Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mzimu Umafufuza . . . Zinthu Zozama za Mulungu”

“Mzimu Umafufuza . . . Zinthu Zozama za Mulungu”

 “Mzimu Umafufuza . . . Zinthu Zozama za Mulungu”

“Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”​—1 AKOR. 2:10.

1. Kodi pa 1 Akorinto 2:10 Paulo anafotokoza kuti mzimu woyera umagwira ntchito yotani, ndipo kodi zimenezi zikubweretsa mafunso ati?

TIKUYAMIKIRA kwambiri kuti mzimu woyera wa Yehova ukugwira ntchito masiku ano. Malemba amati mzimu woyera ndi mthandizi, mphatso, wochitira umboni ndiponso umachonderera m’malo mwa ife. (Yoh. 14:16; Mac. 2:38; Aroma 8:16, 26, 27) Mtumwi Paulo anafotokoza mbali ina yofunika kwambiri imene mzimu woyera umachita. Iye anati: “Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:10) Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kuti atithandize kumvetsa mfundo zozama za choonadi. Popanda thandizo la mzimu woyera sitikanatha kumvetsa zolinga za Yehova. (Werengani 1 Akorinto 2:9-12.) Komabe pali mafunso ofunika kuwaganizira. Kodi ‘mzimu umafufuza bwanji zinthu zozama za Mulungu?’ Kodi m’nthawi ya atumwi Yehova anagwiritsa ntchito ndani poulula zinthu zimenezi? Kodi masiku ano mzimu umafufuza bwanji zinthu zozama ndipo kodi umachita zimenezi kudzera mwa ndani?

2. Kodi mzimu unali kudzagwira ntchito m’njira ziwiri ziti?

2 Yesu anasonyeza kuti mzimu udzagwira ntchito m’njira ziwiri. Atatsala pang’ono kuphedwa, anauza atumwi ake kuti: “Koma mthandizi, mzimu woyera, umene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.” (Yoh. 14:26) Choncho mzimu woyera unali kudzawaphunzitsa Akhristu zinthu  zimene poyamba sanazimvetse. Unalinso kudzawakumbutsa zinthu zimene anaphunzira kuti azigwiritse ntchito moyenera.

M’nthawi ya Atumwi

3. Kodi ndi mawu ati a Yesu amene anasonyeza kuti “zinthu zozama za Mulungu” zidzaululidwa pang’onopang’ono?

3 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mfundo zambiri za choonadi zimene ophunzirawo sankazidziwa. Komabe panali zinthu zambiri zoti aphunzire. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma simungathe kuzimvetsa zonsezo pakali pano. Koma iyeyo akadzafika, mzimu wa choonadi, adzakutsogolerani m’choonadi chonse.” (Yoh. 16:12, 13) Choncho Yesu anasonyeza kuti zinthu zozama zauzimu zidzaululidwa pang’onopang’ono kudzera mwa mzimu woyera.

4. Pa Pentekosite mu 33 C.E., kodi mzimu woyera unagwira bwanji ntchito yophunzitsa ndiponso yokumbutsa?

4 Pa Pentekosite mu 33 C.E., Akhristu 120 amene anasonkhana pamodzi ku Yerusalemu analandira “mzimu wa choonadi.” Anthu anaona ndiponso kumva umboni wakuti Akhristuwo alandira mzimu. (Mac. 1:4, 5, 15; 2:1-4) Ophunzirawo analankhula m’malilime osiyanasiyana “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:5-11) Iyi inali nthawi yoti zinthu zina zatsopano zidziwike. Mneneri Yoweli anali atalosera kale za kutsanulidwa kwa mzimu woyera. (Yow. 2:28-32) Anthu amene analipo anaona kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu m’njira imene aliyense sankayembekezera. Ndipo mtumwi Petulo anafokoza zimene zinkachitikazi. (Werengani Machitidwe 2:14-18.) Apatu mzimu woyera unaphunzitsa Petulo kuti zimene zinachitikira ophunzirawo zinali zogwirizana ndi zimene ulosi wakalewu unalosera. Popeza Petulo sanangogwira mawu a m’buku la Yoweli lokha koma anagwiranso mawu a Masalmo awiri a Davide, ndiye kuti mzimuwo unamukumbutsanso zinthu zimene anaphunzira. (Sal. 16:8-11; 110:1; Mac. 2:25-28, 34, 35) Zimene anthu amene anasonkhana patsikuli anaona ndiponso kumva, zinalidi zinthu zozama za Mulungu.

