Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Chilungamo Kungatiteteze

Kufunafuna Chilungamo Kungatiteteze

 Kufunafuna Chilungamo Kungatiteteze

“Muthange mwafuna . . . chilungamo [cha Mulungu].”​—MATEYU 6:33.

1, 2. Kodi Mkristu wina wachitsikana anasankha kuchitanji, ndipo anatero chifukwa chiyani?

MKRISTU wina wachitsikana ku Asia anali mlembi mu ofesi inayake ya boma. Anali wolimbikira ntchito, ankafika mofulumira ndipo sanali kugwira ntchito mwaulesi. Komabe, popeza kuti ntchito yakeyo sinali yokhalitsa, inafika nthawi yoti akuluakulu aone ngati akuyenera kupitiriza. Mkulu woyang’anira dipatimentiyo anauza mtsikanayo kuti angamulembenso kuti apitirize ntchitoyo ndiponso akhoza kumukweza udindo ngati atachita naye zachisembwere. Mtsikanayo anakana kwamtuwagalu, ngakhale kuti kuteroko kunatanthauza kuti ntchito ithera pompo.

2 Kodi Mkristu wachitsikana ameneyu anaganiza bwino? Inde, chifukwa anali kutsatira mosamalitsa mawu a Yesu akuti: “Koma muthange mwafuna . . . chilungamo [cha Mulungu].” (Mateyu 6:33) Kwa iye, kutsatira mfundo zolungama za makhalidwe abwino kunali kofunika kwambiri kuposa kupeza mwayi winawake pochita chiwerewere.​—1 Akorinto 6:18.

Kufunika kwa Chilungamo

3. Kodi munthu wolungama ndi wotani?

3 Munthu wolungama ndi munthu amene amatsatira mfundo za makhalidwe abwino ndiponso amakhala woona mtima. Mu Baibulo, mawu a Chigiriki ndi Chihebri akuti “chilungamo” amatanthauzanso “kulondola” kapena “kuwongoka mtima.” Kukhala wolungama si ndiko kudzilungamitsa, kapena kuti kudziyesa wolungama pogwiritsa ntchito mfundo zako zomwe. (Luka 16:15) Ndiko kukhala wowongoka mtima potengera miyezo ya Yehova. Inde, ndiko chilungamo cha Mulungu.​—Aroma 1:17; 3:21.

4. N’chifukwa chiyani chilungamo n’chofunika kwa Mkristu?

4 N’chifukwa chiyani chilungamo chili chofunika? N’chifukwa chakuti Yehova, “Mulungu wa chilungamo,” amayanja anthu ake akamachita chilungamo. (Salmo 4:1; Miyambo 2:20-22; Habakuku 1:13) Aliyense amene sachita chilungamo sangakhale naye paubwenzi wolimba. (Miyambo 15:8) N’chifukwa chake mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo,” limodzi ndi makhalidwe ena ofunika kwambiri. (2 Timoteo 2:22) N’chifukwa chakenso Paulo pondandalika mbali zosiyanasiyana za zovala zathu zankhondo zauzimu anatchulaponso “chapachifuwa cha chilungamo.”​—Aefeso 6:14.

5. Kodi zingatheke bwanji kuti anthu opanda ungwiro afunefune chilungamo?

5 Zoonadi, palibe munthu wolungama kotheratu. Anthu onse anatengera kupanda ungwiro kwa Adamu, ndipo onse amabadwa ochimwa, osalungama. Ngakhale n’choncho, Yesu anati tiyenera kufunafuna chilungamo. Kodi zingatheke bwanji? Zingatheke chifukwa Yesu anapereka moyo wake wangwiro kukhala dipo lotiwombola, ndipo ngati tikhulupirira nsembe imeneyo, Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira machimo athu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; Aroma 5:8, 9, 12, 18) Pa maziko amenewo, tikamaphunzira miyezo yolungama ya Yehova ndi kumayesetsa kuisunga, ndiponso tikamapemphera kuti atithandize kuthana ndi zofooka zathu, Yehova amavomereza kulambira kwathu. (Salmo 1:6; Aroma 7:19-25; Chivumbulutso 7:9, 14) Zimenezitu n’zokhazika mtima pansi kwambiri!

