Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amalandira Anthu a Mitundu Yonse

Mulungu Amalandira Anthu a Mitundu Yonse

 Mulungu Amalandira Anthu a Mitundu Yonse

JOHN paulendo wake woyamba wa ku Mali, anachita chidwi ndi momwe Mamadou ndi banja lake anamulandirira bwino. Pamene John anali kudya chakudya ndi banjalo anaganizira momwe angam’patsire mwininyumbayo mphatso yamtengo wapatali ya uthenga wabwino wa Ufumu wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ngakhale kuti John ankadziŵa Chifalansa chomwe anthu amalankhula ku Mali, ankadzifunsa kuti angalankhule bwanji ndi banja la chipembedzo china ndiponso loganiza mosiyana.

N’zosadabwitsa kuti John anaganiza zankhani ya m’Baibulo ya mzinda wa Babele. Mulungu anasokoneza chilankhulo cha anthu opanduka a kumeneko. (Genesis 11:1-9) Choncho, anthu a zinenero zosiyana, zipembedzo zosiyana ndiponso maganizo osiyana anapezeka m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi. Masiku ano, pamene kuyenda ndiponso kusamuka kuli kofala, anthu ambiri amapeza vuto langati la John, ngakhale m’dera lawo lomwe. Vutolo n’lakuti, Kodi ndi motani mmene angauzire anthu achikhalidwe china chiyembekezo chawo cha m’Baibulo?

Chitsanzo Chakale

Monga ankachitira aneneri ena onse a mu Israyeli, Yona kwenikweni ankalankhula kwa Aisrayeli. Iye ankalosera pa nthaŵi imene ufumu wopanduka wa mafuko khumi unachita poyera zinthu zoipira Mulungu. (2 Mafumu 14:23-25) Tangolingalirani mmene Yona anachitira, atapatsidwa ntchito yapadera yakuti achoke m’dziko lakwawo apite ku Asuri kukalalikira anthu a ku Nineve, omwe anali ndi chipembedzo ndi chikhalidwe china. N’kutheka kuti Yona sankalankhula n’komwe chinenero cha Anineve, kapena ankalankhula koma osati kwenikweni. Mulimonsemo, Yona anaiona ntchitoyi kukhala yovuta ndiponso yaikulu ndipo anathaŵa.​—Yona 1:1-3.

Ndithudi, Yona anafunika kuzindikira kuti Yehova Mulungu saona maonekedwe akunja okha komanso amayang’ana mumtima. (1 Samueli 16:7) Yehova atam’pulumutsa Yona mozizwitsa kuti asamire m’madzi, anamutuma kachiŵiri kuti akalalikire kwa Anineve. Yona anapita ndipo Anineve ambiri analapa. Komabe, Yona anali ndi maganizo oipa. Yehova anam’patsa chitsanzo champhamvu chimene chinamusonyeza kuti anafunika kusintha maganizo ake. Yehova anafunsa Yona kuti: “Sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi aŵiri osadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere?” (Yona 4:5-11)  Bwanji ife masiku ano? Ndi motani mmene tingathandizire anthu achikhalidwe china?

Kulandira Asamariya Ndiponso Amene Sanali Ayuda

Yesu m’zaka za zana loyamba, analamula otsatira ake kuphunzitsa anthu a mitundu yonse. (Mateyu 28:19) Izi zinali zowavuta. Ophunzira a Yesu anali Ayuda ndipo monga Yona, anazoloŵera kulankhula ndi anthu achikhalidwe ndi miyambo yawo basi. Mwachibadwa, ayeneranso kuti anali kukhudzidwa ndi tsankho limene linali lofala nthaŵi imeneyo. Koma, Yehova anatsogolera zinthu kuti atumiki ake pang’onopang’ono azindikire zimene iye ankafuna kwa anthu ameneŵa.

Choyamba chinali kuthetsa tsankho pakati pa Ayuda ndi Asamariya. Ayuda sankayenderana ndi Asamariya. Koma Yesu kangapo konse anakonza njira yakuti m’tsogolo Asamariya adzamve uthenga wabwino. Anasonyeza kuti analibe tsankho mwa kulankhula ndi mkazi wachisamariya. (Yohane 4:7-26) Nthaŵi inayake, mwa fanizo la m’Samariya wachifundo, Yesu anasonyeza Myuda wa chipembedzo kuti anthu ena amene sanali Ayuda ankatha kusonyeza kukonda anansi. (Luka 10:25-37) Nthaŵi itakwana yakuti Yehova abweretse Asamariya mu mpingo wachikristu, Filipo, Petro, ndi Yohane, omwe anali Ayuda, analalikira kwa Asamariya. Uthenga wawo unadzetsa chimwemwe chachikulu m’mudzimo.​—Machitidwe 8:4-8, 14-17.

Ngati Akristu achiyuda zinkawavuta kukonda Asamariya amene anali achibale awo, ndiye kuti zinkawavuta kwambiri kusonyeza chikondi kwa anansi amene sanali Ayuda, kapena kuti Akunja, amene Ayuda ankawanyoza ndi kuwada. Komabe, Yesu atamwalira, malire amene anali pakati pa Akristu Achiyuda ndi Akunja anachotsedwa. (Aefeso 2:13, 14) Yehova pothandiza Petro kuti atsatire dongosolo latsopanoli, anamusonyeza masomphenya ndi kumuuza kuti ‘chimene Mulungu anayeretsa, asachiyese chinthu wamba [“chodetsedwa,” NW].’ Ndiyeno mzimu wa Yehova unam’tsogolera kwa Korneliyo, munthu wakunja. Petro atazindikira malingaliro a Mulungu akuti asayese munthu wa amitundu ameneyu wodetsedwa chifukwa Mulungu wamuyeretsa, anauziridwa kunena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:9-35) Petro anadabwa kwambiri pamene Mulungu anasonyeza kuti walandira Korneliyo ndi banja lake mwa kuwatsanulira mzimu woyera.

Paulo​—Chotengera Chosankhika kwa Amitundu

Utumiki wa Paulo ndi chitsanzo chapadera kwambiri cha mmene Yehova pang’onopang’ono amathandizira atumiki ake kukonda ndi kuthandiza anthu amitundu yonse. Nthaŵi imene Paulo amatembenuka, Yesu ananena kuti Paulo akakhala chotengera chosankhika cha kunyamula dzina Lake pamaso pa amitundu. (Machitidwe 9:15) Ndiyeno Paulo anapita ku Arabiya, mwina kukasinkhasinkha cholinga cha Mulungu  choti amutume kukalalikira uthenga wabwino kwa amitundu.​—Agalatiya 1:15-17.

Paulo paulendo wake woyamba wa umishonale, analalikira mwachangu kwa anthu amene sanali Ayuda. (Machitidwe 13:46-48) Yehova anadalitsa ntchito ya Paulo, ndipo umenewu unali umboni wakuti mtumwiyo anali kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Yehova anakonza. Paulo anasonyeza kuti anazindikira kwambiri malingaliro a Yehova mwa kudzudzula Petro molimba mtima, amene anali kusonyeza tsankho mwa kusayanjana ndi abale ake amene sanali Ayuda.​—Agalatiya 2:11-14.

Umboni wina wakuti Mulungu anali kutsogolera ntchito ya Paulo tikuupeza mu ulendo wake wachiŵiri wa umishonale pamene mzimu woyera unam’letsa kulalikira ku chigawo cha Roma cha Bituniya. (Machitidwe 16:7) Inde, sinali nthaŵi yake. Komabe, kenako, Abituniya ena anakhala Akristu. (1 Petro 1:1) M’masomphenya, munthu wina wa ku Makedoniya anadandaulira Paulo kuti: “Muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.” Paulo anaganiza zosintha ulendo wake kuti akalalikire uthenga wabwino ku chigawo cha Roma chimenecho.​—Machitidwe 16:9, 10.

Luso la Paulo losintha kuti agwirizane ndi kumaloko, linayesedwa kwambiri pamene anali kulalikira kwa Aatene. Chilamulo cha Agiriki ndi Aroma chinkaletsa kuphunzitsa za milungu yachilendo ndi miyambo yatsopano ya chipembedzo. Paulo kukonda kwake anthu kunamulimbikitsa kupenda bwinobwino ziphunzitso za chipembedzo chawo. Ku Atene anaona guwa la nsembe lolembedwa kuti “KWA MULUNGU WOSADZIŴIKA.” Anatchula zimenezi mu ulaliki wake. (Machitidwe 17:22, 23) Imeneyi inali njira yabwino kwambiri yoyambira uthenga wake mokoma mtima ndi mwaulemu.