5, 6. (a) Pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., ndi nkhani ziti zokhudza pangano latsopano zimene zinafunika kuzimvetsa? (b) Kodi ndani anabweretsa nkhanizi kuti akambirane, ndipo anasankha bwanji zochita?

5 Panali zinthu zambiri zimene Akhristu oyambirira anafunikabe kuzimvetsa. Mwachitsanzo, anafunika kudziwa za pangano latsopano limene linakhazikitsidwa pa Pentekosite chaka cha 33 C.E. Kodi amene anali m’pangano latsopanoli anali Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda okha? Kodi anthu amitundu ina akanakhala nawonso m’panganoli ndiponso kudzozedwa ndi mzimu woyera? (Mac. 10:45) Kodi amuna amitundu ina akanafunika kudulidwa ndiponso kutsatira Chilamulo cha Mose? (Mac. 15:1, 5) Mafunso amenewa anali ofunika kwambiri. Pamenepatu panafunika mzimu wa Yehova kuti ufufuze zinthu zozama zimenezi. Koma kodi mzimuwu ukanagwira ntchito kudzera mwa ndani?

6 Abale amene anali ndi udindo ndi amene anabweretsa mafunso oti akambirane okhudza nkhanizi. Petulo, Paulo ndi Baranaba anali pa msonkhano wa bungwe lolamulira ndipo anafotokoza mmene Yehova anali kuchitira ndi anthu a mitundu ina amene anali osadulidwa. (Mac. 15:7-12) Bungwe lolamulira litakambirana za umboniwu, kuona zimene Malemba a Chiheberi amanena pa nkhaniyi ndiponso mzimu woyera utawathandiza, anasankha zochita. Kenako analembera mipingo makalata ofotokoza zimene anasankhazo.​—Werengani Machitidwe 15:25-30; 16:4, 5; Aef. 3:5, 6.

7. Kodi n’chiyani chinathandiza kuti mfundo zozama za choonadi zimveketsedwe bwino?

7 Nkhani zina zinamveketsedwa bwino m’makalata ouziridwa amene Yohane, Petulo, Yakobe ndi Paulo analemba. Koma pa nthawi ina, Malemba Achigiriki Achikhristu atamaliza kulembedwa, mphatso za kunenera ndiponso kudziwa zinthu m’njira yozizwitsa zinatha. (1 Akor. 13:8) Koma kodi mzimu ukanapitirizabe kuphunzitsa anthu ndiponso kuwakumbutsa zinthu? Kodi ukanathandizabe Akhristu kufufuza zinthu zozama za Mulungu? Ulosi unasonyeza kuti zidzaterodi.

 M’nthawi ya Chimaliziro

8, 9. Kodi aphunzitsi amene anali ‘kudzawala’ m’nthawi ya chimaliziro ndi ndani?

8 Ponena za nthawi ya chimaliziro, mngelo analosera kuti: “Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi ku nthawi za nthawi . . . ndi chidziwitso chidzachuluka.” (Dan. 12:3, 4) Kodi aphunzitsi amene anali kudzawala ndi ndani? Yesu akutithandiza kupeza yankho m’fanizo lake la tirigu ndi namsongole. Ponena za “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” iye ananena kuti: “Panthawi imeneyo olungama adzawala ngwee ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.” (Mat. 13:39, 43) Pofotokoza tanthauzo la fanizoli, Yesu anasonyeza kuti “olungama” ndi “ana a ufumu,” amene ndi Akhristu odzozedwa.​—Mat. 13:38.

