Mmene Angelo Amakhudzira Moyo Wathu
Zimene Tikuphunzira kwa Yesu
Mmene Angelo Amakhudzira Moyo Wathu
Yesu anali kukhala ndi Atate wake kumwamba “dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:5) Choncho, iye ndi amene angayankhe bwino mafunso otsatirawa.
Kodi angelo amakhala ndi chidwi ndi anthufe?
▪ Zimene Yesu ananena zimatiphunzitsa kuti angelo amakonda kwambiri anthu. Iye ananena kuti: “Kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”—Luka 15:10.
Yesu anasonyeza kuti angelo anapatsidwa udindo woonetsetsa kuti atumiki a Mulungu zinthu zikuwayendera bwino mwauzimu. Choncho pochenjeza ophunzira ake kuti asamakhumudwitse ena, iye anati: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” (Mateyu 18:10) Pamenepa sikuti Yesu ankatanthauza kuti wotsatira wake aliyense ali ndi mngelo wakewake amene amamuteteza. Koma iye ankatanthauza kuti angelo amene amagwira ntchito moyandikana kwambiri ndi Mulungu amachita chidwi kwambiri ndi anthu a mu mpingo wachikhristu.
Kodi Mdyerekezi angatisocheretse bwanji?
▪ Yesu anachenjeza otsatira ake kuti Satana amafuna kulepheretsa anthu kudziwa zoona zenizeni za Mulungu. Iye anati: “Munthu aliyense akamva mawu a ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo amabwera n’kukwatula zomwe zafesedwa mumtima wa munthuyo.”—Mateyu 13:19.
Yesu anasonyeza njira imodzi imene Satana amasocheretsera anthu ponena fanizo la munthu amene anafesa tirigu m’munda wake. Munthu ameneyu akuimira Yesu ndipo tirigu akuimira Akhristu oona amene adzalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. Koma Yesu ananena kuti mdani anabwera ndipo “anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo.” Namsongole akuimira Akhristu onyenga. Ndipo “mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi.” (Mateyu 13:25, 39) Anthu ena amene amanena kuti ndi Akhristu, angamaonekedi ngati Akhristu enieni monga mmene namsongole amafananira ndi tirigu akamamera. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa zinthu zabodza zimachititsa anthu kuti asamamvere Mulungu. Satana akugwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga pofuna kulepheretsa anthu kuti asakhale pa ubwenzi ndi Yehova.
Kodi tingatani kuti Satana asatisocheretse?
▪ Yesu ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa dziko” lapansi. (Yohane 14:30) Popempherera ophunzira ake kwa Mulungu, Yesu ananena mawu osonyeza zimene tingachite kuti tikhale otetezeka kwa Satana. Iye anati: “Muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko. Ayeretseni ndi choonadi. Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:15-17) Zimenezi zikusonyeza kuti kuphunzira Mawu a Mulungu kungatiteteze kuti tisatengere maganizo a dziko lolamulidwa ndi Satanali.
Kodi angelo amatithandiza bwanji masiku ano?
▪ Yesu ananena kuti ‘pa mapeto a nthawi ino, angelo adzapita n’kukachotsa oipa pakati pa olungama.’ (Mateyu 13:49) Panopa tikukhala m’nthawi ‘yamapeto’ ndipo anthu ambiri akumvetsera uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:3, 14.
Komano sikuti anthu onse amene ayamba kuphunzira Mawu a Mulungu amapitirizabe kusangalatsa Mulungu. Angelo akutsogolera ntchito imene atumiki a Yehova akugwira, ndipo anthu amene amakondadi Mulungu kuchokera pansi pa mtima akusiyanitsidwa ndi anthu amene satsatira zimene akuphunzira. Ponena za anthu amene Mulungu amasangalala nawo, Yesu ananena kuti anthu amenewa ndi “amene pambuyo pomva mawuwo ndi mtima woona komanso wabwino, amawagwiritsitsa ndi kubereka zipatso mwa kupirira.”—Luka 8:15.
Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 10 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 16]
Angelo amagwira ntchito yofunika kwambiri yosonkhanitsa anthu oona mtima kuti abwere mu mpingo wachikhristu.