Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Usaope Ndidzakuthandiza”

“Usaope Ndidzakuthandiza”

 “Usaope Ndidzakuthandiza”

YESU anachenjeza ophunzira ake kuti “Mdyerekezi adzapitiriza kuponya m’ndende ena a inu, kuti muyesedwe kotheratu.” Koma asanawachenjeze zimenezi ananena kuti: “Usachite mantha ndi mavuto amene uti ukumane nawo.” Popeza Satana akupitirizabe kuopseza anthu mwa kuwatsekera m’ndende n’cholinga cholepheretsa ntchito yolalikira za Ufumu, n’zoonekeratu kuti maboma ena adzazunza Akhristu oona. (Chiv. 2:10; 12:17) Choncho potsatira malangizo a Yesu, kodi n’chiyani chingatithandize kukonzekera misampha ya Satana komanso ‘kusachita mantha’?

Kunena zoona ambiri a ife pa nthawi ina tinachitapo mantha. Komabe, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova angatithandize kuti tithetse mantha. Kodi angachite bwanji zimenezi? Njira imodzi imene Yehova amatithandizira kukonzekera chitsutso, ndi mwa kutiuza misampha imene Satana ndi ziwanda zake amagwiritsa ntchito. (2 Akor. 2:11) Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tikambirane nkhani imene inachitika m’nthawi ya Baibulo. Tionanso zitsanzo za masiku ano za Akhristu anzathu okhulupirika amene ‘anachirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi.​—Aef. 6:11-13.

Mfumu Yoopa Mulungu Inaopsezedwa ndi Wolamulira Woipa

M’zaka za m’ma 700 B.C.E., Mfumu Sanakeribu ya Asuri, yomwe inali yoipa, inagonjetsa mitundu yambiri ya anthu motsatizanatsatizana. Chifukwa cha zimenezi, mfumuyi inakhala ndi chikhulupiriro chakuti igonjetsanso anthu a Yehova ndi likulu lawo ku Yerusalemu, kumene Mfumu Hezekiya yoopa Mulungu inkalamulira. (2 Maf. 18:1-3, 13) Mosakayikira, Satana anapezerapo mpata wolimbikitsa Sanakeribu kukwaniritsa zolinga za Satanayo kuti athetse kulambira koona padziko lapansi.​—Gen. 3:15.

Sanakeribu anatumiza nthumwi ku Yerusalemu kuti zikauze anthu a mumzindawo kuti avomereze kugonja popanda nkhondo. Mmodzi mwa anthu amene anatumidwa anali Rabisake yemwe anali nduna ya mfumu ndiponso wolankhulira mfumuyo. * (2 Maf. 18:17) Cholinga cha Rabisake chinali kufooketsa Ayuda n’kuwachititsa kuti angogonja popanda kumenyana. Kodi iye anagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kuti Ayuda achite mantha?

Anakhalabe Okhulupirika Ngakhale Kuti Anali Paokha

Rabisake anauza nthumwi za Hezekiya kuti: “Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri, Chikhulupiriro ichi n’chotani uchikhulupirira? . . . Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Aigupto; ndilo munthu akatsamirapo lidzam’lowa m’dzanja lake ndi kuliboola.” (2 Maf. 18:19, 21) Zimene Rabisake ananenazi  zinali zabodza chifukwa Hezekiya sanapange mgwirizano ndi Iguputo. Komabe mawu onyozawa akusonyeza kuti Rabisake ankafuna kuti Ayuda azikumbukira bwinobwino kuti palibe amene adzawathandiza ndipo anali okha.

Masiku anonso anthu amene amatsutsa kulambira koona amaopseza Akhristu oona powauza kuti ali okha. Mlongo wina amene anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake anaikidwa kwayekha kwa zaka zingapo. Pofotokoza zimene zinamuthandiza kuti asachite mantha, iye anati: “Pemphero linandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. . . . Ndinkakumbukira zimene lemba la Yesaya 66:2 limanena kuti, Mulungu amayang’ana ‘munthu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka.’ Zimenezi zinkandilimbikitsa ndiponso kunditonthoza kwambiri.” M’bale winanso amene anakhala m’ndende kwayekha kwa zaka zambiri anati: “Ndinazindikira kuti ngati munthu ali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, sangaone ngati ali yekha ngakhale atatsekeredwa yekhayekha m’kachipinda kakang’ono ka kundende.” Kunena zoona, ubwenzi wabwino ndi Yehova unapatsa mphamvu Akhristu awiriwa kuti athe kupirira pamene anali kwaokha. (Sal. 9:9, 10) Anthu owazunzawo anasiyanitsa abale ndi alongowa ndi mabanja awo, mabwenzi awo ndiponso okhulupirira anzawo koma sanawasiyanitse ndi Yehova.​—Aroma 8:35-39.

