Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ziwanda zidzakhala kuti pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu?

Baibulo siliyankha funso limeneli mwachindunji. Komabe, tikaona mfundo zingapo, tikhoza kudziwa kumene ziwanda zidzakhale pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu.

Posonyeza zomwe zidzachitike kumayambiriro ndi kumapeto kwa Zaka 1,000 zimenezi, mtumwi Yohane anati: “Ndipo ndinaona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi, nam’ponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.” (Chivumbulutso 20:1-3) Mavesi amenewa akunena za kumangidwa kwa Satana yekha ndi kumasulidwa kwake kwa kanthawi. Ngakhale kuti ziwanda sanazitchulepo, m’pomveka kunena kuti mngelo wokhala ndi chifungulo cha phompho, amene ali Yesu Kristu waulemerero, akadzagwira Mdyerekezi ndi kumuponya kuphompho, adzachitanso chimodzimodzi ndi ziwanda.​—Chivumbulutso 9:11.

Yesu Kristu atakhala Mfumu kumwamba mu 1914 anachita zinthu zimene zinasintha kwambiri moyo wa Satana ndiponso wa ziwanda. Lemba la Chivumbulutso 12:7-9 limati: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake [ziwanda] chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Chiyambireni nthawi imeneyo, Satana ndi ziwanda zake akukhala kufupi ndi dziko lapansi ndipo saloledwanso kupita kwina kulikonse. Choncho m’pomveka kukhulupirira kuti Yesu Kristu akadzaletsa Satana kuchita zinthu zina zimene akutha kuchita panopa kuti padziko lapansi pasadzakhalenso mphamvu yake, Iye adzachitanso chimodzimodzi ndi ziwanda.

Taganiziraninso ulosi woyambirira wa m’Baibulo. Ulosiwo umati: “[Ine Mulungu] ndidzaika udani pakati pa iwe [Satana] ndi mkaziyo [gulu lakumwamba la Yehova], ndi pakati pa mbewu yako [ya Satana] ndi mbewu yake [Yesu Kristu]; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Kulalira mutu wa njoka kumaphatikizapo kuponya Satana kuphompho pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu. Ulosiwo ukusonyezanso kuti pali udani pakati pa Iye amene akulalirayo ndi mbewu ya Satana. Mbewu imeneyi, kapena kuti gulu, limaphatikizapo mbali yake yosaoneka ya angelo, kapena kuti ziwanda. Choncho m’pomveka kunena kuti Yesu akadzaponya Satana kuphompho, adzamanga ndi kuponyanso ziwanda kuphompho. Mizimu yoipa yasonyeza kale kuti imaopa kwambiri kuponyedwa kuphompho, zimene zikutanthauza kuti ikudziwa kuti m’tsogolo muno ntchito yawo idzaletsedwa zimenezi zikadzachitika.​—Luka 8:31.

Koma kodi n’kutheka kuti lemba la Chivumbulutso 20:1-3 silitchula ziwanda chifukwa choti zidzakhala zitawonongedwa pa Armagedo limodzi  ndi mbali yooneka ya mbewu ya Satana? Baibulo limasonyeza kuti zimenezi sizingakhale choncho. Ponena za zimene zidzachitikire Satana pamapeto penipeni, Baibulo limati: “Mdyerekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.” (Chivumbulutso 20:10) Chilombo ndiponso mneneri wonyenga zikuimira mabungwe a ndale, omwe ali mbali imodzi ya gulu looneka la Satana. (Chivumbulutso 13:1, 2, 11-14; 16:13, 14) Adzawonongedwa pa Armagedo, pamene Ufumu wa Mulungu udzaphwanya ndi kutha maufumu onse a padziko lapansi. (Danieli 2:44) Baibulo limanena za ‘moto wa nthawi zonse wokolezedwera Mdyerekezi ndi amithenga ake.’ (Mateyu 25:41) Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa “m’nyanja ya moto ndi sulfure” yomwe mudzaponyedwenso chilombo ndi mneneri wonyenga chifukwa chakuti Satana ndi ziwanda zakezo nawonso adzawonongedwa kosatha. Zikanakhala kuti ziwanda, zomwe zili mbali yamphamvu kwambiri yauzimu ndiponso yosaoneka ya mbewu ya Satana, zidzawonongedwa pa Armagedo, bwenzi zitatchulidwa kuti zili kale mu nyanja yophiphiritsira imeneyo limodzi ndi chilombo ndi mneneri wonyenga. Popeza sizikutchulidwa pa Chivumbulutso 20:10, zikutanthauza kuti ziwanda sizidzawonongedwa pa Armagedo.

Popeza ziwanda sizinachite kutchulidwa kuti zinaponyedwa kuphompho, sizinatchulidwenso kuti zinatulukako. Koma zomwe zidzazichitikire n’chimodzimodzi ndi zimene zidzachitikire Mdyerekezi. Zikadzatulutsidwa limodzi ndi Mdyerekezi n’kuthandizana naye pa nthawi imene anthu adzayesedwe komaliza pamapeto pa zaka 1000, ziwandazo zidzaponyedwanso m’nyanja ya moto ndipo zidzawonongedwa kosatha.​—Chivumbulutso 20:7-9.

Choncho, ngakhale kuti lemba la Chivumbulutso 20:1-3 limafotokoza za Satana yekha kuti anagwidwa ndi kuponyedwa kuphompho komwe sadzathanso kuchita chilichonse, malinga ndi mfundo zomwe taonazi tinganene kuti angelo ake nawonso adzamangidwa ndi kuponyedwa kuphompho. Satana ndi ziwanda zake zambirimbiri sadzaloledwa kudodometsa Mulungu kuti asakwaniritse cholinga chake choti dziko lapansi lisanduke paradaiso ndi choti anthu akhalenso angwiro pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu.