Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?

N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?

 N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?

“Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo.”​—Mateyu 28:19.

1, 2. (a) Kodi maubatizo ena achitika motani? (b) Kodi ndi mafunso ati amene afunsidwa pa nkhani ya ubatizo?

MFUMU ya Afulanki, Shalameni, inaumiriza anthu a mtundu wa Saxon amene anawagonjetsa kuti abatizidwe onse mu 775-77 C.E. Wolemba mbiri wina, John Lord, analemba kuti: “Anawaumiriza kutembenuka kuloŵa Chikristu cha dzina lokha.” Wolamulira wa ku Russia, Vladimir 1, atakwatira mfumukazi ya tchalitchi cha Greek Orthodox, anaganizanso chimodzimodzi kuti anthu ake onse akhale “Akristu.” Analamula kuti anthu onse abatizidwe ndipo okana kubatizidwa anali kuwaopseza kuti awapha.

2 Kodi maubatizo amenewo anali oyenera? Kodi ali ndi tanthauzo lenileni? Kodi ndi munthu aliyense amene angabatizidwe?

Kodi Ubatizo Uyenera Kuchitika Motani?

3, 4. Kodi n’chifukwa chiyani kuwaza kapena kuthira madzi pamutu suli ubatizo woyenerera wachikristu?

3 Pamene Shalameni ndi Vladimir 1 anaumiriza anthu kuti abatizidwe, olamulira ameneŵa anachita mosemphana ndi Mawu a Mulungu. Ndipotu, n’zopanda phindu ngati ubatizo wake ndiwo kuwaza madzi, kuthira madzi pamutu, kapena ngakhale kumiza anthu omwe sanaphunzitsidwe choonadi cha m’Malemba.

4 Tiyeni tione zimene zinachitika pamene Yesu wa ku Nazarete anapita kwa Yohane Mbatizi mu 29 C.E. Yohane anali kubatiza anthu mu mtsinje wa Yordano. Anthuwo anafuna okha kupita kwa iye kuti awabatize. Kodi anangowauza anthuwo kuima mu Yordano iye n’kumawathira madzi pang’ono a mu mtsinjewo pa mitu yawo kapena kuwawaza nawo? Kodi n’chiyani chinachitika pamene Yohane anabatiza Yesu? Mateyu ananena kuti “Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi.” (Mateyu 3:16) Iye analoŵa m’madzimo, anamizidwa mu mtsinje wa Yordano. N’chimodzimodzi ndi mdindo wodzipereka  wa ku Aitiopiya. Anabatizidwa mu “madzi akuti [“ambiri,” NW].” Madzi ambiri otero anali ofunika chifukwa maubatizo a Yesu ndi ophunzira ake anali omiza thupi lonse.​—Machitidwe 8:36.

5. Kodi Akristu oyambirira ankabatiza motani anthu?

5 Mawu a Chigiriki amene anawatembenuza kuti “batiza,” “ubatizo,” ndi ena otero, amatanthauza kumiza kapena kunyika m’madzi. Buku lotanthauzira mawu a m’Baibulo lakuti Smith’s Bible Dictionary limati: “Ubatizo moyenerera ndiponso m’tanthauzo lake lenileni ndiwo kumiza.” N’chifukwa chake mabaibulo ena amati “Yohane Womiza” ndiponso “Yohane wonyika.” (Mateyu 3:1, Rotherham; Diaglott, mawu achingelezi amene ali pakati pa mizere yachigiriki) Buku la Augustus Neander lakuti History of the Christian Religion and Church, During the Three First Centuries limati: “Poyambirira ubatizo unali kuchitika mwa kumiza.” Buku lotchuka la ku France lakuti Larousse du XXe Siècle (Paris, 1928) limati: “Akristu oyambirira anali kubatizidwa mwa kuwamiza kulikonse kumene madzi ankapezeka.” Ndiponso buku lakuti New Catholic Encyclopedia limati: “N’zodziŵikiratu kuti Ubatizo m’Tchalitchi choyambirira unali womiza.” (1967, Voliyumu II, tsamba 56) Motero masiku ano, kubatizidwa kuti ukhale wa Mboni za Yehova ndi chinthu chimene munthu amasankha yekha ndipo umakhala ubatizo womiza thupi lonse m’madzi.

Chifukwa Chatsopano Chobatizidwira

6, 7. (a) Kodi Yohane anali kubatiza n’cholinga chotani? (b) Kodi n’chiyani chinali chatsopano pa ubatizo wa otsatira a Yesu?

6 Cholinga cha maubatizo amene Yohane anali kuchita chinasiyana ndi maubatizo amene anali kuchita otsatira a Yesu. (Yohane 4:1, 2) Yohane anali kubatiza anthu monga chizindikiro chapoyera cha kulapa kwawo machimo ochimwira Chilamulo. * (Luka 3:3) Koma panali chinthu china chatsopano mu ubatizo wa otsatira a Yesu. Pa Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro anauza omvera ake kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu.” (Machitidwe 2:37-41) Ngakhale kuti Petro anali kulankhula kwa Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda, iye sanali kunena za ubatizo wosonyeza kulapa machimo ochimwira Chilamulo. Ndiponso sanatanthauze kuti kubatizidwa m’dzina la Yesu kunasonyeza kuyeretsa machimo.​—Machitidwe 2:10.

7 Nthaŵi imeneyo, Petro anagwiritsa ntchito “mafungulo a Ufumu” oyamba. Kodi cholinga chake chinali chiyani? Chinali chakuti avumbulire omvera ake za mwayi umene anali nawo woloŵa mu Ufumu wa kumwamba. (Mateyu 16:19) Popeza Ayuda anali atakana Yesu monga Mesiya, kulapa ndi kumukhulupirira chinali chinthu chatsopano ndiponso chofunika kwambiri pofuna kuti Mulungu awakhululukire. Akanachitira umboni poyera chikhulupiriro chimenecho mwa kumizidwa m’madzi m’dzina la Yesu Kristu. Mwakutero, iwo akanasonyeza kudzipatulira kwa Mulungu kudzera mwa Kristu. Anthu onse amene akufuna kuti Mulungu awayanje lerolino, ayenera kusonyeza chikhulupiriro ngati chimenechi, kudzipatulira kwa Yehova Mulungu, ndi kubatizidwa ubatizo wachikristu posonyeza kudzipatulira kwawo kotheratu kwa Mulungu Wam’mwambamwamba.

Kudziŵa Zolondola N’kofunika Kwambiri

8. N’chifukwa chiyani si munthu aliyense amene amayenerera ubatizo wachikristu?

8 Si munthu aliyense amene amayenerera ubatizo wachikristu. Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Anthu asanabatizidwe ayenera ‘kuphunzitsidwa kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamulira ophunzira ake.’ Motero, kubatiza moumiriza anthu amene analibe chikhulupiriro chozikidwa pa kudziŵa zolondola za Mawu a Mulungu n’kopanda phindu ndipo n’kosemphana ndi ntchito imene Yesu anapatsa otsatira ake.​—Ahebri 11:6.

9. Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate” kumatanthauza chiyani?

9 Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate” kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kuti wobatizidwayo  akuzindikira udindo ndi ulamuliro wa Atate wathu wakumwamba. Motero, amazindikira Yehova Mulungu kukhala Mlengi wathu, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” ndiponso Wolamulira wa Chilengedwe Chonse.​—Salmo 83:18; Yesaya 40:28; Machitidwe 4:24.

10. Kodi kubatizidwa ‘m’dzina la Mwana’ kumatanthauza chiyani?

10 Kubatizidwa ‘m’dzina la Mwana’ kumatanthauza kuzindikira udindo ndi ulamuliro wa Yesu monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. (1 Yohane 4:9) Amene amayenerera ubatizo amavomereza kuti Mulungu wapereka “dipo la anthu ambiri” kudzera mwa Yesu. (Mateyu 20:28; 1 Timoteo 2:5, 6) Ofuna kubatizidwa ayeneranso kuzindikira “udindo wapamwamba” umene Mulungu anakweza Mwana wake.​—Afilipi 2:8-11; Chivumbulutso 19:16.

11. Kodi kubatizidwa ‘m’dzina la mzimu woyera’ kumatanthauza chiyani?

11 Kodi kubatizidwa ‘m’dzina la Mzimu woyera’ kumatanthauza chiyani? Kumatanthauza kuti wofuna kubatizidwayo akuzindikira kuti mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova, imene amaigwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana mogwirizana ndi zolinga zake. (Genesis 1:2; 2 Samueli 23:1, 2; 2 Petro 1:21) Amene amayenerera ubatizo amazindikira kuti mzimu woyera umawathandiza kumvetsa “zakuya za Mulungu,” kuti achite ntchito yolalikira Ufumu, ndiponso kuti asonyeze chipatso cha mzimu cha “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.”​—1 Akorinto 2:10; Agalatiya 5:22, 23; Yoweli 2:28, 29.

Kufunika kwa Kulapa ndi Kutembenuka

12. Kodi ubatizo wachikristu umagwirizana motani ndi kulapa?

12 Ubatizo wa anthu onse kupatulapo wa Yesu yemwe analibe uchimo, ndiwo chizindikiro chimene Mulungu anachivomereza chomwe n’chogwirizana ndi kulapa. Tikalapa, timamva chisoni chachikulu chifukwa cha zimene tachita kapena zimene talephera kuchita. Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino amene anafuna kukondweretsa Mulungu anafunika kulapa machimo awo ochimwira Kristu. (Machitidwe 3:11-19) Akunja ena okhulupirira a ku Korinto analapa chifukwa cha chigololo, kulambira mafano, kuba, ndi machimo ena aakulu. Chifukwa cha kulapa kwawo, ‘anasambitsidwa’ m’mwazi wa Yesu; ‘anayeretsedwa’ kapena kupatulidwa, kuti atumikire Mulungu; ndipo ‘anayesedwa olungama’ m’dzina la Kristu ndi mwa mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Kulapa ndi sitepe lofunika kwambiri pofuna kupeza chikumbumtima chabwino ndi mpumulo umene Mulungu amapereka kuti timasuke ku uchimo.​—1 Petro 3:21.

13. Pa nkhani ya ubatizo, kodi kutembenuka kumafuna chiyani?

13 Tiyenera kutembenuka tisanabatizidwe kukhala Mboni za Yehova. Munthu amafuna yekha kutembenuka akasankha ndi mtima wonse kuti atsatire Kristu Yesu. Munthu wotero amasiya zochita zake zoipa zakale ndipo amatsimikiza mtima kuchita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti n’zabwino. M’Malemba, aneni a Chihebri ndi Chigiriki otanthauza kutembenuka ali ndi ganizo la kubwerera, kusiya. Kumasonyeza kusiya zoipa ndi kutembenukira kwa Mulungu. (1 Mafumu 8:33, 34) Kutembenuka kumafuna kuchita “ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20) Kumafuna kuti tisiye kulambira konyenga mmalo mwake kutsatira malamulo a Mulungu, ndi kulambira Yehova yekha basi. (Deuteronomo 30:2, 8-10; 1 Samueli 7:3) Kutembenuka kumatichititsa kusintha mmene tinkaganizira, zolinga zathu, ndiponso mtima wathu. (Ezekieli 18:31) ‘Timabwerera’ pamene umunthu watsopano uloŵa m’malo mwa makhalidwe oipa.​—Machitidwe 3:19; Aefeso 4:20-24; Akolose 3:5-14.

Kudzipatulira ndi Mtima Wonse N’kofunika Kwambiri

14. Kodi kudzipatulira kwa otsatira a Yesu kumatanthauza chiyani?

14 Ubatizo wa otsatira a Yesu uyeneranso kuchitika munthu atadzipatulira ndi mtima wonse kwa Mulungu. Kudzipatulira kumatanthauza kudziika padera chifukwa cha zolinga zopatulika. Sitepe limeneli n’lofunika kwambiri moti tiyenera kumuuza Yehova m’pemphero chosankha chathu chofuna kumulambira mosagawanika kunthaŵi zonse. (Deuteronomo 5:9) Ndipotu, kudzipatulira  kwathu sitinadzipatulire pa ntchito kapena kwa munthu koma kwa Mulungu.

15. N’chifukwa chiyani anthu ofuna kubatizidwa amawamiza m’madzi?

15 Tikadzipatulira kwa Mulungu kudzera mwa Kristu, timasonyeza kutsimikiza mtima kwathu kugwiritsa ntchito moyo wathu pochita zimene Mulungu amafuna zomwe zili m’Malemba. Ofuna kubatizidwa amawamiza m’madzi monga chizindikiro cha kudzipatulira koteroko monganso mmene Yesu anabatizidwira mu mtsinje wa Yordano monga chizindikiro cha kudzipereka kwake kwa Mulungu. (Mateyu 3:13) N’zochititsa chidwi kuti Yesu anali kupemphera pa nthaŵi yofunika kwambiri imeneyo.​—Luka 3:21, 22.

