Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wokhazikika

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wokhazikika

Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wokhazikika

“Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima.”​—SALMO 57:7.

1. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza mtima monga anachitira Davide?

YEHOVA angatithandize kukhala okhazikika m’chikhulupiriro chachikristu kuti timamatire ku chikristu choona monga atumiki ake odzipatulira. (Aroma 14:4) Motero, tingakhale otsimikiza mtima monga wamasalmo Davide amene anaimba kuti: “Wakhazikika mtima wanga, Mulungu.” (Salmo 108:1) Mtima wathu ukakhala wokhazikika, udzatilimbikitsa kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Mulungu. Ndipo ngati tipempha iye kuti atitsogolere ndi kutipatsa mphamvu, tingakhale olimba pa kutsimikiza mtima kwathu ndi chikhulupiriro chathu monga anthu okhulupirika, “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse.”​—1 Akorinto 15:58.

2, 3. Kodi malangizo a Paulo amene ali pa 1 Akorinto 16:13 akutanthauza chiyani?

2 Mtumwi Paulo polangiza otsatira a Yesu mu mpingo wakale wa Korinto, malangizo omwe akugwiranso ntchito kwa Akristu lerolino, anati: “Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.” (1 Akorinto 16:13) M’Chigiriki, mawu onseŵa akusonyeza kuti zimenezi ziyenera kuchitika mopitiriza. Kodi malangizo ameneŵa akutanthauza chiyani?

3 ‘Tingadikire’ mwauzimu mwa kutsutsa Mdyerekezi ndi kuyandikira kwa Mulungu. (Yakobo 4:7, 8) Kudalira Yehova kumatithandiza kukhalabe ogwirizana ndi ‘kuchirimika m’chikhulupiriro chachikristu.’ Ife​—kuphatikizapo akazi ambiri amene tili nawo limodzi​—‘timadzikhalitsa amuna’ mwa kutumikira Mulungu molimba mtima monga olengeza Ufumu. (Salmo 68:11) ‘Timalimbika’ mwa kupitiriza kupempha Atate wathu wakumwamba kuti atipatse mphamvu kuti tichite zimene iye amafuna.​—Afilipi 4:13.

4. Kodi tinachita chiyani kuti tibatizidwe monga Akristu?

4 Tinasonyeza kuti talandira choonadi pamene tinadzipatulira kotheratu kwa Yehova ndi kusonyeza zimenezo mwa kumizidwa m’madzi. Koma kodi tinachita chiyani kuti tibatizidwe? Choyamba, tinadziŵa zolondola za Mawu a Mulungu. (Yohane 17:3) Zimenezi zinabala chikhulupiriro ndipo zinatichititsa kulapa, kusonyeza kumva chisoni chifukwa cha zolakwa zimene tinachita m’mbuyomo. (Machitidwe 3:19; Ahebri 11:6) Kenako tinatembenuka, popeza tinasiya zoipa zimene tinkachita kuti titsatire zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:2; Aefeso 4:23, 24) Ndiyeno tinadzipatulira ndi mtima wonse kwa Yehova m’pemphero. (Mateyu 16:24; 1 Petro 2:21) Tinapempha Mulungu kuti atipatse chikumbumtima chabwino ndipo tinabatizidwa kusonyeza kuti tadzipatulira kwa iye. (1 Petro 3:21) Kukumbukira masitepe ameneŵa kudzatithandiza kuikabe mtima pa kufunika kopitiriza kuyesetsa kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu ndi kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wokhazikika.

Pitirizani Kufunafuna Chidziŵitso Cholondola

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kupeza chidziŵitso cha m’Malemba?

5 Tiyenera kupitiriza kupeza chidziŵitso cha m’Malemba cholimbitsa chikhulupiriro kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu kwa Mulungu. Zinalitu zosangalatsa kudya chakudya chauzimu titangodziŵa kumene choonadi cha Mulungu. (Mateyu 24:45-47) “Zakudya” zimenezo zinali zokoma ndipo zinatipatsa thanzi labwino lauzimu. Tsopano tifunika kupitiriza kudya chakudya chabwino chauzimu kuti tikhalebe ndi mtima wokhazikika monga atumiki odzipatulira a Yehova.