Si mmene Paulo anasangalalira ataona zotsatira za ntchito yake monga mtumwi kwa amitundu. Anathandiza kukhazikitsa mipingo ya Akristu ambiri amene sanali achiyuda ku Korinto, Filipi, Tesalonika, ndi m’matauni a ku Galatiya. Anathandiza amuna ndi akazi achikhulupiriro, monga Damarisi, Dionisiyo, Sergio Paulo, ndi Tito. Unali mwayi waukulu  kuona anthu amene sankadziŵa n’komwe Yehova kapena Baibulo akuphunzira choonadi chachikristu. Paulo ponena za ntchito imene anagwira pothandiza anthu amene sanali Ayuda kuphunzira choonadi, anati: “Ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira uthenga wabwino, pamalopo Kristu asanatchulidwe kale, . . . koma monga kwalembedwa, iwo amene uthenga wake sunawafikire, adzaona, ndipo iwo amene sanamve, adzadziŵitsa.” (Aroma 15:20, 21) Kodi tingathandize nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu amene si achikhalidwe chathu?

Kuthandiza Anthu Onse a Dziko Lapansi

Solomo anapemphera kwa Yehova za amene sanali Aisrayeli, amene ankafika pa kachisi wa ku Yerusalemu kudzalambira. Anapempha kuti: ‘Mverani inu m’Mwamba mokhala inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziŵe dzina lanu.’ (1 Mafumu 8:41-43) Lerolino m’mayiko ambiri, anthu olengeza Ufumu ochuluka zedi akunena mawu ofananawo. Amakumana ndi anthu onga Anineve amene mwauzimu, ‘sadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.’ Ndipo olengeza Ufumu ndi atcheru kuthandiza kukwaniritsa maulosi okhudza kusonkhanitsa olambira oona kuchokera m’mitundu yosiyanasiyana.​—Yesaya 2:2, 3; Mika 4:1-3.

Monga mmene anthu a Matchalitchi Achikristu alandirira uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo, anthu azipembedzo zina akuchitanso chimodzimodzi. Kodi inuyo panokha, zimenezi ziyenera kukukhudzani motani? Dzipendeni nokha moona mtima. Ngati mukuona kuti tsankho linamera mizu mumtima mwanu, lichotseni mwa kukulitsa chikondi. * Musakane anthu amene Mulungu akufuna kuwalandira.​—Yohane 3:16.

Musanakalankhule anthu achikhalidwe china, muziyamba mwafufuza. Dziŵani zimene amakhulupirira, zimene zimawadetsa nkhaŵa, ndiponso momwe amaganizira. Ndiyeno fufuzani zimene mumafanana. Khalani wokoma mtima ndi wachifundo kwa ena. Peŵani mikangano, khalani wololera ndi wolimbikitsa. (Luka 9:52-56) Mukatero, mudzakondweretsa Yehova, “amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.”​—1 Timoteo 2:4.

Ndife osangalala kwambiri kuti m’mipingo yathu tili ndi anthu ambiri azikhalidwe zosiyanasiyana. (Yesaya 56:6, 7) Masiku ano zimasangalatsa zedi tikamamva mayina osati monga Mariya, Yohane, Stefano ndi Tomasi basi, komanso monga Mamadou, Jegan, Reza, ndi Chan. Ndithudi, ‘latitsegukira khomo lalikulu’ la ntchito. (1 Akorinto 16:9) Tiyeni tigwiritse ntchito mipata imene tili nayo kuuza ena zimene Yehova, Mulungu wopanda tsankho wanena, kulandira anthu amitundu yonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Onani Galamukani! ya July 8, 1996, masamba 5-7, “Makoma Opinga Kulankhulana.”

[Zithunzi patsamba 23]

Paulo anauza anthu uthenga wabwino kulikonse mwa kusintha kuti agwirizane ndi kumaloko

. . . ku Atene

. . . ku Filipi

. . . ali paulendo