Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusankha Mfundo za Chikhalidwe

Kusankha Mfundo za Chikhalidwe

Kusankha Mfundo za Chikhalidwe

KODI mumatsatira mfundo za makhalidwe abwino? Kapena kodi mumaona makhalidwe abwino kukhala achikale? Kunena zoona, aliyense amatsatira mfundo za chikhalidwe zinazake zomwe amakhulupirira kuti n’zofunika. Dikishonale ya The New Shorter Oxford English Dictionary, imamasulira mawu akuti mfundo za chikhalidwe kukhala “muyezo wa makhalidwe abwino wa munthu.” Mfundo za chikhalidwe zimasonkhezera zosankha zathu ndiponso zochita zathu m’moyo. Izo zili ngati kampasi.

Mwachitsanzo, Yesu analangiza otsatira ake kusunga Lamulo la Chikhalidwe lomwe lili pa Mateyu 7:12, lakuti: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” Anthu otsatira Confucius, amatsatira mfundo za chikhalidwe za li ndi jen zomwe zimatchula makhalidwe monga kukoma mtima, kudzichepetsa, ulemu, ndiponso kukhulupirika. Ngakhale anthu amene sapembedza ali ndi mfundo zomwe amakonda kutsatira pakhalidwe lawo.

Kodi Tizisankha Mfundo za Chikhalidwe Zotani?

Komabe, tiyenera kukumbukira kuti mfundo za chikhalidwe zitha kukhala zabwino kapena zoipa. Mwachitsanzo, anthu ambiri akuchita zinthu mosonkhezeredwa ndi mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense umene watchuka m’zaka pafupifupi khumi zapitazi. Ngakhale kuti ambiri sangadziŵe kuti kuli mzimuwu kapena mwina angaone kuti sukuwakhudza, mzimu umenewu ungakhudze aliyense amene sakutsatira mfundo zina za chikhalidwe. Choncho, ambiri amasiya miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino ndi kulola mzimu umenewu kuti uziwatsogolera. Kaya timaudziŵa ndi dzina kapena ayi, mzimuwu uli chizindikiro cha kudzikonda, kaŵirikaŵiri kophatikizana ndi kukonda chuma kwadyera. Mkulu wa wailesi yakanema ina ku China ananena kuti: “Tili ndi mfundo za chikhalidwe ziŵiri zokha basi. Yoyamba ndiyo kukwaniritsa chilakolako chofuna kugula zinthu, ndipo inayo ndi kupeza ndalama zochuluka.”

Mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense umakhala ngati maginito. Kodi maginito amatani ndi kampasi? Maginito akakhala pafupi ndi kampasi, muvi wa kampasiyo umasokonezeka n’kuloza kolakwika. N’chimodzimodzinso ndi mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense. Mzimuwu ungasokoneze kampasi ya munthu ya makhalidwe abwino mwa kuchititsa chilichonse chomwe n’chosafunika kwenikweni kukhala chomwe munthuwe ukuchilakalaka kwambiri.

Kodi mungadabwe kumva kuti mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense sunayambe lero? Kutsatira mzimu umenewu kunayambira m’munda wa Edene pamene makolo athu oyamba anasiya miyezo ya chikhalidwe yomwe Mlengi wathu anakhazikitsa. Zimenezi zinasintha kampasi yawo ya makhalidwe abwino. Monga mbadwa za Adamu ndi Hava, anthu amavutika ndi mzimu womwewu “wofuna kukhala patsogolo pa aliyense.”​—Genesis 3:6-8, 12.

Kufala kwa mzimu umenewu kukuonekera bwino kwambiri masiku ano omwe ulosi wa m’Baibulo umawatcha “masiku otsiriza” odziŵika ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Anthu ambiri ali “odzikonda okha.” N’zosadabwitsa kuti timavutika kwambiri kulimbana ndi mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense umenewu.​—2 Timoteo 3:1-5.

Mwina mukuvomerezana ndi mnyamata wina dzina lake Olaf yemwe analembera ku nthambi ina ya Mboni za Yehova ya ku Ulaya kuti: “N’kovuta kwambiri kukhalabe ndi makhalidwe abwino makamaka kwa ife achinyamata. Chonde pitirizani kumatikumbutsa kufunika kotsatira kwambiri mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo.”

Olaf anasonyeza maganizo anzeru. Mfundo za chikhalidwe za Mulungu zingatithandize tonsefe, achinyamata ndi achikulire omwe, kuti titsatire miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino. Kaya mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense timaudziŵa ndi dzina kapena ayi, mfundo za chikhalidwe zimenezi zingatithandize kuukana. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri zokhudza mmene mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo zingakuthandizireni, ŵerengani nkhani yotsatirayi mofatsa.

[Zithunzi patsamba 4]

Anthu ambiri masiku ano saganizira zomwe ena amafuna