Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikhulupiriro Chanu mwa Mulungu N’cholimba Motani?

Kodi Chikhulupiriro Chanu mwa Mulungu N’cholimba Motani?

 Kodi Chikhulupiriro Chanu mwa Mulungu N’cholimba Motani?

“Muthange mwafuna Ufumu.”​—MATEYU 6:33.

1, 2. Kodi mnyamata wina anachita zotani pantchito imene ankagwira, ndipo anachita zimenezo chifukwa chiyani?

MNYAMATA wina ankafuna kuti azithandiza kwambiri mpingo wawo. Koma vuto linali lakuti ntchito imene anali kugwira sinkamupatsa mpata woti azifika pa misonkhano nthawi zonse. Kodi analithetsa bwanji? Anaganiza zokhala ndi moyo wosalira zambiri, ndipo anasiya ntchito imene anali kugwirayo. M’kupita kwanthawi anapeza ntchito ina yomwe inkamupatsa mpata wochita ntchito zake zachikristu. Ndalama zimene panopa akulandira ndi zochepa kwambiri kusiyana ndi zimene anali kulandira poyamba, komatu iye akukwanitsabe kusamalira banja lake ndipo akuthandiza kwambiri mu mpingo wawo.

2 Kodi mukumvetsa chifukwa chake mnyamata ameneyu anachita zimenezi? Kodi mukuganiza kuti inunso mukanachita zomwezi mukanakhala kuti zinthu pa moyo wanu zinali zofanana ndi mmene zinalili kwa iye? Chosangalatsa n’chakuti Akristu ambiri achita zimenezi. Izi zimasonyeza kuti amakhulupirira lonjezo la Yesu lakuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Iwo amakhulupirira kuti Yehova ndiye angathetse nkhawa zawo, osati dzikoli.​—Miyambo 3:23, 26.

3. N’chifukwa chiyani anthu ena angakayikire ngati kufuna Ufumu wa Mulungu choyamba kuli kothandiza masiku ano?

3 Chifukwa chakuti masiku amene tikukhalamo ano ndi ovuta, ena angakayikire ngati mnyamata uja anachita zanzeru. Masiku ano, anthu ena ali pa umphawi wadzaoneni pamene ena amakhala moyo wawofuwofu. Anthu ambiri okhala m’mayiko osauka sangakane mwayi uliwonse wowathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino. Pamene m’mayiko olemera, kusadalirika kwa zachuma, kusowa kwa ntchito, ngakhalenso mabwana ofuna kuti antchito awo azigwira ntchito kwambiri, zimachititsa anthu ambiri kuvutika kuti akwanitsebe kukhala ndi moyo wawofuwofu. Poona mmene zikuvutira kuti anthu azitha kupeza zofunika pa moyo, ena angakayikire kuti, ‘Kodi kufuna Ufumu choyamba kudakali kothandiza?’ Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tiganizire za anthu amene Yesu anali kulankhula nawo.

“Musadere Nkhawa”

4, 5. Kodi Yesu anapereka mafanizo otani posonyeza kuti n’zomveka kuti anthu a Mulungu asamadere nkhawa kwambiri kupeza zofunika za tsiku ndi tsiku?

4 Yesu anali ku Galileya, ndipo anali kulankhula ndi khamu la anthu ochokera m’madera ambiri. (Mateyu 4:25) Ngati ena mwa anthuwo anali olemera, ndiye kuti analipo ochepa zedi. Mosakayikira ochuluka a iwo anali osauka. Ngakhale n’choncho, Yesu anawalimbikitsa kuti aziyamba kukundika, osati chuma chakuthupi, koma chuma chauzimu, chomwe ndi cha mtengo wapatali zedi. (Mateyu 6:19-21, 24) Iye anati: “Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?”​—Mateyu 6:25.

5 Mwina anthu ambiri amene anali kumvetsera Yesu akulankhula anaganiza kuti zimenezo zinali zosathandiza. Anali kudziwa kuti ngati sangagwire ntchito molimbika, ndiye kuti mabanja awo avutika. Komabe Yesu anawakumbutsa za mbalame. Mbalame zimafunafuna chakudya ndi pokhala tsiku lililonse, komatu Yehova amazisamalira. Yesu anatchulanso za mmene Yehova amasamalira maluwa  akuthengo, omwe ndi okongola kuposa mmene analili Solomo mu ulemerero wake wonse. Ngati Yehova amasamalira mbalame ndi maluwa, kuli bwanji ife anthu? (Mateyu 6:26-30) Monga mmene Yesu ananenera, miyoyo yathu ndi matupi athu n’zofunika kwambiri kuposa chakudya chimene timagula kuti chizichirikiza miyoyo yathuyo ndiponso kuposa zovala zimene timagula kuti matupi athuwo azivala. Ngati khama lathu lonse limakhala pochita zinthu zoti tipeze chakudya ndi zovala, popanda kukhala ndi nthawi yokwanira bwino yotumikira Yehova, ndiye kuti talephera kumvetsa cholinga chenicheni chokhalira ndi moyo.​—Mlaliki 12:13.

Musangoyang’ana Mbali Imodzi

6. (a) Kodi Akristu ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Akristu amakhulupirira ndani ndi mtima wawo wonse?

6 N’zoona kuti Yesu sanalimbikitse anthuwo kusiya kugwira ntchito n’kumangodikirira kuti mwa njira inayake Mulungu awapatsa zofunika m’mabanja awo. Ngakhale mbalame nazo zimamka zifunafuna chakudya choti zidye komanso chokadyetsa ana awo. Motero Akristu anafunika kugwira ntchito kuti apeze chakudya. Anafunika kusamalira maudindo awo pa banja. Akristu omwe anali antchito ndiponso akapolo anafunika kugwirira ntchito mabwana awo mwakhama. (2 Atesalonika 3:10-12; 1 Timoteo 5:8; 1 Petro 2:18) Nthawi zambiri mtumwi Paulo anali kugwira ntchito yosoka mahema kuti azipeza zosowa zake. (Machitidwe 18:1-4; 1 Atesalonika 2:9) Komabe, Akristu amenewo sanaone ntchito yakuthupi imene anali kugwira kuti ndiyo iziwathetsera nkhawa zawo. Anali kukhulupirira Yehova. Motero anali ndi mtendere wamumtima, womwe anthu ena analibe. Wamasalmo anati: “Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.”​—Salmo 125:1.

7. Kodi munthu amene sakhulupirira Yehova ndi mtima wonse angakhale ndi maganizo otani?

7 Aliyense amene sakhulupirira Yehova ndi mtima wonse angamaone zinthu mosiyana. Anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi chuma n’kothandiza kwambiri kuti munthu asamade nkhawa. Motero makolo ena alimbikitsa ana awo kuti pa unyamata wawo athere nthawi yochuluka akuchita maphunziro a kukoleji. Amati mwa kutero anawo adzatha kupeza ntchito za malipiro ochuluka. Zachisoni n’zakuti mabanja ena achikristu aona kuti kupatsa ana maphunziro oterowo n’kopweteketsa kwambiri, chifukwa ana awo asiya zinthu zauzimu n’kuika maganizo awo pa zinthu zakuthupi.

8. Kodi Akristu amaiona bwanji ntchito yolembedwa?

8 Choncho, Akristu anzeru amazindikira kuti malangizo a Yesu ndi othandiza masiku ano monga mmenenso analili kwa Akristu oyambirira, ndipo iwo amayesetsa kuti asamangoyang’ana  mbali imodzi. Ngakhale pamene afunika kugwira ntchito yolembedwa kwa maola ochuluka kuti athe kusamalira maudindo awo a m’Malemba, sanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri zauzimu pofuna kupeza ndalama.​—Mlaliki 7:12.

