Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo za Chikhalidwe za Mulungu Zingakupindulitseni

Mfundo za Chikhalidwe za Mulungu Zingakupindulitseni

 Mfundo za Chikhalidwe za Mulungu Zingakupindulitseni

MOSAKAYIKIRA inuyo mumadziŵa kuti nyama zimatsatira chibadwa pochita zinthu. Makina ambiri amapangidwa kuti azitsatira malangizo. Koma anthu analengedwa kuti azitsatira mfundo za chikhalidwe. Kodi mungatsimikize bwanji zimenezi? Eya, pamene Yehova, Woyambitsa wa mfundo zonse za chikhalidwe zolungama ankalenga munthu woyamba, anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.” Mlengi ndi mzimu; ndipo alibe thupi lanyama ngati lathuli. Choncho, tili “m’chifanizo” chake mu lingaliro lakuti titha kusonyeza umunthu wake ndiponso makhalidwe ake abwino. Anthu angawongolere miyoyo yawo mogwirizana ndi mfundo za chikhalidwe. Izi zikutanthauza kuti atha kuwongolera miyoyo yawo mogwirizana ndi mfundo za chikhalidwe zomwe akukhulupirira kuti n’zoyenera. Yehova analemba zambiri mwa mfundo zimenezi m’Mawu ake.​—Genesis 1:26; Yohane 4:24; 17:17.

 Ena anganene kuti, ‘m’Baibulo muli mfundo za chikhalidwe zambirimbiri ndipo sindingathe kuzidziŵa zonse.’ Zimenezo n’zoona. Komabe, taganizirani mfundo iyi: Ngakhale kuti mfundo zonse za chikhalidwe za Mulungu n’zopindulitsa, zina n’zofunika kwambiri kuposa zina. Mungaone zimenezi kuchokera pa Mateyu 22:37-39, pamene Yesu anasonyeza kuti malamulo ndiponso mfundo za chikhalidwe za m’Chilamulo cha Mose zinali zosiyanasiyana, zina zinali zofunika kwambiri kuposa zina.

Kodi mfundo za chikhalidwe zofunika kwambiri ndi ziti? Mfundo zofunika kwambiri za m’Baibulo ndi zimene zimakhudza mwachindunji ubale wathu ndi Yehova. Ngati titatsatira mfundo zimenezo ndiko kuti Mlengi ndiye aziwongolera kampasi yathu ya makhalidwe abwino. Komanso, pali mfundo zomwe zimakhudza ubale wathu ndi anthu ena. Kutsatira mfundo zimenezi kudzatithandiza kukana mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense, mulimonse mmene angautchulire.

Tiyeni tiyambe ndi imodzi mwa mfundo za choonadi zofunika kwambiri zopezeka m’Baibulo. Kodi mfundo ya choonadi imeneyi n’chiyani ndipo kodi imatikhudza motani?

“Wam’mwambamwamba pa Dziko Lonse Lapansi”

Malemba Opatulika amanena mosapita m’mbali kuti Yehova ndiye Mlengi wathu Wamkulu, Mulungu Wamphamvuyonse. Iye sangafanane ndi wina aliyense kapena kuloŵedwa m’malo. Imeneyi ndi mfundo ya choonadi yofunika kwambiri yomwe ili m’Baibulo.​—Genesis 17:1; Mlaliki 12:1.

M’modzi wa anthu omwe analemba buku la Masalmo ananena za Yehova kuti: “Ndinu [nokha] Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Mfumu yakale Davide analemba kuti: “Ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.” Ndipo mneneri wotchukayo Yeremiya anasonkhezereka kulemba kuti: “Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.”​—Salmo 83:18; 1 Mbiri 29:11; Yeremiya 10:6.

Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito motani mfundo za choonadi zimenezi zonena za Mulungu m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.

N’zoonekeratu kuti Mlengi wathu ndiponso Wotipatsa Moyo ndiye ayenera kukhala wofunika kwambiri pa moyo wathu. Ndiyeno, kodi sizingakhale zomveka kukana chizoloŵezi chilichonse chofuna kudziona monga wofunika kwambiri, chomwe chingakhale champhamvu kwambiri kwa ena kuposa ena? Mfundo yanzeru yofunika kuitsatira n’njakuti, “chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Mneneri Danieli anali chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi.

Nkhani yamakedzana imatiuza kuti Mfumu Nebukadinezara ya Babulo nthaŵi ina inavutika maganizo kwambiri ndi loto ndipo inafuna kudziŵa tanthauzo lake. Ena onse atalephera kudziŵa tanthauzo la lotolo, Danieli molondola anauza mfumuyo zomwe inkafuna kudziŵazo. Kodi Danieli anatamandidwa chifukwa cha zimenezi? Ayi, iye anapereka ulemerero wonse kwa “Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi.” Danieli anapitiriza kunena kuti: “Chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo.” Danieli anali munthu wotsatira mfundo za chikhalidwe. Mpake kuti katatu m’buku la Danieli, iye amatchedwa kuti ‘wokondedwa kwambiri’ kwa Mulungu.​—Danieli 2:28, 30; 9:23; 10:11, 19.

Mudzapindula kwambiri ngati mutatsanzira Danieli. Potsanzira chitsanzo cha Danieli mtima wanu ndiwo ukuchititseni zimenezo. Kodi ndani ayenera kulandira ulemu pa zomwe m’machita? Kaya ndinu wotani, mungachite zinthu mogwirizana ndi  mfundo yofunika ya m’Baibulo yakuti, Yehova ndiye Ambuye Mfumu. Kutsatira mfundo imeneyi kudzakuchititsani kukhala ‘wokondedwa kwambiri’ kwa iye.

Tiyeni tsopano tione mfundo zikuluzikulu ziŵiri zomwe zingatitsogolere pankhani zokhudza ubale wa anthu. M’dziko lino mmene kudzikonda kuli kofala kwambiri, nkhani ya ubale wa anthu n’njovuta kwambiri.

“Kudzichepetsa Mtima”

Anthu amene amafuna kukhala oyamba nthaŵi zonse, kaŵirikaŵiri sakhala okhutira. Ambiri amafuna moyo wabwinopo nthaŵi zonse, ndipo amaufuna nthaŵi yomweyo. Kwa iwo, kukhala moyo wosafuna zambiri amati n’kufooka. Kuleza mtima amati ndi khalidwe loyenera anthu ena osati iwo. Ikakhala nkhani yofuna kukhala wotsogola, chilichonse amati n’chovomerezeka. Kodi mukuganiza kuti pali zina zomwe mungasankhe kuchita zosiyana ndi zimenezi?

Atumiki a Mulungu amakumana ndi mzimu umenewu tsiku ndi tsiku, koma suyenera kuwakhudza. Akristu okhwima amavomereza mfundo ya chikhalidwe yakuti “Si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye am’tama ali wovomerezeka.”​—2 Akorinto 10:18.

Kutsatira mfundo ya makhalidwe abwino yopezeka pa Afilipi 2:3, 4 kudzathandiza kwambiri. Lembali limalimbikitsa kuti “musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake om’posa iye mwini.” Kotero kuti “munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”

Munthu wina yemwe anali kudziona moyenera ndiponso yemwe anali kudzipatsa ulemu woyenerera  anali Gideoni, woweruza wa Ahebri akale. Iye sanachite kufuna kuti akhale m’tsogoleri wa Israyeli. Komabe, atasankhidwa kuti akhale paudindowu, Gideoni anadziona wopereŵera. Iye anati: “Banja langa lili loluluka m’Manase, ndipo ine ndine wamng’ono m’nyumba ya atate wanga.”​—Oweruza 6:12-16.

Komanso, Yehova atamuchititsa Gideoni kupambana nkhondo, amuna a Efraimu anakangana naye. Kodi Gideoni anatani? Kodi kupambana kwakeko kunam’chititsa kudziona monga wopambana kuposa ena? Ayi ndithu. Anapeŵa vuto lalikulu mwa kuyankha modekha. Anati: “Ndachitanji tsopano monga inu?” Ndithudi, Gideoni anali ‘wodzichepetsa mtima.’​—Oweruza 8:1-3.

N’zoona kuti nkhani ya Gideoni inachitika kalekale. Komabe, kupendanso nkhani imeneyi n’kopindulitsa kwambiri. Mutha kuona kuti Gideoni anali ndi mzimu wosiyana kwambiri ndi umene wafala masiku ano ndipo anapindula mwa kutsatira mzimu wabwinowo pa moyo wake.

Mzimu wofalawu wongoganizira zako zokha ungawononge maganizo athu pankhani ya kufunika kwathu. Mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo zimawongolera maganizo amenewo, ndipo zimatiphunzitsa kufunika kwathu koyenerera mogwirizana ndi Mlengi ndiponso anthu ena.

Mwa kutsatira mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo timagonjetsa mzimu wofuna kukhala patsogolo pa aliyense. Sititsogozedwanso ndi thupi lathu kapena mtima wathu. Pamene tikuphunzira zambiri zokhudza mfundo za chikhalidwe zolungama m’pamenenso timadziŵana kwambiri ndi Woyambitsa wake. Inde, mpake kumakhala ndi chidwi chapadera ndi mfundo za chikhalidwe za Mulungu pamene tikuŵerenga Baibulo.​—Onani bokosi.

Yehova anachititsa anthu kukhala apamwamba kuposa nyama zimene zimachita zinthu motsatira chibadwa. Kutsatira zomwe Mulungu amafuna kumafuna kugwiritsa ntchito mfundo zake za chikhalidwe. Tikatero ndiye kuti kampasi yathu ya makhalidwe abwino izigwira bwino ntchito yake. Ndipo kampasi yoteroyo idzatitsogolera kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Baibulo limatipatsa chifukwa choyembekezera kuti posachedwapa dziko lapansi latsopano ‘mmene mukhalitsa chilungamo’ lidzafika.​—2 Petro 3:13.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Mfundo Zina za Chikhalidwe Zothandiza za m’Baibulo

M’banja:

“Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”​—1 Akorinto 10:24.

“Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha.”​—1 Akorinto 13:4, 5.

“Yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha.”​—Aefeso 5:33.

“Akazi inu, muzimvera amuna anu.”​—Akolose 3:18.

“Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.”​—Miyambo 23:22.

Ku sukulu, ku ntchito, ku bizinesi:

“Muyeso wonyenga unyansa . . . Woipa alandira malipiro onyenga.”​—Miyambo 11:1, 18.

“Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito.”​—Aefeso 4:28.

“Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.”​—2 Atesalonika 3:10.

“Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye.”​—Akolose 3:23.

“Tikufuna kukhala oona mtima m’zonse.”​—Ahebri 13:18, NW.

Mmene timaonera chuma:

“Wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.”​—Miyambo 28:20.

“Wokonda siliva sadzakhuta siliva.”​—Mlaliki 5:10.

Kudzipezera ulemu:

“Kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.”​—Miyambo 25:27.

“Wina akutame, si m’kamwa mwako ai.”​—Miyambo 27:2.

“Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.”​—Aroma 12:3.

“Ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.”​—Agalatiya 6:3.

[Chithunzi patsamba 5]

Danieli moyenerera anapereka ulemu wonse kwa Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Kuchita ndi ena mogwirizana ndi mfundo za chikhalidwe za Mulungu kumachititsa ubale kukhala wosangalatsa ndiponso kumapatsa chimwemwe

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​Robert Bridges