Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikonda Anthu, Osati Ndalama Kapena Katundu

Muzikonda Anthu, Osati Ndalama Kapena Katundu

Mfundo Yoyamba

Muzikonda Anthu, Osati Ndalama Kapena Katundu

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”​—1 Timoteyo 6:10.

N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMENEZI ZIMAKHALA ZOVUTA? Otsatsa malonda amachititsa kuti anthu asamakhutire ndi zimene ali nazo. Iwo amafuna kuti anthu azigwira ntchito modzipha n’cholinga choti apeze ndalama zambiri zogulira zinthu zatsopano, zabwino komanso zikuluzikulu. Ndalama zimakopa kwambiri ndipo n’zosavuta kuti munthu aliyense ayambe kukonda ndalama. Komabe Baibulo limatichenjeza kuti munthu amene amakonda kwambiri chuma sakhutira ndi zimene ali nazo. Mfumu Solomo analemba kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.”​—Mlaliki 5:10.

ZIMENE MUNGACHITE: Muzitsanzira Yesu ndipo muzikonda kwambiri anthu, osati ndalama kapena katundu. Yesu analolera kutaya zonse zimene anali nazo, ngakhale moyo wake umene, chifukwa chokonda anthu. (Yohane 15:13) Iye anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Tikakhala ndi chizolowezi chopatsa anthu ena zinthu ndiponso nthawi yathu, iwo adzachitanso chimodzimodzi kwa ifeyo. Yesu anati: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.” (Luka 6: 38) Anthu amene amafunitsitsa kukhala ndi ndalama zambiri ndiponso chuma, amadzibweretsera mavuto ndi zopweteka zambiri. (1 Timoteyo 6:9, 10) Koma munthu amakhaladi wokhutira pokhapokha ngati amakonda anthu ena ndiponso ngati anthu amamukonda iyeyo.

Choncho, mungachite bwino kuunikanso mmene zinthu zili pamoyo wanu kuti muone ngati pali zina zimene mungasinthe kuti muzikhala moyo wosafuna zambiri. Mwachitsanzo, kodi mungachepetseko chiwerengero cha zinthu zimene muli nazo kapena zimene mukufuna kugula? Mukachita zimenezi, mudzakhala ndi nthawi ndiponso mphamvu zambiri zochitira zinthu zina zofunika kwambiri. Zinthu zimenezi, zikuphatikizapo kuthandiza anthu ena ndiponso kutumikira Mulungu amene anakupatsani zinthu zonse zimene muli nazo.​—Mateyu 6:24; Machitidwe 17:28.

[Chithunzi patsamba 4]

“Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani”