Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munthu Angakhaledi Wokhutira ndi Zimene ali Nazo?

Kodi Munthu Angakhaledi Wokhutira ndi Zimene ali Nazo?

Kodi Munthu Angakhaledi Wokhutira ndi Zimene ali Nazo?

“Osauka amalemera chifukwa chokhutira ndi zimene ali nazo koma olemera amasauka chifukwa chosakhutira ndi zimene ali nazo.”​—Benjamin Franklin.

MOGWIRIZANA ndi mawu amenewa, anthu ambiri azindikira kuti sichinthu chapafupi kuti munthu azikhutira ndi zimene ali nazo. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri masiku ano sakhutira ndi zimene ali nazo. Izi zili choncho chifukwa anthu m’dzikoli amakonda kusirira za anthu ena ndipo amalimbikitsa mtima wokonda chuma ndiponso kutchuka. Kodi n’kutheka kuti zinthu zotsatirazi zakuchitikiraninso inuyo?

• Otsatsa malonda amachititsa anthu kuganiza kuti angakhale okhutira pa moyo wawo atangogula chinthu chimodzi kuwonjezera pa zimene ali nazo kale.

• Anthu ambiri ku ntchito kapena ku sukulu amalimbikitsa anzawo kuona kuti angakhale ofunika ngati atamachita zimene anthu ena akuchita.

• Anthu ambiri sayamika wina akawachitira zabwino.

• Anthu amafuna kuti anzawo azisilira zinthu iwo ali nazo.

• Anthu ambiri sapeza mayankho a mafunso ofunika amene ali nawo.

Ndiye tikaganizira mavuto onsewa, kodi n’zothekadi kukhala okhutira ndi zinthu zimene tili nazo? Mtumwi Paulo ananena za “chinsinsi chakukhala wokhutitsidwa.” Nthawi zina ankakhala ndi zinthu zambiri pomwe nthawi zina ankakhala ndi zochepa. Anzake ankamusilira pomwe anthu ena ankamunyoza. Komabe iye ananena kuti: “Ndaphunzira chinsinsi chakukhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse.”​—Mawu tapendeketsa tokha; Afilipi 4:11, 12, Chipangano Chatsopano Mu Chichewa Cha Lero.

Anthu amene sanayesepo kukhala moyo wokhutira ndi zimene ali nazo amaganiza kuti n’zosatheka kukhala moyo umenewu. Koma mtumwi Paulo ananena kuti anthu oterewa akhoza kuphunzira kukhala wokhutira. Tsopano tiyeni tione mfundo zisanu zopezeka m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, zimene zingatithandize kukhala okhutira ndi zimene tili nazo.