Malangizo Enanso Othandiza Kuti Munthu Asamade Nkhawa

9. Kodi Yesu anawatsimikizira chiyani anthu amene amakhulupirira Yehova ndi mtima wonse?

9 Mu ulaliki wake wa pa phiri, Yesu analimbikitsa anthu kuti: “Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.” (Mateyu 6:31, 32) Amenewatu ndi mawu olimbikitsa kwambiri. Ngati tikhulupirira Yehova ndi mtima wonse, iye adzatithandiza nthawi zonse. Komabe, mawu a Yesu amenewa ndi ofunanso kuwaganizira kwambiri. Amatikumbutsa kuti ngati ‘tifunitsa’ zinthu zakuthupi, timakhala tikuganiza ngati “anthu akunja,” anthu omwe si Akristu oona.

10. Mnyamata wina atafunsira uphungu kwa Yesu, kodi Yesu ananenanji zomwe zinasonyeza zimene mnyamatayo anali kukonda kwambiri?

10 Panthawi ina, mnyamata wina wolemera kwambiri anafunsa Yesu zoyenera kuchita kuti akapeze moyo wosatha. Yesu anamukumbutsa zomwe Chilamulo chinkafuna. Chilamulocho chinkagwirabe ntchito panthawiyo. Mnyamatayo anatsimikizira Yesu kuti: “Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani?” Zimene Yesu anayankha mnyamatayo zikanaoneka zosathandiza kwa anthu ambiri. Anati: “Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.” (Mateyu 19:16-21) Mnyamatayo anachoka pamenepo atakhumudwa poganizira zotaya chuma chake. Kaya chikondi chake pa Yehova chinali chachikulu motani, iye anakonda kwambiri chuma chake kuposa Yehovayo.

11, 12. (a) Kodi Yesu ananena mawu otani ofunika kuwaganizira kwambiri okhudza chuma? (b) Kodi chuma chingalepheretse bwanji munthu kutumikira Yehova?

11 Zimenezi zinachititsa Yesu kunena mawu ena osayembekezeka, akuti: “Munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba. . . . N’kwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 19:23, 24) Kodi Yesu anatanthauza kuti palibe munthu wolemera amene adzalowa mu Ufumu? Ayi sanatanthauze zimenezo, chifukwa iye anapitiriza kuti: “Zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Mateyu 19:25, 26) Inde, Yehova anathandiza anthu ena olemera kalelo kukhala Akristu odzozedwa. (1 Timoteo 6:17) Komabe, panali chifukwa chabwino chimene Yesu ananenera mawu osayembekezekawa. Iye anali kupereka chenjezo.

12 Ngati munthu aika kwambiri mtima wake pa chuma chake monga anachitira mnyamata wolemera uja, chumacho chikhoza kumulepheretsa kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Izi zingachitike kwa munthu amene ali kale wolemera komanso kwa amene ‘akufuna kukhala wachuma.’ (1 Timoteo 6:9, 10) Kukhulupirira kwambiri chuma kungachititse munthu kusazindikira zosowa zake zauzimu. (Mateyu 5:3) Chotsatira chake n’chakuti sangaonenso kufunika kothandizidwa ndi Yehova. (Deuteronomo 6:10-12) Angayembekezere kuti ena mu mpingo azimulemekeza mwapadera. (Yakobo 2:1-4) Ndipo angamathere nthawi yochuluka posangalala ndi chuma chake m’malo motumikira Yehova.

Khalani ndi Maganizo Oyenera

13. Kodi anthu a mu mpingo wa ku Laodikaya anali ndi maganizo olakwika otani?

13 Anthu ena amene anali kuona chuma molakwika anali anthu a mu mpingo wa ku Laodikaya wa m’nthawi ya atumwi. Yesu anawauza kuti: “Unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa.” Si chuma chawo chomwe chinachititsa anthu a ku Laodikaya kukhala omvetsa chifundo mwauzimu. Koma chinali chifukwa chakuti anali kukhulupirira chuma m’malo mokhulupirira Yehova. Izi zinawachititsa kukhala ofunda mwauzimu, moti anatsala pang’ono ‘kulavulidwa m’kamwa’ mwa Yesu.​—Chivumbulutso 3:14-17.

