Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Yesu Anaphunzira Kumvera

Yesu Anaphunzira Kumvera

KODI nthawi zina zimakuvuta kumvera?​— * Ngati zimakuvuta sizachilendo. Tonsefe nthawi zina zimativuta kumvera. Kodi ukudziwa kuti ngakhale Yesu anachita kuphunzira kumvera?​—

Kodi ukuganiza kuti ana onse ayenera kumvera ndani?​— Inde, ayenera kumvera abambo ndi amayi awo. Baibulo limati: “Muzimvera makolo anu mwa Ambuye.” (Aefeso 6:1) Kodi bambo ake a Yesu ndi ndani?​— Yehova Mulungu, ndipo ifenso ndi Atate wathu. (Mateyo 6:9, 10) Koma ukananenanso kuti bambo ake anali Yosefe ndipo mayi ake anali Mariya, ukanalondolanso. Kodi ukudziwa kuti zinatheka bwanji kuti iwo akhale makolo ake?​—

Mngelo Gabiriele anauza Mariya zimene zidzachitike kuti aberekere mwana ngakhale kuti Mariyayo anali asanagonanepo ndi mwamuna. Yehova anachita zozizwitsa kuti Mariya akhale ndi pathupi. Gabiriele anauza Mariya kuti: “Mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”​—Luka 1:30-35.

Mulungu anatenga moyo wa Mwana wake kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Ndiyeno mwanayo anakula ngati mmene ana onse amakulira m’mimba mwa amayi awo. Itakwana miyezi 9, Yesu anabadwa. Panthawiyi Yosefe anali atakwatira Mariya, ndipo anthu ambiri ankaganiza kuti Yosefe ndiye bambo ake enieni a Yesu. Koma Yosefe anali bambo ake omulera. Choncho, chifukwa cha zimenezi tinganene kuti Yesu anali ndi abambo awiri.

Yesu ali ndi zaka 12 zokha, anachita zinthu zimene zinasonyeza kuti ankakonda kwambiri Atate wake wakumwamba, Yehova. Panthawiyo, banja lonse la Yosefe linkakonda kuyenda ulendo wautali kupita ku Yerusalemu kukachita Pasika. Pobwerera ku Nazarete, Yosefe ndi Mariya sanadziwe kuti Yesu watsala. Kodi ukudabwa kuti zinatheka bwanji kuti iwo asadziwe kuti iyeyo watsala?​—

Panthawiyi Yosefe ndi Mariya anali ndi ana ena. (Mateyo 13:55, 56) Iwo ayenera kuti analinso ndi achibale paulendowu, monga Yakobe ndi Yohane pamodzi ndi bambo awo, a Zebedayo, ndiponso mayi awo, a Salome, amene ayenera kuti anali achemwali ake a Mariya. Choncho, Mariya ayenera kuti ankaganiza kuti Yesu anali ndi azibale akewo.​—Mateyo 27:56; Maliko 15:40; Yohane 19:25.

Yosefe ndi Mariya atazindikira kuti Yesu wasowa anabwerera mofulumira ku Yerusalemu. Iwo anafunafuna mwana wawoyo koma sanam’peze. Anapitirizabe kumufufuza ndipo patsiku lachitatu, anam’peza ali m’kachisi. Mariya anafunsa Yesu kuti: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Taona, bambo ako ndi ine tazunzika m’mitima pokufunafuna iwe.” Koma iye anati kwa iwo: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Simunadziwe kodi kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”​—Luka 2:45-50.

Kodi ukuganiza kuti Yesu analakwa kuwayankha amayi ake choncho?​— Makolo ake ankadziwa kuti iye ankakonda kulambira pa nyumba ya Mulungu. (Salmo 122:1) N’chifukwa chake Yesu anaganiza kuti makolo ake akanayamba kukamuyang’ana kaye mukachisi wa Mulungu. Patapita nthawi, Mariya ankaganizirabe zimene Yesu ananenazo.

Kodi Yesu ankawaona bwanji makolo ake, Yosefe ndi Mariya?​— Baibulo limanena kuti: “[Yesu] ananyamuka nawo limodzi kubwerera ku Nazarete, ndipo anapitiriza kuwamvera.” (Luka 2:51, 52) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachitazi?​— Inde, nafenso tiyenera kumvera makolo athu.

Komabe, Yesu nthawi zina ankaona kuti ndi zovuta kumvera, ngakhale Atate ake akumwamba.

Usiku woti mawa lake afa, Yesu anapempha Yehova kuti ngati angafune asinthe zimene anamutuma kudzachita. (Luka 22:42) Komabe, Yesu anamvera Mulungu ngakhale zinali zovuta. Baibulo limanena kuti “anaphunzira kumvera mwa mavuto amene anakumana nawo.” (Aheberi 5:8) Kodi ukuganiza kuti ifenso tingachite zimenezi?​—

^ ndime 3 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.