9 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Akhristu odzozedwa onse ‘anali kudzawala’? Tikhoza kunena kuti inde. Tikutero chifukwa chakuti onse amagwira nawo ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ndiponso amalimbikitsana pa misonkhano. Akamachita zimenezi amapereka chitsanzo kwa Akhristu ena onse. (Zek. 8:23) Koma kuwonjezera pa zimenezi, zinthu zozama zinali kudzamveketsedwa bwino m’nthawi ya chimaliziro. Ulosi umene Danieli analemba ‘unakhomeredwa chizindikiro’ mpaka nthawi imeneyi. (Dan. 12:9) Kodi mzimu ukanafufuza zinthu zozama zimenezi kudzera mwa ndani, ndipo ukanachita bwanji zimenezi?

10. (a) M’masiku otsiriza ano, kodi mzimu umaulula mfundo zozama za choonadi kudzera mwa ndani? (b) Fotokozani mmene mfundo za choonadi chokhudza kachisi wauzimu wa Yehova zinafotokozedwera.

 10 Masiku ano, ikafika nthawi yoti mfundo ina ya m’Mawu a Mulungu imveketsedwe, mzimu woyera umathandiza abale amene amaimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova kuti azindikire mfundo zozama za choonadi zimene poyamba sizinali kudziwika. (Mat. 24:45; 1 Akor. 2:13) Bungwe Lolamulira limakambirana mfundo zatsopanozo. (Mac. 15:6) Iwo amafalitsa mfundo zimene apeza kuti athandize anthu ambiri. (Mat. 10:27) Pakapita nthawi, pangafunike kufotokozanso bwinobwino mfundo za mu nkhani zina, ndipo zikatero iwo amazifotokoza momveka bwino.​—Onani bokosi lakuti,  “Mmene Mzimu Woyera Unaululira Tanthauzo la Kachisi Wauzimu.”

Mmene Mzimu Woyera Umatithandizira Masiku Ano

11. Kodi Akhristu onse masiku ano amapindula bwanji ndi zimene mzimu woyera umachita poulula zinthu zozama za Mulungu?

11 Akhristu okhulupirika onse amapindula ndi zimene mzimu woyera umachita poulula zinthu zozama za Mulungu. Mofanana ndi Akhristu m’nthawi ya atumwi, ifenso masiku ano timaphunzira, timakumbukira ndi kugwiritsa ntchito mfundo zimene mzimu woyera umatithandiza kuzimvetsa. (Luka 12:11, 12) Sikuti timafunika maphunziro apamwamba kuti timvetse mfundo zozama za choonadi zimene zimafalitsidwa. (Mac. 4:13) Ndiyeno kodi tingatani kuti tizimvetsa kwambiri zinthu zozama za Mulungu? Nawa malangizo ena amene angakuthandizeni.

12. Kodi tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera pa nthawi iti?

12 Muzipempha mzimu woyera. Tisanayambe kuphunzira zinthu zauzimu tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera kuti utitsogolere. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pamene tikuphunzira patokha kapena pamene tili ndi nthawi yochepa yoti tiphunzire. Mapemphero osonyeza kudzichepetsa oterewa amasangalatsa mtima wa Atate wathu wakumwamba. Yesu anasonyeza kuti Yehova adzatipatsa mzimu woyera mowolowa manja ngati titapempha ndi mtima wonse.​—Luka 11:13.

13, 14. Kodi kukonzekera misonkhano kungatithandize bwanji kumvetsa zinthu zozama za Mulungu?

13 Muzikonzekera misonkhano. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa ‘chakudya pa nthawi yoyenera.’ “Kapolo” ameneyu amakwaniritsa udindo wake mwa kufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo, kukonza misonkhano ndiponso ndandanda za misonkhanoyo. Pali zifukwa zomveka zimene zimachititsa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kupempha “gulu lonse la abale” kuti likambirane mfundo zina pa misonkhano. (1 Pet. 2:17; Akol. 4:16; Yuda 3) Tikamachita zonse zimene tingathe potsatira malangizo amene tapatsidwa, timasonyeza kuti tikugwirizana ndi mzimu woyera.​—Chiv. 2:29.