14. N’chifukwa chiyani kunali koyenera kuti Paulo ayamikire Akristu achihebri?

14 Mosiyana ndi amenewo, Paulo anayamikira Akristu achihebri chifukwa cha mtima umene  anaonetsa pamene anali kuzunzidwa pa nthawi ina. Iye anati: “Munamva chifundo ndi iwo a m’ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.” (Ahebri 10:34) Akristuwo sanataye mtima potayikiridwa chuma chawo. Anakhalabe osangalala chifukwa sanataye chuma chawo cha mtengo wapatali kwambiri, “chuma choposa chachikhalire.” Mofanana ndi munthu wa malonda wa m’fanizo la Yesu yemwe anagulitsa zonse anali nazo kuti agule ngale imodzi ya mtengo wapatali, iwo anatsimikiza mtima kusasiya chiyembekezo cha Ufumu chimene anali nacho, ngakhale ngati akanafunika kutaya zambiri. (Mateyu 13:45, 46) Umenewu ndi mtima wabwino kwambiri kukhala nawo.

15. Kodi Mkristu wina wachitsikana ku Liberia anachita chiyani poika zinthu za Ufumu poyamba?

15 Masiku anonso anthu ambiri ali ndi mtima wabwino ngati umenewu. Mwachitsanzo, ku Liberia Mkristu wina wachitsikana anapatsidwa mwayi wokaphunzira ku yunivesite. M’dziko limenelo, anthu amaona kuti kupeza mwayi woterewu ndiye chiyambi cha tsogolo labwino. Komabe iye anali mpainiya, kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse, ndipo anali atalandira kalata yomuuza kuti akachite upainiya wapadera kwa kanthawi ku dera linalake. Iye anasankha kufuna Ufumu choyamba ndi kukhalabe mu utumiki wa nthawi zonse. Anapita ku dera limene anamutumizalo, ndipo m’miyezi itatu anayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 21. Mlongo wachitsikana ameneyu, ndiponso anthu ena ambiri onga iye, amafunafuna Ufumu choyamba, ngakhale pamene kuchita zimenezo kungawamanitse zinthu zinazake zakuthupi. Kodi iwo amatha bwanji kukhala ndi maganizo oterewa m’dziko lokonda chumali? Amakwanitsa chifukwa ayesetsa kukhala ndi makhalidwe ena angapo abwino. Tiyeni tikambiraneko ena mwa makhalidwewa.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani kudzichepetsa n’kofunika kuti tithe kukhulupirira Yehova? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo a Mulungu?

16 Kudzichepetsa: Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru.” (Miyambo 3:5-7) Nthawi zina zochita zinazake zingaoneke zothandiza malinga ndi mmene dzikoli limaonera zinthu. (Yeremiya 17:9) Ngakhale n’choncho Mkristu woona mtima amafuna kuti Yehova amutsogolere. (Salmo 48:14) ‘M’njira zake zonse,’ kaya ndi nkhani za mu mpingo, za maphunziro kapena ntchito yolembedwa, pa nthawi yopuma, kapenanso pa chilichonse, iye modzichepetsa amafunafuna uphungu wa Yehova.​—Salmo 73:24.

17 Kukhulupirira malonjezo a Yehova: Paulo anati: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira  kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumufuna Iye.” (Ahebri 11:6) Ngati tikukayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake, zingaoneke kuti ‘kuchita nalo’ kwambiri dziko lapansi ndiko kwabwino. (1 Akorinto 7:31) Koma ngati chikhulupiriro chathu n’cholimba, tidzatsimikiza mtima kufunafuna Ufumu choyamba. Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba? Mwa kuyandikira Yehova kwambiri popemphera nthawi zonse mochokera pansi pamtima ndiponso pophunzira patokha nthawi zonse. (Salmo 1:1-3; Afilipi 4:6, 7; Yakobo 4:8) Tingapemphere mofanana ndi Mfumu Davide kuti: “Ndakhulupirira Inu, Yehova: Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga. Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga.”​—Salmo 31:14, 19.

18, 19. (a) Kodi kukhala achangu kumatithandiza bwanji kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova? (b) N’chifukwa chiyani Mkristu ayenera kulolera kudzimana?

18 Kuchita khama potumikira Yehova: Paulo anati munthu akamakhulupirira malonjezo a Yehova amakhala wachangu. Iye analemba kuti: “Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.” (Ahebri 6:11) Ngati tikuchita zambiri potumikira Yehova, iye adzatithandiza. Nthawi iliyonse imene watithandiza moteromo, timamudalira kwambiri, ndipo timakhala “okhazikika, osasunthika.” (1 Akorinto 15:58) Chikhulupiriro chathu mwa iye chimalimba, ndiponso timatsimikizira kuti chiyembekezo chathu n’chenicheni.​—Aefeso 3:16-19.

19 Kulolera kudzimana: Paulo, pofuna kutsatira Yesu, anasiya ntchito yomwe ikanamupatsa moyo wawofuwofu. N’zosakayikitsa kuti iye anasankha bwino, ngakhale kuti moyo wake nthawi zina unali wovuta chifukwa chosowa zinthu zina zakuthupi. (1 Akorinto 4:11-13) Yehova salonjeza kuti amene akumutumikira azikhala moyo wofewa, ndipotu nthawi zina atumiki ake amapirira mavuto aakulu. Tikalolera kukhala ndi moyo wosalira zambiri, ndiponso tikalolera kudzimana zinthu zina, timasonyeza kuti ndife otsimikiza mtima kwambiri kutumikira Yehova.​—1 Timoteo 6:6-8.

20. N’chifukwa chiyani kuleza mtima n’kofunika kwambiri kwa munthu amene amaika zinthu za Ufumu poyamba?

20 Kuleza mtima: Wophunzira Yakobo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye.” (Yakobo 5:7) Kuleza mtima n’kovuta m’dziko losinthasinthali. Timafuna zinthu zizichitika mofulumira. Koma Paulo anatilimbikitsa kutsanzira amene ‘ali kulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.’ (Ahebri 6:12) Khalani ndi mtima wofuna kudikira nthawi ya Yehova. Moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso ndithudi ndi woyenera kuudikirira!

21. (a) Kodi timasonyezanji tikamaika zinthu za Ufumu poyamba? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

21 Inde, malangizo a Yesu a kufunafuna Ufumu choyamba ndi othandiza. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timakhulupiriradi Yehova ndiponso kuti tasankha njira yokhalira ndi moyo yomwe ndi yokhayo ingatetezedi Mkristu. Komabe, Yesu anatilangizanso kuti tipitirize ‘kufuna chilungamo’ cha Mulungu. M’nkhani yotsatirayi tidzaona chifukwa chake mawu olimbikitsa amenewa ali ofunika kwambiri makamaka masiku ano.

Kodi Mungalongosole?

• Kodi Yesu anatilimbikitsa kukhala ndi maganizo otani pa zinthu zakuthupi?

• Kodi fanizo la Yesu la ngamila ndi diso la singano likutiphunzitsa chiyani?

• Kodi ndi makhalidwe achikristu ati amene amatithandiza kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Ambiri amene anamvetsera mawu a Yesu anali osauka

[Chithunzi patsamba 23]

Mnyamata wolemera anakonda chuma chake kuposa mmene anakondera Mulungu

[Chithunzi patsamba 23]

Munthu wa malonda wa m’fanizo la Yesu anagulitsa zonse anali nazo kuti agule ngale imodzi ya mtengo wapatali

[Chithunzi patsamba 24]

Ngati tikuchita zambiri potumikira Yehova, iye adzatithandiza