Malinga ndi zimene taonazi, kodi si bwino kuyesetsa kwambiri kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova? (Yak. 4:8) Choncho nthawi zonse tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti Yehova ndi weniweni? Kodi mawu ake amanditsogolera ndikamasankha zochita pamoyo wanga, kaya zazing’ono kapena zazikulu?’ (Luka 16:10) Ngati timayesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu, palibe chifukwa choti tizichitira mantha. Polankhula m’malo mwa Ayuda amene ankavutika, mneneri Yeremiya anati: “Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m’dzenje lapansi. . . . Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.”​—Maliro 3:55-57.

Analephera Kuwafooketsa ndi Mawu Owachititsa Kukayikira

Mochenjera, Rabisake anagwiritsa ntchito mawu ochititsa anthu kukayikira. Iye anafunsa kuti, kodi Yehova “sindiye amene Hezekiya wam’chotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake? . . . Yehova anati kwa ine, kwelera dziko ili ndi kuliwononga.” (2 Maf. 18:22, 25) Apa Rabisake ankatanthauza kuti Yehova sangamenyere nkhondo anthu ake chifukwa chakuti sakusangalala nawo. Koma izi sizinali zoona. Yehova ankasangalala kwambiri ndi Hezekiya ndiponso Ayuda amene anayambiranso kulambira koona.​—2 Maf. 18:3-7.

Masiku anonso, anthu amene amakonza chiwembu kuti atizunze angatiuze zinthu zina zomwe ndi zoona ndithu pofuna kutikopa n’cholinga choti mochenjera atichititse kukhala ndi maganizo okayikira. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena amene anamangidwa, nthawi zina anauzidwapo kuti m’bale waudindo m’dziko lawo wasiya chikhulupiriro chake. Ndiyeno anawauza kuti palibe vuto ngati nawonso atasiya chikhulupiriro chawo. Koma Akhristu ozindikira sayamba kukhala ndi maganizo okayikira ngakhale atauzidwa zinthu zoterezi.

Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iye ali kundende, anamuonetsa mapepala osonyeza kuti m’bale wina waudindo wasiya chikhulupiriro chake. Munthu amene ankafunsa mafunsoyo, anafunsa mlongoyu  ngati ankakhulupirira Mboni imeneyo. Mlongoyo anayankha kuti, “Nayenso ndi munthu wopanda ungwiro.” Anawonjezeranso kuti Mulungu ankamugwiritsa ntchito pa nthawi imene ankatsatira mfundo za m’Baibulo. Kenako anati: “Koma poti zimene walembazi zikusonyeza kuti sakutsatira mfundo za m’Baibulo, tsopano si m’bale wanganso.” Mlongo wokhulupirikayu anachita zinthu mwanzeru potsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”​—Sal. 146:3.

Kudziwa molondola Mawu a Mulungu ndiponso kutsatira malangizo ake kudzatiteteza ku mabodza amene angatilepheretse kupitirizabe kupirira. (Aef. 4:13, 14; Aheb. 6:19) Choncho, tiyenera kukonzekera kuti tiziganiza bwinobwino tikapanikizika. Tingachite zimenezi, mwa kuonetsetsa kuti kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kuphunzira patokha timakuika pamalo oyamba m’moyo wathu. (Aheb. 4:12) Inoyo ndiyo nthawi yophunzira zambiri ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. M’bale wina amene anapirira atatsekeredwa m’ndende kwayekhayekha kwa zaka zambiri anati: “Ndikulimbikitsa aliyense kuti aziona kuti chakudya chauzimu chonse chimene timalandira ndi chofunika kwambiri, chifukwa tikudziwa kuti nthawi ina chakudya chimenechi n’chimene chidzatithandize.” Tikamaphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndi mabuku ofalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, ndiye kuti tikadzakumana ndi mayesero, mzimu woyera ‘udzatikumbutsa zinthu zonse’ zimene tinaphunzira.​—Yoh. 14:26.

Anathandizidwa Kuti Asachite Mantha

Rabisake anayesetsa kuti aopseze Ayuda. Iye anati: “Mukokerane [Mubetcherane] tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo. Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata aang’ono a mbuye wanga?” (2 Maf. 18:23, 24) Kunena zoona, Hezekiya ndi anthu ake sakanatha kumenyana ndi asilikali amphamvu a mfumu ya Asuri.

Masiku anonso anthu otizunza angaoneke ngati amphamvu kwambiri makamaka ngati akuthandizidwa ndi akuluakulu a boma. Ndi mmenetu zinthu zinkaonekeranso ndi a Nazi amene ankazunza Mboni za Yehova pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Iwo anayesetsa kuopseza atumiki ambiri a Mulungu. M’bale wina amene anakhala m’ndende zaka zambiri anafotokoza mmene apolisi anamuopsezera. Pa nthawi ina wapolisi anamufunsa kuti: “Waona mmene mng’ono wakoyu waphedwera? Waphunzirapo chiyani pamenepa?” Iye anayankha kuti: “Ine ndine mboni ya Yehova ndipo ndikhalabe Mboni zivute zitani?” Pamenepo wapolisiyo anamuopseza kuti: “Ndiyetu nawenso uphedwa.” Ngakhale zinali choncho, m’bale wathuyo sanagonje ndipo wozunzayo anamusiya. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kulimba mtima? Iye anati: “Ndinkakhulupirira dzina la Yehova.”​—Miy. 18:10.