6. Kodi ayenera kuti anakuthandizani motani kuyamikira ndi mtima wonse choonadi cha Baibulo?

6 Tifunika kuyesetsa kuti tipeze chidziŵitso china cha m’Malemba. Kuli ngati kufunafuna chuma chobisika kumene kumafuna ntchito yaikulu. Komatu n’zopindulitsa kwambiri “kum’dziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:1-6) Pamene wofalitsa Ufumu anayamba kuphunzira nanu Baibulo, mwina anagwiritsa ntchito buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mwina pankatenga nthaŵi ndithu kuti mumalize mutu uliwonse, mwina munkaphunzira mutu umodzi maulendo angapo. Munapindula pamene munaŵerenga ndi kukambirana Malemba osagwidwa mawu. Ngati mfundo ina inali yovuta kuimvetsa, ankaifotokoza. Amene munkaphunzira naye Baibuloyo ankakonzekera bwino, kupempha mzimu wa Mulungu, ndiponso ankakuthandizani kuyamikira choonadi ndi mtima wonse.

7. Kodi n’chiyani chimamuyeneretsa munthu kuti aphunzitse choonadi cha Mulungu kwa ena?

7 Kuchita zimenezi kunali koyenera chifukwa Paulo analemba kuti: “Iye amene aphunzira mawu, ayenera kuchereza wom’phunzitsayo m’zonse zabwino.” (Agalatiya 6:6) Pano nkhaniyi m’Chigiriki imasonyeza kuti ziphunzitso za Mawu a Mulungu ankaziloŵetsa m’maganizo ndi mumtima mwa amene ‘akuphunzira mawuyo.’ Kuphunzitsidwa kwanu motero kumakuyeneretsani kuphunzitsa ena. (Machitidwe 18:25) Kuti mukhulupirike pa kudzipatulira kwanu, muyenera kukhalabe ndi thanzi lauzimu ndi kukhalabe wokhazikika mwa kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu.​—1 Timoteo 4:13; Tito 1:13; 2:2.

Kumbukirani Kulapa ndi Kutembenuka Kwanu

8. Kodi n’zotheka bwanji kukhalabe ndi khalidwe la Mulungu?

8 Kodi mukukumbukira mpumulo umene munaumva pamene munaphunzira choonadi, kulapa, ndiyeno kuona kuti Mulungu wakukhululukirani pamaziko a kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu? (Salmo 32:1-5; Aroma 5:8; 1 Petro 3:18) Mosakayika, simungafune kubwerera ku moyo wauchimo. (2 Petro 2:20-22) Mwa zina, kupemphera kwa Yehova nthaŵi zonse kudzakuthandizani kukhalabe ndi khalidwe la Mulungu, kukwaniritsa kudzipatulira kwanu, ndi kupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika.​—2 Petro 3:11, 12.

9. Popeza tinasiya ntchito zauchimo, kodi tiyenera kutsatira njira yotani?

9 Popeza munatembenuka mwa kusiya ntchito zauchimo, pitirizani kufunafuna thandizo la Mulungu kuti mukhalebe ndi mtima wokhazikika. Tinganene kuti munali kuyenda mumsewu wolakwika koma munayang’ana pa mapu odalirika ndi kuyamba kuyenda mumsewu wolondola. Tsonotu musapatuke pa njirayo. Pitirizani kudalira chitsogozo cha Mulungu ndipo tsimikizani mtima kukhalabe pa njira yopita ku moyo.​—Yesaya 30:20, 21; Mateyu 7:13, 14.

Musaiwale Kudzipatulira ndi Kubatizidwa Kwanu

10. Kodi tifunika kukumbukira mfundo ziti pankhani ya kudzipatulira kwathu kwa Mulungu?

10 Kumbukirani kuti munadzipatulira kwa Yehova m’pemphero, muli ndi maganizo akuti mudzam’tumikira mpaka kalekale. (Yuda 20, 21) Kudzipatulira kumatanthauza kudziika padera chifukwa cha zolinga zopatulika. (Levitiko 15:31; 22:2) Kudzipatulira kwanu sikunali pangano la kanthaŵi chabe ndipo simunadzipatulire kwa anthu. Munadzipatulira kosatha kwa Wolamulira Wachilengedwe chonse, ndipo kuti mukwaniritse kudzipatulirako mufunika kukhulupirikabe kwa Mulungu moyo wanu wonse. Inde, ‘kaya tikhala ndi moyo kapena tifa’ ndife ake a Yehova. (Aroma 14:7, 8) Tingakhale ndi chimwemwe ngati tigonjera pa zimene iye akufuna ndi kupitiriza kum’tumikira ndi mtima wokhazikika.

