Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale osangalala?

▪ Yesu anayamba ulaliki wake wotchuka kwambiri ndi mfundo zokhudza mmene tingakhalire osangalala. Iye anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Kodi ankatanthauza chiyani? Kodi zosowa zathu zauzimu n’chiyani?

Monga mmene zilili ndi nyama, anthufe timafunika kupuma, kumwa, ndi kudya kuti tikhale ndi moyo. Koma mosiyana ndi nyama, ifeyo kuti tikhale osangalala timafunikanso kuzindikira chifukwa chimene Mulungu anatilengera. Mlengi wa zamoyo zonse ndi yekhayo amene angatiuze chifukwa chimenechi. N’chifukwa chake Yesu anati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’ (Mateyo 4:4) Anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu amakhala osangalala chifukwa amayandikira kwa Yehova, “Mulungu wa chisangalalo.” Iye amawapatsa chiyembekezo, chimene ndi chinthu chofunika kwambiri kuti akhale osangalala.​—1 Timoteyo 1:11.

Kodi Yesu anachita chiyani kuti tikhale ndi chiyembekezo?

▪ Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5) Yesu anatipatsa chiyembekezo pochiritsa odwala komanso poukitsa akufa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi. Iye anatipatsanso uthenga wachiyembekezo, ndipo anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Anthu amene amamvera Mulungu adzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Tangoganizirani, kukhala limodzi ndi anthu omvera Mulungu okhaokha ndiponso kukhalabe wachinyamata mpaka kalekale, osakalamba. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amati: “Kondwerani ndi chiyembekezocho.” (Aroma 12:12) Kuwonjezera pa zimenezi, Yesu anafotokozanso zimene tingachite kuti tikhale osangalala panopo.

Kodi Yesu anaphunzitsa kuti tizichita chiyani kuti tikhale osangalala?

▪ Yesu anapereka malangizo othandiza kwambiri pa nkhani zokhudza kukhala bwino ndi anthu ena, ukwati, kudzichepetsa, ndiponso mmene tiyenera kuonera chuma. (Mateyo 5:21-32; 6:1-5, 19-34) Choncho mungakhale wosangalala ngati mutamatsatira malangizo a Yesu amenewa.

Kukhala wopatsa kumathandiza munthu kukhala wosangalala. (Machitidwe 20:35) Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olemala, ndi akhungu; ndipo udzakhala wosangalala, chifukwa alibe choti adzabweze kwa iwe.” (Luka 14:13, 14) Munthu amakhala wosangalala akamayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa ena, osati kuchita zongodzisangalatsa yekha.

Kodi tingakhale osangalala kwambiri tikamasangalatsa ndani?

▪ Timasangalala tikamachita zinthu zosangalatsa anthu ena. Ngakhale zili choncho, timakhala osangalala kwambiri tikamachita zinthu zosangalatsa Mulungu. Chisangalalo chimene timakhala nacho chimaposa chisangalalo chimene makolo okonda ndiponso kunyadira ana awo amakhala nacho. Zimene zinachitika tsiku lina pamene Yesu anali kuphunzitsa anthu ena zimatsimikizira zimenezi. Baibulo limati: “Mayi wina m’khamu la anthulo anafuula nati kwa iye: ‘N’ngosangalala mayi amene mimba yake inanyamula inu ndi kuyamwa mawere ake!’ Koma iye anati: ‘Ayi, koma, Osangalala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!’”​—Luka 11:27, 28.

Yesu ankasangalala kwambiri kuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba. Mulungu amafuna kuti anthu adziwe kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha. Nthawi ina, Yesu atauza munthu wina wachidwi za moyo wosatha, ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 4:13, 14, 34) Inunso mungakhale wosangalala ngati mukusangalatsa Mulungu mwa kuuzako ena choonadi cha m’Baibulo.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri, werengani mutu 1 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 16]

Timakhala osangalaladi tikazindikira chifukwa chimene Mulungu anatilengera