Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi mawu amene ali pa Ahebri 12:4 akuti: “Simunakana kufikira mwazi” akutanthauza chiyani?

Mawu akuti ‘kukana kufikira mwazi’ akusonyeza kupirira pokana ngakhale kufikira imfa, kukhetsa mwazi wamoyo m’lingaliro lenileni.

Mtumwi Paulo anadziŵa kuti chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Akristu achihebri ena anali ‘atapirira kale chitsutsano chachikulu cha zowawa.’ (Ahebri 10:32, 33) Pofotokoza mfundo imeneyo, Paulo akuoneka kuti anagwiritsa ntchito fanizo la kulimbana m’mipikisano ya masewero achigiriki, imene mwina ina mwa iyo inali mpikisano wothamanga, masewero ogwetserana pansi, masewero a nkhonya, ndi masewero oponya nthungo ndi thabwa lobulungira. Mogwirizana ndi zimenezi, pa Ahebri 12:1, iye analimbikitsa Akristu anzake kuti: ‘Titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.’

M’vesi lachinayi, pa Ahebri 12:4, Paulo ayenera kuti anasintha kuchoka pa mpikisano wothamanga kufika pa mpikisano wa nkhonya. (Pa 1 Akorinto 9:26 Paulo ananenapo za othamanga ndi a nkhonya omwe.) Akatswiri akale a nkhonya ankakulunga nkhonya ndi mfundo za manja awo ndi zingwe zachikopa. M’zingwemo muyeneranso kuti ankamangiriramo “mtovu kapena zitsulo, zimene zinkavulaza omenyanawo modetsa nkhaŵa.” Masewero oopsa ameneŵa ankachititsa omenyanawo kuchucha mwazi, ndipo nthaŵi zina kufa kumene.

Akristu achihebri anali ndi zitsanzo zambiri za atumiki okhulupirika a Mulungu amene anazunzidwa kwambiri ndiponso kuchitidwa nkhanza zosaneneka, ngakhale kuphedwa, “kufikira mwazi.” Onani nkhani imene Paulo anatchulamo zimene zinachitikira atumiki okhulupirika akale:

“Anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa.” Kenaka, Paulo anatchula za Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu kuti: “Anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”​—Ahebri 11:37; 12:2.

Inde, ambiri ‘anakana kufikira mwazi,’ kutanthauza kuti anakana kufikira imfa. Kukana kwawo sikunali kungolimbana ndi uchimo wa kusoŵa chikhulupiriro kwa m’kati chabe, ayi. Anakhulupirika pamene anachitidwa nkhanza zosaneneka. Anakhalabe okhulupirika mpaka imfa.

Akristu atsopano mumpingo wa ku Yerusalemu, amene mwina anakhala Akristu chizunzo chakale chankhanza chitatha, anali asanakumanepo ndi chiyeso chankhanza ngati chimenecho. (Machitidwe 7:54-60; 12:1, 2; Ahebri 13:7) Komabe, ena mwa iwo ziyeso zocheperapo zinali kuwafooketsa m’malo moti apitirize kulimbana. Anali ‘kulema ndi kukomoka m’moyo wawo.’ (Ahebri 12:3) Anafunika kupita patsogolo kuti akhwime mwauzimu. Zimenezi zikanawalimbitsa kuti athe kupirira chilichonse chimene chikanachitika, ngakhale kuti zimenezo zikanaphatikizapo kuzunzidwa mpaka kufa.​—Ahebri 6:1; 12:7-11.

Akristu ambiri m’nthaŵi zamakono ‘akana kufikira imfa,’ aphedwa chifukwa chakuti sanalolere kusiya Chikristu. M’malo mowopsedwa ndi mawu a Paulo amene ali pa Ahebri 12:4, tingawaone monga mawu osonyeza kuti tingakhale otsimikiza mtima kufika pati kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu. Kenako m’kalata yomweyo ya kwa Ahebri, Paulo analemba kuti: “Tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu mom’kondweretsa, ndi kum’chitira ulemu ndi mantha.”​—Ahebri 12:28.