11. N’chifukwa chiyani muyenera kukumbukira ubatizo wanu ndi kufunika kwake?

11 Nthaŵi zonse kumbukirani ubatizo wanu wosonyeza kudzipatulira kwanu kwa Mulungu ndi mtima wonse. Sanakuumirizeni kubatizidwa, munasankha nokha. Kodi pakalipano ndinu wotsimikiza mtima kuchita chifuniro chanu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kwa moyo wanu wonse? Munapempha Mulungu kuti akupatseni chikumbumtima chabwino ndipo munabatizidwa posonyeza kuti mwadzipatulira kwa iye. Khalanibe ndi chikumbumtima chabwinocho mwa kukwaniritsa kudzipatulira kwanu, ndipo Yehova adzakudalitsani kwambiri.​—Miyambo 10:22.

Chifuniro Chanu Chimathandizira

12, 13. Kodi chifuniro chathu chikugwirizana motani ndi kudzipatulira ndiponso ubatizo?

12 Kudzipatulira ndi kubatizidwa kwapindulitsadi kwambiri anthu miyandamiyanda padziko lonse. Tikasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi, timafa pa zimene tinali kuchita kale koma chifuniro chathu chimakhalabe champhamvu. Ife monga anthu okhulupirira amene tinalangizidwa bwinobwino, tinasonyeza chifuniro chathu pamene tinadzipatulira kwa Mulungu m’pemphero ndi kubatizidwa. Kudzipatulira kwathu kwa Mulungu ndi kubatizidwa kumafuna kudziŵa kuti chifuniro cha Mulungu n’chiyani ndiyeno n’kusankha kuchichita. (Aefeso 5:17) Motero, timatsanzira Yesu amene anasonyeza chifuniro chake pamene anasiya ukalipentala, n’kubatizidwa, ndi kudzipereka kotheratu kuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba.​—Salmo 40:7, 8; Yohane 6:38-40.

13 Yehova Mulungu anakonza zoti Mwana wake adzakhala ‘wamphumphu mwa zowawa.’ Motero, Yesu anafunika kusonyeza chifuniro chake kuti apirire zowawa zimenezo mokhulupirika. Kuti akwaniritse zimenezo, iye anapereka “mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi . . . ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu.” (Ahebri 2:10, 18; 5:7, 8) Ngati ifenso tisonyeza kuopa Mulungu kom’patsa ulemu koteroko, tingatsimikize kuti ‘tidzamveka,’ ndiponso kuti Yehova adzatithandiza kukhala okhazikika monga Mboni zake zodzipatulira.​—Yesaya 43:10.

Mungakhalebe ndi Mtima Wokhazikika

14. N’chifukwa chiyani tifunika kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku?

14 Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhalabe ndi mtima wokhazikika ndiponso kukwaniritsa kudzipatulira kwanu kwa Mulungu? Ŵerengani Baibulo tsiku ndi tsiku n’cholinga choti mudziŵe zambiri za m’Mawu a Mulungu. Nthaŵi zonse, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatilimbikitsa kuchita zimenezi. Amapereka malangizo ameneŵa chifukwa choti tifunika kupitirizabe kuyenda m’choonadi cha Mulungu kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu. Gulu la Yehova likanakhala kuti linayambitsa ziphunzitso zonyenga mwadala, silikanalangiza kuti Mboni za Yehova ndiponso anthu amene zimawalalikira aziŵerenga Baibulo.

15. (a) Kodi tiyenera kuganizira chiyani posankha zochita? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolembedwa ndi ntchito yotsatira pambuyo?

15 Posankha zochita, nthaŵi zonse ganizirani mmene zikukhudzira kukwaniritsa kudzipatulira kwanu kwa Yehova. Zimenezi zingakhudze ntchito yolembedwa imene mukugwira. Kodi mumayesetsa kuchititsa ntchitoyo kukuthandizani kupititsa patsogolo kulambira koona? Ngakhale kuti olemba ntchito ambiri amaona kuti Akristu odzipatulira ali odalirika ndipo amagwira bwino ntchito, amaonanso kuti Mboni za Yehova sizikhumbira kwambiri kukhala zotsogola m’dzikoli ndipo sizilimbirana ndi anthu ena maudindo apamwamba. Izi zili choncho chifukwa chakuti cholinga cha Mboni sindicho kupeza chuma chambiri, kutchuka, udindo, kapena ulamuliro. Chinthu chofunika kwambiri kwa anthu amene akukwaniritsa kudzipatulira kwawo kwa Mulungu ndicho kuchita chifuniro chake. Ntchito yolembedwa imene imawathandiza kupeza zosoŵa pa moyo wawo ndi ntchito yotsatira pambuyo. Monga mtumwi Paulo, ntchito yawo yaikulu ndiyo utumiki wachikristu. (Machitidwe 18:3, 4; 2 Atesalonika 3:7, 8; 1 Timoteo 5:8) Kodi inu mumaika zinthu za Ufumu patsogolo?​—Mateyu 6:25-33.

16. Kodi tingatani ngati nkhaŵa zosayenera zikutilepheretsa kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Mulungu?

16 Ena mwina anathodwa ndi nkhaŵa zosiyanasiyana asanaphunzire choonadi. Koma mitima yawo inadzala chimwemwe, chiyamiko, ndi kukonda Mulungu pamene analandira chiyembekezo cha Ufumu. Kusinkhasinkha phindu limene apeza kuyambira nthaŵi imeneyo kungawathandize kukwaniritsa kudzipereka kwawo kwa Yehova. Komabe, bwanji ngati kudera nkhaŵa mavuto amene tikukumana nawo m’dongosolo lino kukuoneka kuti kutsamwitsa “mawu a Mulungu,” monga mmene minga imalepheretsera mbewu kuti zikule bwino ndi kubereka? (Luka 8:7, 11, 14; Mateyu 13:22; Marko 4:18, 19) Mukaona kuti zimenezi zikuyamba kukuchitikirani kapena kuchitikira banja lanu, tulani nkhaŵa zanu kwa Yehova ndi kum’pempha kuti akuthandizeni kukulitsa chikondi ndi kuyamikira. Mukamutulira nkhaŵa zanu, iye adzakuthandizani ndi kukupatsani nyonga kuti mupitirize kum’tumikira mwachimwemwe ndi mtima wokhazikika.​—Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7; Chivumbulutso 2:4.

17. Kodi zingatheke bwanji kupirira mayesero aakulu?

17 Pitirizani kupemphera kwa Yehova Mulungu nthaŵi zonse monga mmene munachitira podzipatulira kwa iye. (Salmo 65:2) Mukayesedwa kuti muchite choipa kapena mukakumana ndi mayesero aakulu, pemphani Mulungu kuti akutsogolereni ndi kukuthandizani kutsatira chitsogozo chake. Musaiwale kufunika kwa chikhulupiriro, pakuti wophunzira Yakobo analemba kuti: “Wina wa inu ikamsoŵa nzeru [kuti apirire mayesero], apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iŵiri akhala wosinkhasinka pa njira zake zonse.” (Yakobo 1:5-8) Ngati mayeserowo akuoneka kuti ndi onkitsa, tingatsimikize za mfundo iyi: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”​—1 Akorinto 10:13.

18. Kodi tingatani ngati tchimo limene tinabisa likufooketsa kutsimikiza mtima kwathu kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu kwa Yehova?

