Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulera Ana Eyiti M’njira za Yehova Inali Ntchito Yovuta Komanso Yosangalatsa

Kulera Ana Eyiti M’njira za Yehova Inali Ntchito Yovuta Komanso Yosangalatsa

Mbiri ya Moyo Wanga

Kulera Ana Eyiti M’njira za Yehova Inali Ntchito Yovuta Komanso Yosangalatsa

YOSIMBIDWA NDI JOYCELYN VALENTINE

Mu 1989 mwamuna wanga anapita kunja kukagwira ntchito. Analonjeza kuti azinditumizira ndalama kuti ndizisamalira ana anga eyiti. Milungu ingapo inadutsa ndisanamve chilichonse. Kenako miyezi inadutsa ndisanamvebe chilichonse kuchokera kwa mwamuna wanga. Ndinkadzilimbitsa mtima kuti, ‘Zinthu zikangomuyendera, abwera.’

POPEZA ndinalibe ndalama zoti ndisamalire banja langa, ndinasowa pogwira. Masiku ambiri usiku ndikamasowa tulo, ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma zoonadi mwamuna wanga angachitire banja lake zimenezi?’ ndipo ndinkalephera kumvetsa. Kenaka ndinazindikira kuti basi, mwamuna wanga watithawa. Panopa, patha zaka pafupifupi 16 chichokereni, koma sanabwerebe. Choncho, ndinalera ndekha ana anga mosathandizidwa ndi mwamuna. Zimenezi zakhala zovuta, koma kuona ana anga akutsatira njira za Yehova kwandibweretsera chimwemwe chachikulu. Koma ndisanafotokoze zomwe tinakumana nazo, ndikufuna ndikuuzeni mmene ndinakulira.

Kufunafuna Malangizo a M’Baibulo

Ndinabadwa mu 1938 ku Jamaica, chomwe ndi chilumba cha m’nyanja ya Caribbean. Ngakhale kuti bambo anga analibe mpingo, iwo ankati anali munthu woopa Mulungu. Usiku nthawi zambiri ankandiuza kuti ndiziwawerengera buku la Masalmo m’Baibulo. Pasanapite nthawi yaitali, ndinkatha kulakatula masalmo ambiri pamtima. Amayi ankapita ku tchalitchi chinachake chakwathuko, ndipo nthawi zina ankanditenga akamapita ku misonkhano yachipembedzo.

Ku misonkhano imeneyo, ankatiuza kuti Mulungu amapititsa anthu abwino kumwamba koma oipa amawawotcha kwamuyaya ku moto. Tinauzidwanso kuti Yesu ndi Mulungu ndipo amakonda ana. Ndinasokonezeka maganizo ndipo ndinkachita mantha kwambiri ndi Mulungu. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amene amatikonda angazunze bwanji anthu kumoto?’

Ndikaganizira za moto umenewo ndinkaopa kwambiri. Kenaka ndinachita kosi ya Baibulo kudzera m’makalata yokonzedwa ndi tchalitchi cha Seventh-Day Adventist. Iwo ankaphunzitsa kuti anthu oipa sadzazunzidwa kwamuyaya koma adzawotchedwa kumoto mpaka kusanduka phulusa. Zimenezi zinkaoneka zomvekako, ndipo ndinayamba kumapita ku misonkhano yawo yachipembedzo. Koma ndinaona kuti zimene ankaphunzitsa zinali zosokoneza, ndipo zimene ndinaphunzira sizinawongolere maganizo anga olakwika pa nkhani ya makhalidwe abwino.

Panthawi imeneyo, anthu ambiri ankavomereza kuti kuchita chiwerewere n’kulakwa. Komabe, ine ndi anthu ena ambiri tinkakhulupirira kuti anthu amene amagonana ndi anthu osiyanasiyana ndi amene amachita chiwerewere. Koma anthu awiri osakwatirana amene ankangogonana awiriwo basi sanali kuchimwa. (1 Akorinto 6:9, 10; Ahebri 13:4) Chifukwa chokhulupirira zimenezo, ndinakhala ndi ana sikisi apatchire.

Kupita Patsogolo Mwauzimu

Mu 1965, Vaslyn Goodison ndi Ethel Chambers anabwera kumadzakhala kufupi ndi kwathu ku Bath. Iwo anali apainiya, kapena kuti atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova, ndipo tsiku lina analankhula ndi bambo anga. Bambo anavomera kuti aziphunzira nawo Baibulo. Ndikakhala kuti ndili panyumba panthawi yomwe abwera, ankalankhulanso nane. Ngakhale kuti ndinkawakayikira kwambiri anthu a Mboni za Yehova, ndinaganiza zophunzira nawo Baibulo kuti ndiwasonyeze kuti anali olakwa.

