Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Wodzichepetsa Ndiponso Wolimba Mtima

Munthu Wodzichepetsa Ndiponso Wolimba Mtima

 Zoti Achinyamata Achite

Munthu Wodzichepetsa Ndiponso Wolimba Mtima

YONA​—GAWO 1

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI YONA 1:1-17; 2:10–3:5.

Kodi mukuganiza kuti panyanjapo pankaoneka bwanji ndiponso pankamveka phokoso lotani chifukwa cha mphepo yamkutho?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti zimene Yona ndiponso anthu oyendetsa chombocho ananena zikusonyeza kuti ankamva bwanji mumtima mwawo?

․․․․․

Fotokozani zimene Yona ayenera kuti ankaganiza panthawi imene ankamira m’nyanja ndiponso ali m’mimba mwa chinsomba. (Werengani Yona 2:1-9.)

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Kodi ku Nineve kunkakhala anthu otani, nanga n’chifukwa chiyani poyamba Yona sanafune kuwalalikira anthu amenewa? (Nahumu 3:1)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Mulungu ankaona kuti Nineve unali “mudzi waukulu pamaso” pake? (Yona 3:3; 2 Petulo 3:9)

․․․․․

Popeza kuti Yona ananena zoona zokhazokha za tchimo lake ndiponso za Mulungu,  kodi zimenezi zikusonyeza kuti iye anali munthu wotani? (Werenganinso Yona 1:9, 10.)

․․․․․

Kodi Yona ayenera kuti anadziwa bwanji zimene zinachitika m’chombocho iye ataponyedwa m’nyanja? (Werenganinso Yona 1:15, 16.)

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . 

Mantha.

․․․․․

Kudzichepetsa.

․․․․․

Kulimba mtima.

․․․․․

Mmene Yehova amaonera anthu ngakhale amene timawaona kuti ndi oipa kwambiri.

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Kuti mudziwe zambiri, werengani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2009, tsamba 25-28.

NGATI MULIBE BAIBULO, MUNGAWERENGE LA PA INTANETI PA WEBUSAITI YATHU YA www.jw.org.