Kodi Mukudziwa?
Kodi Mukudziwa?
Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti thupi lake linali ndi “zipsera za chizindikiro cha kapolo wa Yesu?”—Agalatiya 6:17.
▪ N’kutheka kuti anthu a m’nthawi ya atumwi anaganiza zinthu zingapo zosiyanasiyana atamva mawu a Paulowo. Mwachitsanzo, kale akaidi ogwidwa ku nkhondo, anthu amene aba zinthu m’kachisi komanso akapolo amene athawa ambuyawo ankadindidwa chizindikiro pogwiritsa ntchito chitsulo chotentha ndi cholinga choti azitha kuwazindikira. Anthu ankaona kuti kuikidwa chizindikiro choterechi chinali chinthu chochititsa manyazi.
Komabe sinthawi zonse pamene munthu wodindidwa chizindikiro ankaonedwa kuti ndi wonyozeka. Anthu ambiri m’nthawi imeneyo ankadindidwa chizindikiro chosonyeza mtundu wawo kapena chipembedzo chawo. Malinga ndi zimene buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena, “Pofuna kupereka ulemu kwa milungu yonyenga Hadadi ndi Atarigatisi, Asiriya ankadzidinda chizindikiro pamkono kapena m’khosi . . Ndiponso anthu otsatira mulungu Diyonisiyo pathupi lawo ankakhala ndi chizindikiro cha tsamba la mtengo winawake woyanga.”—Theological Dictionary of the New Testament.
Anthu ena oikira ndemanga nkhani za m’Baibulo amaganiza kuti Paulo ankanena za zipsera zimene anali nazo chifukwa cha nkhanza zimene ena anamuchitira pa maulendo ake aumishonale. (2 Akorinto 11:23-27) Koma n’kuthekanso kuti Paulo sankatanthauza zipsera zenizeni, koma khalidwe limene anali limene linkamudziwikitsa kuti ndi Mkhristu.
Kodi mizinda yothawirako ya ku Isiraeli wakale inadzakhala malo obisalako zigawenga?
▪ Kale akachisi a anthu osalambira Mulungu anali malo obisalako zigawenga kapena anthu othawa milandu. Zimenezi zinkachitikanso m’matchalitchi achikhristu m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500. Koma malamulo a m’mizinda yothawirako ya Aisiraeli ankateteza mizinda imeneyi kuti isakhale malo obisalako zigawenga.
Chilamulo cha Mose chinkanena kuti munthu amene anali wolandiridwa kumzinda wothawirako ndi yekhayo amene wapha munthu mwangozi. (Deuteronomo 19:4, 5) Munthu amene wachita zimenezi ankathawira kumzinda wothawirako umene unali pafupi kuti wachibale wamwamuna wa munthu wophedwayo asamuphe pobwezera imfa ya m’bale wakeyo. Wothawayo atafotokoza mlandu wake kwa akuluakulu a mzinda wothawirakowo, ankapita naye kumzinda wapafupi ndi kumene kunachitikira ngoziyo. Kumeneko ankakafotokoza zifukwa zimene akunenera kuti anapha munthuyo mwangozi. Kenako akuluakuluwo ankafufuzanso ubwenzi wa wophedwayo ndi munthu amene akuimbidwa mlanduyo. Ankachita zimenezo n’cholinga chakuti adziwe ngati anamupha mwadala chifukwa choti ankadana naye.—Numeri 35:20-24; Deuteronomo 19:6, 7; Yoswa 20:4, 5.
Akamupeza kuti siwolakwa, wothawayo anali kubwerera kumzinda wothawirako, ndipo ankayenera kukhala komweko, osatuluka mu mzindawo kapena m’dera loyang’aniridwa ndi mzindawo. Ngakhale zinali choncho, mizinda imeneyi sinali ndende. Munthu amene wathawira kumeneko ankagwira ntchito komanso kuchita nawo zinthu ngati wina aliyense. Mkulu wa ansembe akamwalira, anthu onse amene anathawira kumizinda yothawirako ankaloledwa kubwereka kwawo kuti azikakhala mwaufulu.—Numeri 35:6, 25-28.
[Mapu patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MIZINDA YOTHAWIRAKO
1 KEDESI
2 GOLANI
3 RAMOTI-GILIYADI
4 SEKEMU
5 BEZERI
6 HEBURONI
Mtsinje wa Yorodano