Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dziko Lapansili Lidzatha?

Kodi Dziko Lapansili Lidzatha?

Kodi Dziko Lapansili Lidzatha?

WOLEMBA mabuku wina dzina lake John Scalzi ananena kuti: “Mafilimu osonyeza kutha kwa dziko amachititsa chidwi anthu ambiri.” N’chifukwa chiyani anthu amachita chidwi kwambiri ndi mafilimu amenewa? Scalzi anapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chakuti nkhani imeneyi imawachititsa anthu mantha.” Kodi inunso mumaona kuti kutha kwa dziko n’kochititsa mantha? Kodi pali zifukwa zomveka zoopera kutha kwa dziko?

Pafupifupi tsiku lililonse timamva za masoka achilengedwe amene amawononga zinthu zambiri padziko lonse. Zithunzi zochititsa mantha za masoka amenewa zimasonyezedwa kawirikawiri pa TV ndi pa Intaneti. Tikamaona kawirikawiri zithunzi za anthu akumwalira ndi masoka amenewa ndiponso malo akuwonongedwa, timayamba kuona kuti “kutha kwa dziko” si nkhani yongoyerekeza, koma ndi yeniyeni.

Asayansi amawonjezera mantha amenewa akamafotokoza mmene dziko lidzathere. Asayansi ena afika mpaka potchula tsiku lenileni limene dziko lidzathe. Mwachitsanzo, mu March 2008, bungwe lina la sayansi linatulutsa lipoti lonena kuti akatswiri awiri a sayansi ya zakuthambo ananena kuti dzikoli lidzatha pakatha zaka 7.59 biliyoni. Iwo akuti panthawiyi dzuwa lidzatentha kwambiri ndipo dziko lapansili lidzasungunuka.​—Monthly Notices of the Royal Astronomical Society.

Koma kodi ndi zoona kuti tsiku lina dzikoli lidzatha?

Kodi Dziko Lapansi Lidzafika Potha Ntchito?

Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.” (Mlaliki 1:4) Yehova Mulungu “anakhazika dziko lapansi pa maziko ake” ndipo analipanga kuti likhalepo ‘nthawi yonse.’ (Salmo 104:5) Kodi mumaona kuti mawu ouziridwa amenewa ndi nkhambakamwa chabe? N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira kuti dzikoli silidzatha ngakhale kuti asayansi ena amanena kuti lidzatha?

Taganizirani zinthu zimene zimagulitsidwa mu sitolo. Zina zimalembedwa tsiku limene zidzathe ntchito. Kodi ndi ndani amene amalemba tsiku limeneli? Kodi limalembedwa mongolota ndi mwini wake wa sitoloyo? Ayi. Tsikuli limalembedwa ndi munthu amene anapanga katunduyo. Timakhulupirira kuti katunduyo adzathadi ntchito pa tsiku limenelo chifukwa amene anapangayo amadziwa zambiri zokhudza katunduyo kuposa munthu wina aliyense. Ifenso tiyenera kukhulupirira zimene Mlengi wa dzikoli amanena. Mawu ake amanena momveka bwino kuti iye ‘anakhazikitsa dziko lapansi’ kuti likhale kwa muyaya. Choncho, palibe tsiku limene dzikoli lidzathe.​—Salmo 119:90.

Koma kodi n’zotheka kuti anthu oipa angawononge kwambiri dzikoli moti silingadzathekenso kulikonza? Ayi, sizingatheke chifukwa Yehova ‘akhoza kuchita zonse.’ (Yobu 42:2) N’chifukwa chake iye amanena motsimikiza kuti: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga . . . adzachita chimene ndifuna.” (Yesaya 55:11) Tiyenera kukhulupirira kuti Mlengi wathu sadzalola kuti chilichonse chimulepheretse kukwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga dziko lapansi. (Salmo 95:6) Kodi Mulungu anali ndi cholinga chotani, nanga adzachikwaniritsa bwanji?

Ufumu wa Mulungu Udzakwaniritsa Cholinga cha Mulungu

Mawu a Mulungu amatsimikizira kuti dzikoli silidzatha komanso kuti Mulungu “analiumba [kuti] akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Ngakhale kuti anthu akhala padzikoli kwa zaka zambirimbiri, cholinga cha Mulungu sichinakwaniritsidwebe.

Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo” komanso ‘amakonda chiweruzo.’ (1 Timoteyo 1:11; Salmo 37:28) Cholinga cha Mulungu ndi chakuti anthu akhale padzikoli mosangalala komanso mosaponderezedwa. Kuti akwaniritse cholinga chimenechi, Mulungu analosera kuti adzakhazikitsa Ufumu kumwamba umene udzalamulire dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44) Ali padziko lapansi pano, Yesu nthawi zonse ankalalikira za boma la Ufumu wa Mulungu. Iye anauza ophunzira ake kuti azipempherera Ufumu umenewu chifukwa ankadziwa madalitso onse amene Ufumuwo udzabweretse padziko lapansi. (Mateyo 6:9, 10; 24:14) Ena mwa madalitsowa ndi awa:

Padziko lapansi padzakhala mtendere ndi chitetezo chifukwa Mulungu analonjeza kuti adzathetsa nkhondo.​—Salmo 46:9.

Aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira.​—Salmo 72:16.

Anthu onse adzakhala ndi moyo wathanzi chifukwa “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24.

Anthu sadzakhala ndi chisoni chifukwa “imfa sidzakhalaponso.”​—Chivumbulutso 21:4.

Mulungu analonjeza kuti anthu ake adzamanga nyumba zawo, adzakhala ndi chitetezo chokwanira ndiponso adzakhala ‘mosangalala nthawi zonse.’​—Yesaya 65:17-24.

Tikukhulupirira kuti nanunso mukulakalaka kudzasangalala ndi zinthu zimenezi. Yehova akufunitsitsa kukwaniritsa zonse zimene analonjeza. (Yesaya 9:6, 7) Komabe, mwina mungamakayikire kuti: ‘Popeza kuti patha zaka zambirimbiri kuchokera pamene malonjezowa analembedwa m’Baibulo, n’chifukwa chiyani zimene Mulungu analonjezazi sizikuchitika?’

Mulungu Akuleza Nafe Mtima Kuti Tidzapulumuke

Dziwani kuti Mulungu “sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake.” Baibulo limafotokoza kuti Mulungu amatikonda kwambiri ndipo amatilezera mtima. Choncho, tikulimbikitsidwa ‘kuona kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.’ (2 Petulo 3:9, 15) Koma kodi kuleza mtima kwa Mulungu ndi chipulumutso chathu motani?

Mulungu amadziwa kuti asanapatse olungama malo abwino okhala, choyamba ayenera “kuwononga iwo owononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Komabe popeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu, iye “safuna kuti wina akawonongeke.” N’chifukwa chake Atate wathu wakumwamba akhala ‘kuchenjeza anthu oipa kuti aleke njira zawo zoipa.’ (Ezekieli 3:17, 18) Choncho, Yehova akuonetsetsa kuti uthenga wa Ufumu wake ukulalikidwa padziko lonse. * (Ezekieli 3:17, 18) Onse amene akumvera machenjezo a Mulungu n’kusintha moyo wawo kuti ugwirizane ndi mfundo zolungama za Mulungu, adzapulumutsidwa ndipo adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.

Yang’anani kwa Mulungu kuti Mudzapulumuke

Kunena zoona, Baibulo lili ndi “uthenga wabwino” kwa ife. (Mateyo 24:14) Lili ndi mawu olimbikitsa a Mulungu osonyeza kuti dziko lapansili silidzatha. Komanso, mogwirizana ndi maulosi a m’Baibulo, tiyenera kukhulupirira kuti ‘katsala kanthawi ndipo oipa adzatha psiti.’ Posachedwapa, anthu amene Mulungu amawaona kuti ndi olungama, “adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:9-11, 29; Mateyo 5:5; Chivumbulutso 21:3, 4) Koma pakali pano Mulungu apitirizabe kutilezera mtima ndi kutipempha kuti: “Yang’anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko.” (Yesaya 45:22) Kodi inuyo mumvera pempho limeneli?

Mungachite bwino kuyesetsa kuyang’ana kwa Mulungu. Lemba la Salmo 37:34 limati: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.” Mboni za Yehova zingakuthandizeni kudziwa zambiri za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi ndi zimene mungachite kuti mudzaone cholinga chimenechi chikukwaniritsidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Pomvera lamulo la Yesu la pa Mateyo 28:19, 20, Mboni za Yehova zoposa 7 miliyoni m’mayiko 236 zimatha maola 1.5 biliyoni chaka chilichonse kuphunzitsa anthu za cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansili.

[Mawu a Chithunzi patsamba 22]

NASA photo