Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena

PAMOYO wake wonse, Petulo ayenera kuti ankakumbukirabe mmene zinamupwetekera mumtima nthawi imene anaphana maso ndi Yesu. Kodi panthawiyi iye ankaganiza kuti Yesu wakhumudwa kapena wakwiya ndi zimene iye anachita? Sitikudziwa, chifukwa mawu a Mulungu amangonena kuti: “Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo.” (Luka 22:61) Yesu ananeneratu kuti Petulo adzamukana. Koma Petulo ananena kuti sangachite zimenezi. Choncho panthawiyi Yesu atamuyang’ana, Petulo anadziwa kuti walakwa kwambiri. Ndipo anazindikira kuti wachita zimene ankanena kuti sangachite zija. Zimenezi zinam’khumudwitsa kwambiri ndipo ayenera kuti anali asanakhumudwepo chonchi pamoyo wake.

Komabe, sikuti Petulo analibiretu chiyembekezo. Chifukwa choti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba, anali ndi mwayi wokhululukidwa zimene anachitazo komanso kuphunzira kwa Yesu mfundo ina yofunika kwambiri yokhudza kukhululuka. Tonsefe tifunika kuphunzira mfundo imeneyi. Tiyeni tikambirane mmene Petulo anaphunzirira mfundo yovuta kuiphunzira imeneyi.

Panali Zambiri Zoti Aphunzire

Petulo ali mumzinda wa kwawo ku Kaperenao, kutatsala pafupifupi miyezi 6 kuti zimenezi zichitike, anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira? Mpaka nthawi 7 kodi?” Pamenepa mwina Petulo ankaganiza kuti kukhululukira munthu nthawi 7 ndiye kuti wamukhululukira kwambiri. Nthawi imeneyo atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa kuti munthu azikhululukira mnzake katatu kokha basi. Choncho, Yesu anamuyankha kuti: “Osati nthawi 7 zokha ayi, koma, mpaka nthawi 77.”​—Mateyo 18:21, 22.

Kodi Yesu ankatanthauza kuti Petulo azilemba m’buku zimene munthu wamulakwira? Ayi, chifukwa Yesu ponena kuti Petulo azikhululukira munthu nthawi 77 osati nthawi 7 zokha, ankatanthauza kuti kukhululuka kulibe malire. Yesu anasonyeza kuti Petulo anatengera mtima wosakhululukira ena womwe unali wofala kwambiri nthawi imeneyo. Anthu amene anali ndi maganizo amenewa ankachita kukumbukira nthawi zonse zimene mnzawo wawalakwira. Iwo ankachita zimenezi ngati kuti analemba penapake monga mmene wokongoza ndalama ankachitira polemba ngongole zimene ena atenga. Komabe, Mulungu amafuna kuti tizikhululukira ena mopanda malire.

Petulo sanatsutse zimene Yesu ananenazo. Koma kodi mfundo imeneyi inamufika pamtima? Nthawi zambiri timazindikira kuti kukhululuka n’kofunika zikakhala kuti ifeyo ndi amene tikufuna kuti ena atikhululukire. Choncho, tiyeni tionenso zimene zinachitika Yesu atatsala pang’ono kuphedwa. Nthawi yovuta imeneyi, Petulo analakwa ndipo anafunika kuti Mbuye wake amukhululukire.

Panali Zambiri Zoti Amukhululukire

Unali usiku wapadera kwambiri chifukwa unali usiku womaliza wa moyo wa Yesu padziko lapansi monga munthu. Yesu anali ndi zambiri zoti aphunzitse atumwi ake, monga kudzichepetsa. Yesu anapereka chitsanzo pankhani imeneyi pomwe anadzichepetsa n’kusambitsa mapazi awo, ntchito imene nthawi zambiri inali ya akapolo. Poyamba Petulo anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi ndipo anakana kuti Yesu amusambitse mapazi. Kenako, iye anauza Yesu kuti asangomusambitsa mapazi okha koma amusambitsenso manja ndi mutu womwe. Yesu sanam’psere mtima Petulo koma anamufotokozera bwinobwino tanthauzo la zimene anali kuchitazo.​—Yohane 13:1-17.