Ndinkafunsa mafunso ambiri paphunzirolo, ndipo a Mboniwo ankayankha mafunso onsewo ndi Baibulo. Chifukwa cha thandizo lawo, ndinazindikira kuti anthu akufa sadziwa kanthu kalikonse ndipo sazunzika ku moto. (Mlaliki 9:5, 10) Ndinaphunziranso za chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Ngakhale kuti bambo anga anasiya kuphunzira Baibulo, ine ndinayamba kumapita ku misonkhano ku mpingo wakwathuko wa Mboni za Yehova. Popeza misonkhano yake inkachitika mwabata ndiponso mwadongosolo, ndinatha kuphunzira zambiri zokhudza Yehova. Ndinkapitanso ku misonkhano yadera ndi yachigawo, yomwe ndi misonkhano ikuluikulu yokonzedwa ndi Mboni. Kuphunzira Baibulo m’njira imeneyi kunandichititsa kufunitsitsa kupembedza Yehova moyenera. Koma ndinali ndi chopinga chimodzi.

Panthawi imeneyo, ndinali kukhala ndi mwamuna amene ndinabereka naye ana atatu mwa ana sikisi omwe ndinali nawo, ngakhale kuti sindinachite naye ukwati. Ndinaphunzira m’Baibulo kuti Mulungu amadana ndi kugonana ndi munthu amene sunakwatirane naye, ndipo chikumbumtima changa chinayamba kundivutitsa. (Miyambo 5:15-20; Agalatiya 5:19) Nditayamba kukonda kwambiri choonadi, ndinafunitsitsa kukhala moyo wogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Kenaka ndinadziwa chochita. Ndinauza mwamuna amene ndinali kukhala nayeyo kuti tiyenera kukwatirana, apo ayi chibwenzi chathu chitha. Ngakhale kuti mwamunayo sankakhulupirira zimene ineyo ndinkakhulupirira, tinakwatirana mwalamulo pa August 15, 1970, patatha zaka zisanu kuchokera pamene a Mboni analankhula nane koyamba. Mu December 1970, ndinasonyeza kuti ndadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi.

Pankhani ya utumiki, sindidzaiwala tsiku langa loyamba kulalikira. Ndinali ndi mantha kwambiri ndipo sindinkadziwa momwe ndingayambire kulankhula ndi munthu wina pa nkhani ya m’Baibulo. Moti ndinasangalala pamene munthu amene ndinalankhula naye panyumba yoyamba ananena kuti sakufuna kulankhula nane. Koma patatha kanthawi kochepa ndinasiya kuchita mantha. Pamapeto pa tsiku limenelo, ndinali wosangalala kwambiri, chifukwa ndinalankhulako mwachidule ndi anthu angapo za m’Baibulo ndipo ndinawasiyira mabuku athu ena.

Kuthandiza Banja Langa Kukhala Lolimba Mwauzimu

Pofika mu 1977, m’banja mwathu munali ana eyiti. Ndinafunitsitsa kuchita zonse zomwe ndikanatha kuti ndithandize banja langa kutumikira Yehova. (Yoswa 24:15) Choncho ndinachita khama kuti ndizichititsa phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse. Nthawi zina, chifukwa chotopa, ndinkayamba kuwodzera pamene mmodzi mwa anawo anali kuwerenga ndime mokweza, ndipo anawo ankachita kundidzutsa. Koma kutopa sikunatilepheretse kuphunzira limodzi Baibulo monga banja.

Ndinkapempheranso nthawi zambiri limodzi ndi ana anga. Mwana aliyense akangofika pa msinkhu wabwino ndithu, ndinkamuphunzitsa kupemphera kwa Yehova payekha. Ndinkaonetsetsa kuti aliyense wa iwo azipemphera payekha asanagone. Ndinkapemphera limodzi ndi mwana aliyense amene anali wamng’ono moti sakanatha kupemphera yekha.

Poyamba, mwamuna wanga ankandiletsa kutenga anawo kupita nawo ku misonkhano ya mpingo. Komabe, akaganizira zoyang’anira yekha anawo ine ndili ku misonkhano, sankandiletsanso. Usiku, ankakonda kupita kukacheza ndi anzake, koma sakanatha kutero limodzi ndi ana eyiti. Ndipo patapita nthawi anayamba kundithandiza kuwakonzekeretsa anawo kuti apite ku Nyumba ya Ufumu.

Anawo posakhalitsa anazolowera kupita ku misonkhano yonse ndi kuchita nawo ntchito yolalikira. Akakhala patchuthi, nthawi zambiri ankapita kolalikira limodzi ndi apainiya, kapena kuti atumiki a nthawi zonse, a mu mpingomo. Zimenezi zinathandiza ana anga kuyamba kukonda kwambiri mpingowo ndi ntchito yolalikira.​—Mateyu 24:14.

