Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sanapite Mofulumira?

Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Sanapite Mofulumira?

YESU wamva kuti mnzake wapamtima, Lazaro, akudwala kwambiri. Iye wamva uthengawu kwa munthu wina amene watumidwa ndi Mariya ndi Marita, omwe ndi alongo a Lazaro. Munthuyu wachokera ku Betaniya kumene Lazaro ndi alongo ake amakhala. Mariya ndi Marita akukhulupirira kuti Yesu akhoza kuchiritsa Lazaro ngakhale kuti ali kutali kwambiri ndi Yesu, kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. Iwo akudziwa kuti Yesu wachiritsapo anthu ena ali kutali ndi anthuwo.​—Mateyo 8:5-13; Yohane 11:1-3.

Munthu wodzanena uthenga womvetsa chisoniwu atauza Yesu uthengawu, Yesu sakuchita chilichonse. Baibulo limati: “Anakhalabe masiku awiri kumalo kumene iye analiko.” (Yohane 11:6) Kodi ukudziwa chifukwa chimene Yesu sakupitira mofulumira kukathandiza Lazaro?​— * Tiye tikambirane nkhani imeneyi.

Yesu wadziwa kuti Lazaro wamwalira ndipo akuuza atumwi ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Koma atumwiwo sakugwirizana ndi zimenezi, ndipo akunena kuti: “Posachedwa pomwepa Ayudeya anafuna kukuponyani miyala, ndiye mukufuna kupitanso komweko kodi?” Yesu akuwauza kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukam’dzutsa ku tulo take.”

Atumwiwo akuyankha kuti: “Ambuye, ngati iye akupumula apeza bwino.” Pamenepo Yesu akuwafotokozera kuti: “Lazaro wamwalira.” Kenako Yesu akunena mawu amene mwina akudabwitsa atumwiwo. Iye akuti: “Ndikukondwera chifukwa cha inu kuti sindinali kumeneko . . . Koma tsopano tiyeni tipite kwa iye.”

Yesu atanena zimenezi, Tomasi akulankhula molimba mtima kuti: ‘Tiyeni tipite, kuti tikafe pamodzi ndi Yesu.’ Tomasi akudziwa kuti adani ayeseranso kupha Yesu ndipo atumwiwo akhozanso kuphedwa. Komabe onse akupita naye. Patatha masiku awiri kapena kuposerapo Yesu akufika ku Betaniya, kwawo kwa Lazaro. Umenewu ndi ulendo wa makilomita oposa atatu.​—Yohane 11:7-18.

Kodi ukudziwa chifukwa chiyani Yesu akusangalala kuti sanafike mofulumira?​—Yesu anaukitsapo anthu akufa, koma anthu amenewo anawaukitsa iwo atangofa kumene. (Luka 7:11-17, 22; 8:49-56) Mosiyana ndi anthu amenewo, Lazaro wakhala ataikidwa m’manda kwa masiku angapo. Choncho palibe amene angakayikire m’pang’ono pomwe kuti Lazaro wamwaliradi.

Malita, mlongo wake wa Lazaro, atamva kuti Yesu watsala pang’ono kufika ku Betaniya, akuthamanga kukamuchingamira. Atakumana, akuuza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” Koma Yesu akumulimbikitsa kuti: “Mlongo wako adzauka.” Kenaka Malita akuthamanga kubwerera kunyumba ndipo atafika akuuza mbale wake, Mariya, mwamseri kuti: “Mphunzitsi ali pano ndipo akukuitana.”

Nthawi yomweyo, Mariya akufulumira kukakumana ndi Yesu. Koma anthu ambiri amene ali pamaliropo akuganiza kuti iye akupita kumanda, choncho akumulondola. Yesu ataona Mariya ndi anthuwo akulira, nayenso ‘akugwetsa misozi.’ Posakhalitsa, onse akufika kumanda a Lazaro. Pakhomo pa mandawo atsekapo ndi chimwala chachikulu. Kenako Yesu akulamula kuti: “Chotsani chimwalachi.” Koma Malita akutsutsa zimenezo ndipo akuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, pakuti lero ndi tsiku lachinayi chimuikireni m’manda.”

Anthuwo akuchita zimene Yesu wanena ndipo akuchotsa chimwalacho. Kenako Yesu akupemphera, kuthokoza Mulungu chifukwa cha mphamvu imene amupatse kuti aukitse Lazaro. Yesu akufuula “mokweza mawu nati: ‘Lazaro, tuluka!’” Iye akutulukadi ali ‘wokulungidwa m’nsalu za maliro.’ Pamenepo Yesu akuti: “M’masuleni ndi kumuleka apite.”​—Yohane 11:19-44.

Kodi tsopano wamvetsa chifukwa chimene Yesu sanapitire mofulumira kukachiritsa Lazaro?​— Iye anadziwa kuti akadikira pang’ono, apeza mpata wophunzitsa ena za Atate wake, Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anasankha nthawi yabwino kwambiri yochitira zimenezi, anthu ambiri anayamba kukhulupirira Mulungu. (Yohane 11:45) Kodi waona zimene tingaphunzire pa zimene Yesu anachita?​—

Iwenso ukhoza kusankha nthawi yabwino yophunzitsa ena zinthu zodabwitsa zimene Mulungu wachita ndi zimene adzachite. Mwina ukhoza kuuzako anzako akusukulu kapena aphunzitsi ako. Ana ena, ngakhale ali m’kalasi, apezapo mpata wofotokoza za madalitso aakulu amene Ufumu wa Mulungu udzabweretsera anthu. Iweyo sungathe kuukitsa akufa koma ungathandize ena kuti nawonso adziwe Mulungu amene adzaukitsa akufa.

^ ndime 4 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzere muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.