16. Kodi tingasangalale bwanji moyenera tikamaona anthu akubatizidwa?

16 Ubatizo wa Yesu sunali chinthu chamaseŵera komabe unali wosangalatsa. N’chimodzimodzinso ndi ubatizo wachikristu lerolino. Tikamaona anthu akusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu, tingasangalale mwa kuwomba m’manja mwaulemu ndi kuwayamikira mwachikondi. Koma timapewa kukuwa, kuimba malikhweru, ndi kuchita zina zofanana ndi zimenezi poganizira kuti kusonyeza chikhulupiro kumeneku n’kopatulika. Timasangalala mwaulemu.

17, 18. Kodi n’chiyani chimathandiza kuona ngati munthu akuyenerera ubatizo?

17 Mosiyana ndi amene amawaza madzi makanda kapena kuumiriza anthu amene sanaphunzire Malemba kuti abatizidwe, Mboni za Yehova siziumiriza munthu kuti abatizidwe. Ndipotu, izo sizibatiza munthu amene alibe ziyeneretso za Malemba. Munthu asanakhale wofalitsa uthenga wabwino wosabatizidwa, akulu achikristu amaonetsetsa kuti munthuyo akudziŵa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, akutsatira ziphunzitsozo, ndipo amayankha kuti inde funso lakuti, “Kodi mukufunadi kukhala Mboni ya Yehova?”

18 Nthaŵi zambiri, munthu akamagwira nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kufuna kubatizidwa, akulu achikristu amakambirana naye munthuyo kuti atsimikize kuti ndi wokhulupiriradi amene wadzipatulira kwa Yehova ndipo akukwanitsa ziyeneretso za Mulungu za ubatizo. (Machitidwe 4:4; 18:8) Akulu amaona ngati munthuyo akukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba kuti abatizidwe pamene ayankha yekha mafunso oposa 100 okhudza ziphunzitso za m’Baibulo. Ena sakwaniritsa ziyeneretsozo motero sawalola kubatizidwa.

Kodi Pali Chinachake Chimene Chikukulepheretsani?

19. Malinga ndi Yohane 6:44, kodi ndani amene adzalamulira limodzi ndi Yesu?

19 Anthu ambiri amene anawaumiriza kubatizidwa ayenera kuti anawauza kuti adzapita kumwamba akamwalira. Koma Yesu ponena za otsatira mapazi ake, anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Yehova wakokera kwa Kristu anthu 144, 000 amene adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa kumwamba. Kubatiza moumiriza sikunayeneretse wina aliyense kuti akakhale malo aulemerero amenewo m’makonzedwe a Mulungu.​—Aroma 8:14-17; 2 Atesalonika 2:13; Chivumbulutso 14:1.

20. Kodi n’chiyani chingathandize anthu amene sanabatizidwe mpaka pano?

20 Khamu la anthu amene akuyembekeza kudzapulumuka “chisautso chachikulu” ndi kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aloŵa nawo m’gulu la “nkhosa zina” za Yesu makamaka kuyambira pakati pa m’ma 1930. (Chivumbulutso 7:9, 14; Yohane 10:16) Amayenerera ubatizo chifukwa chakuti amatsatira Mawu a Mulungu pa zochita zawo ndipo amamukonda ndi ‘mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi mphamvu zawo zonse, ndi  nzeru zawo zonse.’ (Luka 10:25-28) Ngakhale kuti anthu ena amadziŵa kuti Mboni za Yehova ‘zimalambira Mulungu mumzimu ndi m’choonadi,’ sanatsatirebe chitsanzo cha Yesu ndi kusonyeza poyera umboni wa chikondi chenicheni ndi kulambira Yehova yekha mwa kubatizidwa. (Yohane 4:23, 24; Deuteronomo 4:24; Marko 1:9-11) Mapemphero ochokera pansi pa mtima ndiponso osapita m’mbali angawalimbikitse ndi kuwapatsa nyonga kuti atsatire Mawu a Mulungu, kudzipatulira kotheratu kwa Yehova Mulungu, ndi kubatizidwa.

21, 22. Kodi n’zifukwa ziti zimene zimalepheretsa ena kudzipatulira ndi kubatizidwa?

21 Ena sadzipatulira ndi kubatizidwa chifukwa chakuti atanganidwa kwambiri ndi zinthu za m’dzikoli kapena kufunafuna chuma kotero kuti alibe nthaŵi yokwanira yochita zinthu zauzimu. (Mateyu 13:22; 1 Yohane 2:15-17) Koma ngati akanasintha maganizo awo ndi zolinga zawo akanasangalalatu kwambiri. Kuyandikira kwa Mulungu kukanawalemeretsa mwauzimu, kukanawathandiza kuchepetsa nkhaŵa, ndiponso kukanawapatsa mtendere ndi chikhutiro zimene zimabwera ngati munthu achita chifuniro cha Mulungu.​—Salmo 16:11; 40:8; Miyambo 10:22; Afilipi 4:6, 7.

22 Ena amanena kuti amakonda Yehova koma sadzipatulira ndi kubatizidwa chifukwa amaganiza kuti kusadzipatulira kuwathandiza kupeŵa kukhala ndi udindo kwa Mulungu. Komatu tonsefe, aliyense payekha ayenera kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu. Tinalandira udindo titamva mawu a Yehova. (Ezekieli 33:7-9; Aroma 14:12) Aisrayeli akale monga ‘anthu osankhidwa,’ anabadwira mu mtundu wodzipatulira kwa Yehova ndipo motero anali ndi udindo womutumikira mokhulupirika mogwirizana ndi malamulo ake. (Deuteronomo 7:6, 11) Lerolino, palibe amene amabadwira mumtundu wodzipatulira kwa Yehova, koma ngati talandira malangizo olondola a m’Malemba, tifunika kuchitapo kanthu mwachikhulupiriro.

23, 24. Kodi ndi zinthu ziti zimene siziyenera kulepheretsa munthu kubatizidwa?

23 Ena angalephere kubatizidwa chifukwa chodzikayikira kuti sakudziŵa zambiri. Komatu, pali zambiri zoti tonsefe tiziphunzire chifukwa “palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11) Taganizani za mdindo wa ku Etiopia. Iye monga wotembenukira ku Chiyuda, ankadziŵa  Malemba koma sakanatha kuyankha mafunso onse okhudza zolinga za Mulungu. Komabe, ataphunzira za makonzedwe a Yehova a chipulumutso kudzera mu nsembe ya dipo ya Yesu, anabatizidwa m’madzi nthaŵi yomweyo.​—Machitidwe 8:26-38.

24 Ena amazengereza kudzipatulira kwa Mulungu chifukwa amaopa kuti sadzakwaniritsa kudzipatulira kwawo. Mtsikana wina wa zaka 17 dzina lake Monique anati: “Ndakhala ndikukayika zoti ndibatizidwe chifukwa choopa kuti sindidzatha kupitiriza kukwaniritsa kudzipatulira kwanga.” Komabe, ngati tikhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, ‘adzawongola mayendedwe athu.’ Adzatithandiza ‘kuyendabe m’choonadi’ monga atumiki ake odzipatulira okhulupirika.​—Miyambo 3:5, 6; 3 Yohane 4.

25. Kodi ndi funso liti limene lifunika kukambirana?

25 Kukhulupirira Yehova kotheratu ndi kumukonda ndi mtima wonse kumachititsa anthu ambirimbiri kudzipatulira ndi kubatizidwa chaka chilichonse. Ndipo n’zosachita kufunsa kuti atumiki odzipatulira a Mulungu onse amafuna kukhulupirika kwa iye. Komabe, tikukhala m’nthaŵi zowawitsa ndipo timakumana ndi mayeso a chikhulupiriro osiyanasiyana. (2 Timoteo 3:1-5) Kodi tingatani kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu kwa Yehova? Tikambirana funso limeneli m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Popeza Yesu alibe tchimo, ubatizo wake sunali chizindikiro cha kulapa machimo. Ubatizo wake unasonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu kuti achite chifuniro cha Atate wake.​—Ahebri 7:26; 10:5-10.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ubatizo wachikristu umachitika motani?

• Kodi munthu amene akufuna kubatizidwa ayenera kudziŵa chiyani?

• Kodi ndi masitepe ati amene amafunika kuti munthu ayenerere ubatizo wa Akristu oona?

• Kodi n’zinthu ziti zimene zimalepheretsa ena kubatizidwa, koma kodi angathandizidwe bwanji?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 14]

Kodi mumadziŵa tanthauzo la kubatizidwa ‘m’dzina la Atate, Mwana, ndi mzimu woyera’?