Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubwino wa Mtima Wopatsa

Ubwino wa Mtima Wopatsa

Mayi wina dzina lake Alexandra anakwera basi yopita m’dziko lina la ku South America. Atafika paboda anamva wapolisi akunena kuti: “Basiyi ikhoza kumapita koma Mtchainayu atsale.” Alexandra anatsika kuti aone zimene zinkachitika. Ndiye anapeza munthu wa ku China akulephera kufotokozera bwinobwino wapolisiyo vuto lake m’Chisipanishi. Popeza Alexandra anaphunzira Chitchainizi kuti athandize mumpingo wachitchainizi wa Mboni za Yehova, anapempha kuti athandize kumasulira zimene munthuyo ankanena.

Munthu wa ku Chinayo ananena kuti ali ndi mapepala omuvomereza kukhala m’dzikolo koma vuto ndi loti athu ena anamubera ndalama komanso mapepalawo. Poyamba, wapolisiyo sankakhulupirira zimene munthuyo ankanena ndipo anayamba kuganiza kuti Alexandra amapanga bizinezi yogulitsa anthu. Kenako anavomereza zimene munthuyo ananena koma anati ayenera kupereka chindapusa chifukwa chosakhala ndi mapepala akewo. Popeza analibenso ndalama, Alexandra anamubwereka madola 20. Munthuyo anathokoza kwambiri ndipo analonjeza kuti adzamubwezera ndalama zoposa madola 20. Alexandra ananena kuti safuna kupatsidwa ndalama zowonjezera chifukwa iye amaona kuti ndi bwino kuthandiza anthu amene ali pa mavuto. Anapatsa munthuyo mabuku othandiza pophunzira Baibulo n’kumuuza kuti ayambe kuphunzira ndi Mboni za Yehova.

Zimasangalatsa kwambiri tikamva za anthu amene athandiza anthu achilendo. Mosakayikira anthu azipembedzo zosiyanasiyana ngakhalenso amene alibe chipembedzo amachitanso zimenezi. Kodi mukanakhala inuyo mukanadzipereka kuti muthandize munthuyo? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa chakuti Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Asayansi nawonso amanena kuti kupatsa kumathandiza kwambiri anthu. Koma kodi kumathandiza bwanji?

MUNTHU WOPATSA AMAKHALA WOSANGALALA

Nthawi zambiri munthu amene amakonda kupatsa amakhala wosangalala. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Iye ankanena za Akhristu amene ankapereka zinthu mowolowa manja kuti athandize Akhristu anzawo amene anakumana ndi mavuto. (2 Akorinto 8:4; 9:7) Koma Paulo sankatanthauza kuti kusangalala n’kumene kunachititsa anthuwo kuti apereke. M’malomwake ankatanthauza kuti ankakhala osangalala chifukwa choti anali ndi mtima wopatsa.

Anthu ena atachita kafukufuku anapeza zimene zimachitika munthu akapatsa mnzake kanthu. Anapeza kuti zimenezi zimakhudza mbali ina ya ubongo wake yomwe imachititsa kuti munthu azimva bwino mumtima, azicheza bwino ndi anthu, azikhulupirira ena ndipo zonsezi zimachititsa kuti azikhala wosangalala. Kafukufuku wina anasonyeza kuti kupatsa munthu wina ndalama kumathandiza woperekayo kukhala wosangalala kuposa mmene amamvera akazigwiritsa ntchito yekha.

Kodi munayamba mwadandaulapo chifukwa choti mulibe zinthu zambiri zimene mungapatse ena? Koma zoona zake n’zakuti aliyense angakhale ndi mtima wopatsa n’kumasangalala. Tikapereka zinthu tili ndi zolinga zabwino, zilibe kanthu kuti zimene tikupereka ndi zambiri kapena ayi. Wa Mboni za Yehova wina anatumiza ndalama kwa ofalitsa magaziniyi ndipo m’kalata yake anati: “Kwa zaka zambiri ndakhala ndikungopereka ndalama zochepa kwambiri ku Nyumba ya Ufumu.” Kenako anati: “Yehova Mulungu wandibwezera zambiri kuposa zimene ndapereka. . . . Ndikuthokoza kwambiri kuti mwandilola kuti ndipereke mphatsoyi chifukwa zikundithandiza kukhala wosangalala.”

Koma tikhoza kusonyeza mtima wopatsa m’njira zambiri osati kungopereka ndalama basi.

KUPATSA KUNGATHANDIZE KUTI MUKHALE ATHANZI

Kuchita chifundo kumathandiza inuyo komanso anthu ena

Baibulo limanena kuti: “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake, koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.” (Miyambo 11:17) Munthu wokoma mtima amafunitsitsa kugwiritsa ntchito zinthu zake, nthawi yake komanso mphamvu zake kuti athandize ena. Zimene amachitazi zimamuthandiza m’njira zambiri ndipo imodzi mwa njirazo ndi yoti zimathandiza kuti akhale wathanzi.

Kafukufuku wina anasonyeza kuti munthu amene amathandiza ena amachepetsa ululu umene amamva m’thupi komanso nkhawa zimene amakhala nazo. Mwachidule tingati amakhala wathanzi kuposa anthu oumira. Mtima wopatsa umathandizanso ngakhale anthu amene akudwala matenda aakulu monga edzi. Zikuonekanso kuti anthu amene akufuna kusiya kumwa mowa amakhala osangalala akamathandiza ena ndipo salakalaka kwambiri kumwa mowawo.

Pofotokoza zimene zimachititsa, anthu amanena kuti mtima wachifundo komanso wofuna kuthandiza ena umathandiza kuti tisamaganizire zinthu zokhumudwitsa. Mtima wopatsa ungathandizenso munthu kuti asamade nkhawa komanso asakhale ndi vuto lothamanga magazi. Ngakhale anthu amene mwamuna kapena mkazi wawo wamwalira amayamba kumva bwino ngati akuthandiza ena.

Choncho n’zosachita kufunsa kuti mtima wopatsa ndi wothandiza kwambiri.

MUKAKHALA OPATSA, ENA AMAYAMBANSO KUPATSA

Yesu ananena kuti: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.” (Luka 6:38) Mukapatsa anthu zinthu zinazake, amayamikira kwambiri ndipo nawonso amapatsa ena zinthu. Izi zikusonyeza kuti mtima wopatsa umathandiza kuti anthu azigwirizana.

Mtima wopatsa umathandiza anthu kuti azigwirizana

Kafukufuku wina anasonyezanso kuti “anthu amene amakonda kuthandiza anzawo amachititsa kuti anthu ena azichitanso zomwezo.” Ndipotu “munthu akangowerenga nkhani za anthu amene anathandiza kwambiri anzawo angalimbikitsidwe kuti nayenso akhale ndi mtima wopatsa.” Kafukufuku winanso anasonyeza kuti “munthu aliyense amene amapatsa zinthu anzake amathandiza anthu ambirimbiri kuti akhalenso ndi mtima wopatsa. Ena mwa anthuwo amakhala oti sakuwadziwa ndipo mwina sanakumanepo nawo.” Mwachidule tingati anthu amatha kupatsirana mtima wopatsa. Kodi inuyo simungakonde kukhala m’dera la anthu opatsa okhaokha? Kunena zoona, zinthu zikhoza kumayenda bwino ngati anthu ambiri ali ndi mtima wopatsa.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika ku Florida m’dziko la United States. A Mboni za Yehova anadzipereka kuti akathandize anthu amene anali pa mavuto chifukwa cha mphepo yamkuntho. Podikira zipangizo zoti agwiritse ntchito pokonza nyumba inayake, anaona kuti mpanda wa munthu wina wawonongeka ndipo anamuthandiza kuukonza. Munthuyo analemba kalata yopita kulikulu la Mboni za Yehova ndipo m’kalatayo ananena kuti: “Ndikuthokoza kwambiri. Anthu amene anandithandizawo ndi achifundo kwambiri.” Chifukwa choyamikira, anatumiza ndalama zambiri n’kunena kuti zithandize pa ntchito yaikulu imene a Mboni akugwira.

TSANZIRANI MULUNGU PA NKHANI YOPATSA

Asayansi anapeza kuti “anthufe timabadwa ndi mtima wofuna kuthandiza ena.” Anapezanso kuti ana “amakonda kuthandiza ena ngakhale asanayambe kulankhula.” Baibulo limafotokoza chifukwa chake zili choncho. Limanena kuti anthu analengedwa “m’chifaniziro” cha Mulungu, kapena kuti analengedwa ndi makhalidwe ofanana ndi ake.—Genesis 1:27.

Khalidwe lina labwino limene Yehova Mulungu ali nalo ndi kuwolowa manja. Iye watipatsa moyo komanso zinthu zonse zofunika kuti tikhale osangalala. (Machitidwe 14:17; 17:26-28) Tingadziwe Atate wathu wakumwamba komanso zinthu zabwino zimene watikonzera tikamaphunzira Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. Baibulo limafotokozanso zimene Mulungu wachita kuti tidzakhale ndi tsogolo labwino. * (1 Yohane 4:9, 10) Popeza kuti Mulungu ndi wowolowa manja ndipo ife tinalengedwa m’chifaniziro chake, n’zosadabwitsa kuti tikamatsanzira mtima wake wopatsa zinthu zimatiyendera bwino ndipo iye amasangalala nafe.—Aheberi 13:16.

Kodi mukudziwa mmene nkhani ya Alexandra, amene tamutchula kumayambiriro uja, inathera? Munthu wina wa m’basiyo anamuuza kuti wangotaya ndalama zake. Koma munthu amene anamuthandizayo anaimbira anzake amene amakhala mumzinda umene basiyo inaima ndipo anamupatsira ndalamazo kuti abwezere Alexandra. Munthuyo anatsatiranso zimene Alexandra anamuuza ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita miyezi itatu, Alexandra anasangalala kwambiri kukumananso naye pamsonkhano wachitchainizi wa Mboni za Yehova ku Peru. Pothokoza zimene Alexandra anachita, iye anamuitana limodzi ndi anzake kuti akadye kulesitanti yake.

Kupatsa ndiponso kuthandiza ena kumatithandiza kukhala osangalala. Mungasangalale kwambiri ngati pothandiza anthu mumawathandizanso kuti adziwe bwino Yehova Mulungu, yemwe amatipatsa mphatso iliyonse yabwino. (Yakobo 1:17) Nanunso mukhoza kukhala osangalala mukakhala ndi mtima wopatsa.

^ ndime 21 Kuti mudziwe zambiri, werengani buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Likupezekanso pawebusaiti ya www.jw.org/ny. Limapezeka pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU.