Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Osaleka Kusonkhana Pamodzi

Osaleka Kusonkhana Pamodzi

 Osaleka Kusonkhana Pamodzi

Malemba amati: “Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:25) Inde, olambira oona ayenera kusonkhana pamodzi pamalo olambirira kuti ‘aganizirane wina ndi mnzake kuti afulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.’​—Ahebri 10:24.

PAMENE mtumwi Paulo amalemba mawu ameneŵa m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, n’kuti kachisi wochititsa kaso ku Yerusalemu akugwira ntchito monga malo olambiriramo a Ayuda. Kunalinso masunagoge. Yesu ‘anaphunzitsa m’sunagoge ndi m’Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse.’​—Yohane 18:20.

Kodi Paulo ankaganiza za malo otani pamene analangiza Akristu kuti azisonkhana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake? Kodi nyumba zikuluzikulu za Matchalitchi Achikristu zimatengera kachisi wa ku Yerusalemu? Kodi nyumba zikuluzikulu zachipembedzo zinayamba liti kwa omwe amati ndi Akristu?

Nyumba ya Dzina la Mulungu’

Malangizo oyamba a malo olambiriramo Mulungu amapezeka m’buku la m’Baibulo la Eksodo. Yehova Mulungu analangiza anthu ake amene anawasankha, Aisrayeli, kuti amange “chihema,” kapena “chihema chokumanira.” Likasa la chipangano ndiponso zinthu zina zopatulika zinali zoti azizisunga mmenemo. “Ulemerero wa Yehova unadzaza chihema”  chitatha kumangidwa mu 1512 B.C.E. Chihema chomwe ankatha kuchinyamulacho chinali chinthu chofunika kuti anthuwo athe kufika kwa Mulungu ndipo chinagwira ntchito kwa zaka mazana anayi. (Eksodo, machaputala 25-27; 40:33-38) Baibulo limatchanso chihema chimenechi kuti “kachisi wa Yehova” ndiponso “nyumba ya Yehova.”​—1 Samueli 1:9, 24.

Pambuyo pake, Davide atakhala mfumu mu Yerusalemu, anasonyeza kuti anali wofunitsitsa ndi mtima wonse kumanga nyumba yoti ilemekeze Yehova. Koma popeza Davide anali munthu wankhondo, Yehova anamuuza kuti: “Sudzamangira dzina langa nyumba.” Mmalo mwake, Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti amange kachisi. (1 Mbiri 22:6-10) Solomo anapatulira kachisi ameneyu mu 1026 B.C.E., atamaliza ntchito yomanga yomwe inatenga zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Yehova anavomereza nyumba imeneyi mwakunena kuti: “Ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthaŵi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.” (1 Mafumu 9:3) Yehova akanabweretsa madalitso pa nyumba imeneyo ngati Aisrayeli akanakhalabe okhulupirika. Koma ngati akanasiya kuchita zabwino, Yehova sakanayanjanso malo amenewo, ndipo nyumbayo ikanakhala bwinja.​—1 Mafumu 9:4-9; 2 Mbiri 7:16, 19, 20.

Patapita nthaŵi, Aisrayeli anasiya kulambira koona. (2 Mafumu 21:1-5) Motero “[Yehova] anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye . . . anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, nawononga zipangizo zake zonse zokoma. Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nawo ku Babulo, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake.” Malinga n’kunena kwa Baibulo, zimenezi zinachitika mu 607 B.C.E.​—2 Mbiri 36:15-21; Yeremiya 52:12-14.

Monga momwe mneneri Yesaya analoserera, Mulungu anautsa Mfumu Koresi ya ku Perisiya kuti imasule Ayuda mu ukapolo wa ku Babulo. (Yesaya 45:1) Utatha ukapolo wa zaka 70, anabwerera ku Yerusalemu mu 537 B.C.E. n’cholinga chakuti akamangenso kachisi. (Ezara 1:1-6; 2:1, 2; Yeremiya 29:10) Kachisi amene anatenga nthaŵi yaitali anamalizidwa kumangidwa m’chaka cha 515 B.C.E., ndipo kulambira Mulungu koona kunabwezeretsedwa. Kachisiyo anakhalapo kwa zaka pafupifupi 600, koma sanali wokongola ngati kachisi wa Solomo. Komabe, chifukwa chakuti Aisrayeli ananyalanyaza kulambira Yehova, kachisi ameneyunso sanali kumusamalira. Pamene Yesu Kristu ankabwera padziko lapansi n’kuti Mfumu Herode akumanganso kachisiyu pang’onopang’ono. Kodi n’chiyani chinali kudzachitikira kachisi ameneyu?

