Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingatani Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova?

Kodi Tingatani Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova?

Kodi Tingatani Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova?

“Dzulo maola aŵiri amtengo wapatali anatayika. Sizingathekenso kuwabwezeretsa chifukwa apitiratu!”​—Anatero Lydia H. Sigourney, wolemba mabuku wa ku America (1791-1865).

MASIKU a moyo wathu amaoneka kuti ndi ochepa ndiponso amatha mofulumira. Wamasalmo Davide anasinkhasinkha kufupika kwa moyo wa munthu ndipo zimenezi zinamuchititsa kupemphera kuti: “Yehova, mundidziŵitse chimaliziro changa, ndi maŵerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu.” Nkhaŵa ya Davide inali yoti akhale ndi moyo umene ungasangalatse Mulungu, mwa zolankhula ndiponso zochita zake. Polankhula za kudalira kwake Mulungu, iye anati: “Chiyembekezo changa chili pa Inu.” (Salmo 39:4, 5, 7) Yehova anamumvera. Anaonadi zimene Davide anachita ndipo anam’patsa mphoto malinga ndi zochita zakezo.

N’zosavuta kukhala wotanganidwa nthaŵi zonse ndi kukhala ndi moyo wodzala ndi zochita. Zimenezi zingatiyambitse nkhaŵa, makamaka chifukwa chokhala ndi zochita zambiri pamene nthaŵi yoti tichite zimenezo ndi yochepa kwambiri. Kodi nkhaŵa yathu ili ngati ya Davide, yoti tikhale ndi moyo umene ungasangalatse Mulungu? Kunena zoona, Yehova amationa ndipo amatipenda mosamala tonsefe. Yobu, mwamuna amene ankaopa Mulungu anazindikira zaka pafupifupi 3,600 zapitazo kuti Yehova anaona njira zake zonse ndipo anaŵerenga moponda mwake monse. Yobu anafunsa kuti: “Pondizonda Iye ndidzam’yankha chiyani?” (Yobu 31:4-6, 14) Tingathe kuchita zoti masiku a moyo wathu asangalatse Mulungu ngati tiika zinthu zauzimu patsogolo, kumvera malamulo ake, ndi kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu mwanzeru. Tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane mbali zimenezi.

Tiike Zinthu Zauzimu Patsogolo

Malemba ouziridwa moyenerera amatilimbikitsa kuika zinthu zauzimu patsogolo pamene amanena kuti: “Mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri.” Kodi zinthu zofunika kwambiri zimenezi ndi ziti? Yankho lake limakhudza “chidziŵitso cholondola ndi kuzindikira konse.” (Afilipi 1:9, 10, NW) Kudziŵa zolinga za Yehova kumafuna kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu mwanzeru. Komabe, kuika zinthu zauzimu patsogolo kudzatithandiza kukhala ndi moyo wopindulitsa ndiponso wosangalatsa.

Mtumwi Paulo akutikumbutsa “kuyesera [“kupitiriza kutsimikizira,” NW] chokondweretsa Ambuye n’chiyani.” Kutsimikizira kwathu kuyenera kuphatikizapo kupenda zolinga zathu ndi zimene mtima wathu ukufuna. Mtumwiyo anapitiriza kuti: “Dziŵitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:10, 17) Motero, kodi n’chiyani chimene Yehova amavomereza? Mwambi wa m’Baibulo umayankha kuti: “Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m’kutenga kwako konseko utenge luntha. Uilemekeze, ndipo idzakukweza.” (Miyambo 4:7, 8) Yehova amakondwera ndi munthu amene amapeza ndiponso kusonyeza nzeru ya Mulungu. (Miyambo 23:15) Ubwino wa nzeru imeneyo ndi wakuti siingachotsedwe kapena kuwonongedwa. Ndipotu, imatchinjiriza ndi kutetezera ‘ku njira yoipa ndi kwa anthu onena zokhota.’​—Miyambo 2:10-15.

Ndiyetu n’kwanzeru kupeŵa kunyalanyaza zinthu zauzimu. Tiyenera kukhala ndi mtima woyamikira mawu a Yehova ndi kumuopa. (Miyambo 23:17, 18) Ngakhale kuti munthu angathe kukhala ndi mtima woterowo pa usinkhu uliwonse, ndi bwino kukhala ndi njira yabwino imeneyi ndi kukhomereza mfundo za m’Baibulo mumtima mwathu tili achinyamata. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 12:1.

