Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Taphunzitsidwa Kuchitira Umboni Mokwanira

Taphunzitsidwa Kuchitira Umboni Mokwanira

 Taphunzitsidwa Kuchitira Umboni Mokwanira

“Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”​—MACHITIDWE 1:8.

1, 2. Kodi ntchito ya Petro inali yotani ndipo ndani anamupatsa ntchito imeneyo?

“YESU wa ku Nazarete . . . anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.” (Machitidwe 10:38, 42) Ndi mawu amenewo, mtumwi Petro anafotokozera Korneliyo ndi banja lake ntchito imene Petroyo anapatsidwa yoti akhale mlaliki.

2 Kodi Yesu anawapatsa liti ntchito imeneyo? Mwachidziwikire, Petro anali kuganizira zimene Yesu ananena ataukitsidwa, patangotsala nthawi yochepa kuti akwere kumwamba. Panthawi imeneyo, Yesu anauza ophunzira ake okhulupirika kuti: “Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Komabe, kwa kanthawi ndithu nthawi imeneyi isanafike, Petro anali atadziwa kale kuti monga wophunzira wa Yesu, anayenera kulankhula ndi anthu ena za chikhulupiriro chake mwa Yesu.

Kuphunzitsidwa Zaka Zitatu

3. Kodi Yesu anachita zodabwitsa zotani, ndipo anauza Petro ndi Andreya kuti ayambe kuchita chiyani?

3 Patapita miyezi ingapo Yesu atabatizidwa m’chaka cha 29 C.E., anakalalikira pamalo pamene Petro ndi mchimwene wake Andreya anali kusodza m’Nyanja ya Galileya. Anali atagwira  ntchito usiku wonse koma osaphula kanthu. Komabe, Yesu anauza Petro kuti: “Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.” Atachita zomwe Yesu ananena, “anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka awo analinkung’ambika.” Ataona zodabwitsazi, Petro anadzazidwa ndi mantha, koma Yesu anamukhazika mtima pansi, n’kumuuza kuti: “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.”​—Luka 5:4-10.

4. (a) Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kukonzekera kudzachitira umboni? (b) Kodi utumiki wa ophunzira a Yesu anati udzakhala wotani poyerekezera ndi wa Yesuyo?

4 Nthawi yomweyo, Petro ndi Andreya, komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anasiya mabwato awo n’kutsatira Yesu. Kwa zaka pafupifupi zitatu, anapitira limodzi ndi Yesu ku maulendo ake okalalikira ndipo Yesu anawaphunzitsa kulalikira. (Mateyu 10:7; Marko 1:16, 18, 20, 38; Luka 4:43; 10:9) Kumapeto kwa nthawi imeneyo, pa Nisani 14 m’chaka cha 33 C.E., Yesu anawauza kuti: “Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi.” (Yohane 14:12) Yesu anati ophunzira ake a m’tsogolo adzachitira umboni mokwanira ngati mmene iye anachitira, koma kudera lalikulu kuposa limene Yesu analalikira. Monga momwe Yesu anawauzira pasanapite nthawi yaitali, iwo ndi ophunzira onse a m’tsogolo anayenera kudzachitira umboni ku “mitundu yonse” mpaka “chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.”​—Mateyu 28:19, 20.

5. Kodi tingapindule bwanji ndi maphunziro amene Yesu anapatsa otsatira ake?

5 Ifeyo tikukhala mu “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3) Mosiyana ndi ophunzira oyambirirawo, sitingapitire limodzi ndi Yesu n’kuona momwe akulalikira kwa anthu. Komabe, tingaphunzire kwa iye mwa kuwerenga m’Baibulo za mmene ankalalikira ndi malangizo amene anapereka kwa otsatira ake. (Luka 10:1-11) Kuwonjezera apo, nkhani ino ifotokoza chinthu china chofunika kwambiri chomwe Yesu anasonyeza ophunzira ake. Chinthu chimenecho ndicho mtima wofunika kukhala nawo pa ntchito yolalikira.

Kumvera Anthu Chisoni

6, 7. Kodi ndi khalidwe liti la Yesu limene linachititsa kuti utumiki wake ukhale wogwira mtima, ndipo kodi tingamutsanzire bwanji pankhani imeneyi?

