Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumafuna Kukhala ndi Moyo Wosatha?

Kodi Mumafuna Kukhala ndi Moyo Wosatha?

 Kodi Mumafuna Kukhala ndi Moyo Wosatha?

“INE sindiopa kufa,” anatero mayi wina wokalamba ku Japan. “Koma zimandipweteka kuganizira kuti ndidzasiyana ndi maluwa anga.” Mtumiki wachikristu amene anapita kunyumba kwa mayiyu anatha kumvetsetsa zimenezi, popeza mayiyo anali ndi munda wokongola wa maluwa. Ambiri amene amati saopa kufa amasangalala ndi kukongola kwa chilengedwe ndipo n’kutheka kuti amafuna kukhala ndi moyo wosatha.

Kukhala ndi moyo wosatha? Ambiri sangagwirizane nawo maganizo amenewa. Ena angafike ngakhale ponena kuti alibe chidwi chokhala ndi moyo wosatha. Koma n’chifukwa chiyani munthu angafike poganiza choncho?

Kodi Moyo Wosatha Udzakhala Wotopetsa?

Ena amaganiza kuti moyo wosatha udzakhala  wotopetsa. Akhoza kumanena za moyo wosasangalatsa umene anthu ambiri opuma patchito amakhala nawo, womangokhalira kuonerera TV chifukwa chosowa chochita. Ngati inunso mumaona choncho, talingalirani zimene ananena katswiri wina wa sayansi ya zakuthambo dzina lake Robert Jastrow pamene anafunsidwa ngati moyo wosatha ungakhale dalitso kapena temberero. Jastrow anayankha kuti: “Ungakhale dalitso kwa anthu amene ali ndi chidwi chofuna kuti azingophunzirabe. Angasangalale kwambiri kuganizira kuti azikhalabe akuphunzira zinthu mpaka muyaya. Koma kwa anthu amene amaona kuti anamaliza kuphunzira zonse zomwe angathe kuziphunzira ndiponso safuna kuphunzira, zimenezi zingakhale temberero lalikulu zedi, chifukwa azidzasowa chochita.”

Kaya mukuganiza kuti moyo wosatha ungakhale wotopetsa kapena ayi, zimenezo zikudalira mmene inuyo mumaonera zinthu. Ngati muli ndi ‘chidwi chofuna kuti muzingophunzirabe,’ talingalirani zimene mungakwanitse kuchita pa luso la zojambulajambula, luso la zoimbaimba, luso la zomangamanga, za ulimi, kapena zilizonse zimene zimakusangalatsani mukamachita. Moyo wosatha padziko lapansi pano ungakupatseni mwayi wopititsa patsogolo luso losiyanasiyana limene muli nalo.

Moyo wamuyaya uyenera kukhalanso wosangalatsa chifukwa ungatipatse mpata wokonda anthu ena ndiponso woti iwowo atikonde mpaka muyaya. Tinalengedwa m’njira yoti tizitha kukonda ena, ndiponso zimatilimbikitsa ena akamatikonda. Kukondana ndi mtima wonse kumatipatsa chimwemwe chenicheni chimene sichitha ndi kupita kwa nthawi. Kukhala ndi moyo wosatha kudzatipatsa mwayi wosatha wotha kukonda kwambiri, osati anthu anzathu okha komanso makamaka Mulungu. Mtumwi Paulo anati: “Ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.” (1 Akorinto 8:3) Kutha kudziwa Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse ndiponso kudziwidwa ndi Iye n’chinthu chosangalatsa kwambiri chimene tingayembekezere. Kuwonjezeranso pamenepo, kuphunzira za Mlengi wathu wachikondi sikutha. Ndiyeno zingatheke bwanji kuti moyo wosatha ukhale wotopetsa ndi wosasangalatsa?

Kodi Moyo Umakhala Wamtengo Wapatali Chifukwa Choti Ndi Waufupi?

Ena amaona kuti chimene chimapangitsa moyo kukhala wamtengo wapatali n’chifukwa choti ndi waufupi. Angamayerekeze moyo ndi golide, amene sapezeka wambawamba. Iwo amati golide akanati azipezeka paliponse, sakanakhalanso wamtengo wapatali. Ngakhale zikanakhala choncho, golide akanakhalabe wokongola. N’chimodzimodzinso ndi moyo.

Kukhala ndi moyo wamuyaya tingakuyerekeze ndi kukhala ndi mpweya wambiri. Anthu amene ali mu sitima ya m’madzi imene yamira angaone mpweya kukhala wofunika kwambiri.  Kodi pambuyo pakuti apulumutsidwa, mukuganiza kuti angamadandaule chifukwa chakuti tsopano ali ndi mpweya wambiri? Ayi ndithu!

Monga anthu okwera sitima amenewo, ifenso tingapulumutsidwe koma ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Kudzera mu nsembe ya Yesu, Mulungu adzachotsa kupanda ungwiro kumene anthu ali nako ndi imfa ndipo adzapereka mphatso ya moyo wosatha kwa anthu omvera. Tiyeneradi kukhala oyamikira kwambiri chifukwa cha chikondi chimene Mulungu watisonyeza potikonzera zinthu zimenezi.

Nanga Bwanji za Anthu Amene Mumawakonda?

Anthu ena angamaganize kuti: ‘Nanga bwanji za anthu amene ndimawakonda? Moyo wosatha padziko lapansi udzakhala wopanda tanthauzo kwa ine ngati sindidzakhala nawo limodzi.’ Mwinamwake mwaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndipo mwaphunzira za moyo wosatha wosangalatsa umene udzakhalapo m’dziko lapansi la paradaiso. (Luka 23:43; Yohane 3:16; 17:3) Mwachibadwa, mumafuna achibale anu, anthu ena amene mumawakonda, ndi anzanu ena amene mumacheza nawo kuti adzapezekemo, n’cholinga choti nawonso adzasangalale ndi zinthu zimene mukuyembekezera kudzasangalala nazo m’dziko latsopano la chilungamo limene Mulungu walonjeza.​—2 Petro 3:13.

Koma nanga bwanji ngati anzanu ndi okondedwa anuwo akuonetsa kuti alibe chidwi chodzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi? Musalole zimenezo kukubwezani m’mbuyo. Pitirizanibe kuphunzira zinthu zolondola za m’Malemba, ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene mukuphunzirazo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mungadziwe bwanji, inu mkazi, mwina mungapulumutse mwamuna wanu? Kapena mudziwa bwanji, inu mwamuna, mwina mungapulumutse mkazi wanu?” (1 Akorinto 7:16, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Anthu amatha kusintha. Mwachitsanzo, bambo wina amene anali wotsutsa Chikristu anasintha ndipo m’kupita kwa nthawi anakhala mkulu mu mpingo wachikristu. Iye anati: “Ndikuthokoza kwambiri kuti banja langa linapitirizabe kutsatira mfundo za m’Baibulo mokhulupirika kwa nthawi yonse imene ndinali kuwatsutsa.”

Mulungu amadera nkhawa kwambiri moyo wanu limodzinso ndi miyoyo ya okondedwa anu. Ndithudi, ‘Yehova . . . safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Yehova Mulungu akufuna kuti inuyo limodzi ndi okondedwa anu mukhale ndi moyo wosatha. Chikondi chake n’chachikulu kuposa cha anthu opanda ungwiro. (Yesaya 49:15) Ndiye bwanji osayesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu? Mukatero mungathenso kuthandiza okondedwa anu kuti nawonso akhale ndi ubwenzi wabwino ndi iye. Ngakhale kuti panopa sangakhale ndi chiyembekezo ngati chanu chodzakhala ndi moyo wosatha, maganizo awo akhoza kusintha akamakuonani mukuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zolondola za m’Baibulo.

Nanga bwanji za okondedwa anu amene anamwalira? Baibulo limanena nkhani yosangalatsa yoti anthu mamiliyoni amene anamwalira adzauka n’kukhalanso ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. Yesu Kristu analonjeza kuti: “Ikudza nthawi, imene onse ali m’manda . . . adzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Ngakhale amene anamwalira asakudziwa Mulungu adzakhalanso ndi moyo, popeza Baibulo limanena kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Tidzakhaladi osangalala kwambiri kulandira anthu amenewa pamene adzakhalanso ndi moyo.

Moyo Wosatha Udzakhala Wosangalatsa

Ngati mumatha kukhala ndi moyo wachimwemwe ndi wokhutiritsa panopa ngakhale kuti pali mavuto ochuluka m’dzikoli, ndithudi mudzathanso kusangalala ndi moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi pano. Mboni ina ya Yehova itafotokoza za madalitso amene moyo wosatha udzabweretse, mayi wina ananena kuti: “Sindifuna kukhala ndi moyo wosatha.  Moyo unowu, wokhala zaka 70 kapena 80 wandikwanira.” Mkulu wina wachikristu amene anali pomwepo anafunsa mayiyo kuti: “Kodi munayamba mwaganizapo mmene ana anu zingawakhudzire inuyo mutati mwafa?” Misozi inayenderera m’masaya a mayiyo ataganizira za chisoni chimene ana ake angakhale nacho chifukwa cha kumwalira kwa mayi awo. “Kwa nthawi yoyamba, ndinazindikira kuti ndinali wodzikonda,” iye anatero, “ndipo ndinazindikira kuti kukhala ndi moyo wosatha sikudzikonda koma kuti kumakhudzanso ubwenzi wathu ndi anthu ena.”

Ena amaganiza kuti kaya akhale ndi moyo kaya afe palibe amene zingamukhudze. Komatu, amene anatipatsa moyo zimamamukhudza. Iye anati: “Pali Ine, . . . sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo.” (Ezekieli 33:11) Popeza Mulungu amadera nkhawa ngakhale moyo wa oipa, ndiye kuti amaderadi nkhawa kwambiri anthu amene amam’konda.

Mfumu Davide ya Israyeli wakale anakhulupirira kuti Yehova adzamusamalira mwachikondi. Nthawi ina Davide anati: ‘Pakuti [ngati] wandisiya atate wanga ndi amayi wanga Yehova anditola.’ (Salmo 27:10) Davide ankakhulupirira kuti makolo ake anali kumukonda. Koma ngakhale ngati makolo ake, amene anali achibale ake apafupi kwambiri, akanamutaya, iye ankadziwa kuti Mulungu sadzamutaya. Chifukwa cha chikondi chake ndi kutidera nkhawa, Yehova akutipatsa mphatso ya moyo wosatha ndi mwayi woti tikhale pa ubwenzi wosatha ndi iye. (Yakobo 2:23) Kodi sitikuyenera kulandira moyamikira mphatso zabwino kwambiri zimenezi?

[Chithunzi patsamba 7]

Kukonda Mulungu ndi anthu anzathu kudzapangitsa moyo wosatha kukhala wosangalatsa