Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wetani Gulu la Mulungu”

“Wetani Gulu la Mulungu”

 “Idzani Kuno kwa Ine . . . Ndipo Ine Ndidzakupumulitsani Inu”

“Wetani Gulu la Mulungu”

“Nthaŵi zonse mumamvetsera zonena zathu ndiponso mumaŵerenga nafe mawu a m’Baibulo amene amatilimbikitsa kwambiri.”​—Anatero Pamela.

“Zikomo kwambiri chifukwa cha zonse zimene mumatichitira. Zimenezi zimatithandiza kwambiri.”​—Anatero Robert.

PAMELA ndi Robert analembera akulu achikristu a kumipingo yawo mawu oyamikira ameneŵa. Enanso mwa atumiki a Mulungu padziko lonse amayamikira chithandizo ndi chilimbikitso chimene amalandira kuchokera kwa amene ‘amaweta gulu la Mulungu.’ (1 Petro 5:2) Ndithudi, anthu a Yehova amayamikira zinthu zambiri zimene akulu amawachitira ndiponso mmene akuluwo amachitira zimenezi.

‘Ochuluka mu Ntchito’

Akulu achikristu amaikizidwa maudindo ambiri. (Luka 12:48) Amakonzekera nkhani zokakamba pa nthaŵi ya misonkhano ya mpingo ndiponso amapita nawo kokalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ntchito yawo imaphatikizaponso kupanga ulendo wa ubusa kwa okhulupirira anzawo. Akulu amapezanso nthaŵi yothandizira anthu amene akufuna chithandizo chapadera monga okalamba ndi ena, koma saiwala kuthandiza mabanja awo mwauzimu ndiponso powapezera zosoŵa zawo. (Yobu 29:12-15; 1Timoteo 3:4, 5; 5:8) Akulu ena amathandiza pa ntchito yomanga nawo Nyumba za Ufumu. Ena amatumikira m’Makomiti Olankhula ndi Achipatala kapena ali m’Magulu Ozonda Odwala. Ndipo ambiri amagwira ntchito yongodzipereka pa misonkhano ikuluikulu. Inde, akulu alidi ndi ‘zochuluka mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Ndiyetu m’posadabwitsa kuti akulu otere amayamikiridwa kwambiri ndi anthu amene amawasamalirawo.​—1 Atesalonika 5:12, 13.

Akulu amene amayendera Akristu anzawo nthaŵi ndi nthaŵi ku nyumba zawo kapena kulikonse n’cholinga chowalimbikitsa mwauzimu ndi olimbikitsadi. “Ngati akulu akanapanda kundilimbikitsa, sindikuganiza kuti panopa ndikanakhala ndikutumikira Yehova monga mtumiki wa nthaŵi zonse,” anatero Thomas amene anakulira pa khomo lopanda bambo. Achinyamata ambiri amene analeredwa m’banja la kholo limodzi amavomereza kuti thandizo limene anapeza kuchokera kwa akulu linawathandiza kukulitsa unansi wawo ndi Mulungu.

Maulendo a ubusa amayamikiridwanso kwambiri ndi anthu achikulire mu mpingo. Akulu atakachezera banja lina lomwe anali amishonale, a zaka za  m’ma 85, banjali linalemba kuti: “Tikufuna kukuthokozani podzatichezera. Mutapita, tinaŵerenganso malemba amene munaŵerenga nafe. Sitidzaiŵala mawu anu olimbikitsa.” Mkazi wina wamasiye wa zaka 70 analembera akulu kuti: “Ndakhala ndikupemphera kwa Yehova kuti andithandize, ndipo anatumiza abale inu aŵiri ku nyumba yanga. Ulendo wanu unali dalitso lochokera kwa Yehova.” Kodi inuyo mwapindula ndi ulendo waubusa wa akulu mu mpingo wanu posachedwapa? Inde, tonsefe timayamikira khama la akulu poweta gulu limene akuliyang’anira.

Abusa Amene Amatsanzira Mulungu ndi Kristu

Yehova ndi Mbusa wachikondi. (Salmo 23:1-4; Yeremiya 31:10; 1 Petro 2:25) Yesu Kristu nayenso ndi Mbusa wabwino amene amasamalira zosowa zathu zauzimu. Ndipotu iye amatchedwa “Mbusa Wabwino,” ndi “Mbusa wamkulu.” (Yohane 10:11; Ahebri 13:20; 1 Petro 5:4) Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi anthu amene ankafuna kukhala ophunzira ake? Anawaitana mokoma mtima kuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”​—Mateyu 11:28.

Mofananamo akulu masiku ano amayesetsa kuti akhale otsitsimula ndiponso kuti ateteze gulu. Akulu otere ‘amakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.’ (Yesaya 32:2) Akulu oteteza oterowo amabweretsa mpumulo, gulu limawalemekeza ndipo Mulungu amawayanja.​—Afilipi 2:29; 1 Timoteo 5:17.

Thandizo Lofunika Kwambiri la Akazi Awo

Anthu a Mulungu amayamikira kwambiri akulu Achikristu ndiponso chilimbikitso chimene akuluwa amapeza kwa akazi awo. Nthaŵi zambiri, akazi a akuluwa amafunika kudzimana kuti athandize. Nthaŵi zina, akazi a akulu amakhala ali kunyumba pamene amuna awo akusamalira nkhani za mpingo kapena akupanga ubusa. Nthaŵi zina, amasintha zimene anakonza kuti achite pakabuka mavuto ofunika kuwasamalira mwamsanga mu mpingo. Mkazi wina dzina lake Michelle anati: “Ngakhale zikatero, ndikaona mwamuna wanga akutanganidwa ndi kukonzekera misonkhano kapena kupanga ulendo wa ubusa, ndimadziŵa kuti akuchita ntchito ya Yehova, ndipo ndimayesetsa kukhala wothandiza momwe ndingathere.”

Cheryl, yemwenso anakwatiwa ndi mkulu anasimba kuti: “Ndimadziŵa kuti abale ndi alongo mu mpingo amafunanso akulu kuti alankhule nawo, ndipo ndimafuna kuti adziŵe kuti angathe kubwera kwa mwamuna wanga nthaŵi iliyonse imene akufuna.” Akazi othandiza, monga Michelle ndi Cheryl, mwa kufuna kwawo amadzimana kuti amuna awo athe kusamalira nkhosa za Mulungu. Akazi a akulu amayamikiridwa chifukwa cha mtima wothandizawu.

Ngakhale zili choncho, mkulu wotanganidwa sayenera kunyalanyaza zinthu zauzimu ndi zinthu zinanso zofunika kwa mkazi ndi ana ake. Mkulu wokwatira ayenera kukhala “wopanda chirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nawo ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mawu.” (Tito 1:6) Ayenera kusamalira banja lake m’njira ya Mulungu imene Baibulo limavomereza kwa oyang’anira achikristu.​—1 Timoteo 3:1-7.

Kwa mkulu wotanganidwa, mkazi wothandiza ndi wofunika kwambiri. Ndi mmene akulu okwatira oganizira ena amamvera. Zili ngati mmene Baibulo limanenera kuti: “Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino.” (Miyambo 18:22) Mwa mawu ndi zochita, akulu oterowo amayamikira akazi awo kuchokera pansi pamtima. Kuwonjezera pa pemphero lochokera pansi pamtima ndi phunziro losangalatsa lomwe amachitira pamodzi, mabanja achikristu ameneŵa amapatula nthaŵi kuti asangalale ndi zinthu ngati kukayenda kunyanja, kunkhalango, kapena kukawongola miyendo ku paki. Ndithudi, akulu amasangalala posamalira akazi awo.​—1 Petro 3:7.

Akulu amene amaweta gulu la Mulungu mopanda dyera amakhala olimbikitsa zedi mwauzimu kwa anthu a Yehova. Amakhaladi “mphatso mwa amuna,” dalitso ku mpingo.​—Aefeso 4:8 NW, 11-13.