14 Tikamakonzekera misonkhano, ndi bwino kuwerenga Malemba osagwidwa mawu n’kuona kugwirizana kwa malembawo ndi nkhani imene tikuphunzirayo. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kumvetsa mfundo zozama za m’Baibulo. (Mac. 17:11, 12) Kuwerenga malemba m’Baibulo kumathandiza kuti akhazikike m’maganizo mwathu moti mzimu woyera ukhoza kutithandiza kuwakumbukira. Chinanso n’chakuti tikawerenga lemba m’Baibulo timaona pamene  lembalo lili ndipo izi zingachititse kuti tizilionabe m’maganizo mwathu. Zimenezi zingathandize kuti tikalifuna lembalo tizilipeza mosavutikira.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuwerenga zofalitsa zonse zatsopano, ndipo inuyo mumachita chiyani kuti mukwanitse kuchita zimenezi?

15 Muziwerenga zofalitsa zatsopano. M’mabuku ndi magazini athu mumakhalanso nkhani zina zimene sitiphunzira kumpingo koma zimakonzedwa kuti zitithandize. Ngakhale nkhani za m’magazini amene timagawira zimakonzedwanso kuti zitithandize ifeyo. M’dzikoli zochitika ndi zambirimbiri ndipo izi zimachititsa kuti nthawi zina tiziyembekezera munthu wina kapena zinthu zina. Choncho ngati titamayenda ndi mabuku kapena magazini amene sitinawerenge kapena amene sitinamalize kuwerenga, tikhoza kumawerenga pamene tikuyembekezera zinthu zina. Ena amamvetsera makaseti ndi ma CD a zofalitsa zathu pamene akuyenda pansi kapena pamene akwera galimoto. Nkhani zofufuzidwa bwino ndiponso zothandiza kwa anthu ambiri zimenezi zimatichititsa kuyamikira kwambiri zinthu zauzimu.​—Hab. 2:2.

16. Tikamaphunzira, kodi kulemba mafunso ndiponso kufufuza mayankho ake kungatithandize bwanji?

16 Muzisinkhasinkha. Mukamawerenga Baibulo kapena mabuku ofotokoza Baibulo muzikhala ndi nthawi yoganizira kwambiri zimene mukuwerengazo. Mukamaitsatira bwinobwino nkhaniyo mungayambe kukhala ndi mafunso ena. Ndi bwino kulemba mafunsowo kuti mufufuze mayankho ake pa nthawi ina. Nthawi zambiri tikamafufuza nkhani zimene zikutivuta kumvetsa, m’pamene timaphunzira zinthu zozama. Zinthu zimene tazimvetsa bwino zimakhala ngati chuma chimene tasunga m’maganizo mwathu ndipo timazigwiritsa ntchito zikafunika.​—Mat. 13:52.

17. Kodi inuyo mumachita zotani pa nthawi ya kulambira kwa pabanja kapena yophunzira panokha?

17 Muzikhala ndi nthawi yochita kulambira kwa pabanja. Bungwe Lolamulira likutilimbikitsa tonsefe kuti mlungu uliwonse tizipeza nthawi yophunzira patokha kapena monga banja. Misonkhano yathu inasinthidwa n’cholinga chakuti tikhale ndi nthawi yokwanira yochita zimenezi. Kodi mumaphunzira chiyani pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja? Ena amawerenga Baibulo, kufufuza mavesi amene akuwavuta kumvetsa ndipo amalemba manotsi m’Baibulo lawo. Mabanja ambiri amakambirana mmene angagwiritsire ntchito mfundo zimene aphunzira. Mitu ina ya mabanja imasankha nkhani imene akuona kuti ingathandize banja lawo kapena amasankha nkhani imene munthu wina m’banjamo wapempha kuti aiphunzire. Mosakayikira nthawi ikamapita muzipeza nkhani zina zimene mungadzaphunzire. *

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kuphunzira mfundo zozama za choonadi cha m’Mawu a Mulungu?