‘Sipadzakhala Mwala Umodzi pa Unzake’

Pofotokoza za kachisi wa ku Yerusalemu, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.” (Mateyu 24:1, 2) Mogwirizanadi ndi mawu amenewo, malo amene kwa zaka mazana ambiri ankadziŵika ngati oyenera kulambira Mulungu anawonongedwa mu 70 C.E. ndi magulu ankhondo a Aroma amene anabwera kudzathetsa kupanduka kwa Ayuda. * Kachisi ameneyu sanamangidwenso. Ndipo m’zaka za m’ma 600, malo ameneŵa omwe kale Ayuda ankalambirirapo, Asilamu anamangapo malo awo opatulika otchedwa Dome of the Rock ndipo alipo mpaka pano.

Kodi otsatira Yesu ankafunika kulambira motani? Kodi Akristu oyambirira achiyuda akanafunika kupitiriza kulambira Mulungu kukachisi  amene sakanatenga nthaŵi yaitali kuti awonongedwe? Kodi Akristu omwe sanali Ayuda akanalambirira kuti Mulungu? Kodi nyumba zachipembedzo za Matchalitchi Achikristu zikanalowa mmalo mwa kachisi? Zimene Yesu anakambirana ndi mkazi wachisamariya zingatithandize kumvetsa nkhani imeneyi.

Kwa zaka mazana ambiri, Asamariya ankalambira Mulungu kukachisi wamkulu pa phiri la Gerizimu ku Samaria. Mkazi wachisamariya anauza Yesu kuti, “Makolo athu analambira m’phiri ili; ndipo inu munena, kuti m’Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.” Poyankha Yesu anati: “Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthaŵi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena m’Yerusalemu.” Kachisi weniweni sakanakhalanso malo oyenera kulambiriramo Yehova, chifukwa Yesu anafotokoza kuti: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:20, 21, 24) Pambuyo pake mtumwi Paulo anauza anthu a ku Atene kuti: “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja.”​—Machitidwe 17:24.

Ndiyetu n’zachionekere kuti nyumba zachipembedzo za Matchalitchi Achikristu n’zosagwirizana ndi dongosolo la kachisi yemwe analipo Chikristu chisanayambe. Ndipo, Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino analibe chifukwa chomangira malo otero. Komabe atumwi atatha kufa, zimene analosera kuti ena adzapotoza chiphunzitso choona zinachitika. (Machitidwe 20:29, 30) Zaka zambiri Mfumu Kositantini ya Roma isanatembenuzidwe kuloŵa Chikristu mu 313 C.E. odzinenera kukhala Akristu anayamba kusintha zinthu zimene Yesu anali ataphunzitsa.

Kositantini anathandiza nawo mwa kusakaniza “Chikristu” ndi chipembedzo chachikunja cha Aroma. Buku lakuti The Encyclopædia Britannica limati: “Kositantini analamula kuti amange matchalitchi atatu akuluakulu achikristu ku Rome; tchalitchi cha St. Peter, S. Paolo Fuori le Mura, ndiponso S. Giovanni ku Laterano. Iye . . . anakonza mamangidwe amene matchalitchi a kumadzulo kwa Ulaya a m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500 anatengera.” Tchalitchi cha St. Peter chimene chinamangidwanso ku Rome chimaonedwabe ngati malo ofunika kwambiri kwa anthu a Tchalitchi cha Roma Katolika.

