Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinaphunzira Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse

Tinaphunzira Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse

 Mbiri ya Moyo Wanga

Tinaphunzira Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse

YOSIMBIDWA NDI NATALIE HOLTORF

Tsiku lina m’mwezi wa June m’chaka cha 1945, mwamuna wooneka wodwala anafika kunyumba kwathu n’kuima pakhomo lakumaso kwa nyumbayo. Mwana wanga wamng’ono, Ruth, anadzidzimuka n’kukuwa kuti: “Amama, pakhomo pabwera mlendo!” Iye sankadziwa kuti mlendoyo ndi bambo ake, mwamuna wanga wokondedwa, Ferdinand. Zaka ziwiri m’mbuyomo, patangotha masiku atatu Ruth atabadwa, Ferdinand anachoka panyumba, anagwidwa, ndipo anatumizidwa ku ndende ya Nazi yozunzirako anthu. Koma tsopano Ruth anatha kukumana ndi bambo ake ndipo banja lathu linagwirizananso. Ine ndi Ferdinand tinali ndi nkhani zambiri zoti tiuzane!

FERDINAND anabadwa m’chaka cha 1909 mu mzinda wa Kiel, ku Germany, ndipo ine ndinabadwa m’chaka cha 1907 mu mzinda wa Dresden, ku Germany komweko. Pamene ndinali ndi zaka 12, banja lathu linakumana koyamba ndi Ophunzira Baibulo, amene panopa amatchedwa Mboni za Yehova. Ndili ndi zaka 19, ndinasiya kupita ku tchalitchi cha Evangelical ndipo ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova.

Panthawi imeneyi, Ferdinand anamaliza maphunziro ake kukoleji yophunzitsa kuyendetsa sitima zapamadzi ndipo anayamba kuyendetsa sitima yapamadzi. Pamaulendo ake, ankaganizira mafunso okhudza Mlengi, kuti kaya alipo kapena kulibe. Atabwerako, Ferdinand anapita kukacheza kwa mchimwene wake, amene anali Wophunzira Baibulo. Atangocheza ndi mchimwene wakeyo anakhulupirira kuti Baibulo lili ndi mayankho a  mafunso amene anali kumuvutitsa. Anasiya kupita ku tchalitchi cha Lutheran, ndipo anasiyanso ntchito yoyendetsa sitima. Pamapeto pa tsiku lake loyamba mu ntchito yolalikira, anakhala ndi chilakolako chachikulu chofuna kuchita ntchito imeneyi moyo wake wonse. Usiku umenewo, Ferdinand anapatulira moyo wake kwa Yehova. Anabatizidwa mu August m’chaka cha 1931.

Mlaliki Woyendetsa Sitima Yapamadzi

Mu November m’chaka cha 1931, Ferdinand anakwera sitima kupita ku Netherlands kuti akathandize pa ntchito yolalikira kumeneko. Ferdinand atauza mbale amene ankayendetsa ntchito yolalikira m’dzikolo kuti kale ankagwira ntchito yoyendetsa sitima, mbaleyo ananena mwansangala kuti: “Timafuna munthu ngati iweyo!” Abalewo anali atachita lendi bwato kuti gulu la apainiya (atumiki a nthawi zonse) azitha kulalikira kwa anthu okhala m’mphepete mwa madzi m’chigawo chakumpoto kwa dzikolo. Bwatolo linali ndi ogwira ntchito asanu, koma palibe aliyense wa iwo amene ankadziwa kuliyendetsa. Choncho Ferdinand anakhala woyendetsa bwatolo.

Patatha miyezi isanu, Ferdinand anapemphedwa kuti akachite upainiya ku Tilburg, kummwera kwa dziko la Netherlands. Panthawi imeneyo, inenso ndinafika ku Tilburg kudzachita upainiya, ndipo ndinakumana ndi Ferdinand. Koma nthawi yomweyo anatipempha kuti tisamukire ku Groningen, kumpoto kwa dzikolo. Titafika kumeneko tinakwatirana mu October m’chaka cha 1932 ndipo tchuthi chosangalala kuti talowa m’banja tinachitira m’nyumba inayake mmene mumakhalanso apainiya ena, uku tikuchita upainiya!

M’chaka cha 1935 mwana wathu wamkazi Esther anabadwa. Ngakhale kuti tinalibe ndalama zambiri, tinatsimikiza zopitirizabe kuchita upainiya. Tinasamukira kumudzi, kumene tinkakhala m’kanyumba kakang’ono kwambiri. Ine ndikamasamalira mwanayo kunyumba, mwamuna wanga ankatha tsiku lonse ali mu utumiki. Tsiku lotsatira tinkasinthana. Tinachita zimenezi mpaka pamene Esther anali wamkulu mokwanira kuti tikanatha kumutenga mu utumiki.