Komabe patangopita nthawi pang’ono, atumwiwo anasonyeza mtima wodzikuza, anayamba kukangana kuti wamkulu n’ndani. N’zosakayikitsa kuti nayenso Petulo ankakangana nawo pankhani yochititsa manyaziyi. Ngakhale zinali choncho, Yesu anawalangiza mwachifundo ndipo anawayamikira kuti anachita bwino pokhalabe okhulupirika kwa iye monga Mbuye wawo. Komabe, iye analosera kuti atumwi akewo adzamuthawa. Koma Petulo anayankha kuti sangamusiye Yesu ngakhale atawopsezedwa kuti aphedwa. Koma Yesu analosera kuti usiku womwewo Petulo adzakana Mbuye wake katatu, tambala asanalire kawiri. Komabe, Petulo anatsutsa zimenezi ndipo anachita kunena modzitama kuti iye adzakhala wokhulupirika kwambiri kuposa atumwi ena onse.​—Mateyo 26:31-35; Maliko 14:27-31; Luka 22:24-28.

Kodi Yesu anam’psera mtima? Ayi, ndipo panthawi yovuta yonseyi, Yesu ankakonda kuona zinthu zabwino zokha mwa atumwi ake opanda ungwirowo. Yesu ankadziwa kuti Petulo amulakwira, komabe iye anati: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe; chotero iwenso, pamene ubwerera, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32) Choncho, Yesu anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Petulo adzazindikira kulakwa kwake ndipo adzayambiranso kutumikira mokhulupirika. Zimenezi zikusonyezeratu kuti Yesu anali munthu wokoma mtima ndiponso wokhululuka.

Patapita nthawi, ali m’munda wa Getsemane, Petulo anafunikanso kulangizidwa pankhani zingapo. Yesu anauza Petulo, komanso Yakobe ndi Yohane, kuti akhale maso iye akamakapemphera. Yesu anali akuvutika maganizo ndipo ankafunika kulimbikitsidwa, koma Petulo ndi atumwi enawo anagona tulo kangapo konse. Yesu ananena mawu osonyeza kuti anawamvera chisoni komanso anawakhululukira. Iye anati: “Inde, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”​—Maliko 14:32-38.

Posakhalitsa, panafika chigulu cha anthu chitanyamula zounikira, malupanga ndi zibonga. Imeneyi inali nthawi yoti ophunzira ake achite zinthu mwanzeru. Koma Petulo anachita zinthu mopupuluma ndipo anatenga lupanga n’kudula nalo khutu la munthu wina dzina lake Makasi. Iye anali kapolo wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu anadzudzula Petulo mwachikondi n’kupoletsa balalo, kenako anafotokoza mfundo yofunika kwambiri pankhani yopewa zachiwawa ndipo ndi imene Akhristu masiku ano amatsatira. (Mateyo 26:47-55; Luka 22:47-51; Yohane 18:10, 11) Petulo anali atachita zinthu zambirimbiri zofunika kuti Mbuye wake amukhululukire. Zimenezi zingatikumbutse mfundo yakuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobe 3:2) Tonse timafuna kuti Mulungu azitikhululukira tsiku lililonse. Komabe usiku umenewu Petulo anachita zinthu zambiri ndipo anachita chinthu china chokhumudwitsa kwambiri.

Chimene Petulo Analakwitsa Kwambiri

Yesu anafotokozera gulu la anthulo kuti ngati akufuna iyeyo, asiye atumwi ake kuti azipita. Petulo ankangoyang’ana mothedwa nzeru gululo likugwira Yesu. Kenako Petulo anathawa monga mmene anachitira atumwi enawo.

Petulo ndi Yohane atathawa, ayenera kuti anakaima pafupi ndi nyumba ya Anasi, yemwe nthawi ina anali mkulu wa ansembe, ndipo kumeneku n’kumene anayambira kumuzenga Yesu mlandu. Pomwe Yesu ankachoka naye kumeneko, Petulo ndi Yohane ankatsatira “chapatali ndithu.” (Mateyo 26:58; Yohane 18:12, 13) Zimenezi zikusonyeza kuti Petulo sanali wamantha chifukwa panafunika kulimba mtima kuti munthu azitsatira Yesu popeza gululo linanyamula zida ndipo Petulo anali atavulaza kale mmodzi wa anthu omwe anali pagululo. Komabe zimene Petulo anachitazi n’zosiyana ndi zimene iye ankanena, kuti adzakhalabe wokhulupirika komanso kuti adzalolera kufa ndi Mbuye wake ngati pangafunike kutero.​—Maliko 14:31.

Anthu ambiri masiku ano amatsatira Khristu “chapatali ndithu” ngati mmene anachitira Petulo moti anthu samadziwa n’komwe zoti iwo akutsatira Khristu. Komabe monga Petulo ananenera nthawi ina, njira yabwino yotsatirira Khristu ndi kuyenda naye nthawi zonse mmene tingathere ndiponso kutsatira chitsanzo chake pa zinthu zonse mosaopa kanthu.​—1 Petulo 2:21.