6 Kodi n’chifukwa chiyani umboni wa Yesu unali wogwira mtima kwambiri? Chifukwa chimodzi n’choti ankachita chidwi ndi anthu ndiponso ankawamvera chisoni. Wamasalmo ananeneratu kuti Yesu “adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi.” (Salmo 72:13) Iye anakwaniritsadi ulosi umenewo. Baibulo limati panthawi ina, Yesu “poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Ngakhale anthu ochimwa kwambiri anatha kuona kuti iye ankawamvera chisoni ndipo anafuna kupita kwa iye.​—Mateyu 9:9-13; Luka 7:36-38; 19:1-10.

7 Masiku ano, ifenso umboni wathu ungakhale wogwira mtima tikamamvera anthu chisoni mofanana ndi Yesu. Musanalowe mu utumiki, bwanji osayamba mwaima kaye n’kuganizira mmene anthu a m’dera lanu akufunikira kumva uthenga umene mukuwapititsirawo? Ganizirani mavuto amene ali nawo amene ndi Ufumu wokha womwe udzathetse. Khalani ndi maganizo oti aliyense akhoza kumvetsera, chifukwa simukudziwa amene angalabadire uthengawo. Mwina munthu wotsatira amene mukumane naye wakhala akupemphera kuti munthu ngati inuyo apite akamuthandize!

Kulalikira Chifukwa cha Chikondi

8. Potsanzira Yesu, kodi otsatira ake amalalikira uthenga wabwino chifukwa chiyani?

8 Uthenga wabwino umene Yesu ankalalikira unali wonena za kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Yehova, kuyeretsedwa kwa dzina Lake, ndi kusonyeza kuti Iye ndiye woyenera kulamulira. Nkhani zimenezi ndiye nkhani zofunika kwambiri zimene zikukhudza anthu masiku ano. (Mateyu 6:9, 10) Chifukwa chokonda Atate wake, Yesu anakhalabe wokhulupirika mpaka mapeto kuti achitire umboni mokwanira za Ufumu, umene udzathetse nkhani zimenezo. (Yohane 14:31) Chifukwa choti anthu otsatira Yesu masiku ano nawonso amafuna zomwezo, amachita khama akamalalikira mu utumiki. Mtumwi Yohane anati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo  ake,” kuphatikizapo lamulo loti tilalikire uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira.​—1 Yohane 5:3; Mateyu 28:19, 20.

9, 10. Kupatulapo kukonda Mulungu, kodi ndi chikondi china chiti chimene chimatilimbikitsa kuchitira umboni mokwanira?

9 Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine.” (Yohane 14:15, 21) Choncho chifukwa chokonda Yesu, tiyenera kuchitira umboni za choonadi ndi kumvera zinthu zina zomwe iye analamula. Panthawi ina pamene Yesu anaonekera kwa anthu ataukitsidwa, anauza Petro kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga. . . . Weta nkhosa zanga. . . . Dyetsa nkhosa zanga.” Kodi n’chiyani chinayenera kulimbikitsa Petro kuchita zimenezo? Yesu anasonyeza yankho lake pamene anafunsa Petro mobwerezabwereza kuti: “Kodi undikonda Ine? . . . Ukonda Ine kodi? . . . Kodi undikonda Ine?” Inde, chikondi chimene Petro anali nacho pa Yesu n’chimene chikanamulimbikitsa kuchitira umboni mokwanira, kupeza “ana a nkhosa” a Yesu, kenaka n’kukhala mbusa wawo wauzimu.​—Yohane 21:15-17.