18 Bwanji ngati tchimo lalikulu limene munabisa likuvutitsa chikumbumtima chanu ndi kufooketsa kutsimikiza mtima kwanu kuti mukwaniritse kudzipatulira kwanu kwa Mulungu? Ngati mwalapa, kudziŵa kuti Yehova ‘sadzapeputsa mtima wosweka ndi wolapa’ kungakulimbikitseni. (Salmo 51:17) Funani thandizo kwa akulu achikondi, mukudziŵa kuti iwo potsanzira Yehova, sadzapeputsa kufuna kwanu kuti mukhalenso ndi ubwenzi wabwino ndi Atate wanu wa kumwamba. (Salmo 103:10-14; Yakobo 5:13-15) Ndiyeno mutapezanso nyonga yauzimu ndi mtima wokhazikika, mudzatha kuwongola mayendedwe anu ndipo mudzatha kukwaniritsa kudzipatulira kwanu kwa Mulungu.​—Ahebri 12:12, 13.

Pitirizani Kutumikira ndi Mtima Wokhazikika

19, 20. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kupitirizabe kukwaniritsa kudzipatulira kwathu?

19 Tiyenera kuyesetsa kukwaniritsa kudzipatulira kwathu ndi kupitiriza kutumikira Mulungu ndi mtima wokhazikika m’nthaŵi zovuta zino. Yesu anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Popeza tikukhala mu “masiku otsiriza,” mapeto angafike nthaŵi ina iliyonse. (2 Timoteo 3:1) Ndiponso, palibe amene angadziŵe kuti mawa adzakhala ali moyo. (Yakobo 4:13, 14) Motero n’kofunika kwambiri kukwaniritsa kudzipatulira kwathu lero!

20 Mtumwi Petro anatsindika zimenezi m’kalata yake yachiŵiri. Anasonyeza kuti monga mmene anthu osaopa Mulungu anawonongekera pa Chigumula, dziko lophiphiritsa, kapena anthu oipa adzawonongedwa pa “tsiku la Ambuye.” Motero Petro ananena kuti: “Muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo.” Ndiyeno anawalimbikitsa kuti: “Okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi [aphunzitsi onyenga ndi anthu osaopa Mulungu], mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.” (2 Petro 3:5-17) Zingakhaletu zomvetsa chisoni ngati munthu wobatizidwa asocheretsedwa ndiyeno n’kumwalira atalephera kukhalabe ndi mtima wokhazikika.

21, 22. Kodi mawu a pa Salmo 57:7 akhaladi oona motani kwa Davide ndi kwa Akristu oona?

21 Kutsimikiza mtima kwanu kupitirizabe kukwaniritsa kudzipatulira kwanu kwa Mulungu kungalimbe ngati simuiwala tsiku losangalatsa la ubatizo wanu ndiponso kupempha Mulungu kukuthandizani kuti zimene mumalankhula ndi kuchita zisangalatse mtima wake. (Miyambo 27:11) Yehova sakhumudwitsa anthu ake, ndipo mosakayika tiyenera kukhulupirikabe kwa iye. (Salmo 94:14) Anasonyeza chifundo ndi chisoni polepheretsa zolinga za adani a Davide ndi kum’landitsa iye. Poyamikira zimenezi, Davide analongosola mmene anam’kondera kwambiri Mlanditsi wakeyo. Anaimba ndi mtima wonse kuti: “Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.”​—Salmo 57:7.

22 Monga Davide, Akristu oona sanaleke kudzipatulira kwawo kwa Mulungu. Iwo, ndi mitima yokhazikika, amadziŵa kuti Yehova ndi amene wawalanditsa ndi kuwateteza ndipo amamuimbira zitamando mosangalala. Ngati mtima wanu uli wokhazikika, mudzadalira Mulungu, ndipo mothandizidwa ndi iye mudzatha kukwaniritsa kudzipatulira kwanu. Inde, mungakhale ngati “wolungama” amene wamasalmo anaimba za iye kuti: “Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.” (Salmo 112:6, 7) Mungakwaniritse kudzipatulira kwanu ndi kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wokhazikika ngati mukhulupirira Mulungu ndi kumudalira kotheratu.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kupeza chidziŵitso cholondola cha m’Baibulo?

• N’chifukwa chiyani tifunika kukumbukira kulapa ndi kutembenuka kwathu?

• Kodi kukumbukira kudzipatulira ndiponso ubatizo wathu kumatipindulitsa motani?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wokhazikika?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Kuona utumiki wachikristu kukhala ntchito yathu yaikulu kumatithandiza kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wokhazikika

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mukukhalabe ndi thanzi lauzimu mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku?