Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Malo Obisalirako Mphepo

Malo Obisalirako Mphepo

 Malo Obisalirako Mphepo

PAMWAMBA pa mapiri a Alps ku Ulaya, pamamera zitsamba zolimba zimene amazitcha maluŵa a kuphiri. Nthaŵi zambiri, maluŵa ameneŵa omwe amakhala aafupi, amamera m’zitsamba zambiri zounjikana zimene zimakangamira ku nthaka kuti zitetezeke ku mphepo yamkuntho ya kumapiriko. Zomera za kumapiri zimavutika kuti zikhale ndi moyo chifukwa cha mphepo yosalekeza imene imawomba kumeneko. Mphepoyo imaziziritsa kwambiri, kuumitsa mpweya ndi nthaka, ndiponso imazula zomerazo.

Nthaŵi zambiri, maluŵa a kuphiriŵa amapulumuka ku mphepo yamkunthoyi mwa kumera m’ming’alu ya miyala. Ngakhale kuti dothi m’malo amenewo lingakhale lochepa, ming’aluyi imateteza maluŵawo ku mphepo ndiponso imawathandiza kuti asunge madzi. Kwa miyezi yambiri, maluŵawo saoneka, koma m’chilimwe amakongoletsa mapiriwo ndi maluŵa ofiira owala kwambiri.

Mneneri Yesaya anafotokoza kuti Mulungu adzaika “akalonga” ndipo kalonga aliyense adzakhala “pobisalira mphepo.” (Yesaya 32:1, 2) Akalonga kapena oyang’anira ameneŵa, motsogozedwa ndi Mfumu, Kristu Yesu, adzakhala ngati miyala yokhazikika, yosasunthika m’nthaŵi za nkhaŵa kapena nsautso. Adzakhala pothaŵirapo podalirika m’nthaŵi za mavuto ndi kuthandiza amene akuvutika kuti ateteze madzi awo auzimu amene anasungira ochokera m’Mawu a Mulungu.

Mphepo ya chizunzo, kutaya mtima, ndi matenda ingakanthe Mkristu mobwerezabwereza ndi kuchititsa chikhulupiriro chake kufota. Akulu achikristu angateteze mwa kumvetsera mwatcheru pamene munthuyo akufotokoza vuto lake, kum’patsa malangizo ozikidwa m’Baibulo, ndi kum’limbikitsa kapena kum’thandiza mogwira mtima. Akulu, mofanana ndi mfumu yawo yoikidwa, Kristu Yesu, amafuna kuthandiza anthu amene ‘amwazikana.’ (Mateyu 9:36) Ndiponso amafuna kuthandiza anthu amene awonongedwa ndi mphepo ya chiphunzitso chonyenga. (Aefeso 4:14) Thandizo limenelo panthaŵi yoyenera lingakhale lofunika kwambiri.

Mlongo wina dzina lake Miriam anafotokoza kuti: “Ndinavutika maganizo kwambiri pamene anzanga apamtima anasiya choonadi ndiponso, panthaŵi yomweyo, bambo anga anadwala matenda a kukha mwazi muubongo. Pofuna kuthetsa kuvutika maganizoko, ndinayamba chibwenzi ndi mnyamata wakudziko. Nditangochita kumene zimenezi, ndinadziona kukhala wopanda pake, ndipo ndinauza akulu mumpingo kuti ndinaganiza zosiya choonadi, chifukwa ndinaona kuti Yehova sakanandikondanso.

“Panthaŵi yovuta imeneyi, mkulu wina wachifundo anandikumbutsa za zaka zimene ndinakhala ndikuchita upainiya wokhazikika. Anandiuza kuti iye nthaŵi zonse anali kuyamikira kukhulupirika kwanga, ndipo anandipempha mokoma mtima kuti ndilole akulu andithandize, kuti anditsimikizire kuti Yehova amandikonda. Nkhaŵa yawo yachikondi panthaŵi yovuta imeneyo inali ngati ‘pobisalirapo’ panga pamene mkuntho wauzimu unali kundivutitsa. Mwezi usanathe, ndinathetsa chibwenzi ndi mnyamata uja, ndipo ndakhala ndikuyenda m’choonadi kuyambira nthaŵi imeneyo.”

Akulu amasangalala akamaona Akristu anzawo akupita patsogolo mwauzimu chifukwa cha kuwateteza panthaŵi imene anafunikira kutero. Ndipo ‘malo obisalirako’ ameneŵa akutipatsa chithunzi cha thandizo lauzimu lochuluka limene tidzakhala nalo mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi.