Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bizinezi yogulitsa akapolo kuchokera ku Africa kupita ku America inali yandalama zambiri

Akapolo Anapeza Ufulu M’mbuyomu Komanso Masiku Ano

Akapolo Anapeza Ufulu M’mbuyomu Komanso Masiku Ano

Blessing * anapita ku Europe kuti azikagwira ntchito yokonza tsitsi. Koma atangofika anakakamizidwa kugwira ntchito ya uhule. Izi zinachitika pambuyo pomumenya kwa masiku 10 komanso kumuopseza kuti anthu a m’banja lake achitiridwa nkhanza.

Chithunzi cha akapolo a ku Iguputo

Blessing ankafunika kupeza ndalama zokwana mayuro 200 kapena 300 pa tsiku kuti abweze ngongole yokwana mayuro 40,000 imene abwana ake ananena kuti apereke. * Iye anati: “Ndinkafunitsitsa kuthawa koma ndinkaopa kuti achibale anga azunzidwa kwambiri. Ndinkaona kuti palibe chimene ndingachite.” Panopa, zimene zinachitikira Blessing zikuchitikiranso anthu pafupifupi 4 miliyoni padziko lonse.

Zaka pafupifupi 4,000 zapitazo, mnyamata wina dzina lake Yosefe anagulitsidwa ndi azichimwene ake. Iye anakakhala kapolo m’banja lina lotchuka ku Iguputo. Mosiyana ndi Blessing, Yosefe sankazunzidwa ndi abwana ake. Koma atakana kugona ndi mkazi wa abwana akewo, ananamiziridwa kuti ankafuna kumugwirira. Kenako anatsekeredwa m’ndende ndipo ankakhala atamangidwa maunyolo.Genesis 39:1-20; Salimo 105:17, 18.

Yosefe anali kapolo kalekale pomwe Blessing ndi kapolo wamasiku ano. Koma onse awiri anagulitsidwa ndipo bizinezi yogulitsa anthu inayamba kalekale.

NKHONDO INACHITITSA KUTI UKAPOLO UFALIKIRE

Pa nthawi ya nkhondo, anthu ankapeza akapolo mosavuta. Anthu amati mfumu Thutmose 3 ya ku Iguputo inapeza akapolo 90,000 itamenya nkhondo ku Kanani. Akapolowo ankawagwiritsa ntchito ya m’migodi, yomanga akachisi ndiponso yokumba ngalande.

Mu ulamuliro wa Aroma, anthu ankapezanso akapolo ambiri pa nthawi ya nkhondo moti nthawi zina ankangopita  kunkhondo n’cholinga choti akapeze akapolo ena. Anthu amanena kuti pofika m’chaka cha 1 C.E., hafu ya anthu amene ankakhala mumzinda wa Rome anali akapolo. Akapolo a ku Iguputo ndiponso mu ulamuliro wa Aroma ankachitiridwa nkhanza kwambiri. Mwachitsanzo, akapolo ambiri amene ankagwira ntchito m’migodi ya Aroma ankakhala ndi moyo zaka pafupifupi 30 zokha.

Nkhanza zimene akapolo ankachitiridwa sizinasinthe. M’zaka za pakati pa 1500 ndi m’ma 1800, bizinezi yogulitsa akapolo kuchokera ku Africa kupita ku America inali yandalama zambiri. Nthambi ina ya bungwe la United Nations (UNESCO) inanena kuti ‘amuna, akazi ndi ana pakati pa 25 miliyoni ndi 30 miliyoni anagulitsidwa monga akapolo.’ Anthu masauzande ambiri anafa pa nthawi imene ankawawolotsa nyanja ya Atlantic. Munthu wina dzina lake Olaudah Equiano anali kapolo ndipo anapulumuka pa ulendowo. Iye anati: “Zinali zoopsa kwambiri chifukwa munkangokhalira kumva akazi akufuula ndiponso anthu akubuula atatsala pang’ono kumwalira.”

N’zomvetsa chisoni kuti ukapolo ukuchitikabe mpaka pano. Bungwe lina loona zolemba anthu ntchito linanena kuti masiku ano, amuna, akazi ndi ana pafupifupi 21 miliyoni ndi akapolo ndipo amalandira ndalama zochepa kwambiri kapena salandira n’komwe. Iwo amagwira ntchito m’migodi, m’mafakitale, m’nyumba za mahule ndiponso m’nyumba za anthu. Ngakhale kuti malamulo amaletsa zimenezi, ukapolowu ukuwonjezereka kwambiri.

