Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalani ndi Miyambo Imene Mulungu Sakondwera Nayo

Samalani ndi Miyambo Imene Mulungu Sakondwera Nayo

 Samalani ndi Miyambo Imene Mulungu Sakondwera Nayo

PABWALO la nyumba inayake pali bokosi lamaliro lotsegula, dzuwa lotentha la ku Africa kuno likuswa mtengo. Anamalira akuyenda n’kumadutsa bokosilo posonyeza chisoni chawo, ndipo bambo wina wokalamba akuima kaye. Maso ake atadzaza ndi chisoni, iye akuweramira nkhope ya mwamuna wakufayo ndipo akuyamba kunena kuti: “Bwanji sunanditsazike? N’chifukwa chiyani wandisiya? Poti wabweranso tsopano, kodi upitiriza kundithandiza?”

Kudera lina la ku Africa kuno, kwabadwa mwana. Palibe amene akuloledwa kuona mwanayo. Patatha masiku angapo m’pamene akutulutsa mwanayo panja kuti anthu amuone ndipo akumupatsa dzina pamwambo wapadera.

Kwa anthu ena, kulankhula ndi munthu wakufa kapena kubisa mwana kuti ena asamuone kungaoneke ngati khalidwe lachilendo kwambiri. Komabe, pa chikhalidwe cha anthu ena, khalidwe lawo ndiponso mmene amaonera kufa ndi kubadwa kwa munthu zimatsatira kwambiri chikhulupiriro champhamvu choti anthu akufa amakhala ali moyo ndiponso amadziwa zomwe zikuchitika.

Chikhulupiriro chimenechi n’champhamvu kwambiri moti chimapezeka m’miyambo imene imakhudza pafupifupi mbali zonse za moyo.  Mwachitsanzo, anthu ambiri amakhulupirira kuti zochitika zofunika pamoyo wa munthu monga kubadwa, kutha msinkhu, kukwatira, kubereka, ndi kufa, ndi mbali za ulendo wopita ku dziko la mizimu ya makolo athu. Amakhulupirira kuti kumeneko, munthu wakufayo amapitirizabe kuchita zinthu zimene zimakhudza moyo wa anthu amene wawasiya m’mbuyo. Ndipo munthuyo akhoza kupitiriza kukhalabe ndi moyo mwa kubadwanso.

Pofuna kuonetsetsa kuti munthu ayende bwinobwino podutsa mbali za moyo wake zonsezi, pali miyambo yambirimbiri imene imachitika. Miyambo imeneyi inachokera pa chikhulupiriro choti pali chinachake m’kati mwa munthu chimene sichifa. Akristu oona amapewa miyambo iliyonse yokhudzana ndi chikhulupiriro chimenechi. Chifukwa chiyani?

Kodi N’chiyani Chimachitika Munthu Akafa?

Baibulo limafotokoza momveka bwino zomwe zimachitika munthu akafa. Limanena mosapita m’mbali kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 6, 10) Olambira Mulungu oona akhala akukhulupirira kwa nthawi yaitali mfundo yoona ndiponso yosavuta kumva imeneyi yopezeka m’Baibulo. Iwo amamvetsa kuti palibe mbali inayake ya munthu imene siifa. Iwo akudziwanso kuti kulibe mizimu ya akufa. (Salmo 146:4) Kalekale, Yehova analamulira anthu ake mwamphamvu kuti asamachite nawo miyambo iliyonse yogwirizana ndi chikhulupiriro choti anthu akufa amadziwa zomwe zikuchitika ndipo amatha kuthandiza kapena kupweteka anthu amoyo.​—Deuteronomo 14:1; 18:9-13; Yesaya 8:19, 20.

Akristu a m’zaka 100 zoyambirira nawonso ankapewa miyambo iliyonse yokhudzana ndi ziphunzitso zabodza zachipembedzo. (2 Akorinto 6:15-17) Masiku ano Mboni za Yehova, kaya zikhale za mtundu kapena fuko lotani, ndiponso kaya zikhale zoti zinakulira kuti, sizichita nawo miyambo yokhudzana ndi chiphunzitso chabodza choti m’kati mwa munthu muli chinthu chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthuyo akafa.

Kodi n’chiyani chingatithandize ife monga Akristu kudziwa ngati tingathe kuchita nawo mwambo winawake kapena ayi? Tiyenera kuganizira mofatsa kugwirizana kulikonse kumene kungakhalepo pakati pa mwambo umenewo ndi chiphunzitso chilichonse chabodza, monga choti mizimu ya akufa imathandiza kapena kupweteka anthu amoyo. Chinanso, tiyenera kuganizira ngati anthu ena amene amadziwa zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira ndi kuphunzitsa angakhumudwe ifeyo titachita nawo mwambo umenewo. Poganizira mfundo zimenezi, tiyeni tikambirane mbali ziwiri zofunika kuziona bwinobwino, zomwe ndi kubadwa ndi kufa kwa munthu.

Miyambo Yokhudza Kubadwa kwa Mwana ndi Kumutcha Dzina

Miyambo yambiri yokhudzana ndi kubadwa kwa mwana ndi yabwinobwino. Komabe, kumadera kumene amaona kuti kubadwa kwa mwana kumatanthauza kusamuka kuchoka ku dziko la mizimu kubwera ku dziko la anthu, Akristu ayenera kusamala. Mwachitsanzo, kumadera ena ku Africa kuno, mwana wakhanda samutulutsa m’nyumba ndipo samupatsa dzina mpaka patapita nthawi. Ngakhale kuti nthawi yodikirayo imasiyanasiyana malinga ndi dera lake, pamapeto pake pamakhala mwambo wopatsa mwanayo dzina, pamene mwanayo amamutulutsa panja ndipo amamuonetsa kwa achibale ndi anzawo. Panthawi imeneyi m’pamene amalengeza dzina la mwanayo kwa onse amene abwera.

Pofotokoza tanthauzo la mwambo umenewu, buku lotchedwa Ghana​—Understanding the People and Their Culture (Kuwamvetsa Anthu a ku Ghana ndi Miyambo Yawo), limati: “Pa masiku seveni oyambirira a moyo wake, mwana amaonedwa kuti ‘akudzangoona kaye malo’ asanasamuke ku dziko la mizimu kubwera ku dziko lapansi. . . . Mwanayo nthawi zambiri samutulutsa m’nyumba ndipo anthu omwe si a m’banjamo saloledwa kumuona.”

N’chifukwa chiyani pamadutsa kaye nthawi asanachite mwambo womupatsa mwanayo dzina?  Buku lotchedwa Ghana in Retrospect limafotokoza kuti: “Tsiku la eyiti lisanafike, amati mwanayo amakhala asanasanduke munthu. Amakhala kuti akadali mbali ya dziko limene wachokeralo.” Bukulo limapitiriza kuti: “Popeza dzinalo ndi limene limachititsa kuti mwanayo asanduke munthu, ngati makolowo akuganiza kuti mwina mwanayo akhoza kufa, amadikira kaye osamupatsa dzina mpaka atsimikize kuti akhaladi ndi moyo. . . . Choncho mwambo umenewu, umene nthawi zina amautcha kutulutsa poyera mwana, amauona kuti ndi wofunika kwambiri kwa mwanayo ndi makolo ake. Mwambo umenewu ndi umene umalowetsa mwanayo m’dziko la anthu.”

Wachibale wachikulire wa banjalo ndi amene nthawi zambiri amatsogolera pa mwambo wopatsa mwana dzina. Zochitika pamwambowo zimasiyanasiyana malinga ndi kudera kwake, koma nthawi zambiri zimaphatikizapo kuthira nsembe, kupemphera kwa mizimu ya makolo n’kuithokoza chifukwa chothandiza mwanayo kufika bwino, ndi miyambo ina.

Mwambowo umafika pachimake akalengeza dzina la mwanayo. Ngakhale kuti makolo ndi amene amafunika kupatsa mwanayo dzina, achibale ena nthawi zambiri amawachititsa kusankha dzina limene iwowo akufuna. Mayina ena amakhala ndi tanthauzo m’chilankhulo cha kuderalo, monga “wapita n’kubweranso,” “Mayi abweranso kachiwiri,” kapena “Bambo abweranso.” Mayina ena amakhala ndi matanthauzo amene cholinga chake n’kupempha makolo akufa kuti asatengenso mwanayo kupita naye ku dziko la mizimu.

N’zoona kuti palibe cholakwika ndi kusangalala chifukwa cha kubadwa kwa mwana. Kupatsa mwana dzina la munthu wina wake ndiponso kumupatsa dzina losonyeza zimene zinachitika panthawi imene anabadwa, ndi miyambo yabwinobwino. Ndiponso aliyense akhoza kusankha yekha nthawi imene akufuna kuti apatse mwana wake dzina. Komabe, Akristu amene akufuna kusangalatsa Mulungu amapewa miyambo iliyonse imene imasonyeza kuti akugwirizana ndi chikhulupiriro choti mwanayo “akudzangoona kaye malo” asanasamuke ku dziko la mizimu ya makolo kulowa m’dziko la anthu amoyo.

Kuwonjezera apo, ngakhale kuti anthu ambiri m’deralo angamaone kuti mwambo wopatsa mwana dzina ndi wofunika kwambiri, Akristu ayenera kuganizira chikumbumtima cha anthu ena ndiponso ayenera kuganizira za chithunzi chimene akupatsa anthu osakhulupirira. Mwachitsanzo, kodi ena angaganize chiyani ngati banja lachikristu libisa mwana wawo osamuonetsa kwa anthu ena mpaka padzachitike mwambo womupatsa dzina? Kodi anthu ena angaganize chiyani ngati atapatsa mwana wawoyo mayina osemphana ndi zimene amanena, zoti amaphunzitsa zinthu zoona za m’Baibulo?

Choncho poganizira mmene angapatsire mwana wawo dzina ndiponso nthawi yoti achite zimenezi, Akristu amayesetsa ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu’ kuti asakhumudwitse anthu ena. (1 Akorinto 10:31-33) Iwo ‘sakana lamulo la Mulungu, kuti asunge mwambo wawo,’ umene cholinga chake chachikulu chimakhala kulemekeza anthu akufa. M’malo mwake, amalemekeza Mulungu wamoyo, Yehova.​—Marko 7:9, 13.

Kuchoka ku Imfa Kupita ku Moyo

Imfa, mofanana ndi kubadwa, imaonedwa ndi anthu ambiri ngati msamuko. Munthu akafa amati wachoka ku dziko looneka ndipo wapita ku dziko losaoneka la mizimu ya akufa. Anthu ambiri amakhulupirira kuti ngati pamaliro sipachitika miyambo inayake, mizimu ya makolo, yomwe amakhulupirira kuti ili ndi mphamvu zolanga kapena kupereka mphoto kwa anthu amoyo, ikhoza kukwiya. Chikhulupiriro chimenechi chimakhudza kwambiri zimene zimachitika pamaliro.

Pa maliro amene cholinga chake n’kugoneka mzimu wa munthu wakufayo, anthu amachita zinthu zosiyanasiyana, monga kulira mokuwa pamaso pa mtembowo komanso kuchita phwando lalikulu akaika malirowo. Pamapwando a maliro oterowo nthawi zambiri pamakhala kudyerera, kuledzera, ndi kuvina nyimbo zaphokoso kwambiri. Mwambo wa maliro umaoneka kuti ndi chinthu chofunika kwambiri moti ngakhale mabanja osauka kwambiri amayesetsa kuti apeze ndalama zokwanira kuti akhale ndi “maliro olemekezeka,” ngakhale kuti kuchita zimenezi kungawagwetse m’mavuto kapena m’ngongole.

Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova zasonyeza poyera kuti miyambo ina ya maliro ndi  yosemphana ndi Malemba. * Miyambo imeneyi imaphatikizapo kuchezera pamaliro, kuthira nsembe, kulankhula ndi akufa kapena kuwapempha zinthu zinazake, kukhala ndi mwambo wokumbukira tsiku limene munthu anamwalira, ndi miyambo ina imene inayamba chifukwa chokhulupirira kuti munthu amakhala ndi chinachake m’kati mwake chimene chimakhalabe ndi moyo iye akamwalira. Miyambo yonyoza Mulungu imeneyi ndi ‘yodetsedwa,’ “chinyengo chopanda pake,” yochokera ku “mwambo wa anthu,” osati Mawu a Mulungu a choonadi.​—Yesaya 52:11; Akolose 2:8.

Kukakamizidwa Kutsatira Zomwe Aliyense Amachita

Anthu ena akhala akuvutika kuti apewe miyambo ya kudera kwawo, makamaka m’mayiko amene kulemekeza akufa kumaonedwa kuti n’kofunika kwambiri. Chifukwa choti Mboni za Yehova sizitsatira miyambo yoteroyo, anthu ena amawaona ngati anthu achilendo kapena amawanena kuti amadzisankha ndiponso amanyoza anthu akufa. Chifukwa chonyozedwa ndi kukakamizidwa kwambiri kuchita zomwe aliyense amachita, Akristu ena achita mantha kuti achite zinthu zosiyana ndi ena, ngakhale kuti amamvetsa bwinobwino choonadi cha m’Baibulo. (1 Petro 3:14) Ena amaona kuti miyambo imeneyi ndi mbali ya chikhalidwe chawo ndipo sangaipeweretu. Ena amaganizanso kuti kukana kutsatira miyambo imeneyi kungachititse kuti anthu a m’deralo azidana ndi anthu a Mulungu.

Ife sitifuna kukhumudwitsa dala anthu ena popanda chifukwa. Komabe, Baibulo limatichenjeza kuti tikamatsatira choonadi mosamala, dziko lodana ndi Mulunguli lidzadana nafe. (Yohane 15:18, 19; 2 Timoteo 3:12; 1 Yohane 5:19) Ife timatsatirabe choonadicho modzipereka, chifukwa tikudziwa kuti tiyenera kukhala osiyana ndi anthu omwe ali mu mdima wauzimu. (Malaki 3:18; Agalatiya 6:12) Mofanana ndi momwe Yesu anakanira kumvera Satana pamene ankamuyesa kuti achite zinthu zomwe Mulungu sasangalala nazo, ifenso timakana kumvera anthu omwe amafuna kuti tichite zinthu zosasangalatsa Mulungu. (Mateyu 4:3-7) M’malo mochita zinthu chifukwa choopa anthu, Akristu oona amafuna makamaka kusangalatsa Yehova Mulungu ndi kumulemekeza monga Mulungu wa choonadi. Amachita zimenezo potsatirabe mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi kulambira koona ngakhale ena aziwakakamiza kuchita zinthu zosemphana ndi zimenezi.​—Miyambo 29:25; Machitidwe 5:29.

Kulemekeza Yehova Powaona Moyenera Anthu Akufa

Si zachilendo kumva kupweteka kwambiri mumtima ndiponso chisoni munthu amene timamukonda akamwalira. (Yohane 11:33, 35) Kukumbukira munthu amene tinali kumukonda akamwalira ndiponso kumukonzera mwambo wamaliro waulemu ndi njira zabwinobwino zosonyezera chikondi chathu. Mboni za Yehova zimamva chisoni kwambiri wokondedwa wawo akamwalira, koma sizitsatira miyambo imene Mulungu sakondwera nayo. Zimenezi si zophweka kwa anthu amene anakulira kumadera kumene anthu amaopa kwambiri akufa. Zikhoza kukhala zovuta kuti tiziganiza bwinobwino tikamamva kupweteka mumtima chifukwa cha imfa ya munthu amene tinali kugwirizana naye kwambiri. Komabe, Akristu okhulupirika amalimbikitsidwa ndi Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse,” ndipo amathandizidwa ndi okhulupirira anzawo amene amawakonda. (2 Akorinto 1:3, 4) Akristu oona ali ndi chikhulupiriro champhamvu choti anthu akufa, amene panopa sakudziwa chilichonse, ndipo Mulungu akuwakumbukira, adzakhalanso ndi moyo tsiku lina. Chikhulupiriro chimenechi chimalimbikitsa Akristuwo kukaniratu miyambo yamaliro yachikunja imene imasemphana ndi chiphunzitso choti akufa adzauka.

Kodi sitikusangalala kuti Yehova ‘anatiitana kuti tituluke mumdima, n’kulowa mu kuunika kwake kodabwitsa’? (1 Petro 2:9) Tikamasangalala ndi kubadwa kwa mwana kapena kupirira chisoni chobwera chifukwa cha imfa, tiyeni tipitirizebe ‘kuyenda monga ana a kuunika’ nthawi zonse chifukwa choti timafunitsitsa kuchita zabwino ndiponso timakonda kwambiri Yehova Mulungu. Tisalole kuti tidetsedwe mwauzimu ndi miyambo yachikunja imene Mulungu sakondwera nayo.​—Aefeso 5:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 23 Onani timabuku takuti Mizimu ya Akufa​—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? ndi Njira ya ku Moyo Wosatha​—Kodi Mwaipeza? tofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.