18 Yesu ananena kuti mzimu udzakhala mthandizi. Choncho tisasiye kuphunzira zinthu zozama za choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Choonadi chimenechi ndi mbali ya zinthu zamtengo wapatali zokhudza ‘kum’dziwa Mulungu’ ndipo tikulimbikitsidwa kufufuza zinthu zimenezi. (Werengani Miyambo 2:1-5.) Kufufuza zinthu zimenezi kumatithandiza kudziwa “zimene Mulungu wakonzera om’konda.” Tikamayesetsa kuphunzira zambiri m’Mawu a Yehova, mzimu woyera udzatithandiza chifukwa chakuti “mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.”​—1 Akor. 2:9, 10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2008, tsamba 8.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mzimu umatithandiza kufufuza “zinthu zozama za Mulungu” m’njira ziwiri ziti?

• M’nthawi ya atumwi, kodi mzimu woyera unaulula mfundo zozama za choonadi kudzera mwa ndani?

• Kodi masiku ano, mzimu woyera umagwira ntchito bwanji kuti mfundo zina zimveketsedwe?

• Kodi mungatani kuti mupindule ndi ntchito imene mzimu ukugwira?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 22]

 Mmene Mzimu Woyera Unaululira Tanthauzo la Kachisi Wauzimu

Zina mwa “zinthu zozama za Mulungu” zimene zinadziwika m’nthawi ya atumwi zinali zakuti chihema ndipo kenako kachisi zinkaimira zinthu zina zauzimu zofunika kwambiri. Mtumwi Paulo anati zinthu zimenezi, ndi “chihema choona, chomangidwa ndi Yehova, osati munthu.” (Aheb. 8:2) Chihema chimenechi chinali kachisi wamkulu wauzimu yemwe ndi njira yofikira kwa Mulungu ndipo inatsegulidwa ndi nsembe ndiponso udindo wa Yesu Khristu monga wansembe.

“Chihema choona” chinakhalapo mu 29 C.E. pamene Yesu anabatizidwa ndipo Yehova anamulandira kuti akhale nsembe yangwiro. (Aheb. 10:5-10) Yesu atafa n’kuukitsidwa analowa m’Malo Opatulikitsa a kachisi wauzimu n’kupereka nsembe “pamaso pa Mulungu.”​—Aheb. 9:11, 12, 24.

Pa lemba linanso mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu odzozedwa ‘akukula kukhala kachisi woyera wa Yehova.’ (Aef. 2:20-22) Kodi kachisi ameneyu, ndi “chihema choona” chimene iye anachifotokoza m’kalata yake yopita kwa Aheberi? Kwa zaka zambiri atumiki a Yehova ankaganiza zimenezi. Zinkaoneka ngati Akhristu odzozedwa ankakonzekeretsedwa padziko lapansi kuti adzakhale “miyala” m’kachisi wakumwamba wa Yehova.​—1 Pet. 2:5.

Koma cha m’ma 1971 abale odzozedwa audindo anazindikira kuti kachisi amene Paulo anatchula m’kalata yopita kwa Aefeso ndi wosiyana ndi kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Zikanakhala kuti odzozedwa oukitsidwa ndi amene amapanga “chihema choona,” ndiye kuti chihemacho chikanayamba kukhalapo pamene iwo anayamba kuukitsidwa “pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye.” (1 Ates. 4:15-17) Ponena za chihemachi, Paulo analemba kuti: “Chihema chimenecho chinali chifaniziro cha nthawi yoikika imene tsopano yafika.”​Aheb. 9:9.

Atayerekezera bwinobwino malemba amenewa ndi malemba ena, zinadziwika kuti kachisi wauzimu sakumangidwa panopa ndiponso kuti Akhristu odzozedwa si “miyala” imene ikukonzedwa padzikoli kuti akamangire m’kachisiyo. Akhristu odzozedwa akutumikira m’bwalo ndi m’malo Opatulika a kachisi wauzimu ndipo tsiku ndi tsiku akupereka kwa Mulungu “nsembe ya chitamando.”​—Aheb. 13:15.

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi tingatani kuti tizimvetsa bwino “zinthu zozama za Mulungu”?