Tinakumana ndi Mayesero

Pofuna kupeza ndalama zowonjezereka zothandizira banja lathu, mwamuna wanga anayamba kumapita kunja kukagwira ntchito. Ankachokapo kwa nthawi yaitali, ndipo ankabwerera nthawi ndi nthawi. Koma mu 1989, anachoka osabwereranso. Monga ndanenera koyambirira kuja, kuchoka kwa mwamuna wanga kunandichititsa kuti ndisoweretu pogwira. Masiku ambiri usiku, ndinkalira ndi kupemphera ndi mtima wonse kwa Yehova kuti andilimbikitse ndi kundithandiza kupirira, ndipo ndinaona kuti anayankha mapemphero anga. Malemba monga Yesaya 54:4 ndi 1 Akorinto 7:15 anandipatsa mtendere wa mumtima ndi mphamvu kuti ndithe kupirira. Mu mpingo, achibale ndi anzanga anandithandizanso pondilimbikitsa maganizo ndi kundipatsa zinthu zina ndi zina. Ndimayamikira kwambiri Yehova ndi anthu ake chifukwa chondithandiza.

Tinakumananso ndi mayesero ena. Panthawi ina, mmodzi mwa ana anga aakazi anachotsedwa mumpingo chifukwa cha khalidwe losemphana ndi Malemba. Ana anga onse ndimawakondadi kwambiri, koma kukhulupirika kwanga kwa Yehova ndimakuika pamalo oyamba. Choncho panthawi imeneyo, ine ndi ana anga ena tinamvera kwambiri malangizo a m’Baibulo a mmene tiyenera kuchitira ndi anthu ochotsedwa. (1 Akorinto 5:11, 13) Anthu amene sankatimvetsa bwino anatinyoza kwambiri. Komabe, mwana wanga atabwezeretsedwa mu mpingo, mwamuna wake anandiuza kuti kulimba mtima kwathu potsatira mfundo za m’Baibulo kunamukhudza mtima kwambiri. Panopa, mwamunayo akutumikira Yehova limodzi ndi banja lake.

Mavuto Azachuma

Mwamuna wanga atatithawa, nthawi zambiri kunali kovuta kupeza ndalama, ndipo sankatitumiziranso thandizo lililonse. Zimenezi zinatiphunzitsa kukhutira ndi moyo wosalira zambiri ndi kuona kuti zinthu zauzimu ndi zamtengo wapatali kwambiri kuposa zinthu zakuthupi. Anawo anaphunzira kukondana ndi kuthandizana, ndipo anayamba kugwirizana kwambiri. Ana okulirapowo atayamba kugwira ntchito, ankathandiza azing’ono awo mosanyinyirika. Mwana wanga wamkazi wamkulu, Marseree, anathandiza mng’ono wake Nicole, kumaliza maphunziro ake a ku sekondale. Ndiponso, ineyo ndinali ndi kagolosale kakang’ono. Ndalama zochepa zomwe ndinkapeza kumeneko zinandithandiza kupeza zosowa zathu zina ndi zina.

Nthawi yonseyi Yehova sanatisiye. Nthawi ina ndinauza mlongo wina wauzimu kuti popeza tinalibe ndalama sitikanatha kupita ku msonkhano wachigawo. Iye anandiyankha kuti: “Mlongo Val, akangolengeza za msonkhano, muyambe kukonzeka. Yehova adzakuthandizani.” Ndinamvera malangizo akewo. Yehova anatithandizadi, ndipo wapitirizabe kutithandiza. Banja lathu silinaphonyepo msonkhano wadera kapena wachigawo chifukwa chosowa ndalama.

Mu 1988 mphepo yamkuntho yotchedwa Gilbert inasakaza zinthu ku Jamaica, ndipo tinachoka ku nyumba kwathu kukabisala ku malo ena otetezeka. Kutachitako bata, ine ndi mwana wanga wamwamuna tinachoka kobisalako kukaona nyumba yathu yomwe inali itawonongekeratu. Ndikufufuza pa zinthu zowonongekazo, ndinaona chinachake chomwe ndinkafuna kuchisunga. Kenaka mwadzidzidzi kunayambanso chimphepo, koma ndinanyamulabe chinthu chomwe ndinapezacho. “Amayi, taisiyani TV’yo. Kodi ndinu mkazi wa Loti?” (Luka 17:31, 32) Mawu amenewo ochokera kwa mwana wanga anandithandiza kuti ndiyambenso kuganiza bwino. Ndinaponya pansi TV yonyowayo ndipo tonsefe tinathawira kumalo otetezeka aja.