Petulo anatsatirabe mochenjera gulu limene linagwira Yesu lija mpaka anafika pachipata cha nyumba ina yokongola kwambiri ya ku Yerusalemu. Nyumbayi inali ya Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe wolemera komanso wolemekezeka kwambiri. Nthawi zambiri nyumba zotere zinkakhala ndi bwalo kunja kwake, ndipo kutsogolo kwake kunkakhala chipata. Petulo anafika pachipatapo koma anakanizidwa kulowa. Yohane, yemwe panthawiyi anali atalowa kale, anabwera n’kudzapempha mtsikana yemwe anali mlonda wapachipatapo kuti amulole Petulo kuti alowe. Zikuoneka kuti Petulo atalowa sanakakhale limodzi ndi Yohane komanso sanafune kukalowa m’nyumba mmene munali Yesu kuti akakhale pafupi ndi Mbuye wake. Iye anakakhala pabwalo ndi akapolo ndi antchito ena omwe ankaotha moto chifukwa kunja kunkazizira. Petulo ankangoonerera anthu akupereka umboni wabodza.​—Maliko 14:54-57; Yohane 18:15, 16, 18.

Chifukwa cha kuwala kwa motowo, mtsikana amene analola kuti Petulo alowe uja anayamba kumuona bwinobwino ndipo anamuzindikira. Kenako anamuulula kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!” Petulo anadzidzimuka ndi mawu amenewa ndipo anakana zoti akudziwa Yesu mpaka anachita kunena kuti mtsikanayo sakudziwa zimene akunena. Kenako anachoka n’kukaima pafupi ndi chipata pofuna kuti anthu asamuzindikire. Koma mtsikana wina anamuzindikira ndipo ananena mawu angati amene mtsikana uja ananena, amvekere: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazareteyo.” Koma Petulo anakanitsitsa ndipo ananena kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” (Mateyo 26:69-72) Mwina Petulo atakana Yesu kachiwiri ndi pamene anamva kulira kwa tambala. Koma ankaganiza zambiri moti sanakumbukire ulosi umene Yesu ananena maola angapo izi zisanachitike.

Patangopita nthawi pang’ono, gulu lina la anthu lomwe linali m’bwalomo linamuyandikira, koma Petulo anayesetsabe kuti anthuwo asamuzindikire. Mmodzi wa anthuwo anali m’bale wake wa Makasi, kapolo amene Petulo anamuvulaza uja. Munthuyo anafunsa Petulo kuti: “Ndinakuona iwe m’munda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” Petulo anawatsimikizira kuti zimenezi sizoona. Choncho iye analumbira, ndipo zikuoneka kuti ankatanthauza kuti iye akhale wotembereredwa ngati akunama. Asanamalize kulankhula, tambala analira ndipo kameneka kanali kachiwiri Petulo kumva tambala akulira usiku umenewu.​—Yohane 18:26, 27; Maliko 14:71, 72.

Panthawiyi, Yesu anali atangotuluka m’nyumbayo n’kukhala pakhonde limene amatha kuona bwinobwino bwalo la nyumbayo. Nthawi imeneyi, monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino, maso ake anaphana ndi a Petulo. Petulo anazindikira kuti walakwira kwambiri Mbuye wake. Kenako iye anachoka pabwalopo, ali ndi chisoni kwambiri ndi zimene anachita. Anayamba kuyenda n’kumalowera mumzindawo ndipo ankatha kuona njira chifukwa kunja kunali mwezi. Iye anali atakhumudwa kwambiri ndipo m’maso mwake munali mutalengeza misozi. Kenako anayamba kulira kwambiri mopwetekedwa mtima.​—Maliko 14:72; Luka 22:61, 62.

Munthu akazindikira kuti walakwa kwambiri, amaganiza kuti wachita tchimo losakhululukidwa ndipo mwina ndi mmene Petulo ankaganizira. Koma kodi iye anachitadi tchimo losakhululukidwa?

Kodi Petulo Anachita Tchimo Losakhululukidwa?

