Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu amene Stefano ananena pa Machitidwe 7:59 akusonyeza kuti mapemphero athu ayenera kupita kwa Yesu?

Lemba la Machitidwe 7:59 limati: “Ndipo anam’ponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Mawu amenewa adzutsa mafunso m’maganizo mwa anthu ena, chifukwa Baibulo limati Yehova ndiye “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Kodi Stefano anapempheradi kwa Yesu? Ngati anatero, kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yesu n’chimodzimodzi ndi Yehova?

Baibulo la King James limati Stefano “anali kupemphera kwa Mulungu.” Choncho m’pomveka kuti anthu ambiri akawerenga mawu amenewa amakhala ndi maganizo ofanana ndi a katswiri wina wa Baibulo dzina lake Matthew Henry, amene ananena kuti: “Pamenepa Stefano anapemphera kwa Kristu, ndipo ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi.” Komabe, maganizo amenewo ndi olakwika. Chifukwa chiyani?

Buku lakuti Barnes’ Notes on the New Testament, limati: “Mawu akuti Mulungu m’mabuku oyambirira mulibe, ndipo sanayenera kupezeka m’mabaibulo ochita kumasuliridwa. [M’zolembedwa zapamanja] zoyambirira zonse mawu amenewa mulibe.” Kodi mawu oti “Mulungu” anapezeka bwanji m’vesi limeneli? Katswiri wina dzina lake Abiel Abbot Livermore, anati chimenechi ndi “chitsanzo cha mmene omasulira ena ankasinthira zinthu kuti zigwirizane ndi zimene iwowo ankakhulupirira.” Choncho mabaibulo ambiri amakono amachotsa mawu oti Mulungu amenewa, amene sanayenera kupezeka pa vesi limeneli.

Komabe, mabaibulo ambiri amanena kuti Stefano “anapemphera” kwa Yesu. Ndipo mawu a m’munsi a m’Baibulo la New World Translation amati mawu oti “alikuitana” angatanthauzenso “kupempha, pemphero.” Kodi zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu ndiye Mulungu Wamphamvuyonse? Ayi. Buku lakuti Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limafotokoza kuti, pa vesi limeneli mawu oyambirira achigiriki amene anawagwiritsa ntchito oti e·pi·ka·leʹo, amatanthauza: “Kupempha thandizo; . . . kupempha munthu waudindo kuti akuthandize.” Paulo anagwiritsa ntchito mawu omwewo pamene ananena kuti: “Nditulukira [“Ndikuchita apilo,” NW] kwa Kaisara.” (Machitidwe 25:11) Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limanena molondola kuti Stefano ‘anali kuitana’ Yesu.

Kodi n’chiyani chinachititsa Stefano kuitana Yesu mwa njira yoteroyo? Malinga ndi lemba la Machitidwe 7:55, 56, Stefano “pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.” Nthawi zonse Stefano ankapemphera mapemphero ake kwa Yehova kudzera m’dzina la Yesu. Koma chifukwa choona m’masomphenya Yesu amene anali ataukitsidwa, zikuoneka kuti Stefano anaona kuti anali womasuka kumulankhula mwachindunji, ndipo anamupempha kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Stefano ankadziwa kuti Yesu anali atapatsidwa udindo woukitsa akufa. (Yohane 5:27-29) Choncho anapempha Yesu kuti asunge mzimu wake, kapena mphamvu ya moyo wake, kufikira tsiku limene adzamuukitse kuti akhale ndi moyo wosafa kumwamba.

Kodi mawu achidule amene Stefano ananenawa ndi chitsanzo kwa ife choti tizipemphera kwa Yesu? Ayi ndithu. Chinthu chimodzi chomwe tikuona apa n’choti Stefano anasiyanitsa bwinobwino Yesu ndi Yehova, chifukwa nkhaniyo imati anaona Yesu “alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.” Komanso, zimene zinali kuchitika pamenepa si zinthu zoti zimachitikachitika. Munthu winanso yekhayo amene ananena mawu ngati amenewo mwachindunji kwa Yesu anali mtumwi Yohane. Nayenso anamulankhula Yesu mwachindunji atamuona m’masomphenya.​—Chivumbulutso 22:16, 20.

Ngakhale kuti Akristu masiku ano moyenera amapemphera mapemphero awo kwa Yehova Mulungu, nawonso ali ndi chikhulupiriro cholimba choti Yesu ndiye “kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Chikhulupiriro choti Yesu ali ndi mphamvu yotha kuukitsa otsatira ake akufa chingatithandize ndi kutilimbikitsa panthawi za mavuto monga momwe chinathandizira ndi kulimbikitsira Stefano.