“Tchalitchi chinatengera miyambo ina ya chipembedzo ndi mitundu ina ya kalambiridwe imene inali yodziŵika Chikristu chisanayambe ku Rome,” anatero wolemba mbiri wina dzina lake Will Durant. Zimenezi zinaphatikizapo “mamangidwe a tchalitchi.” Kuyambira m’zaka za m’ma 900 mpaka m’ma 1400 ankamanga matchalitchi ambiri aang’ono ndi aakulu omwe, amene nkhani yaikulu inagona pa kamangidwe kaluso. Apa m’pamene panayambira nyumba zikuluzikulu za Matchalitchi Achikristu zimene masiku ano anthu amaziona kuti ndi nyumba zochititsa chidwi zosonyeza luso la zomangamanga.

Kodi anthu nthaŵi zonse amatsitsimulidwa ndi kulimbikitsidwa mwauzimu pokalambira kutchalitchi? Francisco wa ku Brazil anati: “Kwa ine, tchalitchi chinali chinthu chosasangalatsa ndiponso chotopetsa pankhani ya chipembedzo. Misa inali yopanda tanthauzo, mwambo wongobwerezabwereza umene sunandikhutiritse zinthu zimene ndinkafunadi. Ndinkapeza mpumulo mwambo wa Misa ukatha.” Ngakhale zili choncho, okhulupirira oona amalamulidwa kusonkhana pamodzi. Kodi ayenera kusonkhana m’njira yotani?

 ‘Mpingo wa M’nyumba Mwawo’

Mmene Akristu amachitira pa nkhani yosonkhana zinayamba atapenda mosamalitsa mmene okhulupirira a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino ankachitira. Malemba amasonyeza kuti nthaŵi zambiri ankasonkhana pamodzi mnyumba za anthu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulankhule Priska ndi Akula, antchito anzanga m’Kristu Yesu, ndipo mulankhule mpingo wa Ambuye wa m’nyumba mwawo.” (Aroma 16:3, 5; Akolose 4:15; Filemoni 2) M’mabaibulo ena a Chingelezi, liwu la Chigiriki lakuti “mpingo” (ek·kle·siʹa) amalimasulira kuti “tchalitchi.” Koma liwuli limaimira gulu la anthu amene asonkhana pamodzi okhala ndi cholinga chimodzi, osati nyumba. (Machitidwe 8:1; 13:1) Kulambira kwa Akristu oona sikufuna nyumba zachipembedzo zapamwamba.

Kodi m’mipingo yachikristu yoyambirira ankachita motani misonkhano? Wophunzira Yakobo anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti sunagoge kutanthauza msonkhano wachikristu. (Yakobo 2:2) Mawu a Chigiriki ameneŵa amatanthauza “kusonkhanitsa pamodzi” ndipo angagwire ntchito mofanana ndi mawu akuti ek·kle·siʹa. Komabe, patapita nthaŵi, mawu akuti “sunagoge” anakhala ndi tanthauzo la malo kapena nyumba imene ankachitiramo misonkhano. Akristu oyambirira achiyuda ankadziŵa bwino zimene zinkachitika kusunagoge. *

Ayuda ankagwiritsa ntchito kachisi wa ku Yerusalemu posonkhana kuti achite mapwando awo apachaka pamene masunagoge ankawagwiritsa ntchito monga malo ophunzirirako za Yehova ndiponso Chilamulo. Zikuoneka kuti zina mwa zimene zinkachitika pa sunagoge ndizo kupemphera ndi kuŵerenga Malemba. Panalinso kukambirana Malemba mwatsanetsane ndiponso kulimbikitsana. Paulo pamodzi ndi anthu ena amene anali naye atalowa mu sunagoge ku Antiokeya “akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nawo mawu akudandaulira anthu, nenani.” (Machitidwe 13:15) Akristu achiyuda oyambirira atakumana mnyumba za anthu, mosakayikira anachitanso chimodzimodzi. Anachititsa misonkhano yawo kukhala yolangiza ndiponso yolimbikitsa mwauzimu.

