Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa . . .

“Kodi Anthu Onse Ali ndi Mwayi Wofanana Wophunzira za Mulungu?”

“Kodi Anthu Onse Ali ndi Mwayi Wofanana Wophunzira za Mulungu?”

Atafunsidwa kuti lamulo lalikulu kuposa onse ndi liti, Yesu anayankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyo 22:37) Komabe, munthu asanayambe kukonda Mulungu, choyamba ayenera kudziwa zenizeni zokhudza Mulungu. (Yohane 17:3) Kodi anthu onse adzakhala ndi mwayi wofanana wophunzira zimenezi?

Baibulo ndi limene limatiphunzitsa zambiri zokhudza Mulungu. (2 Timoteyo 3:16) Anthu ambiri amakhala m’madera amene Baibulo ndi losavuta kupeza. Kawirikawiri anthu amenewa amapemphedwa kuti aziphunzira Baibulo n’cholinga choti amudziwe bwino Mulungu. (Mateyo 28:19) Ena akukulira m’mabanja amene makolo amayesetsa kuwathandiza kuti amudziwe bwino Mulungu.​—Deuteronomo 6:6,7; Aefeso 6:4.

Koma kwa ena zinthu ndi zosiyanako chifukwa analeredwa ndi makolo ovuta amene sanali kukonda ana awo. (2 Timoteyo 3:1-5) Anthu okulira m’mabanja otero angavutike kuti ayambe kuona Mulungu monga Atate wachikondi wakumwamba. Ena sukulu sanapite nayo patali, zimene zimachititsa kuti azilephera kuwerenga Baibulo. Ndipo palinso ena amene maganizo awo anachititsidwa khungu ndi ziphunzitso zonyenga zimene zipembedzo zosiyanasiyana zimaphunzitsa. Enanso mabanja awo, malo amene akukhala, kapena dziko limene akukhala sililola anthu kuphunzira Baibulo. (2 Akorinto 4:4) Kodi zimenezi zingachititse anthuwo kuti asapeze mwayi wophunzira za Mulungu n’kuyamba kumukonda?

Panthawi ina, Yesu anauza ophunzira ake kuti chifukwa cha mavuto amene anthu ena amakumana nawo, n’zovuta kuti akonde ndi kumvera Mulungu. (Mateyo 19:23, 24) Komabe iye anawakumbutsa kuti, ngakhale kuti mavuto ena amaoneka ngati ovuta kuwathetsa, “zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.”​—Mateyo 19:25, 26.

Ganiziraninso mfundo izi: Yehova Mulungu anaonetsetsa kuti Baibulo, limene ndi Mawu ake, likhale buku lofala kwambiri kuposa buku lina lililonse. Baibulo linaneneratu kuti uthenga wabwino wonena za Mulungu ndiponso chifuniro chake udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyo 24:14) Masiku ano, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino m’mayiko oposa 230 ndipo zikufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero pafupifupi 500. Ngakhale kuti ena alibe mwayi wowerenga Baibulo, akhoza kuphunzira za Mulungu woona mwa kuona ndi kuganizira kwambiri zinthu zimene analenga.​—Aroma 1:20

Kuwonjezera pamenepo, Mawu a Mulungu amanena kuti: “Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukam’funafuna iye udzam’peza.” (1 Mbiri 28:9) Choncho ngakhale kuti Yehova sakulonjeza kuti aliyense adzakhala ndi mwayi wofanana wophunzira za iye, amaonetsetsa kuti munthu aliyense woona mtima akhale ndi mwayi wophunzira za iye. Adzaonetsetsanso kuti anthu amene sanakhalepo ndi mwayi wophunzira za iye adzakhalenso ndi mwayi umenewo mwa kuwaukitsa kwa akufa m’dziko latsopano lachilungamo.​—Machitidwe 24:15.