Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwirizana Chifukwa Chokonda Mulungu

Kugwirizana Chifukwa Chokonda Mulungu

 Kugwirizana Chifukwa Chokonda Mulungu

MPINGO wachikristu utapangidwa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo ino imene inayamba Yesu atabadwa, unadziwika kwambiri chifukwa cha kugwirizana kwa otsatira ake, ngakhale anali ochokera kosiyanasiyana. Olambira Mulungu oona amenewo anachokera ku mayiko a ku Asia, ku Ulaya, ndi ku Africa kuno. Anali anthu oti anakula mosiyanasiyananso. Ena a iwo kale anali ansembe, asilikali, othawa kwawo, ochita zamalonda, akatswiri osiyanasiyana, ndi eni mabizinezi. Ena anali Ayuda pamene ena anali Akunja. Ambiri a iwo kale anali achigololo, ogonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, zidakwa, mbala, kapena olanda. Komabe, atasanduka Akristu anasiya makhalidwe awo oipawo n’kuyamba kugwirizana kwambiri chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro chimodzi.

Kodi n’chiyani chimene chinachititsa kuti Chikristu cha m’zaka 100 zoyambirira chithe kugwirizanitsa anthu onsewa? N’chifukwa chiyani anali pamtendere pakati pawo ndiponso ndi anthu ena? N’chifukwa chiyani sankachita nawo zipolowe ndi mikangano yobuka chifukwa chosiyana maganizo? N’chifukwa chiyani Chikristu choyambirira chinali chosiyana kwambiri ndi zipembedzo za masiku ano?

 N’chiyani Chinagwirizanitsa Anthu mu Mpingo?

Okhulupirira a m’zaka 100 zoyambirira anali ogwirizana makamaka chifukwa chokonda Mulungu. Akristu amenewo anazindikira kuti udindo wawo waukulu unali woti azikonda Mulungu woona, Yehova, ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi nzeru zawo zonse. Mwachitsanzo, mtumwi Petro, yemwe anali Myuda, anauzidwa kuti apite ku nyumba ya munthu wakunja, amene kale sakanacheza naye. Chimene chinamuchititsa kumvera chinali makamaka kukonda Yehova. Petro ndi Akristu ena oyambirira anali ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu umene unayamba chifukwa chodziwa molondola khalidwe Lake, zimene amakonda, ndi zimene sakonda. Patapita nthawi, olambira onse anazindikira kuti Yehova ankafuna kuti ‘amangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.’​—1 Akorinto 1:10; Mateyu 22:37; Machitidwe 10:1-35.

Okhulupirira amenewo ankagwirizananso chifukwa chokhulupirira Yesu Kristu. Ankafuna kutsatira kwambiri mapazi ake. Iye anawalamulira kuti: “Mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu . . . Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Kukondana kwake kunayenera kukhala kodziperekadi, osati kwachiphamaso chabe. Kodi zotsatirapo zake zikanakhala zotani? Yesu popempherera anthu omukhulupirira anati: ‘Ndipempherera iwo . . . kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife.’​—Yohane 17:20, 21; 1 Petro 2:21.

Yehova anatsanulira mzimu wake, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, pa atumiki ake oona. Mzimu umenewu unalimbikitsa mgwirizano pakati pawo. Unawathandiza kumvetsetsa ziphunzitso za m’Baibulo, ndipo mipingo yonse inkagwirizana nazo ziphunzitso zimenezi. Olambira Yehova analalikira uthenga wofanana, wonena za kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Mesiya, umene uli boma lakumwamba lomwe lidzalamulire anthu onse. Akristu oyambirira anamvetsa udindo wawo woti ‘sanali a dziko lapansi.’ Choncho anthu akamaukira boma kapena pakakhala nkhondo, Akristu sankatenga nawo mbali. Ankayesetsa kukhala pamtendere ndi aliyense.​—Yohane 14:26; 18:36; Mateyu 6:9, 10; Machitidwe 2:1-4; Aroma 12:17-21.

Okhulupirira onse anachita mbali yawo kuti alimbikitse mtendere. Anachita zimenezi motani? Mwa kuonetsetsa kuti khalidwe lawo linali logwirizana ndi Baibulo. Choncho mtumwi Paulo analembera Akristu kuti: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, . . . nimuvale munthu watsopano.”​—Aefeso 4:22-32.

Anapitirizabe Kukhala Ogwirizana

Komabe, okhulupirira a m’zaka 100 zoyambirira sanali angwiro, ndipo panachitika zinthu zimene zikanatha kusokoneza mgwirizano wawo. Mwachitsanzo, lemba la Machitidwe 6:1-6 limati panabuka kusamvana pakati pa Akristu omwe anali Ayuda amene ankalankhula Chigiriki ndi amene ankalankhula Chihebri chifukwa olankhula Chigirikiwo ankaona kuti akuchitiridwa tsankho. Koma atumwi atauzidwa nkhaniyo, anachitapo kanthu mwamsanga ndiponso mwachilungamo. Kenaka, chiphunzitso cha mpingo pa nkhani yokhudza zimene anthu omwe sanali Ayuda anayenera kuchita mumpingo wachikristu, chinayambitsanso kusiyana maganizo. Chigamulo chinaperekedwa potsatira mfundo za m’Baibulo, ndipo aliyense anagwirizana nacho chigamulocho.​—Machitidwe 15:1-29.

