Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chake Anthu Ambiri Amakayikira Zoti Zipembedzo Zingagwirizanitse Anthu Onse

Chifukwa Chake Anthu Ambiri Amakayikira Zoti Zipembedzo Zingagwirizanitse Anthu Onse

Chifukwa Chake Anthu Ambiri Amakayikira Zoti Zipembedzo Zingagwirizanitse Anthu Onse

“UZIKONDA mnzako.” (Mateyu 22:39) Zipembedzo zambiri zimagwirizana nalo lamulo la makhalidwe abwino lofunika limeneli. Zipembedzo zimenezi zikanati ziziphunzitsadi anthu awo kukonda anzawo, bwenzi anthu awowo akumakhala okondana ndi ogwirizana. Komabe, kodi zimenezo n’zimene mwaona zikuchitika? Kodi zipembedzo zimagwirizanitsa anthu? Pa kafukufuku wina amene anachitika posachedwapa ku Germany anafunsa anthu kuti: “Kodi zipembedzo zimagwirizanitsa anthu, kapena kodi nthawi zambiri zimawagawanitsa?” Pa anthu amene anayankha funso limeneli, anthu 22 pa anthu 100 alionse anati zipembedzo zimagwirizanitsa anthu, pamene anthu 52 pa anthu 100 alionse anati zimagawanitsa anthu. Mwina anthu m’dziko mwanu amaonanso chimodzimodzi.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri sakhulupirira kuti zipembedzo zingagwirizanitse anthu onse? Mwina n’chifukwa cha zimene zakhala zikuchitika m’mbiri ya anthu. M’malo mogwirizanitsa anthu, zipembedzo nthawi zambiri zawagawanitsa. Nthawi zina, anthu achita zinthu zoipa kwambiri m’dzina la chipembedzo. Taganizirani zitsanzo zina zomwe zachitika m’zaka 100 zapitazi.

M’dzina la Chipembedzo

Panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, Akroati a Chikatolika ndi Asebu a Chiorthodox m’mayiko a ku Balkan anamenyana koopsa. Magulu awiri onsewa ankati akutsatira Yesu, amene anaphunzitsa otsatira ake kukonda anzawo. Komabe, kumenyana kwawoko kunachititsa kuti “anthu wamba ochuluka kwambiri m’mbiri yonse ya anthu aphedwe mwankhanza kwambiri,” malinga ndi momwe ananenera munthu winawake wochita kafukufuku. Anthu padziko lapansi anangoti kukamwa yasa, kusowa chonena, poona chiwerengero chokwana 500,000 cha amuna, akazi, ndi ana amene anaphedwa pa kumenyana kumeneko.

Mu 1947, chiwerengero cha anthu a m’dziko la India chinali anthu pafupifupi mamiliyoni 400, amene ankaimira munthu mmodzi pa anthu asanu alionse a padziko lonse lapansi. Anthuwa anali makamaka Ahindu, Asilamu, ndi Asikhi. Pamene dziko la India analigawa, dziko la Chisilamu la Pakistan linapangidwa. Panthawi imeneyo, anthu ambirimbiri othawa kwawo ochokera m’mayiko awiriwa anawotchedwa, kumenyedwa, kuzunzidwa, ndi kuphedwa ndi mfuti pankhondo zosiyanasiyana zachipembedzo zimene zinachitika.

Kuwonjezera pa zitsanzo zoipa zimenezi, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 2000 zino uchigawenga unayamba kufalikira. Masiku ano, uchigawenga wachititsa kuti mayiko onse a padziko lapansi akhale tcheru chifukwa cha mantha, ndipo magulu ambiri a zigawenga amanena kuti ndi a chipembedzo chinachake. Choncho, zipembedzo sizionedwa ngati zolimbikitsa mtendere. M’malo mwake, nthawi zambiri zimaonedwa kuti n’zimene zimalimbikitsa chiwawa ndi kusagwirizana. Motero n’zosadabwitsa kuti magazini ya ku Germany yotchedwa FOCUS inayerekezera zipembedzo zikuluzikulu za padziko lapansili ndi onga, kapena kuti ufa wopezeka m’kati mwa zipolopolo. Zipembedzo zake ndi monga Chibuda, Matchalitchi Achikristu, Chikomfyushani, Chihindu, Chisilamu, Chiyuda, ndi Chitao.

Kusagwirizana kwa Anthu a Chipembedzo Chimodzi

Pamene zipembedzo zina zimakangana ndi zipembedzo zinzawo, zina zimakhala ndi vuto la kusagwirizana kwa anthu a m’chipembedzo chimodzi chomwecho. Mwachitsanzo, m’zaka zaposachedwapa, anthu a m’Matchalitchi Achikristu asemphana maganizo chifukwa cha kusagwirizana pa nkhani ya ziphunzitso za matchalitchiwo. Atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba amafunsa mafunso monga: Kodi kulera n’kololeka? Nanga bwanji kuchotsa mimba? Kodi akazi ayenera kukhala ansembe? Kodi tchalitchi chiyenera kuwaona bwanji amuna ogonana ndi amuna anzawo kapena akazi ogonana ndi akazi anzawo? Kodi chipembedzo chiyenera kuvomereza nkhondo? Poona kusagwirizana koteroko, anthu ambiri amadzifunsa kuti, ‘Kodi chipembedzo chingagwirizanitse bwanji anthu onse ngati chikulephera kugwirizanitsa anthu ake omwe?’

N’zachionekere kuti zipembedzo zalephera kugwirizanitsa anthu. Koma kodi zipembedzo zonse zimagawanitsa anthu? Kodi pali chipembedzo chimene chili chosiyana ndi zina, chimene chingagwirizanitse anthu onse?

[Chithunzi patsamba 3]

Apolisi ovulazidwa pa zipolowe za pakati pa anthu osiyana zipembedzo ku India mu 1947

[Mawu a Chithunzi]

Photo by Keystone/​Getty Images