Kukhala Wolungama M’dziko Lopanda Chilungamo

6. N’chifukwa chiyani dziko linali malo oopsa kukhalamo kwa Akristu oyambirira?

6 Pamene ophunzira a Yesu anapatsidwa ntchito yokhala mboni zake “kufikira malekezero ake a  dziko,” zinthu sizinali bwino m’dziko. (Machitidwe 1:8) Gawo lonse limene anapatsidwa kuti azilalikiramo linali ‘kugona mwa woipayo,’ Satana. (1 Yohane 5:19) Dziko linali litadzala ndi mzimu woipa umene iye amalimbikitsa, ndipo Akristu ukanawafika. (Aefeso 2:2) Kwa iwo, dziko linali malo oopsa kukhalamo. Chimene chikanawathandiza kupirira ndi kukhalabe okhulupirika ndicho kufunafuna choyamba chilungamo cha Mulungu. Ambiri anapirira bwinobwino, koma ena ochepa anapatutsidwa pa “khwalala la chilungamo.”​—Miyambo 12:28; 2 Timoteo 4:10.

7. Kodi ndi maudindo otani amene Akristu ali nawo, omwe kuti awakwanitse amafunika kukana zinthu zoipitsa za m’dzikoli?

7 Kodi masiku ano dziko ndi malo abwino Akristu kukhalamo? Ayi, si abwino. N’loipa kwambiri kuposa mmene linalili m’nthawi ya Akristu oyambirira. Ndiponso, Satana anaponyedwa ku dziko lapansi ndipo ali pa nkhondo yoopsa ndi Akristu odzozedwa, “otsala a mbewu [ya mkazi], amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:12, 17) Satana amalimbananso ndi aliyense amene amagwirizana ndi “mbewu” imeneyo. Komabe, Akristu sangachoke m’dzikoli n’kukabisala kwinakwake. Iwo ayenerabe kukhala m’dzikoli ngakhale kuti saali mbali yake. (Yohane 17:15, 16) Ndipo ayenera kulalikira m’dziko lomweli kuti afufuze anthu a mitima yabwino ndi kuwaphunzitsa kukhala ophunzira a Kristu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Motero, popeza kuti Akristu sangapeweretu zinthu zoipitsa zomwe zili m’dzikoli, afunika kukana zinthu zoterozo. Tiyeni tikambirane zinayi mwa zinthu zoipitsa zimenezi.

Msampha wa Chiwerewere

8. N’chifukwa chiyani Aisrayeli anayamba kulambira milungu ya Amoabu?

8 Ulendo wawo wa zaka 40 uli pafupi kutha, Aisrayeli ambiri anapatuka pakhwalala, kapena kuti njira, ya chilungamo. Iwo anali ataona Yehova akuwalanditsa pa nthawi zochuluka, ndipo tsopano anatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Komatu panthawi yofunika kwambiri imeneyo, anayamba kutumikira milungu ya Amoabu. N’chifukwa chiyani anatero? Anagonjera “chilakolako cha thupi.” (1 Yohane 2:16) Nkhani yake imati: “Anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Moabu.”​—Numeri 25:1.

9, 10. Kodi n’chiyani masiku ano chimene chimachititsa kuti kukhale kofunika kwambiri kumakumbukira nthawi zonse kuti zilakolako zolakwika zathupi zikhoza kuipitsa munthu?