Panopa ndimanjenjemera ndikaganiza kuti ndinaika moyo wanga pachiswe chifukwa cha TV. Koma ndimasangalala ndikaganizira mawu auzimu amene mwana wanga wamwamuna ananena panthawi imeneyo. Chifukwa chophunzitsidwa zinthu za m’Baibulo kumpingo, anatha kundithandiza kuti ndisavulale mwakuthupi ndipo mwinanso mwauzimu.

Mphepo yamkunthoyo inawononga nyumba ndi katundu wathu, ndiponso inatisiya tili otaya mtima. Koma kenaka abale athu achikristu anabwera. Anatilimbikitsa kuti ngakhale tatayikiridwa zinthu zambiri tikhulupirirebe Yehova ndi kupitiriza kuchita khama mu utumiki, ndipo anatithandiza kumanganso nyumba yathu. Tinakhudzidwa mtima kwambiri poona chikondi ndi kudzimana kwa a Mboni odzipereka amenewo, amene anachokera ku Jamaica konkuno ndi ku mayiko ena akunja.

Kuika Yehova Patsogolo

Melaine, mwana wanga wachiwiri, atamaliza maphunziro ake anayamba kuchita utumiki waupainiya. Kenaka anavomera kukakhala mpainiya ku mpingo wina, zomwe zinatanthauza kuti anafunika kusiya ntchito yake yolembedwa. Ngakhale kuti ali pantchito imeneyo ankatha kutipatsa ndalama zambiri ndithu zothandizira banja lathu, tinali ndi chikhulupiriro kuti Yehova atisamalira ngati aliyense wa ife aika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mateyu 6:33) Kenaka mwana wanga wamwamuna Ewan, nayenso anapemphedwa kukhala mpainiya. Panthawi imeneyo anali akuthandiza banja lathu ndi ndalama, koma tinamulimbikitsa kuvomera utumiki umenewo ndipo tinamufunira madalitso a Yehova. Sindinaletsepo mwana aliyense kuchita zambiri mu utumiki wa Ufumu, ndipo amene tinatsala pakhomofe sitinavutikepo. M’malo mwake, takhala ndi chimwemwe chochuluka, ndipo nthawi zina, tatha kuthandizaponso ena ovutika.

Masiku ano, ndimasangalala kwambiri kuona ana anga “ali kuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Mmodzi mwa ana anga aakazi, Melaine, panopa amatsagana ndi mwamuna wake pa ntchito yake yoyendayenda monga woyang’anira dera. Mwana wanga wina wamkazi, Andrea ndi mwamuna wake ndi apainiya apadera, ndipo amatsagana ndi mwamuna wake akamayendera mipingo monga woyang’anira dera wogwirizira. Mwana wanga wamwamuna, Ewan, ndi mkazi wake ndi apainiya apadera, ndipo Ewan ndi mkulu mumpingo. Mwana wanga wina wamkazi, Ava-Gay akugwira ntchito limodzi ndi mwamuna wake ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Jamaica. Jennifer, Genieve, ndi Nicole akutumikira limodzi ndi amuna awo ndi ana awo monga ofalitsa achangu m’mipingo mwawo. Marseree akukhala ndi ineyo, ndipo awirife timasonkhana mu mpingo wa Port Morant. Ndadalitsidwa kwambiri, chifukwa ana anga onse eyiti akupitirizabe kulambira Yehova.

Pamene ndikukalamba, thanzi langa layamba kufooka. Panopa ndimadwala nyamakazi, koma ndimasangalalabe kutumikira monga mpainiya. Koma panthawi ina m’mbuyomu, kuyenda m’malo amapiri akwathu kuno kunayamba kundivuta kwambiri. Zinkandivuta kupita mu utumiki. Ndinayesera kukwera njinga, ndipo ndinaona kuti zinali zophwekerako kusiyana ndi kuyenda. Choncho ndinagula njinga kwa munthu wina. Poyamba ana anga sankasangalala kuona amayi awo odwala nyamakazi akupalasa njinga. Komabe, anali osangalala kundiona ndikupitirizabe kulalikira monga momwe mtima wanga unali kufunira.

Ndimasangalala kwambiri kuona anthu amene ndaphunzira nawo akuyamba kutsatira choonadi cha m’Baibulo. Ndimapemphera nthawi zonse kuti Yehova athandize banja langa lonse kukhalabe lokhulupirika kwa iye mu nthawi zamapeto zino mpaka kufika muyaya. Ndimatamanda ndi kuthokoza Yehova, “Wakumva pemphero” Wamkulu, chifukwa chondithandiza kukwanitsa ntchito yolera ana anga eyiti m’njira zake.​—Salmo 65:2.

[Chithunzi patsamba 10]

Ndili ndi ana anga, azimuna awo ndi azikazi awo, ndi zidzukulu zanga

[Chithunzi patsamba 12]

Tsopano ndimakwera njinga pochita utumiki wanga