Pasanapite nthawi yaitali, ndale ku Ulaya zinayamba kuvuta. Tinamva zoti Mboni za ku Germany zinali kuzunzidwa, ndipo tinadziwa kuti pasanapite nthawi yaitali ifenso tiyamba kuzunzidwa. Sitinadziwe kuti tidzapirira bwanji tikadzakumana ndi chizunzo choopsa. M’chaka cha 1938 boma la Netherlands linaika lamulo loti anthu omwe si nzika za m’dzikomo sanali ololedwa kugwira ntchito yogawira mabuku achipembedzo. Mboni zachidatchi pofuna kutithandiza pa utumiki wathu, zinatipatsa mayina a anthu achidwi ndipo tinatha kuphunzira Baibulo ndi ena a iwo.

Chapanthawi imeneyo, panakonzedwa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Tinafunitsitsa kukapezeka pa msonkhanowo, ngakhale kuti tinalibe ndalama zoti tingakwerere sitima yopita ku malo a msonkhanowo. Choncho tinayenda panjinga masiku atatu, titamuika Esther m’chikwama chomangirira ku mahandulo a njingayo. Usiku tinkagona m’nyumba za Mboni zomwe zinkakhala m’malo amene tinali kudutsa. Tinali osangalala kwambiri kupezeka pa msonkhano wachigawo woyamba wa  dziko lonselo. Msonkhanowo unatipatsa mphamvu zoti tithe kulimbana ndi mavuto amene anali patsogolo pathu. Koposa zonse, tinakumbutsidwa kukhulupirira Mulungu. Mawu a pa Salmo 31:6 ndi amene tinayamba kuyendera pamoyo wathu. Mawuwo amati: “Ndikhulupirira Yehova.”

Kusakidwa ndi a Nazi

Mu May m’chaka cha 1940 a Nazi anadzalowa m’dziko la Netherlands. Patangopita nthawi yochepa a gulu la Gestapo, kapena kuti apolisi akabisalira, anabwera mwadzidzidzi kunyumba kwathu pamene tinali kulongosola mtokoma wa mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Anamutengera Ferdinand ku likulu la gulu la Gestapo. Ine ndi Esther tinkapita kukamuona nthawi ndi nthawi, ndipo nthawi zina ankamufunsa mafunso ndi kumumenya ife tili pomwepo. Mu December, Ferdinand anatulutsidwa mwadzidzidzi, koma ufulu wake sunakhalitse. Madzulo enaake tikubwera kunyumba, tinaona galimoto ya Gestapo ili pafupi ndi nyumba yathu. Ferdinand anatha kuthawa pamene ine ndi Esther tinkalowa m’nyumbamo. A Gestapowo anali kutidikirira. Anali kufuna Ferdinand. Usiku womwewo, a Gestapowo atachoka, apolisi achidatchi anabwera n’kunditenga kuti akandifunse mafunso. Tsiku lotsatiralo ine ndi Esther tinakabisala m’nyumba ya banja linalake la Mboni limene linali litangobatizidwa kumene, banja la a Norder, limene linatisunga ndi kutiteteza.

Chakumapeto kwa January m’chaka cha 1941, banja lina la apainiya amene anali kukhala m’bwato anagwidwa. Tsiku lotsatira, woyang’anira dera (mtumiki woyendayenda) ndi mwamuna wanga anapita m’bwatolo kuti akatenge katundu wina wa banja limene linagwidwa lija, koma anthu ogwirizana ndi a Gestapo anawapezerera. Ferdinand anatha kuthawa panjinga yake. Koma woyang’anira derayo anamutengera kundende.

Abale audindo anapempha Ferdinand kuti atenge malo a woyang’anira dera uja. Zimenezo zinatanthauza kuti akanatha kubwera kunyumba kwa masiku pafupifupi atatu basi pamwezi. Limeneli linali vuto latsopano kwa ife, koma ndinapitirizabe kuchita upainiya. A Gestapo anayamba kufufuza Mboni mwakhama, choncho tinafunika kumasamukasamuka. M’chaka cha 1942 tinasamuka katatu. Pamapeto pake tinasamukira mu mzinda wa Rotterdam, kutali kwambiri ndi kumene Ferdinand anali kuchita utumiki wake mwakabisira. Panthawi imeneyo ndinali woyembekezera mwana wathu wachiwiri. Banja la a Kamp, amene ana awo aamuna awiri anali atatengedwa kupita ku ndende zozunzirako anthu, anatikomera mtima n’kutilola kuti tizikhala m’nyumba mwawo.

A Gestapo Anali Kutifunafunabe

Mwana wathu wachiwiri, Ruth, anabadwa mu July m’chaka cha 1943. Ruth atabadwa, Ferdinand anatha kukhala nafe masiku atatu, koma kenaka anachoka, ndipo sitinamuonenso kwa nthawi yaitali. Patatha pafupifupi milungu itatu, Ferdinand anagwidwa ali ku Amsterdam. Anamutengera ku ofesi ya gulu la Gestapo, kumene apolisiwo anatha kutsimikiza kuti ndi yemweyodi. A Gestapo anamufunsa mafunso ambiri pofuna kuti aulule za ntchito yathu yolalikira mwakabisira. Koma Ferdinand anangoulula zoti anali wa Mboni za Yehova ndiponso kuti sankachita nawo ntchito iliyonse yandale. Akuluakulu a Gestapo anakwiya kwambiri kuti Ferdinand, amene anali nzika ya ku Germany, sanakalembetse usilikali, ndipo anamuopseza kuti amupha chifukwa chosathandiza dziko lake.

Kwa miyezi isanu yotsatira, Ferdinand anamusunga m’chipinda cha m’ndende, mmene anapirira pamene nthawi zonse anali kumuuza kuti amupha pomuwombera ndi mfuti. Koma sanasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kukhalabe wolimba mwauzimu? Mawu a Mulungu, Baibulo. Popeza anali Mboni, Ferdinand sanali kuloledwa kukhala ndi Baibulo. Koma akaidi ena ankatha kuitanitsa Baibulo. Choncho Ferdinand anauza munthu amene anali naye m’chipinda chimodzi kuti apemphe banja lake kuti limutumizire Baibulo, ndipo mwamunayo anachitadi zimenezo. Patatha zaka zambiri, nthawi iliyonse Ferdinand akamanena za nkhani imeneyi, nkhope yake inkaoneka yosangalala kwambiri ndipo ankati: “Baibulo limenelo linandilimbikitsa kwabasi!”

Kumayambiriro kwa January m’chaka cha 1944, Ferdinand mwadzidzidzi anamutengera  ku ndende yozunzirako anthu ku Vught, ku Netherlands. Mosayembekezera, kusamuka kumeneku kunadzakhala dalitso kwa iye chifukwa kumeneko anakumana ndi Mboni zina 46. Nditamva zoti wasamuka, ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti akadali moyo!

Kupitirizabe Kulalikira M’ndende Yozunzirako Anthu

Moyo wa kundende yozunzirako anthuyo unali wopweteka kwambiri. Kuvutika chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi, kusowa zovala zotentha, ndi kuzizira kwambiri, kunali kofala. Ferdinand anadwala matenda aakulu a zilonda zapakhosi. Atakhala nthawi yaitali pamzere pamene anali kuitana mayina kuti adziwe yemwe alipo, kunja kukuzizira kwambiri, anapita ku chipinda cha odwala. Odwala amene anatentha thupi kufika pa madigiri 40 analoledwa kukhala kumeneko. Koma Ferdinand sanaloledwe kukhalako, chifukwa thupi lake linatentha madigiri 39 okha! Anauzidwa kuti abwerere kuntchito. Koma akaidi anzake anamumvera chisoni ndipo anamuthandiza pomamubisa kwa kanthawi pamalo ofunda. Kenaka anapezako mpumulo pamene kunja kunayamba kufunda. Ndiponso abale ena akalandira phukusi la chakudya, ankagawana ndi ena zakudyazo, choncho Ferdinand anatha kupezako timphamvu.

Mwamuna wanga asanamangidwe, kulalikira ndiye inali ntchito yake, ndipo m’ndendemo anapitiriza kuuza ena zikhulupiriro zake. Oyang’anira ndendeyo nthawi zambiri ankanena zinthu zomunyoza chifukwa cha kansalu kake kofiirira, komwe kanali chizindikiro cha akaidi omwe anali Mboni. Koma Ferdinand ankaona ndemanga zoterozo ngati mwayi woti ayambe kucheza nawo. Poyamba, malo oti abalewo akanatha kulalikira anali chabe nyumba imene okhalamo ake ambiri anali Mboni. Abalewo anadzifunsa kuti, ‘Kodi tingalalikire bwanji kwa akaidi ambiri?’ Mosadziwa, akuluakulu a ndendeyo ndi amene anathetsa vuto limeneli. Kodi anatero motani?

Abalewo anali ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo ndi mabaibulo 12 omwe ankawasunga mobisa. Tsiku lina alonda anapeza mabuku angapo, koma analephera kudziwa kuti mwiniwake anali ndani. Choncho akuluakulu a ndendeyo anaganiza zoti ayenera kuthetsa mgwirizano wa Mbonizo. Ndipo powalanga, abale onsewo anawalekanitsa n’kuwapititsa m’nyumba zimene mumakhalanso akaidi ena oti si Mboni. Ndiponso pakudya abalewo anayenera kukhala moyandikana ndi akaidi oti si Mboni. Limeneli linali dalitso lalikulu. Tsopano abalewo anatha kuchita zimene anakhala akufuna kuchita kuyambira pachiyambi, kulalikira kwa akaidi ambiri.

Kulera Ndekha Ana Awiri

Panthawi imeneyi ine ndi ana anga aakazi awiri tinali kukhalabe ku Rotterdam. Nyengo yozizira ya m’chaka cha 1943 ndi 44 inali yovuta kwabasi. Kuseri kwa nyumba yathu kunali gulu la asilikali achijeremani omwe anali ndi zida zankhondo zophulitsira ndege. Kutsogolo kwa nyumbayo kunali malo otchedwa Waal Harbor, omwe asilikali otsutsana ndi Ajeremaniwo ankafuna kwambiri kuwaphulitsa. Choncho malo amene tinali kukhalawo anali oopsa kubisalako. Kuwonjezera apo, chakudya chinali kusowa kwambiri. Koposa kale lonse, tinaphunzira kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse.​—Miyambo 3:5, 6.

Esther, amene anali ndi zaka eyiti, anathandiza banja lathu laling’onolo pomaima pamzere kuti akatilandirire chakudya. Koma nthawi zambiri akafika poti alandire chakudyacho amapeza chitatha. Paulendo wake wina wokalandira chakudya, ndege zinayamba kuponya mabomba iye akadali panja. Ndinachita mantha kwambiri nditamva kuphulikako, koma pasanapite nthawi nkhawa yanga inasanduka misozi yachimwemwe pamene Esther anabwerera kunyumbako osavulala, atatenganso zakudya zinazake zingapo zonga mbatata. Mawu anga oyamba anali oti, “Chinachitika n’chiyani?” Iye anayankha mtima uli m’malo kuti: “Mabomba atayamba kugwa, ndinangochita zimene bambo anandiuza kuti ndizichita, kuti ‘Uzigona pansi, osadzuka, n’kupemphera.’ Ndipo zinandithandizadi!”

Chifukwa cha mmene ndinkalankhulira pokhala Mjeremani, zinali bwino kuti Esther azikagula zinthu zimene tinali kufunikira zomwe zinali kupezekabe. Asilikali achijeremani anaona zimenezi, ndipo anayamba kumufunsa Esther mafunso. Koma sanaulule chinsinsi chilichonse. Kunyumba, ndinamuphunzitsa Esther zinthu za  m’Baibulo, ndipo popeza sakanatha kupita ku sukulu, ndinamuphunzitsanso kuwerenga, kulemba, ndi zinthu zina.

Esther ankandithandizanso mu utumiki. Ndisanapite kukaphunzira Baibulo ndi munthu, Esther ankatsogola kaye kukaona ngati zonse zinali bwino. Ankaona ngati zizindikiro zimene ndinagwirizana ndi wophunzira Baibuloyo zinalipo. Mwachitsanzo, munthu amene ndimakamuchezerayo ankaika mphika wamaluwa pawindo mwanjira inayake kuti ndidziwe kuti ndingathe kulowa m’nyumbamo. Ndikamachititsa phunziro la Baibulolo, Esther ankakhala panja kuti aone ngati kukubwera zoopsa zilizonse uku akukankha chikuku Ruth ali m’kati mwakemo, kumakweza ndi kutsika nawo msewuwo.

Kupita ku Sachsenhausen

Kodi Ferdinand zinthu zinali kumuyendera bwanji? Mu September m’chaka cha 1944, iye limodzi ndi akaidi ena ambiri anatengedwa kupita ku siteshoni ya sitima kumene magulu a akaidi 80 ankalongedzedwa m’ ngolo za sitima imene inali kuwadikirira. M’ngolo iliyonse munali chidebe chimodzi chomwe anali kuchigwiritsa ntchito ngati chimbudzi ndi chidebe china cha madzi akumwa. Ulendowo unatenga masiku atatu, usana ndi usiku, ndipo panalibe malo oti munthu n’kukhala pansi! Munalibe mpweya wokwanira, chifukwa ngolozo zinali zotseka, kupatulapo tizibowo ting’onoting’ono apo ndi apo. Zimene anavutika nazo mmenemo, monga kutentha, njala, ludzu, ndiponso kununkha, n’zosaneneka.

