Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Pitiriza Kudzipereka pa Kuphunzitsa’

‘Pitiriza Kudzipereka pa Kuphunzitsa’

‘Pitiriza Kudzipereka pa Kuphunzitsa’

YESU anauza ophunzira ake kuti: “Inu mumanditcha kuti ‘Mphunzitsi,’ ndi, ‘Ambuye,’ mumalondola, pakuti ndinedi.” (Yoh. 13:13) Mwa kunena mawu amenewa, Yesu anatsindika udindo wake monga mphunzitsi. Ndiyeno Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba analamula otsatira ake kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse . . . kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mat. 28:19, 20) Kenako mtumwi Paulo anatsindikanso kufunika kokhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Iye analangiza Timoteyo yemwe anali mkulu wachikhristu kuti: “Pitiriza kudzipereka pa kuwerenga pamaso pa anthu, kuwadandaulira, ndi kuwaphunzitsa. . . . Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.”​—1 Tim. 4:13-15.

Masiku anonso, kuphunzitsa n’kofunika kwambiri mu utumiki ndiponso pa misonkhano ya mpingo. Kodi tingatani kuti tipitirize kudzipereka pa kuphunzitsa, ndipo kodi kuchita zimenezi kungatithandize bwanji kuti tipite patsogolo monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu?

Tsanzirani Mphunzitsi Waluso

Anthu ambiri ankakopeka ndi kaphunzitsidwe ka Yesu. Taonani mmene anthu ambiri anakhudzidwira ndi mawu ake m’sunagoge wa ku Nazareti. Mu Uthenga Wabwino umene Luka analemba, anati: “Onse anayamba kumutamanda ndi kudabwa ndi mawu ogwira mtima otuluka pakamwa pake.” (Luka 4:22) Ophunzira a Yesu anatengera chitsanzo cha Mbuye wawo polalikira. Ndipotu mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.” (1 Akor. 11:1) Chifukwa chakuti Paulo anatengera kaphunzitsidwe ka Yesu, anali wogwira mtima kwambiri ‘pophunzitsa poyera komanso ku nyumba ndi nyumba.’​—Mac. 20:20.

Ankaphunzitsa “Pamsika”

Nkhani ya pa Machitidwe chaputala 17, imasonyeza kuti Paulo ankaphunzitsa mwaluso kwambiri. Chaputala chimenechi chimafotokoza zimene iye anachita ku Girisi mumzinda wa Atene. Paulo anaona kuti m’misewu ndiponso m’malo mmene mumapezeka anthu ambiri mumzindawu munali mafano. Mpake kuti Paulo anadabwa kwambiri ndi zimenezi. Koma sanakwiye kapena kupsa mtima ndi zimenezi. M’malo mwake, iye ‘anayamba kukambirana ndi anthu m’sunagoge. Anateronso tsiku ndi tsiku ndi amene anali kuwapeza pa msika.’ (Mac. 17:16, 17) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Tikamayesetsa kulalikira kwa anthu onse, osati mowatsutsa koma mwaulemu, zingathandize kuti amvetsere ndiponso kuti kenako amasuke ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga.​—Mac. 10:34, 35; Chiv. 18:4.

Anthu ambiri amene Paulo anawapeza pamsika sanamvetsere uthenga wake. Ena mwa anthuwa anali akatswiri a maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba ndipo mfundo zimene ankayendera zinali zotsutsana ndi choonadi chimene Paulo ankalalikira. Anthuwa atayamba kumutsutsa, iye anaganizira kwambiri mfundo zimene anthuwo ankanena. Anthu ena anamutcha “wotola njere” mawu amene m’Chigiriki amatanthauza “wobwetuka.” Ena ankanena kuti: “Akuoneka kuti ndi wofalitsa milungu yachilendo.”​—Mac. 17:18.

Komabe Paulo sanakhumudwe ndi mawu onyoza a anthu amene ankawalalikirawa. Iye atafunsidwa kuti afotokoze zimene ankaphunzitsa anapezerapo mwayi ndipo anakamba nkhani yogwira mtima kwambiri imene inasonyeza kuti anali ndi luso lophunzitsa. (Mac. 17:19-22; 1 Pet. 3:15) Tsopano tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane nkhani imene iye anakamba. Nkhani imeneyi itithandiza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa.

Yambani ndi Zinthu Zimene Sangatsutse

Paulo anati: “Amuna inu a mu Atene, ndaona kuti m’zinthu zonse inu m’maopa kwambiri milungu kuposa mmene ena amachitira. Mwachitsanzo, pamene ndinali . . . kuyang’anitsitsa zinthu zimene m’mazilambira, ndapezanso guwa la nsembe lolembedwa kuti ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Chotero wosadziwikayo amene inuyo mukum’lambira, ameneyo ndi amene ndikum’lalika kwa inu.”​—Mac. 17:22, 23.

Paulo ankachita chidwi kwambiri ndi zinthu zimene waona. Zinthu zimene ankaona zinkamuthandiza kudziwa zambiri zokhudza anthu amene ankawalalikirawo. Ifenso tingadziwe zambiri za anthu amene tikuwalalikira ngati tichita chidwi kwambiri ndi zinthu zimene taona pakhomo pawo. Mwachitsanzo, zidole zimene zili pakhomo kapena zizindikiro zimene zili pachitseko zingatithandize kudziwa zambiri. Ngati tadziwa zinthu zina zokhudza mwininyumbayo, tikhoza kusankha bwino mawu ndiponso mmene tingalankhulire.​—Akol. 4:6.

Paulo ankalalikira uthenga wake m’njira yolimbikitsa. Iye anaona kuti anthu a ku Atene anali okonda ‘kulambira’ koma vuto lawo linali lakuti sankadziwa zinthu molondola. Paulo anawasonyeza bwinobwino zimene akanachita kuti azilambira Mulungu woona. (1 Akor. 14:8) Ndiyetu m’pofunika kuti tizilankhula momveka bwino ndiponso molimbikitsa tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu.

Muzikhala Osamala Ndiponso Opanda Tsankho

Paulo anapitiriza kunena kuti: “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, Iyeyu ndiye Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja. Satumikiridwanso ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu, chifukwa ndi iye amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.”​—Mac. 17:24, 25.

Pa lembali, Paulo anauza anthu kuti Yehova ndiye amapereka moyo. Iye anachita zimenezi mwaluso ponena kuti, Yehova ndi “Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndi mwayitu waukulu kuthandiza anthu a mtima wabwino a m’zipembedzo ndiponso a zikhalidwe zosiyanasiyana kumvetsa kuti amene amapereka moyo ndi Yehova Mulungu.​—Sal. 36:9.

Kenako Paulo anafotokoza kuti: “Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu, . . . Iye anakhazikitsanso nthawi zoikika ndi kuika malire a pokhalapo anthu. Anatero kuti anthuwo afunefune Mulungu, ngati angam’papase ndi kum’pezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”​—Mac. 17:26, 27.

Kaphunzitsidwe kathu kangathandize anthu kudziwa Mulungu amene timamulambira. Chifukwa chakuti Yehova alibe tsankho, amalola kuti anthu a mitundu yonse ‘am’papase ndi kum’pezadi.’ Ifenso timalalikira mopanda tsankho anthu amene timakumana nawo. Timayesetsa kuthandiza anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mlengi kuti akhale naye paubwenzi umene ungawathandize kudzapeza madalitso osatha. (Yak. 4:8) Koma kodi tingathandize bwanji anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu? Tingachite zimenezi mwa kutsatira chitsanzo cha Paulo. Taonani zimene iye kenako ananena.

