) Tiyenera kudziwa kuti sitingasangalatse Yehova ngati timakayikira kuti adzatipatsa mphoto. (Yakobo 1:17; 1 Petulo 5:7) Munthu yemwe amanena kuti Mulungu satisamalira, satiyamikira ndiponso kuti ndi woumira, sadziwa Mulungu amene Baibulo limanena.

Kodi Yehova amapereka mphoto kwa ndani? Paulo ananena kuti amapereka mphoto “kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Buku lina lomasulira Baibulo linanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “omufunafuna ndi mtima wonse” satanthauza ‘kungomufunafuna’ chabe, koma amatanthauza “kulambira Mulungu mwakhama.” Buku linanso limafotokoza kuti verebu lachigiriki limeneli, limanena za kuchita zinthu mobwerezabwereza kapena mwakhama. Choncho, Yehova amapereka mphoto kwa anthu amene amamulambira ndi mtima wonse.—Mateyu 22:37.

Sitingasangalatse Yehova ngati timakayikira kuti adzatipatsa mphoto

Kodi Yehova amapereka bwanji mphoto kwa atumiki ake okhulupirika? Iye amawalonjeza mphoto ya mtengo wapatali imene imasonyeza kuti ndi wachikondi komanso si woumira. Mphoto imeneyi ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Koma ngakhale pano, anthu amene amafunafuna Yehova ndi mtima wonse amadalitsidwa kwambiri. Iwo amadalitsidwa ndi mzimu woyera komanso amakhala anzeru chifukwa chotsatira Mawu ake. Amakhalanso ndi moyo wabwino umene amakhutira nawo.—Salimo 144:15; Mateyu 5:3.

Apatu taona kuti Yehova amayamikira zimene atumiki ake okhulupirika amachita pomutumikira. Kodi zimenezi sizikukupangitsani kufuna kumudziwa bwino Mulungu? Ngati ndi choncho, muyenera kuphunzira zambiri zimene zingakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro chenicheni chimene chingapangitse kuti Yehova adzakupatseni mphoto.

Mavesi amene mungawerenge mu November

Tito 1-3; Filimoni 1-25; Aheberi 1-13 mpaka Yakobo 1-5