10 Masiku ano, sitimuona Yesu pamaso m’pamaso, choncho sitimudziwa bwino monga momwe Petro ankamudziwira. Komabe, timamvetsa bwino tanthauzo la zimene Yesu anatichitira. Mitima yathu imakhudzidwa chifukwa cha chikondi chachikulu chimene chinamuchititsa kuti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Ahebri 2:9; Yohane 15:13) Timamva ngati mmene Paulo anamvera pamene analemba kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; . . . Adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye.” (2 Akorinto 5:14, 15) Timasonyeza kuti timayamikira kwambiri chikondi cha Yesu kwa ife ndi kuti ifenso timamukonda mwa kuyesetsa kumvera lamulo loti tichitire umboni mokwanira. (1 Yohane 2:3-5) Sitifuna kuiona mopepuka ntchito yolalikira, ngati kuti nsembe ya Yesu ndi nsembe wamba.​—Ahebri 10:29.

Kuika Maganizo Onse pa Zinthu Zofunika

11, 12. Kodi Yesu anabwera padziko lapansi kudzatani, ndipo anasonyeza bwanji kuti maganizo ake onse anali pantchito imeneyo?

11 Pamene Yesu anali pamaso pa Pontiyo Pilato, anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu sanalole kuti chilichonse chimudodometse pantchito yake yochitira umboni za choonadi. Zimenezo n’zimene Mulungu ankafuna kuti achite.

12 Satana anamuyesa kwambiri Yesu pankhani imeneyi. Yesu atangobatizidwa kumene, Satana anamuuza kuti adzamuthandiza kukhala munthu wotchuka padziko lonse lapansi, ndipo adzamupatsa “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo.” (Mateyu 4:8, 9) Kenaka, Ayuda anafuna kumuveka ufumu. (Yohane 6:15) Anthu ena masiku ano angamaganize kuti mwina zikanakhala bwino Yesu akanalola kuchita zimenezo, ndipo angamaganize kuti ngati Yesu akanakhala mfumu padziko lapansi, akanathandiza kwambiri anthu. Koma Yesu anakana maganizo amenewo. Maganizo ake onse anali pa kuchitira umboni za choonadi.

13, 14. (a) Kodi Yesu sanadodometsedwe ndi chiyani pantchito yake yofunika kwambiri? (b) Ngakhale kuti Yesu analibe chuma, kodi anakwanitsa kuchita chiyani?

13 Kuwonjezera apo, Yesu sanadodometsedwe chifukwa chofuna kupeza chuma. Choncho sanali munthu wolemera. Analibe ngakhale nyumba yakeyake. Panthawi ina, Yesu anati: “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Yesu atafa, chinthu chimodzi chokha cha mtengo wapatali chimene Baibulo limanena kuti anali nacho chinali malaya ake, amene asilikali achiroma anachitira maere. (Yohane 19:23, 24) Kodi pachifukwa chimenechi tingati Yesu anali munthu wolephera? Kutalitali!

14 Yesu anachita zinthu zambiri kuposa zomwe  munthu wolemera kwambiri wofuna kuthandiza anthu osauka akanachita. Paulo anati: “Mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.” (2 Akorinto 8:9; Afilipi 2:5-8) Ngakhale kuti Yesu analibe chuma, zimene anachita zinathandiza anthu osauka kuti athe kukhala ndi moyo wosatha ndiponso wangwiro. Timamuyamikira kwambiri chifukwa chochita zimenezo! Ndipo ndife osangalala kwambiri ndi mphoto imene anapatsidwa chifukwa choika maganizo ake onse pa kuchita chifuniro cha Mulungu.​—Salmo 40:8; Machitidwe 2:32, 33, 36.

15. Kodi n’chiyani chomwe chili chofunika kwambiri kuposa chuma?

15 Akristu amene amayesetsa kutsanzira Yesu masiku ano nawonso safuna kudodometsedwa ndi chuma. (1 Timoteo 6:9, 10) Amavomereza kuti chifukwa cha chuma munthu angakhale ndi moyo wofewa, koma amadziwa kuti sichingathandize munthu kupeza moyo wosatha. Mkristu akafa, chuma chake chimakhala chopanda phindu kwa iye, monga momwe malaya a Yesu analili opanda phindu kwa iye atafa. (Mlaliki 2:10, 11, 17-19; 7:12) Mkristu akafa, chinthu chokhacho chaphindu chimene amakhala nacho ndicho ubwenzi wake ndi Yehova ndi Yesu Kristu.​—Mateyu 6:19-21; Luka 16:9.