Anthu ambirimbiri adakali mu ukapolo

AKAPOLO ENA ANAPEZA UFULU

Nkhanza zimene akapolo amachitiridwa zinachititsa kuti ambiri ayambe kumenyera ufulu wawo. Chaka cha 1 B.C.E. chisanafike, kapolo wina dzina lake Spartacus anatengana ndi anzake pafupifupi 100,000 kuti aukire ulamuliro wa Aroma koma sizinathandize. M’zaka za m’ma 1700, akapolo akuchilumba cha Hispaniola anayambanso kuukira mabwana awo. Nkhanza zimene akapolowa ankachitiridwa m’minda ya nzimbe zinachititsa kuti payambike nkhondo yapachiweniweni. Nkhondoyi inachitika kwa zaka 13 ndipo inatha mu 1804. Itangotha, anapanga dziko la Haiti n’kumadzilamulira okha.

Aisiraeli amene anali ku Iguputo anapeza ufulu m’njira yodabwitsa. Zikuoneka kuti panali anthu pafupifupi 3 miliyoni amene anamasulidwa ku ukapolowu. Baibulo limanena kuti ku Iguputoko ankawagwiritsa ntchito ya ‘ukapolo wa mtundu uliwonse mwankhanza.’ (Ekisodo 1:11-14) Mfumu ina ya ku Iguputo  inafika polamula kuti ana aamuna onse a Aisiraeli aziphedwa n’cholinga choti mtunduwo usachuluke.Ekisodo 1:8-22.

Zimene zinachitika pa nthawi imene anamasulidwayo zinali zapadera chifukwa choti Mulungu ndi amene anawathandiza. Mulungu anauza Mose kuti: “Ndikudziwa bwino zowawa zawo. Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse.” (Ekisodo 3:7, 8) Mpaka pano, Ayuda amachita mwambo wa Pasika chaka chilichonse pokumbukira zimene zinachitikazo.Ekisodo 12:14.

UKAPOLO UDZATHERATU

Baibulo limati: “Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo,” ndipo limatitsimikizira kuti sanasinthe. (2 Mbiri 19:7; Malaki 3:6) Mulungu anatumiza Yesu kuti ‘akalalikire za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo ndiponso kumasula oponderezedwa kuti akhale mfulu.’ (Luka 4:18) Koma kodi zimenezi zinkatanthauza kuti Yesu adzamasula anthu onse amene ali pa ukapolo weniweni? Zikuoneka kuti ayi. Yesu anatumizidwa kuti akamasule anthu ku uchimo ndi imfa. Komanso pa nthawi ina, iye anati: “Choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Mpaka pano, choonadi chimene Yesu anaphunzitsa chimamasula anthu m’njira zambiri.—Onani bokosi lakuti “ Anamasulidwa ku Ukapolo Wamtundu Wina.”

Komabe Mulungu anathandiza Yosefe ndi Blessing kuti amasuke ku ukapolo. Mukhoza kuwerenga zinthu zodabwitsa zimene zinachitikira Yosefe m’Baibulo pa Genesis chaputala 39 mpaka 41. Zimene zinachitika kuti Blessing achoke ku ukapolo zinalinso zodabwitsa.

Atathamangitsidwa kudziko lina la ku Europe, Blessing anapita ku Spain. Kumeneko, anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Iye ankafunitsitsa kusiya makhalidwe oipa, choncho anapeza ntchito ina. Anagwirizananso ndi abwana ake akale aja kuti atsitse ndalama za ngongole imene ankayenera kulipira mwezi uliwonse ija. Tsiku lina, abwanawo anamuimbira foni n’kumuuza kuti akhululuka ngongoleyo ndipo anamupempha kuti nayenso awakhululukire. Anachita zimenezi chifukwa chakuti nawonso anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Blessing anati: “Choonadi chimatimasula m’njira zodabwitsa kwambiri.”

Yehova Mulungu zinamupweteka kwambiri ataona nkhanza zimene Aisiraeli ankachitiridwa ku Iguputo. Ayenera kuti zimamupwetekanso akaona zopanda chilungamo zimene zikuchitika masiku ano. N’zoona kuti pali zambiri zimene ziyenera kusinthidwa m’dzikoli kuti ukapolo utheretu. Koma Mulungu walonjeza kuti adzachita zimenezi. Baibulo limanena kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”2 Petulo 3:13.

^ ndime 2 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 3 Pa nthawiyo mphamvu ya mayuro inali yofanana ndi ya madola a ku United States.