 Mipingo ndi Malo Olimbikitsiranako

Mboni za Yehova masiku ano, mofanana ndi Akristu oyambirira, zimasonkhana pa malo olambiriramo omwe si apamwamba kwambiri kuti zilangizidwe za m’Baibulo ndi kusangalala ndi mayanjano abwino. Kwa zaka zambiri Mboni za Yehova zakhala zikusonkhana mnyumba za anthu ndipo zimaterobe m’madera ena. Koma tsopano chiŵerengero chamipingo chawonjezeka kupitirira 90,000, ndipo malo awo osonkhanira odziŵika bwino amatchedwa Nyumba za Ufumu. Nyumba zimenezi si zapamwamba kwambiri kapena zooneka ngati matchalitchi. Izo ndi nyumba zabwino zosakhala ndi zinthu zambiri zimene anthu okwana 100 kufika 200 amatha kusonkhanamo mlungu uliwonse kuti amvetsere ndi kuphunzira Mawu a Mulungu.

Mipingo yambiri ya Mboni za Yehova imasonkhana katatu pa mlungu. Msonkhano wina ndi wa nkhani ya onse imene imafotokoza mfundo zimene anthu panthaŵiyo akufunika kuzidziŵa. Ikatha nkhaniyi, pamakhala kuphunzira nkhani kapena ulosi wa m’Baibulo, pogwiritsa ntchito magazini ya Nsanja ya Olonda monga gwero lake. Msonkhano wina ndi sukulu imene inakonzedwa n’cholinga chophunzitsa kulalikira uthenga wa m’Baibulo. Ukatha msonkhano umenewu pamabweranso msonkhano umene cholinga chake ndi kupereka malingaliro othandiza mu utumiki wachikristu. Kamodzi pa mlungu uliwonse, Mboni zimakumana kuti ziphunzire Baibulo m’magulu ang’onoang’ono mnyumba za anthu. Anthu onse akhoza kupita ku misonkhano imeneyi. Sipakhala kuyendetsa mbale ya zopereka.

Francisco, amene tamutchula koyambirira uja, anaona kuti misonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu ndi yothandiza kwambiri. Iye anati: “Malo osonkhanira oyamba amene ndinakapezekako anali nyumba yabwino pakati pa mzinda, ndipo ndinachoka pa nyumbayo ndili wosangalala zedi. Anthu onse amene anabwera anali ochezeka ndipo ndinkatha kuona kuti amakondana. Ndinkafuna tsiku lina nditapitakonso. Ndingoti, kuyambira nthaŵi imeneyo sindinaphonyeko msonkhano. Misonkhano yachikristu imeneyi imakhala yolimbikitsa, ndipo imandikhutiritsa zosoŵa zanga zauzimu. Ngakhale ndikakhumudwa pa zifukwa zina, ndimapita ku Nyumba ya Ufumu, ndili ndi chikhulupiriro kuti ndikabwerako nditalimbikitsidwa.”

Inunso muli ndi mwayi wophunzira Baibulo, wokhala ndi mayanjano olimbikitsa, ndiponso wotamanda Mulungu pa misonkhano yachikristu ya Mboni za Yehova. Tikukupemphani kuti mukasonkhane nawo ku Nyumba ya Ufumu imene ili kufupi ndi kwanuko. Mukadzatero mudzasangalala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kachisiyo anawonongedweratu ndi Aroma. Khoma limene analitcha Wailing Wall, kumene Ayuda ambiri ochokera kutali amapita kukapempherako, si mbali ya kachisiyo. Ndi mbali chabe ya linga la bwalo la kachisi.

^ ndime 20 Zikuoneka kuti masunagoge anayambika m’nthaŵi ya ukapolo wa zaka 70 wa ku Babulo, nthaŵi imene panalibe kachisi, kapena anayambika atangochoka kumene ku ukapolo pamene kachisi ankamangidwanso. Pofika m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, tauni iliyonse ku Palesitina inali ndi sunagoge, ndipo mizinda ikuluikulu inali ndi masunagoge angapo.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Chihema ndipo pambuyo pake akachisi anakhala malo abwino olambiriramo Yehova

[Chithunzi patsamba 6]

Tchalitchi cha St. Peter ku Rome

[Chithunzi patsamba 7]

Akristu oyambirira ankasonkhana pamodzi mnyumba za anthu

 [Zithunzi pamasamba 8, 9]

Mboni za Yehova zimakhala ndi misonkhano yachikristu mnyumba za anthu ndi ku Nyumba ya Ufumu