Sitimayo inaima pa ndende yozunzirako anthu yotchuka kwambiri chifukwa cha nkhanza zake ya Sachsenhausen. Akaidi onse anawalanda katundu wawo yense yemwe anabweretsa, kupatulapo mabaibulo 12 aja amene Mbonizo zinatenga paulendowo.

Ferdinand ndi abale ena eyiti anatumizidwa ku ndende ina yomwe inali kuyang’aniridwa ndi ndende ya Sachsenhausen, ku Rathenow, kuti azikapanga zida zankhondo. Abalewo anakana kugwira ntchito imeneyo, ngakhale kuti nthawi zambiri ankawaopseza kuti awapha. Kuti athandizane kukhalabe olimba, m’mawa ankauzana lemba la m’Baibulo, monga Salmo 18:2, kuti aliganizire tsiku limenelo. Zimenezi zinawathandiza kusinkhasinkha zinthu zauzimu.

Pamapeto pake, mkokomo wa zida zankhondo unasonyeza kuti asilikali achirasha ndi asilikali otsutsana ndi Ajeremani anali kuyandikira. Asilikali achirashawo ndi amene anayamba kufika pa ndende imene Ferdinand ndi anzake anali. Anawapatsa akaidiwo chakudya n’kuwauza kuti achoke pandendepo. Kumapeto kwa April m’chaka cha 1945, asilikali achirashawo analola akaidiwo kupita kwawo.

Kukhalanso Limodzi Monga Banja

Pa June 15, Ferdinand anafika ku Netherlands. Abale a ku Groningen anamulandira ndi manja awiri. Kenaka anauzidwa kuti tinali moyo, ndiponso kuti tinali kukhala kwinakwake m’dzikomo, ndipo ifenso tinamva zoti wabwera. Nthawi inkachedwa kwambiri pamene tinali kudikirira kuti afike. Koma tsiku lina Ruth anaitana kuti: “Amama, pakhomo pabwera mlendo!” Mwamuna wanga wokondedwa, ndiponso bambo wokondedwa wa anawo, anali atabwera!

Panali mavuto ambiri amene tinayenera kuthana nawo tisanayambe kukhalanso bwinobwino monga banja. Tinalibe malo okhala, ndipo vuto lalikulu lomwe tinali nalo linali kupezanso ziphaso zotiloleza kukhazikika ku Netherlands. Popeza  tinali Ajeremani, kwa zaka zingapo akuluakulu aboma achidatchi anatichitira zinthu ngati kuti tinali anthu oipa. Koma pamapeto pake tinatha kukhazikika n’kuyamba kuchita zinthu zimene tinkafuna kwambiri kuchita, kutumikira Yehova limodzi monga banja.

“Ndikhulupirira Yehova”

M’zaka zotsatira, nthawi iliyonse imene ine ndi Ferdinand tinali kucheza ndi anzathu ena omwe anavutikanso mofanana ndi ife panthawi yovuta ija, tinkakumbukira momwe Yehova anatitsogolera pa nthawi zovuta zimenezo. (Salmo 7:1) Tinasangalala kuti pa zaka zonsezo, Yehova anatilola kuchita nawo zinthu zopititsa patsogolo Ufumu. Nthawi zambiri tinkanenanso kuti tinali osangalala kwambiri kuti tinathera zaka zaunyamata wathu mu utumiki wopatulika wa Yehova.​—Mlaliki 12:1.

Nthawi ya chizunzo cha a Nazi itatha, ine ndi Ferdinand tinatumikira Yehova limodzi kwa zaka zopitirira 50. Ferdinand anamaliza moyo wake wapadziko lapansi pa December 20, 1995. Posachedwapa ndikwanitsa zaka 98. Tsiku lililonse ndimayamikira Yehova kuti ana athu anatithandiza kwambiri pa zaka zovuta zija. Ndimayamikiranso Yehova chifukwa choti ndikadali ndi timphamvu totha kumutumikira, zimene zimalemekeza dzina lake. Ndikuyamikira zonse zimene Yehova wandichitira, ndipo cholinga changa n’choti pamoyo wanga ndipitirizebe kuyendera mawu oti: “Ndikhulupirira Yehova.”​—Salmo 31:6.

[Chithunzi patsamba 19]

Ndili ndi Ferdinand mu October, m’chaka cha 1932

[Chithunzi patsamba 19]

Bwato lochitira ulaliki lotchedwa “Almina” ndi anthu ogwiramo ntchito

[Chithunzi patsamba 22]

Ndili ndi Ferdinand ndi ana athu