Osafooka Chifukwa Chotsutsidwa

16. Kodi Yesu anatani pamene anali kutsutsidwa?

16 Pamene Yesu anali kutsutsidwa, sanaiwale ntchito yake yochitira umboni za choonadi. Ndipo ngakhale anadziwa kuti pamapeto pa utumiki wake wapadziko lapansi adzaphedwa monga nsembe, sanafooke. Ponena za Yesu, Paulo anati: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Taonani kuti Yesu ‘ananyoza manyazi.’ Iye sanavutike ndi zimene adani ake ankamuganizira. Maganizo ake onse anali pa kuchita chifuniro cha Mulungu.

17. Kodi tingaphunzire chiyani pa kupirira kwa Yesu?

17 Potengapo phunziro pa kupirira kwa Yesu, Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.” (Ahebri 12:3) N’zoona, tikhoza kufooka chifukwa chotsutsidwa kapena kusekedwa tsiku ndi tsiku. Zikhoza kukhala zotopetsa kupitirizabe kulimbana ndi zokopa za m’dzikoli, zimene mwina zingakhumudwitse achibale athu, amene amatilimbikitsa kuti “tichite zaphindu” ndi moyo wathu. Komabe, mofanana ndi Yesu, timayembekezera Yehova kuti atithandize pamene tikuyesetsa kuika Ufumu patsogolo m’moyo wathu.​—Mateyu 6:33; Aroma 15:13; 1 Akorinto 2:4.

18. Kodi tingatengepo phunziro labwino lotani pa mawu amene Yesu ananena kwa Petro?

18 Zoti Yesu anatsimikiza mtima kuti asadodometsedwe zinaoneka pamene anayamba kuuza ophunzira ake kuti imfa yake yayandikira. Petro analimbikitsa Yesu kuti ‘adzichitire chifundo’  ndipo anamutsimikizira kuti: “Sichidzatero kwa Inu ayi.” Yesu sanafune kumva zilizonse zimene zikanam’lepheretsa kuchita chifuniro cha Yehova. Iye anapotolokera Petro n’kumuuza kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.” (Mateyu 16:21-23) Ifenso tizikhala otsimikiza chimodzimodzi kukana maganizo a anthu. M’malo mwake, tiyeni nthawi zonse tizitsatira maganizo a Mulungu.

Ufumu Ndiwo Udzabweretse Madalitso Enieni

19. Ngakhale kuti Yesu ankachita zodabwitsa, kodi mbali yofunika kwambiri ya utumiki wake inali yotani?

19 Yesu anachita zodabwitsa zambiri posonyeza kuti anali Mesiya. Anaukitsa ngakhale akufa. Zodabwitsa zimenezo zinakopera anthu ambiri kwa iye, koma Yesu sanangobwera padziko lapansi kudzathandiza anthu ovutika. Anabwera kudzachitira umboni za choonadi. Ankadziwa kuti thandizo lililonse limene angapatse anthu lidzawathandiza kwa nthawi yochepa chabe. Ngakhale anthu amene anawaukitsa anafanso. Kokha mwa kuchitira umboni za choonadi m’pamene akanathandiza anthu ena kupeza moyo wosatha.​—Luka 18:28-30.

20, 21. Kodi Akristu oona amatani posonyeza kuti amaiona moyenera ntchito yochitira ena zabwino?

20 Masiku ano, anthu ena amayesera kutengera ntchito zabwino za Yesu pomanga zipatala kapena kuchita zinthu zina zothandiza anthu osauka. Nthawi zina amavutika kwambiri kuti achite zimenezi, ndipo timayamikira mtima wawo wabwino, koma thandizo lililonse lomwe angapereke limangothandiza anthu kwa nthawi yochepa basi. Ndi Ufumu wokha womwe udzathandize anthu kupeza mpumulo wosatha. Choncho Mboni za Yehova zimalimbikira ntchito yochitira umboni za choonadi cha Ufumu, monga momwe Yesu anachitira.