Tikamakhulupirira kwambiri Yehova timanyamula chishango chachikulu chimene chimatiteteza ku zida zonse zimene Satana amagwiritsa ntchito kuti ativulaze mwauzimu. (Aef. 6:16) Choncho ndi bwino kuti tizipempha Yehova kuti atithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu. (Luka 17:5) Tiyenera kugwiritsanso ntchito bwino zinthu zonse zolimbitsa chikhulupiriro zimene gulu la kapolo wokhulupirika limatipatsa. Tikamaopsezedwa, timalimbikitsidwa pokumbukira mawu amene Yehova anauza mneneri Ezekieli yemwe ankalalikira anthu ouma khosi. Yehova anamuuza kuti: “Ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zawo; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yawo. Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa.” (Ezek. 3:8, 9) Mofanana ndi Ezekieli, Yehova angatilimbitse ngati mwala wolimbitsitsa ngati patafunika kutero.

Tizigonjetsa Mayesero

Anthu otsutsa akazindikira kuti njira zawo zonse zalephera, amaona kuti kunyengerera  anthu kuti awapatsa zinthu kungachititse kuti anthuwo asiye kukhala okhulupirika. Rabisake nayenso anagwiritsa ntchito njira imeneyi. Iye anauza anthu a ku Yerusalemu kuti: “Itero mfumu ya Asuri, mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, . . . mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafa ayi.” (2 Maf. 18:31, 32) Lonjezo lakuti akadya mkate ndi kumwa vinyo watsopano linamveka labwino kwambiri kwa anthu amene anali mumzinda umene unali utazunguliridwa ndi adani.

Apolisi ena anagwiritsa ntchito lonjezo ngati limeneli pofuna kufooketsa chikhulupiriro cha m’mishonale wina amene anali m’ndende. Iye anauzidwa kuti akaikidwa “kunyumba yabwino” yokhala ndi “malo okongola” kwa miyezi 6 n’cholinga choti akaganize bwinobwino. Koma m’baleyu anakhalabe wokhulupirika ndipo sanasiye kutsatira mfundo za m’Baibulo. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye ananena kuti: “Nthawi zonse ndinkaona kuti lonjezo la Ufumu ndi lodalirika. . . . Kudziwa bwino za Ufumu wa Mulungu, ndiponso kuukhulupirira, osakayikira ngakhale pang’ono, kunandilimbitsa moti ndinakhalabe wokhulupirika.”

Kodi ifeyo timaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni? Abulahamu, mtumwi Paulo ndi Yesu anapirira mayesero chifukwa chakuti Ufumu wa Mulungu unalidi weniweni kwa iwo. (Afil. 3:13, 14; Aheb. 11:8-10; 12:2) Ifenso tiyenera kupitirizabe kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo m’moyo wathu n’kumaganizira madalitso osatha amene udzabweretse. Tikamatero, sitidzakopeka ndi zinthu zongobweretsa mpumulo wosakhalitsa.​—2 Akor. 4:16-18.

Yehova Sadzatisiya

Ngakhale kuti Rabisake anayesetsa kuchita zonse zimene akanatha poopseza Hezekiya ndi Ayuda onse, iwo anakhulupirirabe Yehova ndi mtima wonse. (2 Maf. 19:15, 19; Yes. 37:5-7) Ndiyeno Yehova anayankha mapemphero awo mwa kutumiza mngelo amene anapha asilikali 185,000 mumsasa wa Asuri usiku umodzi. Tsiku lotsatira Senakeribu mwamanyazi anabwerera ku Nineve, lomwe linali likulu la dziko lake, ndi asilikali ochepa amene anatsala.​—2 Maf. 19:35, 36.

Apa zikuonekeratu kuti Yehova sanasiye anthu amene ankamukhulupirira. Zitsanzo za masiku ano za abale ndi alongo amene akhalabe okhulupirika poyesedwa, zikusonyezanso kuti Yehova sasiya atumiki ake. Choncho mpake kuti Atate wathu wa kumwamba akutitsimikizira kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.”​—Yes. 41:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 “Rabisake” linali dzina la udindo m’boma la Asuri. Dzina lenileni la munthuyu silitchulidwa m’nkhaniyi.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

M’Mawu ake, Yehova amatsimikizira atumiki ake maulendo 30 kuti, “Usaope”

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi njira zimene Rabisake anagwiritsa ntchito zimafanana bwanji ndi njira zimene adani a anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito masiku ano?

[Zithunzi patsamba 15]

Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kumatithandiza kukhalabe okhulupirika tikamakumana ndi mayesero