Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Tcheru Kumakhala ndi Zotsatira Zabwino

Kukhala Tcheru Kumakhala ndi Zotsatira Zabwino

 Kukhala Tcheru Kumakhala ndi Zotsatira Zabwino

KODI mumakhala tcheru kuti muzindikire zimene zikuchitika m’gawo la mpingo wanu zomwe zingakupatseni mwayi wolalikira? Abale athu omwe amakhala ku Finland mumzinda wa Turku, womwe uli m’mphepete mwa nyanja, pa nthawi ina anachita zinthu zosonyeza kuti anali tcheru ndipo zotsatira zake zinali zabwino.

Pa nthawi ina, abale a ku Turku anazindikira kuti m’dera lawo mwabwera gulu la Amwenye. Amwenyewa anapita kumaloku kuti akamalizitse ntchito yokonza sitima yaikulu yapamadzi imene inkakonzedwa padoko lina lokonzera sitima. Ndiyeno, m’bale wina anafufuza mahotela amene anthuwa ankakhalamo. Iye anazindikiranso kuti m’mawa uliwonse anthuwa ankatengedwa pa mabasi kuchokera m’mahotela kupita kudokoli. Nthawi yomweyo, anadziwitsa abale a mpingo wa Chingelezi a mumzinda wa Turku.

Akulu mumpingowu anaona kuti kufika kwa alendowa kuwapatsa mwayi woti awalalikire uthenga wa Ufumu ndipo nthawi yomweyo anakonza zoti pakhale ntchito yapadera yolalikira. Mlungu womwewo pa tsiku Lamlungu, ofalitsa 10 anasonkhana pasiteji ya basi 7 koloko m’mawa. Atafika pasitejipo sanapeze munthu aliyense. Ndiye anayamba kufunsana kuti: ‘Kodi tachedwa eti? Kapena apita kale?’ Koma kenako panafika munthu wina atavala ovolosi. Kenako panafikanso anthu ena. Pasanapite nthawi gulu la anthu ambirimbiri linafika pamalowo. Abale ndi alongo aja anayamba kulalikira pogwiritsa ntchito mabuku a Chingelezi. Mwamwayi, panatenga pafupifupi ola lathunthu kuti anthu onse apeze malo okhala m’mabasi. Izi zinapereka mwayi kwa abale aja kuti akhale ndi nthawi yokwanira yowalalikira. Pamene mabasiwo ankanyamuka n’kuti abalewa atawapatsa anthuwo timabuku 126 ndi magazini 329.

Zimenezi zinalimbikitsa abalewo ndipo anaganiza zobwererako mlungu wotsatira pa nthawi imene anali ndi woyang’anira dera. Tsiku limene amabwererako kunali mvula ndipo woyang’anira dera anachititsa msonkhano wokonzekera utumiki 6:30 m’mawa. Ofalitsa okwana 24 anapita kukalalikira pamalo okwerera basi aja. Pa tsikuli iwo anatenga mabuku a Chitagalogi chifukwa chakuti anazindikira kuti ena mwa anthuwo anali ochokera ku Philippines. Pamene mabasiwa ankanyamuka, n’kuti abalewo atagawira mabuku 7, timabuku 69 ndi magazini 479. Kodi mukuganiza kuti abale ndi alongo amene anagwira ntchitoyi anamva bwanji?

Pa nthawi imene anthuwa anali kuderali, abale ena ankapita m’mahotela amene ankakhala kuti akakambirane nawo zambiri zokhudza uthenga wa Ufumu. Ena mwa anthuwa ananena kuti anakumanapo ndi Mboni m’mayiko ena. Iwo anayamikira kwambiri abalewa chifukwa choyesetsa kuwalalikira pa nthawi imene anali ku Finland.

Kodi inunso mumakhala tcheru ndi zimene zikuchitika m’gawo la mpingo wanu, kuti mulalikire ngati mwayi utapezeka? Kodi mumayesetsa kuti mulalikire kwa anthu a mitundu ndi zikhalidwe zosiyanasiyana? Mukamatero mudzasangalala ngati mmene anachitira abale athu a ku Turku.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 32]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

FINLAND

HELSINKI

Turku

[Mawu a Chithunzi]

STX Europe