Njira yabwino kwambiri yosonyeza kuyamikira Yehova ndiyo kupemphera kwa iye tsiku ndi tsiku. Davide anazindikira kufunika kouza Yehova zakukhosi, chifukwa anati: “Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga.” (Salmo 39:12) Kodi nthaŵi zina ubwenzi wathu wapamtima ndi Mulungu umakhudza kwambiri mtima wathu mpaka kufika pogwetsa misozi? Inde, tikamamuuza Yehova zakukhosi ndi kusinkhasinkha Mawu ake, iye amatiyandikira kwambiri.​—Yakobo 4:8.

Phunzirani Kumvera

Munthu winanso wachikhulupiriro amene anadalira Mulungu anali Mose. Mofanana ndi Davide, Mose anaona kuti moyo ndi wodzala ndi mavuto. Motero, iye anapempha Mulungu kuti amudziŵitse ‘kuŵerenga masiku ake motero, kuti akhale nawo mtima wanzeru.’ (Salmo 90:10-12) Munthu angakhale ndi mtima wanzeru mwa kuphunzira ndi kutsatira malamulo ndi mfundo za makhalidwe abwino za Yehova. Mose anadziŵa zimenezi ndipo kenako anayesetsa kukhomereza choonadi chofunika chimenechi kwa mtundu wa Israyeli mwa kuwabwerezera malamulo a Mulungu asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa. Mfumu iliyonse imene Yehova anali kudzaisankha kuti ilamulire Israyeli inayenera kukopera Chilamulo m’buku lake ndi kuŵerenga m’bukulo masiku onse a moyo wake. Chifukwa chiyani? Kuti iphunzire kuopa Mulungu. Zimenezi zikanayesa kumvera kwa mfumu. Zikanaithandiza kupeŵa kudzikuza pa abale ake ndiponso masiku a ufumu wake akanachuluka. (Deuteronomo 17:18-20) Lonjezo limeneli analibwereza pamene Yehova anauza mwana wa Davide, Solomo, kuti: “Ukadzayenda m’njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, ine ndidzachulukitsa masiku ako.”​—1 Mafumu 3:10-14.

Kumvera ndi nkhani yaikulu kwa Mulungu. Ngati titapeputsa mbali zina za zimene Yehova amafuna ndi malamulo ake, kuziona ngati zosafunika, iye mosakayika adzaona maganizo oterowo. (Miyambo 15:3) Kudziŵa zimenezi kuyenera kutichititsa kupitirizabe kulemekeza kwambiri malangizo a Yehova, ngakhale kuti kuchita zimenezo n’kovuta nthaŵi zina. Satana amachita zonse zimene angathe kuti ‘atiletse’ pamene tikuyesetsa kumvera malamulo a Mulungu.​—1 Atesalonika 2:18.

N’kofunika kwambiri makamaka kumvera langizo la m’Malemba losonkhana pamodzi kuti tilambire ndi kuyanjana. (Deuteronomo 31:12, 13; Ahebri 10:24, 25) Motero tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatsimikiza mtima ndiponso kulimbikira kuchita zinthu zopindulitsadi?’ Kunyalanyaza mayanjano ndi malangizo a pamisonkhano yachikristu chifukwa chofuna kuti tipeze chuma kudzafooketsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti [Yehova] anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Kumvera malamulo a Yehova mofunitsitsa kumasonyeza kuti timam’khulupirira ndi mtima wonse kuti adzatisamalira.

Yesu anaphunzira kumvera ndipo anapindula nako. Ifenso tingatero. (Ahebri 5:8) Tikakhala ndi mtima womvera, sitidzavutika kumvera ngakhale pa zinthu zazing’ono. N’zoona kuti chifukwa cha kukhulupirika kwathu, tingafunike kulimbana ndi zinthu zosasangalatsa kapena ngakhale nkhanza zimene ena angatichitire. Zimenezi zingakhale choncho makamaka kuntchito, kusukulu, kapena m’banja la anthu a zipembedzo zosiyana. Komabe, timalimbikitsidwa ndi mawu amene Aisrayeli anauzidwa, kuti ngati iwo ‘akanakonda Yehova mwa kumvera mawu ake ndiponso mwa kum’mamatira, iye akanakhala moyo wawo ndi masiku awo ochuluka.’ (Deuteronomo 30:20) Lonjezo limeneli likugwiranso ntchito kwa ife.

Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Mwanzeru

Kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yathu kudzatithandizanso kuchita zoti masiku athu asangalatse Yehova. Mosiyana ndi ndalama zimene zingasungidwe, nthaŵi imayenera kugwiritsidwa ntchito, koma ngati osatero, idzatayika. Ola lililonse limene lapita ndiye kuti lapitiratu. Popeza nthaŵi zonse timakhala ndi zambiri zoti tichite kuposa zimene tingathe, kodi tikugwiritsa ntchito nthaŵi yathu m’njira yoti tikwaniritse zolinga zathu pamoyo? Cholinga chachikulu cha Akristu onse ndicho kugwira nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira nthaŵi zonse.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Tingagwiritse ntchito mwanzeru nthaŵi yathu ngati tizindikira bwino kufunika kwake. Moyenera, Aefeso 5:16 amatilimbikitsa ‘kuchita machawi [‘kuwombola nthaŵi,’ NW]’ ndipo zimenezi zimatanthauza “kugula” nthaŵiyo, kuleka kuchita zinthu zina zosafunika kwambiri. Kumatanthauza kuchepetsa zochita zimene zingatiwonongere nthaŵi. Kuonera kwambiri TV kapena kufufuza zinthu pa Intaneti, kuŵerenga mabuku opanda phindu a kudziko, kapena kuchita maseŵero olimbitsa thupi ndi zosangalatsa zopambanitsa zingatitopetse kwambiri. Ndiponso, kukundika chuma mopambanitsa kungatiwonongere nthaŵi yofunika kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

Anthu odziŵa kusamala nthaŵi amati: “N’zosatheka kugwiritsa ntchito bwino nthaŵi yanu popanda kuika zolinga zomveka ndiponso zolunjika.” Iwo amapereka miyezo isanu yokhazikitsira zolinga. Amati ziyenera kukhala: zolunjika, zotsatirika, zotheka, zoti ungakwanitse, ndiponso kuika nthaŵi yake.

Chimodzi mwa zolinga zabwino kwambiri ndicho kupititsa patsogolo kuŵerenga kwathu Baibulo. Chinthu choyamba ndicho kukonza zoti cholinga chathucho chikhale cholunjika, monga kuŵerenga Baibulo lonse. Chachiŵiri ndicho kukonza zoti cholinga chathucho chikhale chotsatirika. Mwa kuchita zimenezo, tingathe kuona mmene tikupitira patsogolo. Zolinga ziyenera kutilimbikitsa kuchita khama ndi kupita patsogolo. Ziyeneranso kukhala zotheka ndiponso zoti tingakwanitse. M’pofunika kuganizira luso lathu ndiponso nthaŵi imene tingakhale nayo. Kwa ena, pangafunike nthaŵi yambiri kuti akwaniritse cholingacho. Pomaliza, cholingacho chimafunika kuchiikira nthaŵi. Kuikiratu tsiku loti mumalize kuchita chinachake kudzawonjezera kufunitsitsa kwanu kuti muchichitedi chinthucho.

A m’banja la Beteli padziko lonse, amene amatumikira pa likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova kapena m’nthambi zake, ali ndi cholinga cholunjika choŵerenga Baibulo lonse m’chaka chawo choyamba pa Beteli. Amazindikira kuti kuŵerenga Baibulo kopindulitsa kumawathandiza kukula mwauzimu ndiponso kuyandikira kwambiri kwa Yehova, amene akuwaphunzitsa kupindula. (Yesaya 48:17) Kodi ifenso sitingakhale ndi cholinga choŵerenga Baibulo nthaŵi zonse?

Phindu Lochita Zoti Masiku Athu Asangalatse Yehova

Kuika zinthu zauzimu patsogolo kudzatipindulitsa kwambiri. Mwa zina, kudzatithandiza kupeza chimwemwe chakuti takwaniritsa chinachake ndipo moyo wathu udzakhala ndi cholinga. Kupemphera nthaŵi zonse kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kudzatiyandikizitsa kwa iye. Kupemphera kokhako kumasonyeza kuti timamukhulupirira. Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku pamodzinso ndi mabuku ophunzirira Baibulo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa kumasonyeza kuti timafuna kumvera Mulungu pamene akulankhula nafe. (Mateyu 24:45-47) Zimenezi zimatithandiza kukhala ndi mtima wanzeru kuti tisankhe zochita zoyenera pamoyo wathu.​—Salmo 1:1-3.

Timasangalala kumvera malamulo a Yehova, chifukwa kuchita zimenezo sikolemetsa. (1 Yohane 5:3) Pamene tikuchita zoti tsiku lililonse la moyo wathu lisangalatse Yehova, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Timathandizanso kwambiri mwauzimu Akristu anzathu. Kuchita zimenezo kumasangalatsa Yehova Mulungu. (Miyambo 27:11) Ndipotu palibe china chilichonse chabwino choposa kuyanjidwa ndi Yehova panopa ndiponso kosatha!

[Chithunzi patsamba 21]

Akristu saona zinthu zauzimu mopepuka

[Zithunzi patsamba 22]

Kodi mukugwiritsa ntchito nthaŵi yanu mwanzeru?

[Chithunzi patsamba 23]

Timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova pamene tichita zoti tsiku lililonse la moyo wathu limusangalatse