N’zovuta kudziwa mmene Petulo ankamvera kupweteka mumtima mwake dzuwa likutuluka ndipo anthu atayamba kugwira ntchito zawo. Ayenera kuti anadziimba mlandu kwambiri Yesu atafa madzulo a tsiku limenelo, atazunzidwa kwa maola ambiri. Ndipo Petulo ayeneranso kuti ankamva kupweteka kwambiri mumtima mwake akaganizira kuti iye anachititsa nawo kuti Mbuye wake amve kupweteka kwambiri pa tsiku lake lomaliza kukhala ndi moyo padziko lapansi monga munthu. Ngakhale kuti Petulo anali ndi chisoni kwambiri chonchi, iye sanafooke. Tikudziwa zimenezi chifukwa pasanapite nthawi yaitali, iye anayamba kusonkhana ndi atumwi anzake. (Luka 24:33) N’zosakayikitsa kuti atumwi onse anakhumudwa kwambiri ndi zimene iwo anachita usiku wovuta umenewu, choncho anayamba kulimbikitsana.

Apa titha kuona kuti Petulo anaganiza bwino kwambiri. Mtumiki wa Mulungu akachimwa sayenera kufooka koma ayenera kutsimikiza mtima kusiya zimene walakwitsazo ndipo Mulungu amakhala wofunitsitsa kumukhululukira ngakhale tchimo lakelo litakhala lalikulu kwambiri. (Miyambo 24:16) Petulo anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chenicheni ngakhale kuti anakhumudwa kwambiri. Munthu akakhumudwa kwambiri ndi tchimo limene wachita nthawi zambiri amasiya kusonkhana ndi Akhristu anzake, koma zimenezi n’zosathandiza. (Miyambo 18:1) Chinthu chanzeru ndi kupitirizabe kusonkhana ndi atumiki anzathu, kuti tikhale ndi mphamvu mwauzimu.​—Aheberi 10:24, 25.

Chifukwa chakuti Petulo anasonkhana ndi abale ake auzimu, iye anamva nkhani yoti thupi la Yesu lasowa m’manda momwe analiika ngakhale kuti anali atatsekapo bwinobwino. Choncho, Petulo ndi Yohane anathamangira kumandako. Yohane, amene mwina anali wocheperapo, ndi amene anayambirira kufika pamandapo. Koma anachita mantha kulowa m’mandamo, ataona kuti mandawo anali otsegula. Komabe Petulo sanachite mantha. Ngakhale kuti anali akupumira m’mwamba, anangofikira kulowa m’mandamo ndipo anapeza kuti Yesu mulibe.​—Yohane 20:3-9.

Kodi Petulo anakhulupirira kuti Yesu waukitsidwa? Poyamba sanakhulupirire ngakhale kuti akazi ena okhulupirika anamuuza kuti iwo auzidwa ndi angelo kuti akauze anthu kuti Yesu wauka kwa akufa. (Luka 23:55–24:11) Koma pofika madzulo a tsiku limenelo, Petulo anali atasiya kuda nkhawa ndiponso kukaika. Tsopano Yesu anali ndi moyo monga mngelo wamphamvu. Ndipo anaonekera kwa atumwi ake onse. Koma Yesu anayamba wachita chinthu china kumbali. Tsiku limenelo atumwiwo ananena kuti: “N’zoonadi, Ambuye wauka kwa akufa ndipo waonekera kwa Simoni!” (Luka 24:34) Komanso mtumwi Paulo nthawi ina analemba za tsiku lapadera limene Yesu “anaonekera kwa Kefa, kenako kwa khumi ndi awiri aja.” (1 Akorinto 15:5) Kefa ndi Simoni ndi maina ena a Petulo. Zikuoneka kuti tsiku limenelo, Yesu anaonekera kwa Petulo payekha.

Baibulo silinena zimene Yesu ndi Petulo anakambirana panthawi imeneyo. Koma tingathe kuona kuti Petulo anasangalala kwambiri kuona Mbuye wake amene ankamukonda kwambiri ali moyo. Iye anasangalalanso kukhala ndi mwayi womuuza Yesu mmene anamvera chisoni ndi zimene anachita komanso kumuuza kuti walapa. Koma chinthu chimene Petulo ankachifuna kwambiri panthawiyi chinali kukhululukidwa. Ndipo sitingakayikire kuti Yesu anamukhululukiradi ndi mtima wonse. Mkhristu amene wachimwa ayenera kukumbukira nkhani ya Petulo. Tisaganize kuti tachita tchimo limene Mulungu sangatikhululukire. Yesu anasonyeza bwino kwambiri mmene Atate wake alili, kuti ‘amakhululukira koposa.’​—Yesaya 55:7.

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Yesu Anakhululukira Petulo

Yesu anauza atumwi ake kuti apite ku Galileya kuti akakumane naye. Atafika kumeneko, Petulo anaganiza zokapha nsomba kunyanja ya Galileya ndipo anapita ndi anzake angapo. Apa n’kuti patapita nthawi yaitali kuchokera pamene Petulo anachoka kunyanja komwe anakhalako nthawi yaitali mbuyomo. Phokoso la ngalawa, mafunde, ndiponso ntchito yokoka khoka, sizinali zachilendo kwa iye. Kodi mwina usiku umenewu iye ankaganiza zimene azichita pamoyo wake popeza kuti Yesu anali atamaliza utumiki wake wa padziko lapansi? Kodi iye ankaganiza zoyambanso ntchito ya usodzi, n’kumakhala moyo wosafuna zambiri? Kaya ankaganiza chiyani, koma usiku umenewo iwo sanaphe kanthu.​—Mateyo 26:32; Yohane 21:1-3.

Komabe, kunja kukucha, munthu wina amene anali kugombe anawaitana n’kuwauza kuti aponye maukonde awo mbali ina ya ngalawayo. Iwo atachita zimenezi anapha nsomba 153. Petulo anazindikira kuti munthuyo anali Yesu. Kenako iye anachoka m’ngalawayo n’kupita kumtunda. Ali kumtundako Yesu anawapatsa nsomba zowotcha pamakala. Komabe maganizo a Yesu anali pa Petulo.

Yesu anafunsa Petulo ngati amakonda Mbuye wake “koposa izi,” kutanthauza nsomba zija. Yesu ponena mawu amenewa ayenera kuti ankaloza nsombazo. Yesu ankafuna kudziwa ngati Petulo ankakonda kwambiri ntchito yosodza kuposa iyeyo. Choncho, Yesu anamufunsa Petulo mafunso. Monga mmene Petulo anakanira Mbuye wake katatu, katatu konse, Yesu anapatsa Petulo mwayi womutsimikizira kuti amamukonda pamaso pa atumwi ena. Petulo atayankha, Yesu anamuuza kuti asonyeze chikondi chimenechi m’njira ziwiri izi: Kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba ndiponso kudyetsa ndi kuweta nkhosa za Khristu, zomwe ndi atumiki ake okhulupirika.​—Yohane 21:4-17.

Choncho, Yesu anatsimikizira kuti Petulo anali adakali munthu wofunika kwambiri kwa iye komanso kwa Atate wake. Yesu anaona kuti Petulo angagwire ntchito yofunika kwambiri mumpingo motsogoleredwa ndi Khristu. Umenewutu ndi umboni wamphamvu wakuti Yesu anakhululukira Petulo ndi mtima wonse. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinamukhudza mtima kwambiri Petulo.

Petulo anachita utumiki wake mokhulupirika kwa zaka zambiri. Iye analimbikitsa atumiki anzake monga mmene Yesu anamulamulira madzulo atsiku limene anafa. Petulo anagwira ntchito moleza mtima komanso mokoma mtima poweta ndiponso podyetsa otsatira a Khristu. Munthu ameneyu, wodziwikanso kuti Simoni, anachitadi zinthu mogwirizana ndi dzina limene Yesu anam’patsa lakuti Petulo kapena kuti Thanthwe. Iye anakhala wodalirika, wolimba ndiponso wolimbikitsa ena kuchita zabwino mumpingo. Umboni wa zimenezi timaupeza m’makalata awiri amene Petulo analemba ndipo anakhala mabuku ofunika kwambiri ndipo ali m’Baibulo. Makalata amenewa amasonyezanso kuti Petulo sanaiwale phunziro lofunika kwambiri limene anaphunzira kwa Yesu lokhudza kukhululuka.​—1 Petulo 3:8, 9; 4:8.

Nafenso tiphunzirepo mfundo imeneyi. Kodi tsiku lililonse timapempha Mulungu kuti atikhululukire zimene tamuchimwira? Ndiyeno kodi timakhulupirira kuti watikhululukira ndiponso watiyeretsa? Kodi timakhululukiranso anzathu? Ngati timachita zimenezi, ndiye kuti timatsanzira chikhulupiriro cha Petulo ndiponso chifundo cha Mbuye wake.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Petulo analakwitsa zinthu zambiri ndipo ankafunika kuti Mbuye wake amukhululukire, kodi ndani safuna kukhululukidwa tsiku lililonse?

[Chithunzi patsamba 23]

“Ambuye anacheuka ndi kuyang’ana Petulo”

[Chithunzi patsamba 24]

‘Ambuye anaonekera kwa Simoni!’