“Pakuti mwa iye tili ndi moyo, timayenda, ndi kukhalapo, monga mmene andakatulo ena pakati panu anenera kuti, ‘Pakuti tilinso mbadwa zake.’ Popeza kuti tili mbadwa za Mulungu, tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide kapena siliva kapena mwala, kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.”​—Mac. 17:28, 29.

Apatu Paulo pofuna kukopa chidwi cha omvera, anagwira mawu a olemba ndakatulo amene anthu a ku Atenewo ankawadziwa ndiponso kuwakhulupirira. Ifenso tiyenera kuyesetsa kuti tiziyamba ndi kutchula zinthu zimene tikudziwa kuti omvera athu sangatsutse. Mwachitsanzo, fanizo la Paulo m’kalata imene analembera Aheberi ndi logwira mtima ngakhale masiku ano. Iye anati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Kuthandiza omvera athu kuti aganizire fanizo losavuta limeneli, kungawachititse kudziwa kuti zimene tikunena n’zoona. Onaninso kuti m’nkhani yake, Paulo anagwiritsa ntchito njira ina imene inathandiza kuti kaphunzitsidwe kake kakhale kogwira mtima. Iye ankaphunzitsa mwa njira yolimbikitsa munthu kuchitapo kanthu.

Tsindikani Kufunika Kochitapo Kanthu Mwamsanga

Paulo anati: “Inde, Mulungu analekerera nthawi ya kusadziwa koteroko, koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape. Pakuti wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika.”​—Mac. 17:30, 31.

Kanthawi kamene Mulungu walola kuti zoipa zichitike kakutipatsa mpata womusonyeza zimene zili mumtima mwathu. Choncho, m’pofunika kuti tizitsindika kufunika kochitapo kanthu mwamsanga ndiponso tizilankhula mokopa za madalitso amene Ufumu wa Mulungu, umene wayandikira, udzabweretse.​—2 Tim. 3:1-5.

Anthu Amalandira Uthenga Wathu Mosiyanasiyana

“Pamenepo, atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka monyodola, pamene ena anati: ‘Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.’ Choncho Paulo anachoka pakati pawo. Koma anthu ena anadziphatika kwa iye nakhala okhulupirira.”​—Mac. 17:32-34.

Tikamalalikira, anthu ena amalabadira nthawi yomweyo, koma ena amatenga nthawi ndithu kuti akhulupirire zimene tikunenazo. Tikathandiza ngakhale munthu mmodzi kudziwa Yehova molondola, chifukwa chakuti tamufotokozera momveka bwino ndiponso m’njira yosavuta kumva, timasangalala kwambiri. Izi zimakhala choncho chifukwa timadziwa kuti Mulungu watigwiritsa ntchito kukokera anthu kwa Mwana wake.​—Yoh. 6:44.

Zimene Tikuphunzirapo

Tikaganizira nkhani ya Paulo imeneyi, tingaphunzire mfundo zambiri zimene zingatithandize kufotokozera anthu choonadi cha m’Baibulo. Ngati timakamba nkhani za onse mumpingo, tiziyesetsa kutsanzira Paulo mwa kusankha bwino mawu. Tizisankha mawu amene angathandize kuti anthu osakhulupirira amvetse ndiponso kukhulupirira choonadi cha m’Baibulo. Tiyenera kufotokoza choonadi chimenechi momveka bwino koma tiyeneranso kusamala kuti tisanyoze zikhulupiriro za anthu ena amene abwera kudzasonkhana nafe. N’chimodzimodzinso tikamalalikira, tiziyesetsa kulankhula mokopa koma mosamala. Tikamachita zimenezi, timakhala tikutsatira malangizo a Paulo akuti, ‘tipitirize kudzipereka pophunzitsa.’

[Chithunzi patsamba 30]

Paulo ankaphunzitsa mwaluso, momveka bwino ndiponso m’njira yosavuta kumva

[Chithunzi patsamba 31]

Timatsanzira Paulo mwa kuchita zinthu zoganizira anthu amene tikuwalalikirawo