Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Angakhale ndi Moyo Wautali Bwanji?

Kodi Anthu Angakhale ndi Moyo Wautali Bwanji?

 Kodi Anthu Angakhale ndi Moyo Wautali Bwanji?

PA March 3, 1513, Msipanya wina wofufuza malo dzina lake Ponce de León anayamba ulendo wake wochititsa chidwi wa panyanja, kuchokera ku Puerto Rico n’cholinga chofuna kukafika pa chilumba cha Bimini. Nkhani yake imafotokoza kuti ankafuna kasupe winawake wozizwitsa, Kasupe Wopatsa Unyamata. Koma anakapezeka ali m’dziko la United States mu boma limene panopa limatchedwa Florida. Kasupeyo sanamupeze chifukwa kunalibe kasupe woteroyo.

Masiku ano, anthu ambiri sakhala ndi moyo wautali kupitirira zaka 70 kapena 80. Buku lakuti 2002 Guinness Book of World Records limanena kuti munthu amene anakhala ndi moyo wautali kuposa aliyense anakhala zaka 122 ndi masiku 164, ngakhale kuti Baibulo limatchula anthu amene anakhala ndi moyo wautali kuposa pamenepa. (Genesis 5:3-32) Koma wasayansi wina dzina lake John Harris anati: “Kafukufuku watsopano wasonyeza kuti n’zotheka m’tsogolo muno kuti anthu azidzakhala osakalamba ngakhale osafa kumene.” Ochita kafukufuku a m’zaka za m’ma 2000 zino amanena za “moyo wosafa,” “moyo wopanda malire umene anthu azidzakhala nawo pomadzafika m’chaka cha 2099,” ndiponso amanena zoti anthu “azidzatha kukhala ndi maselo osafa,” ndi zina zotero.

M’buku lake lakuti The Dream of Eternal Life, Mark Benecke analemba kuti: “Pamoyo wonse wa munthu pafupifupi [maselo] onse a m’thupi mwake amatha, n’kulowedwa m’malo ndi ena atsopano nthawi zingapo. . . . Ndipo pomatha pafupifupi zaka seveni timakhala anthu atsopano.” Komabe, sikuti zimenezi zimangopitirira mpaka kalekale chifukwa maselo amasiya kuchuluka, poti akafika penapake amasiya kugawikana. Zikanakhala kuti sizinali choncho, anatero Benecke, “bwenzi thupi la munthu likumatha kudzikonza lokha kwa nthawi yaitali, ngakhale kwamuyaya.”

Taganizirani za mphamvu yodabwitsa ya ubongo wa munthu, umene timangogwiritsa ntchito mbali yochepa chabe ya mphamvu zake pa moyo wathu. Malinga ndi Encyclopædia Britannica, ubongo wa munthu “uli ndi mphamvu yotha kuchita zinthu zambiri kuposa  zimene umachita pa moyo wonse wa munthu.” (1976 Edition, Voliyumu 12, tsamba 998) Buku lakuti How the Brain Learns, (Mmene Ubongo Umaphunzirira) lolembedwa ndi David A. Sousa, limanena kuti: “Tingati ubongo uli ndi mphamvu yosunga zinthu yopanda malire.”​—Tsamba 78, Second Edition, ya mu 2001.

N’chifukwa chiyani ochita kafukufuku satha kupeza cholakwika chilichonse ndi mmene thupi lathuli limagwirira ntchito, chimene chimatichititsa kuti tizifa? Ndipo n’chifukwa chiyani ubongo wa munthu uli ndi mphamvu zochuluka choncho? Kodi n’kutheka kuti tinapangidwa kuti tiziphunzira zinthu mpaka muyaya? N’chifukwa chiyani timatha kuganiza za moyo wosatha?

Baibulo limati: “Ndipo [Mulungu] waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu anatiika maganizo okhala ndi moyo wosatha. Zimenezi zikutanthauza kuti, tinayenera kumaphunzira zinthu zatsopano zonena za Mulungu ndi ntchito zake mpaka kalekale. Tikanati tizikhala zaka mabiliyoni osawerengeka, ngakhale kosatha, bwenzi tikukhala ndi zinthu zambiri zokhudza ntchito zodabwitsa za chilengedwe cha Mulungu zoti tiphunzire mpaka kalekale.

Mawu a Yesu Kristu amasonyezanso kuti n’zotheka anthu kukhala ndi moyo wosatha. Iye anati: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.’ (Yohane 17:3) Nanga bwanji inuyo? Kodi mumafuna kukhala ndi moyo wosatha?

[Zithunzi patsamba 3]

Juan Ponce de León anafunafuna kasupe wopatsa unyamata

[Mawu a Chithunzi]

Ponce de León: Harper’s Encyclopædia of United States History