9 Nkhani imeneyi imasonyeza mmene zilakolako zolakwika za thupi zingaipitsire anthu amene saali tcheru. Tiyenera kutengapo phunziro pamenepa, makamaka popeza kuti anthu ambiri masiku ano amaona chiwerewere ngati khalidwe lovomerezeka. (1 Akorinto 10:6, 8) Lipoti lina lochokera m’dziko la United States linati: “Chisanafike chaka cha 1970, kulikonse m’dziko la United States malamulo sanali kulola kuti mwamuna ndi mkazi azikhalira pamodzi popanda kukwatirana mwalamulo. Koma tsopano zili ponseponse. Anthu oposa theka la anthu onse amene amalembetsa ukwati wawo woyamba amakhala oti poyambirira anangolowana.” Zimenezi ndiponso makhalidwe ena otayirira sikuti zikuchitika m’dziko limodzi lokhalo. Zili kulikonse padziko lapansi, ndipo chomvetsa chisoni n’chakuti Akristu ena atengera zimenezi, ena mpaka achotsedwa mu mpingo wachikristu.​—1 Akorinto 5:11.

10 Ndiponso, zinthu zolimbikitsa chiwerewere zikuoneka kuti zili paliponse. Mafilimu ndi mapulogalamu  a pa TV amasonyeza kuti ndi zovomerezeka kwambiri kuti achinyamata azigonana asanalowe m’banja. Kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha amakuonetsa kuti n’kosalakwika. Ndipo mafilimu ambiri akumka naonetsa zithunzi zonyansa kwambiri za anthu akugonana. Zithunzi zoterezi zimapezekanso mosavuta pa Intaneti. Mwachitsanzo, bambo wina amene amalemba nkhani m’nyuzipepala, analemba kuti tsiku lina mwana wake wamwamuna wa zaka seveni atachokera kusukulu anauza bambo akewo mosangalala kuti mnzake wa kusukulu anapeza malo enaake pa Intaneti pamene amaonetsa akazi amaliseche akuchita zachiwerewere. Bambowo anadzidzimuka nazo kwambiri, koma kodi ndi ana angati amene amaona zoterezi pa Intaneti osauza makolo awo? Ndiponso, kodi ndi makolo angati amene amadziwa zomwe zili m’masewera a pa kompyuta kapena pa TV omwe ana awo amasewera? Masewera ambiri otchuka amakhala a zachiwerewere, komanso zauchiwanda ndi zachiwawa.

11. Kodi banja lingatetezedwe bwanji ku chiwerewere chimene chili m’dzikoli?

11 Kodi banja lingatani kuti likane zonyansa zoterezi, zomwe anthu amaziona ngati zosangalatsa? Lingathe kutero mwa kufunafuna choyamba chilungamo cha Mulungu, kukana kukhudzidwa ndi chilichonse choipa. (2 Akorinto 6:14; Aefeso 5:3) Makolo amene amayang’anira bwino ana awo akamachita zinthu zosiyanasiyana n’kumawaphunzitsa kuti azikonda Yehova ndi malamulo ake olungama, amawathandiza kuti azidana zedi ndi zithunzi zolaula, masewera olaula osewerera pa kompyuta kapena pa TV, mafilimu oonetsa zachiwerewere, ndi zokopa zina zosalungama.​—Deuteronomo 6:4-9. *

Kuopsa Kotengera za Anthu a M’dera Lanu

12. Kodi ndi vuto lanji limene linalipo pakati pa Akristu oyambirira?

12 Paulo ali ku Lustra ku Asiyamina, anachiritsa munthu wina mozizwitsa. Nkhani yake imati: “Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mawu awo, nati m’chinenero cha Lukaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu. Ndipo anamutcha Barnaba, Zeu; ndi Paulo, Herme, chifukwa anali wotsogola kunena.” (Machitidwe 14:11, 12) Kenako anthu omwewo anafuna kupha Paulo ndi Barnaba. (Machitidwe 14:19) N’zachionekere kuti anthuwo sankachedwa kutengeka ndi zonena za anzawo a m’deralo. Zikuoneka kuti anthu ena akumeneko atakhala Akristu, sanasiye kukhulupirira zamalodza. M’kalata imene analembera Akristu a ku Kolose, Paulo anawachenjeza za “kugwadira kwa angelo.”​—Akolose 2:18.

13. Kodi miyambo ina imene Mkristu afunika kupewa ndi iti, nanga angatani kuti akhale wolimba mtima kuchita zimenezi?

13 Masiku ano, nawonso Akristu oona afunika kupewa miyambo yotchuka imene inachokera pa malingaliro achipembedzo osemphana ndi mfundo zachikristu. Mwachitsanzo, m’mayiko ena miyambo yambiri yokhudzana ndi kubadwa kwa ana kapena maliro ndi yochokera pa bodza lakuti tili ndi mzimu umene suufa munthu akamwalira. (Mlaliki 9:5, 10) M’mayiko ena muli mwambo  wakuti atsikana aang’ono aziwadula maliseche. * Imeneyi ndi nkhanza kwambiri, ndipo ndi mwambo wosafunikira umene sugwirizana n’komwe ndi chikondi chimene makolo achikristu ayenera kusonyeza ana awo powasamalira. (Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 6:4) Kodi Akristu angakane bwanji kutengera miyambo ya m’dera lawo ndi kuisiya miyamboyo? Angathe kutero mwa kukhulupirira Yehova kotheratu. (Salmo 31:6) Mulungu wolungama amalimbitsa mtima ndiponso amasamalira amene amamuuza ndi mtima wonse kuti: “Pothawirapo panga ndi linga langa [ndinu]; Mulungu wanga, amene ndimukhulupirira.”​—Salmo 91:2; Miyambo 29:25.

Musaiwale Yehova

14. Kodi Yehova anawachenjeza chiyani Aisrayeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa?

14 Aisrayeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawachenjeza kuti asamuiwale. Iye anati: “Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lerolino; kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo; ndipo zitachuluka ng’ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitachulukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitachulukanso zonse muli nazo; mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu.”​—Deuteronomo 8:11-14.

15. Kodi tingatani kuti tionetsetse kuti sitikuiwala Yehova?

15 Kodi zofanana ndi zimenezi zingachitike masiku ano? Inde zingachitike ngati tikutsogoza zinthu zolakwika. Komabe ngati tikufunafuna choyamba chilungamo cha Mulungu, chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu chidzakhala kulambira koyera. Monga mmene Paulo anatilimbikitsira, ‘tidzachita machawi’ ndipo tidzakhala achangu mu utumiki wathu. (Akolose 4:5; 2 Timoteo 4:2) Koma ngati timaona kufika pamisonkhano ndiponso utumiki wa kumunda kukhala zosafunika kwenikweni poyerekeza ndi kupuma kapena kupeza njira zosangalalira, tikhoza kuiwala Yehova m’lingaliro lakuti tingamamuike pa malo achiwiri m’moyo wathu. Paulo ananena kuti m’masiku otsiriza anthu adzakhala “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:4) Akristu oona mtima amadziyang’ana bwinobwino nthawi ndi nthawi kuti aone ngati sakutengera kaganizidwe koteroko.​—2 Akorinto 13:5.

Pewani Mzimu Wodziimira Panokha

16. Kodi ndi mzimu wolakwika wotani umene Hava ndi Akristu ena m’masiku a Paulo anali nawo?

16 M’munda wa Edene, Satana anatha kunyengerera Hava kuti atengeke ndi chikhumbo chake chadyera chofuna kudziimira payekha. Hava anafuna kuti azisankha yekha chabwino ndi choipa. (Genesis 3:1-6) M’nthawi ya Akristu oyambirira, ena mu mpingo wa ku Korinto analinso ndi mzimu ngati womwewo, wofuna kudziimira paokha. Iwo ankaganiza kuti anali kudziwa zambiri kuposa Paulo, ndipo iye anawatchula monyoza kuti atumwi oposatu.​—2 Akorinto 11:3-5; 1 Timoteo 6:3-5.

17. Kodi tingatani kuti tipewe kukhala ndi mzimu wodziimira patokha?

17 Masiku ano, anthu ambiri m’dzikoli ndi “aliuma olimbirira, otukumuka mtima,” ndipo Akristu ena atengera kaganizidwe koteroko. Ena mpaka afika potsutsa choonadi. (2 Timoteo 3:4;  Afilipi 3:18) Pa nkhani yokhudza kulambira koyera, n’kofunika kwambiri kuti tiziyang’ana kwa Yehova kuti atitsogolere ndipo tizigwirizana ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiponso akulu mu mpingo. Imeneyi ndiyo njira yofunira chilungamo, ndipo imatiteteza kuti tisakhale ndi mzimu wodziimira patokha. (Mateyu 24:45-47; Salmo 25:9, 10; Yesaya 30:21) Mpingo wa odzozedwa ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” Yehova wakhazikitsa mpingowu kuti utiteteze ndi kutitsogolera. (1 Timoteo 3:15) Kuzindikira kufunika kwake kudzatithandiza kuti ‘tisachite kanthu mwa ulemerero wopanda pake,’ kapena kuti mwa mzimu wodzikuza, koma kuti tizigonjera modzichepetsa ku chifuniro cholungama cha Yehova.​—Afilipi 2:2-4; Miyambo 3:4-6.

Tsanzirani Yesu

18. Kodi tikulimbikitsidwa kutsanzira Yesu m’njira ziti?

18 Baibulo linalosera za Yesu kuti: “Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa.” (Salmo 45:7; Ahebri 1:9) Umenewutu ndi mtima wabwino kwambiri woyenera kutsanzira. (1 Akorinto 11:1) Yesu sanangodziwa chabe miyezo yowongoka ya Yehova, komanso anaikonda. Motero pamene Satana anamuyesa m’chipululu, Yesu sanazengereze konse kukana, ndipo anakana motsimikiza mtima kuchoka “m’njira ya chilungamo.”​—Miyambo 8:20; Mateyu 4:3-11.

19, 20. Kodi kufunafuna chilungamo kuli n’zotsatirapo zabwino ziti?

19 N’zoona kuti zilakolako zosalungama zathupi zingakhale zamphamvu kwambiri. (Aroma 7:19, 20) Komabe, ngati timaona chilungamo kukhala chofunika kwambiri kwa ife, zingatilimbikitse kukana zoipa. (Salmo 119:165) Kukonda kwambiri chilungamo kungatiteteze tikayang’anizana ndi zoipa. (Miyambo 4:4-6) Kumbukirani kuti nthawi zonse pamene tigonja poyesedwa, Satana ndiye amapambana. Kodi sizingakhale bwino kwambiri kumukaniza kuti Yehova apambane?​—Miyambo 27:11; Yakobo 4:7, 8.

20 Chifukwa chakuti Akristu oona amafunafuna chilungamo, iwo ndi “odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Kristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.” (Afilipi 1:10, 11) Amavala “munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:24) Iwo ndi ake a Yehova ndipo amakhala ndi moyo kuti amutumikire, osati kuti adzikondweretse. (Aroma 14:8; 1 Petro 4:2) Izi ndizo zimalamulira zoganiza zawo ndiponso zochita zawo. Iwo amakondweretsa kwambiri mtima wa Atate wawo wakumwamba.​—Miyambo 23:24.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mungapeze mfundo zothandiza kwambiri zonena za zimene makolo angachite kuti ateteze banja lawo ku chiwerewere mu buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 13 Mwambowu kale ankautcha kuti mdulidwe wa akazi.

Kodi Mungalongosole?

• N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kufunafuna chilungamo?

• Kodi zingatheke bwanji kuti Mkristu wopanda ungwiro afunefune chilungamo?

• Kodi ndi zinthu zina ziti m’dzikoli zimene Mkristu ayenera kupewa?

• Kodi kufunafuna chilungamo kumatiteteza motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Kwa otsatira a Yesu, dziko linali malo oopsa kukhalamo

[Chithunzi patsamba 27]

Ana amene amaphunzitsidwa kukonda Yehova amathandizidwa kudana zedi ndi chiwerewere

[Chithunzi patsamba 28]

Aisrayeli ena atalemera m’Dziko Lolonjezedwa anaiwala Yehova

[Chithunzi patsamba 29]

Mofanana ndi Yesu, Akristu amadana ndi zinthu zosalungama