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti kusemphana maganizo sikunachititse kuti mu mpingo wachikristu woyambirira mukhale kusagwirizana chifukwa chosiyana mitundu kapena chifukwa chokakamira ziphunzitso zinazake. N’chifukwa chiyani kusemphana maganizoko sikunawononge mgwirizano wawo? Chifukwa choti zinthu zimene zinali kuwagwirizanitsa zinali zamphamvu kwambiri moti zinatha kuthandiza anthu a mumpingo  woyambirirawo kupitirizabe kukhala ogwirizana ndiponso kukhala pamtendere. Zinthu zake zinali kukonda Yehova, kukhulupirira Yesu Kristu, kukondana modzipereka, kulolera kuti mzimu woyera uwatsogolere, kumvetsa mofanana ziphunzitso za m’Baibulo, ndi kukhala ofunitsitsa kusintha khalidwe lawo.

Kulambira Mogwirizana Masiku Ano

Kodi masiku ano zingatheke kukhala ogwirizana m’njira yofanana ndi imeneyo? Kodi zinthu zomwezi zingachititsenso anthu a chipembedzo chimodzi kukhala ogwirizana n’kuwathandiza kukhala pamtendere ndi anthu a mitundu yonse padziko lonse lapansi? Inde, zingathe kutero. Mboni za Yehova n’zogwirizana ndipo zili ndi ubale umene umaphatikizapo anthu opezeka m’mayiko ndi zilumba zopitirira 230 padziko lonse lapansi. Ndipo ndi zogwirizana chifukwa cha zinthu zomwezo zomwe zinagwirizanitsa Akristu m’zaka 100 zoyambirira.

Chinthu chachikulu kwambiri chimene chimachititsa kuti Mboni za Yehova zikhale zogwirizana ndicho kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu. Zimenezi zikutanthauza kuti zimayesetsa kukhala zokhulupirika kwa iye pa zochitika za mtundu uliwonse. Mboni za Yehova zimakhulupiriranso Yesu Kristu ndi zimene anaphunzitsa. Akristu amenewa amakondana ndi okhulupirira anzawo ndipo amalalikira uthenga wabwino wofanana wa Ufumu wa Mulungu kulikonse komwe amapezeka. Iwo amasangalala kulankhula za Ufumu umenewu ndi anthu a zipembedzo zonse, a mitundu yonse, ochokera m’mayiko onse, ndiponso a moyo wosiyanasiyana. Chinanso, Mboni za Yehova sizitenga nawo mbali m’zochitika za dziko, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asamagawikane chifukwa cha kusiyana pa ndale, chikhalidwe, ndi nkhani zamalonda, zimene zimagawanitsa kwambiri anthu. Mboni zonse zimadziwa kuti aliyense wa iwo amafunika kuchita mbali yake kuti alimbitse mgwirizano wawo ndipo zimatero mwa kukhala ndi khalidwe logwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.

Kugwirizana Kumakopa Ena

Mgwirizano umenewu nthawi zambiri wachititsa chidwi anthu amene sanali Mboni. Mwachitsanzo, Ilse * anali sisitere wachikatolika amene anali kukhala m’nyumba inayake ya masisitere ku Germany. Kodi n’chiyani chinamukopera kwa Mboni za Yehova? Ilse anati: “Sindinaoneponso anthu abwino kwambiri ngati amenewa. Sachita nawo nkhondo, ndipo sachita chinthu chilichonse chimene chingapweteke munthu wina. Amafuna kuthandiza anthu kuti adzakhale mosangalala pa dziko lapansi la paradaiso lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu.”

Ndiyeno pali Günther, amene anali msilikali wachijeremani amene anatumizidwa ku France pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Tsiku lina wansembe wachipolotesitanti anapempherera asilikali a m’gulu la Günther. Wansembeyo anapempha Mulungu kuti awadalitse, awateteze, ndiponso awathandize kupambana. Mapempherowo atatha, Günther anayamba ntchito yake yolondera gululo. Pogwiritsa ntchito chida choonera kutali, anaona asilikali omwe anali adani awo pankhondoyo nawonso akupemphera motsogozedwa ndi wansembe. Patapita nthawi izi zitachitika, Günther anati: “Mwachidziwikire wansembe winayo anapemphanso Mulungu kuti awadalitse, awateteze, ndiponso awathandize kupambana. Sindinathe kumvetsa chifukwa chake matchalitchi achikristu anapezeka kuti ali kumbali zosiyana pankhondo yomweyomweyo.” Zimenezi Günther sanaziiwale. Atakumana ndi Mboni za Yehova, zomwe sizimenya nawo nkhondo, Günther analowa gulu lawo, limene anthu ake amaonana ngati abale padziko lonse.

Ashok ndi Feema anali m’chipembedzo chinachake chakum’mawa. M’nyumba mwawo anali ndi kachisi wopembedzera mulungu winawake. M’banja mwawo mutagwa matenda aakulu, anaganiziranso mofatsa za chipembedzo chawo. Atakambirana ndi Mboni za Yehova, Ashok ndi Feema anachita chidwi kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa ndiponso chikondi chimene Mbonizo zimasonyezana ndipo panopa Ashok ndi Feema ndi ofalitsa akhama a uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova.

Ilse, Günther, Ashok, ndi Feema ndi ogwirizana ndi Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zomwe ndi gulu la abale la padziko lonse. Amakhulupirira lonjezo la m’Baibulo loti zinthu zimene zimawathandiza kulambira mogwirizana panopa, posachedwapa zidzagwirizanitsanso anthu onse omvera. Panthawi imeneyo sipadzakhalanso nkhanza, kusagwirizana, ndi kugawikana m’dzina la chipembedzo. Anthu padziko lonse lapansi adzakhala ogwirizana, polambira Yehova, Mulungu woona.​—Chivumbulutso 21:4, 5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Mayina ena amene atchulidwa mu nkhani ino asinthidwa.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Ngakhale anali ochokera kosiyana, Akristu oyambirira anali ogwirizana