Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Anthu Ambiri Amaopa

Zimene Anthu Ambiri Amaopa

Zimene Anthu Ambiri Amaopa

“Sikuti ndi anthu opemphera okha amene amaganiza kuti dzikoli latsala pang’ono kukumana ndi zoopsa.”​—STEPHEN O’LEARY, PULOFESA WA PA YUNIVESITE YA SOUTHERN CALIFORNIA. *

KODI mukugwirizana ndi mfundo imene ili pamwambayi? Nkhani zitatuzi zifotokoza zifukwa zina zimene anthu amaopera za m’tsogolo. Komanso zikuthandizani kuona chifukwa chake muyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti anthu adzapitirizabe kukhala padziko lapansi. Tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira zimenezi ngakhale kuti padzikoli pakuchitika zinthu zina zodetsa nkhawa zimene muwerenge m’munsimu.

Mayiko akhoza kuyambitsa nkhondo ya mabomba anyukiliya nthawi ina iliyonse. Mu 2007, magazini ina inati: “Masiku ano zinthu zafika poipa kwambiri pa nkhani ya zida za nyukiliya moti zimene zinachitika pamene mabomba a atomiki anaphulitsidwa m’mizinda ya Hiroshima ndi Nagasaki zikhoza kuchitikanso.” (Bulletin of the Atomic Scientists) N’chifukwa chiyani inanena zimenezi? Magaziniyi inanena kuti mu 2007 panali padakali mabomba anyukiliya okwanira 27,000 ndipo 2,000 mwa mabomba amenewa, “akhoza kungotenga mphindi zochepa chabe kuti awaponye.” Komanso ngakhale ataphulitsa ochepa chabe mwa mabomba amenewa, zotsatira zake zikhoza kukhala zoopsa kwambiri.

Kodi panopa mayiko achepetsako mabomba awo anyukiliya kusiyana ndi mu 2007? Mayiko asanu amene ali ndi mabomba anyukiliya ochuluka kwambiri ndi China, France, Russia, United Kingdom ndi United States. Buku lina linanena kuti, mayiko onsewa “akukonza makina atsopano oponyera mabomba anyukiliya kapena alengeza kuti ayamba kukonza makina oterowo.” (SIPRI Yearbook 2009 * *) Buku limeneli linanenanso kuti pali mayiko enanso amene ali ndi mabomba anyukiliya. Anthu ochita kafukufuku amanena kuti zikuoneka kuti mayiko a India, Pakistan, ndi Israel, lililonse mwa mayikowa lili ndi mabomba anyukiliya pakati pa 60 ndi 80. Iwo amanenanso kuti padziko lonse lapansi pali mabomba anyukiliya okwana 8,392 otcheratchera, ongodikira kuti awaponye.

Padzikoli pakhoza kuchitika zoopsa chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Magazini yomwe taitchula poyamba ija inanena kuti: “Kusintha kwa nyengo kungachititse zinthu zoopsa zimene zingafanane ndi zimene mabomba anyukiliya angachite.” (Bulletin of the Atomic Scientists) Asayansi ena otchuka monga Stephen Hawking, yemwe anali pulofesa pa yunivesite ya Cambridge, komanso Sir Martin Rees, amene ndi mkulu wa pa koleji ya Trinity imene ndi mbali ya yunivesite ya Cambridge, anavomereza chenjezo limeneli. Akatswiri asayansiwa amaganiza kuti moyo padziko lapansi ungasokonekere kwambiri kapena kutha kumene chifukwa cha mmene anthu akugwiritsira ntchito zipangizo zamakono ndiponso mmene akuwonongera chilengedwe.

Kunena zoti dziko lidzatha kumachititsa mantha anthu ambiri. Mutati mufufuze pa Intaneti mawu akuti “kutha kwa dziko” m’Chingelezi komanso chaka cha “2012,” mutha kuona kuti anthu ambiri akhala akulemba zoti dziko lidzatha m’chaka chimenecho. Chifukwa chiyani amalemba zimenezi? N’chifukwa chakuti kalendala inayake yakale kwambiri imene inalembedwa ndi anthu a mtundu wa Maya, idzatha m’chaka cha 2012. Ndiye anthu ambiri amaganiza kuti moyo padziko lapansi udzasinthiratu m’chaka chimenecho.

Anthu ambiri opemphera amakhulupirira kuti Baibulo limanena kuti dziko lenilenili ndi limene lidzawonongeke. Iwo amakhulupirira kuti anthu onse okhulupirika adzapita kumwamba, pomwe anthu ena onse adzatsala padziko lapansi pano n’kumavutika kapena kuwotchedwa ndi moto.

Koma kodi Baibulo limanenadi kuti zonse padziko kapena dziko lapansi lenilenili zidzawonongedwa? Mtumwi Yohane anachenjeza kuti: “Musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1) Choncho m’malo mongokhulupirira zimene anthu amanena, tsegulani Baibulo lanu kuti muone nokha zimene limanena pa nkhani ya kutha kwa dziko. Mwina mudabwa kumva kuti Baibulo limaphunzitsa zosiyana kwambiri ndi zimene anthu amakhulupirira pa nkhani imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mawuwa analembedwa pa October 19, 2005, m’nkhani ya pa Intaneti yakuti, “Masoka Osiyanasiyana Akuchititsa Anthu Kunena kuti Dzikoli Latsala Pang’ono Kutha.”​—MSNBC Web site.

^ ndime 5 SIPRI ndi chidule cha dzina la bungwe lochita kafukufuku pa nkhani zokhazikitsa mtendere padziko lonse la Stockholm International Peace Research Institute.

^ ndime 5 Nkhani imeneyi yochokera m’buku la SIPRI Yearbook 2009 inalembedwa ndi Shannon N. Kile, amene ndi mkulu wakafukufuku m’bungwe la SIPRI ndiponso woyang’anira ntchito yochepetsa mabomba anyukiliya; Vitaly Fedchenko amene ndi katswiri wakafukufuku pa ntchito yochepetsa zida zankhondo m’bungwe la SIPRI; ndiponso Hans M. Kristensen amene ndi mkulu woyang’anira nkhani zokhudza nyukiliya m’bungwe la Federation of American Scientists.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Mushroom cloud: U.S. National Archives photo; hurricane photos: WHO/​League of Red Cross and U.S. National Archives photo