21 Komabe, Akristu oona amachitanso ntchito zabwino. Paulo analemba kuti: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Pakagwa tsoka kapena winawake akafunika thandizo, sitizengereza koma ‘timachitira chokoma’ anthu oyandikana nawo nyumba kapena abale athu achikristu. Komabe timadziwa kuti ntchito yathu yaikulu ndi yochitira umboni za choonadi.

Tengerani Chitsanzo cha Yesu

22. N’chifukwa chiyani Akristu amalalikira kwa anzawo?

22 Paulo analemba kuti: “Tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.” (1 Akorinto 9:16) Sanaione mopepuka ntchito yolalikira uthenga wabwino chifukwa uthenga umenewo ukanapulumutsa moyo wake ndi wa omvera ake. (1 Timoteo 4:16) Ifenso timauona chimodzimodzi  utumiki wathu. Timafuna kuthandiza anzathu. Timafuna kusonyeza kuti timakonda Yehova. Timafunanso kusonyeza kuti timakonda Yesu ndiponso timayamikira chikondi chachikulu chimene anatisonyeza. Choncho timalalikira uthenga wabwino ndipo sitikhalanso “ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.”​—1 Petro 4:1, 2.

23, 24. (a) Kodi tikutengapo phunziro lotani pa zodabwitsa zimene Yesu anachita zokhudza nsomba? (b) Kodi ndani amene akuchitira umboni mokwanira masiku ano?

23 Mofanana ndi Yesu, sitisiya ntchito yathu yofunika kwambiri ngakhale anthu ena azitiseka kapena azikana uthenga wathu mokwiya. Timatengapo phunziro pa zodabwitsa zimene Yesu anachita pamene anaitana Petro ndi Andreya kuti akhale otsatira ake. Timadziwa kuti tikamvera Yesu, n’kuponya makoka athu, kunena kwake titero, ngakhale m’madzi ooneka ngati opanda nsomba, tikhoza kugwira nsomba zambiri. Akristu ambiri, omwe ali ngati asodzi, apeza nsomba zambiri patatha zaka zambiri akusodza m’madzi amene ankaoneka ngati opanda nsomba. Ena atha kusamukira ku malo kumene usodzi ukuyenda bwino ndipo agwira nsomba zambiri kumeneko. Mulimonse mmene zingakhalire, sitidzasiya kuponya makoka athu. Tikudziwa kuti Yesu sananenebe kuti ntchito yolalikira yafika pamapeto m’mbali iliyonse ya dziko lapansi.​—Mateyu 24:14.

24 Mboni za Yehova zopitirira mamiliyoni sikisi panopa zikulalikira mwakhama m’mayiko oposa 230. Nsanja ya Olonda ya February 1, 2005, idzakhala ndi lipoti lapachaka lapadziko lonse losonyeza ntchito yawo ya m’chaka chautumiki cha 2004. Lipoti limenelo lidzasonyeza kuti Yehova wadalitsa kwambiri ntchito yolalikira. Panthawi yomwe yatsala kuti dongosolo la zinthu lino liwonongeke, tiyeni tipitirize kutsatira mawu olimbikitsa a Paulo, oti: “Lalikira mawu; chita nawo pa nthawi yake.” (2 Timoteo 4:2) Tiyeni tipitirize kuchitira umboni mokwanira mpaka pamene Yehova adzanene kuti ntchitoyi yafika pamapeto.

Kuyambira chaka chino, Lipoti la Chaka Chautumiki Lapadziko Lonse la Mboni za Yehova silizituluka mu Nsanja ya Olonda ya January 1. M’malo mwake lizituluka mu Nsanja ya Olonda ya February 1.

Kodi Mungayankhe?

• Kodi tingapindule bwanji ndi zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake?

• Kodi Yesu ankawaona motani anthu amene ankawalalikira?

• Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kuchitira umboni mokwanira?

• Kodi tingaike motani maganizo athu onse pa kuchita chifuniro cha Mulungu monga momwe Yesu anachitira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Utumiki wathu ungakhale wogwira mtima tikamamvera anthu chisoni monga momwe Yesu ankachitira

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Yesu anabwera padziko lapansi makamaka kudzachitira umboni za choonadi

[Zithunzi patsamba 17]

Mboni za Yehova zimalimbikira ntchito yochitira umboni mokwanira